Tinalera Ana Asanu ndi Atatu M’chilangizo cha Yehova
MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI OVERLAC MENEZES
“Iwo anafika okwera panjinga ya mipando iŵiri.” Umu ndi mmene Jornal de Resende inayambira lipoti lake la tsamba lathunthu lonena za banja lathu mu 1988, pamene tinkachoka ku Resende kunka ku Lages kumwera kwa Brazil.
LIPOTILO linapitiriza motere: “Mosakaikira, anthu okalamba adzakumbukira okwatirana omwe anachititsa chidwi Resende kupyolera m’choyendera chawo choyambirira ndi chachilendo: njinga yokhala ndi mtanda waukulu ndi mipando iŵiri. Kutsogolo kwake kunali ‘woyendetsa,’ Overlac Menezes; pampando wachiŵiri, panali mkazi wake, Maria José. Chakachi chinali: 1956.”
Mkonzi wankhaniyi anali mwamuna wotchedwa Arisio Maciel, ndipo iye analinso mtsogoleri wa nyumba yawailesi yakumaloko. Iye anakumana nafe choyamba kalekale mu 1956 pamene mkazi wanga ndi ine tinakhalamo ndi phande mu programu ya pawailesi ya mlungu ndi mlungu ya Watch Tower Society, yotchedwa Things People Are Thinking About. Mu nkhaniyo, iye anandigwira mawu kukhala ndikunena kuti m’kukhalapo kwathu “nyumba zonse za mu Resende zinafikiridwa, khwalala ndi khwalala.”
Kodi mungakonde kudziŵa mmene tinakhalira otchuka chotero mu Resende? Ndipo kodi ndimotani, pamene tinali konko, mmene tinathera kulera ana asanu ndi atatu ‘m’chilangizo cha Yehova’ pamene tinkathandiza kuchezera nyumba zonse mu Resende ndi mbiri yabwino Yaufumu?—Aefeso 6:4.
Kuphunzira Njira za Yehova
Mu January 1950, Maria Minc, mmodzi wa Mboni za Yehova, anayamba kuphunzira Baibulo ndi mlongo wanga Adeilde mu São Paulo. Ndinali ndi zaka 16 zakubadwa panthaŵiyo ndipo ndinali wobatizidwa monga Mkatolika, koma sindinapite ku tchalitchi kwa nthaŵi yaitali. Komabe, ndinakhulupirira mwa Mulungu ndipo ndinafuna kumtumikira. Chotero usiku wina, ndinapita kunyumba kwa Adeilde kukafufuza ponena za chipembedzo chatsopano chimene iye ankaphunzira. Maria Minc anandiitanira kugwirizana nawo m’phunzirolo, ndipo ndinaona Baibulo kwanthaŵi yoyamba m’moyo wanga. M’maphunziro otsatira apa ndinazizwitsidwa kuphunzira kuchokera m’Baibulo kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova, kuti posachedwapa dziko lapansi lidzakhala paradaiso, kuti moto wa helo ndi purigatoriyo kulibeko, ndi kuti munthu alibe moyo wosakhoza kufa. Achibale anga anandiuza motere: “Iwe udzapenga ndi kuŵerenga Baibulo kwambiri chotero!”
Ndinapanga kupita patsogolo kwabwino m’phunziro langa la Baibulo ndipo ndinayamba kupezeka pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu ya Mpingo wa Belém mu São Paulo. Poyembekezera kuwona akulu okha okha opezekapo, ndinadabwitsidwa mochititsa chidwi kupeza achichepere ambiri a msinkhu wanga. Pa February 5, 1950, ndinakhalamo ndi phande m’ntchito yolalikira kwa nthaŵi yoyamba, ndipo pa November 4 wa chaka chomwecho, ndinaphiphiritsira kudzipereka kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wam’madzi.
Mwamsanga pambuyo pake ndinaikidwa monga mlankhuli wapoyera. Panthaŵiyo, ichi chinatanthauza kuti ndinapereka nkhani m’makwalala ndi m’mapaki kugwiritsira ntchito chokuzira mawu cholumikizidwa kutsogolo kwa galimoto. Ntchito ina inali ntchito ya magazine. M’masikuwo tinkaimirira m’ngondya zamakwalala ndi zola za magazine, tikumafuula kuti: “Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Yolengeza Ufumu wa Yehova!” Sindinagawire magazine ambiri, koma ndinapeza kulimba mtima kulankhula poyera.
