Chifukwa Chakuti Anapemphera
PA 1 Atesalonika 5:17, 18, mtumwi Paulo adaati: “Pempherani kosaleka; M’zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Kristu Yesu.” Komabe, kodi nthaŵi zina mumazengereza kupereka chiyamiko pamene mukusangalala ndi chakudya m’malo apoyera, onga ngati kantini? Polingalira za chenjezo la Yesu lotsutsa pemphero lodziwonetsera, mwachiwonekere munthu angafune kupeŵa kukokera chisamaliro cha ena mosayenera kwa iyemwini. (Mateyu 6:5, 6) Komabe, pemphero loperekedwa mwanzeru lingakope ena moyanja.
Ichi chinali chokumana nacho cha minisitala wina wachichepere wotumikira pa Beteli ya Brooklyn, malikulu a padziko lonse a Mboni za Yehova. Iye ankafisula pakantini, akumakonzekera kupita kumpingo wake kukakumana ndi kagulu kamene kanali kudzagaŵana m’ntchito yolalikira Ufumu. Pamene chakudya chakufisula chinadza, anapereka pemphero mwanjira yake yanthaŵi zonse. Atatsegula maso, anatukula maso ake ndikuona woperekera wamkazi ali chiriri kumuyang’anitsitsa.
“Ukupemphera eti?” mkaziyo anafunsa. Pamene iye anayankha movomera, mkaziyo anati: “Uyenera kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Makolo anga alinso. Sindinaphatikizidwedi konse m’chipembedzo chawo, koma ndidziŵa kuti ndiyenera kutero. Mwinamwake ndilembetse Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kodi ndingawapeze kwa iwe?”
“Panatsala nenene kuti nditsamwitsidwe ndichakudya,” akukumbukira motero mbale wachichepereyo. Chikhalirechobe, anakhoza kumgaŵira masabuskiripishoni aŵiri ndi magazini atsopano aŵiri ndi kupanga makonzedwe a ulendo wobwerera—zonsezo chifukwa chakuti anapemphera.