Utumiki wa Nthaŵi Zonse monga Chonulirapo
Chisamaliro changa chinakokedwera mofulumira ku kufunika kwa utumiki waupainiya, kapena ntchito ya kulalikira kwa nthaŵi zonse. Kope la April 1, 1950, la The Watchtower linali ndi mutu wakuti “Apainiya Ambiri a Mbiri Yabwino Akufunika.” Iyi inati: “Kufunafuna Ufumu choyamba kumatanthauza kuti munthu afunikira kukhala ndi zikondwerero za Ufumu kukhala zokulira kwenikweni m’maganizo mwake nthaŵi zonse. Munthuyu akakhala akufunafuna mwaŵi wa kuutumikira, ndipo kusakhala wofunafuna zosoŵa zake zachuma chakuthupi nthaŵi zonse poyamba ndi kupatula zinthu zakudziko kuchilikiza mtsogolo mwake.” Mawuwa anaika mzimu waupainiya mumtima mwanga.
Mwamsanga, msungwana wokongola wachichepere wotchedwa Maria José Precerutti anasintha moyo wanga m’njira yodabwitsa. Iye ankapanga kupita patsogolo kwabwino m’phunziro lake la Baibulo ndi banja la Mboni, José ndi Dília Paschoal. Pa January 2, 1954, iye anakhala mkazi wanga wokondedwa, mnzanga, bwenzi, ndi mthandizi. Nayenso chonulirapo chake, chinali kuchita upainiya. Chotero, polimbikitsidwa ndi zitsanzo za amishonale onga ngati Harry Black, Edmundo Moreira, ndi Richard Mucha, tinafunsira kuloŵa mu utumiki wa upainiya. Tangolingalirani chisangalalo chathu—ndi kudera nkhaŵa—pamene tinalandira yankho ili: “Kuyamikiridwa kwanu kukhala woyang’anira wadera kwavomerezedwa”!
Pamene ndinalandira gawo langa loyamba ladera, ndinali wopanikizidwa. Dera langa latsopanolo linaphatikizapo mipingo khumi mu yomwe panthaŵiyo inali likulu la Brazil, Rio de Janeiro, kuphatikizapo ina yokhala pafupi ndi Beteli. Nyumba ya amishonale a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower inali mu mpingo woyamba womwe ndinagawiridwa kuchezera. Pa msinkhu wa zaka 22 zakubadwa, ndinadzilingalira wopanda kanthu ndipo ndinati kwa Mbale Mucha, panthaŵiyo yemwe anali woyang’anira ntchito mu Brazil: “Kodi anthuwa ndingawaphunzitsenji?” Iye anayankha kuti: “Mbale, tangogwiritsira ntchito uphungu wochokera m’Baibulo ndi gulu.” Uphungu wabwinodi!
Chaka chimodzi pambuyo pake, Maria José anakhala ndi pakati, ndipo tinafunikira kuleka ntchito yadera. Komabe, mwachimwemwe, tinakhalabe mu utumiki wa nthaŵi zonse. Poyankha pempho loperekedwa ndi mabanja a ku Finland aŵiri, a Edvik ndi a Leiniö, Sosaite inatigawira ife ku Resende monga apainiya apadera, gawo latsopano kwenikweni la nzika 35,000. Ndi a Leiniö omwe anatipatsa njinga ya mipando iŵiri yotchulidwa m’nkhani ya mu Jornal de Resende. Poigwiritsira ntchito, tinali okhoza kufesa mbewu zambiri za chowonadi m’gawo lachonde limenelo, ndipo tinapitirizabe kugwira ntchito kumeneko kwa miyezi yambiri pambuyo pa kubadwa kwa mwana wathu wamkazi Alice mu 1956. Pamene tinachoka, alongo aŵiri, Anita Ribeiro ndi Marian Weiler, anabwera kudzathirira mbewuzo ndipo ‘Mulungu anazikulitsa.’ Lerolino, Resende iri ndi mipingo isanu ndi inayi ndipo ili ndi ofalitsa oposa 700.—1 Akorinto 3:7.
Mmodzi wa anthu oyamba omwe ndinakumana nawo mu Resende anali Manoel Queiroz. Pamene ndinkayembekezera basi, ndinagawira mabuku aŵiri kwa iye pomwe ankagwira ntchito. Iye, ndipo pambuyo pake mkazi wake, Piedade, anapanga kupita patsogolo kwabwino ndipo onsewa anabatizidwa. Manoel anakhala mkulu mu mpingo ndipo anapitirizabe kukhulupirika kufikira imfa yake. Ndinaphunziranso ndi Álvaro Soares. Pamsonkhano woyamba umene iye anapezekapo, anadabwitsidwa kuwona anthu asanu ndi mmodzi okha opezekapo, koma lerolino munthuyu ndi woyang’anira wamzinda mu Resende kumene oposa chikwi chimodzi amapezeka pamsonkhano m’mipingo yosiyanasiyana. Mu 1978, Carlos, mwana wamwamuna wa Álvaro anakwatira mwana wathu wamkazi Alice. Lerolino, ziŵalo 60 za banja la a Soares ziri Mboni.
Kuchoka ku Resende kunatanthauza kuti utumiki wathu wanthaŵi zonse unasinthanitsidwa ndi mwaŵi wina Wachikristu, ‘kudzisungira mbumba yathu.’ (1 Timoteo 5:8) Komabe, tinakalamira kusunga mzimu waupainiya, kuupanga utumiki wa nthaŵi zonse kukhala chonulirapo chathu. Ndinapeza ntchito ndi kampani ya mu São Paulo, ndipo m’chaka chimodzi ndinayenda kothera kwa mlungu uliwonse makilomita 300 kunka ku Resende kukathandiza gulu la ofalitsa 15 kumeneko. Kenaka, mu 1960, tinabwerera ku Resende.
Kulera Ana—Mwaŵi Wowonjezereka
Ndithudi ife sitinakonzekere kukhala ndi ana ambiri chotere, komatu anabwera, mmodzi ndi mmodzi. Pambuyo pa kubadwa kwa Alice panadza Léo, kenaka Márcia, Maércio, Plínio, André, ndipo pomalizira, mu 1976, panadza mapasa, Sônia ndi Sofia. Aliyense analandiridwa mwachimwemwe monga ‘cholandira cha kwa [Yehova, NW].’ (Salmo 127:3) Ndipo aliyense analeredwa ‘m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova’ ndi thandizo lake.—Aefeso 6:4.
Komabe, iyi sinali ntchito yopepuka. Nthaŵi zina tinalira chifukwa cha mavuto. Koma chinali chopatsa mphotho. Kodi tinawalera bwanji iwo? Mwaphunziro labanja, mwa kupita nawo kumisonkhano ndi ku uminisitala wakumunda kuchokera pa ubwana wawo, mwakuchitira zinthu pamodzi, mwakutsimikizira kuti iwo anali ndi oyanjana nawo abwino, mwa kuwapatsa uphungu wolimba, ndi mwakukhazikitsa chitsanzo chabwino ife eni.
Zaka zoŵerengeka zapitazo, pa programu ya pa msonkhano mu Cruzeiro, São Paulo, tinafunsidwa ndi woyang’anira wadera. Pambuyo pa kulankhula za phunziro labanja lathu, woyang’anira wadera anandifunsa kuti: “Kodi mkazi wanu anachita mbali yotani mu ichi?” Ndimakumbukira kuti misozi inabwera m’maso mwanga, ndipo ndinatsamwidwa kwakuti sindinathe kuyankha. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ndinayamikiradi thayo labwino koposa limene Maria José anachita m’kusunga banja lathu lateokratiki. Popanda kuchilikiza kwake kokhulupirika, kukanakhala kovutadi!
Kuchokera pa kutomerana kwathu penipeni, Maria José ndi ine tinaphunzirira Baibulo pamodzi. Pamene ana anabwera, chinakhaladi chitokoso kusungabe phunzirolo likupitiriza pa maziko okhazikika. Kuti tithandizire kuchita ichi, mlungu uliwonse pakhomo la firiji ndinkasonyeza nthaŵi yophunzirira mlungu wotsatira ndi zinthu zodzalingaliridwa. Ndinapanganso magawo apadera kutafunika. Mwachitsanzo, tsiku lina Márcia ndi Plínio ankachita ndewu pagome. Chotero tsiku lotsatira, iwo anapeza pafirijipo pali gawo lakuti “Mmene mungakhalire ndi abale anu.” Pa phunziro lotsatira, onse aŵiriwa ananenapo ndipo anathetsa kusemphana kwawoko.
Vuto lina linali pa Sande m’mawa pamene anyamatawo kaŵirikaŵiri anati anadwala kwakuti sangapite mu utumiki wakumunda. Léo ndi Plínio anali akatswiri pa kunamizira kuwawa m’mimba ndi matenda ena kuti apeŵe kupita nafe m’ntchito yolalikira. Nthaŵi zonse nditakaikira kuti kaya anali odwaladi, ndinanena chinachake chonga ichi: ‘Ngati ndinu odwala kwenikweni kwakuti simungapite mu utumiki, pamenepo ndithudi simudzatha kuseŵera mpira wachitanyu pambuyo pake.’ Kaŵirikaŵiri, iwo ankachira msanga.
Nthaŵi zina, ndinafunikira kusamalira mikhalidwe mochenjera. Pamene Léo anali ndi zaka 11, iye anapita kukaseŵera ndi Mboni zinzake, ndipo popanda kutipempha iye anagula kilogramu imodzi ya nyama yankhumba kuti adye. Pambuyo pake, pamene tinalandira unyinji wangongoleyo, Maria José anamfunsa Léo kuti: “Kodi unaiwala kuti unagula nyama yankhumbayi?” “Ayi,” iye anayankha tero mosavutika. “Sindinaigule.” “Eya,” iye anatero, “tiye tipite kukalankhula ndi mwini sitoloyo.” Ali panjira ponka kumeneko, kusokonezeka kwa Léo kunatha. “Tsopano ndakumbukira,” iye anavomereza tero, “ndinalibe ndalama zokwanira, chotero ndinagula pangongole ndipo ndinaiwala kuilipira.” Ndinalipira ndekha ndalamazo ndipo ndinapempha mwiniwakeyo kupatsa Léo ntchito yaganyu, ndi kumulola iye kugwira ntchito kufikira atakhala ndi ndalama zokwanira kundibwezera. Ichi ndicho chinali chilango chake. M’mawa mulimonse pa 4 koloko, Léo ndiye anali woyamba kufika pa ntchito, ndipo m’mwezi umodzi iye anatha kundilipira ndalama yonseyo.
Nyumba yathu nthaŵi zonse inakhala yodzala ndi apainiya, oyang’anira oyendayenda, amishonale, ndi a pa Beteli. Nthaŵi zambiri tinalibe wailesi yakanema m’nyumba, ndipo ichi chinatithandiza kupanga chizoloŵezi cha phunziro labwino ndi mikhalidwe Yachikristu. Munali mumkhalidwewu umene tinalerera ana athuwo. Makalata ena amene iwo anatitumizira pamene anakula anatsimikizira kuti ichi chinagwira ntchito bwino.—Onani bokosi patsamba 30.
Kuchitanso Upainiya!
Pamene ana athu ambiri anakula, ndinakumbukira nkhani ya m’kope la March 1, 1955, la The Watchtower yakuti “Kodi Uminisitala wa Nthaŵi Zonse Ngwanu?” Iyi mwapang’ono inati: “Ena angakhale ndi chikhoterero cha kuwona utumiki wa nthaŵi zonse kukhala wosafunikira kutenga. Koma pakutero amalakwa, pakuti chifukwa cha kuwinda kwa kudzipereka kwake kowona Mkristu aliyense ngwolamulidwa kutumikira kwanthaŵi zonse kusiyapo ngati mikhalidwe yomwe sangathe kuilamulira ichipangitsa kukhala chosatheka.”
Usiku wina ndinapemphera kwa Yehova kutsegula khomo kachiŵirinso kwa ine kuloŵa mu utumiki wanthaŵi zonse. Banja langa linagwirizana nane, ndipo mabwenzi anga anandilimbikitsa. Ndinadabwitsidwa kwakukulu, pamene wotsogolera kampani yomwe ndinagwirako ntchito kwa zaka 26 anandivomereza kugwira ntchito yaganyu kotero kuti ndingatumikire monga mpainiya wokhazikika. Chotero ndinatenga ntchitoyo mwachimwemwe imene ndinaleka kwa zaka zambiri kumbuyoko. Ndipo ana atatu anatsatira chitsanzo changa.
Tinatumikira zaka ziŵiri mu Itatiaia, kumene ndinakhala mkulu kwa zaka 15, ndipo pambuyo pake ndinasankhapo kusamuka kukatumikira kumene kusoŵa kunali kwakukulu. Ichi chinatanthauza kukhalira ndi moyo pandalama zochepa zapenshoni, zofanana pafupifupi ndi nusu ya malipiro abwino. Komabe, podalira m’lonjezo la Yesu la pa Mateyu 6:33, tinalembera Sosaite ponena za makonzedwe athu. Mlungu umodzi pambuyo pake, tinali pafupi kudumpha ndi chisangalalo cha kulandira yankho lawo lakuti: “Chikuwoneka choyenerera kwa ife kulingalira kuti musamukire ku mzinda wa Lages. Mosasamala kanthu za chiŵerengero cha anthu oposa 200,000, uku kuli ofalitsa 100 okha m’mipingo yaing’ono itatu. Inu mudzakhala athandizo lalikulu m’gawo limenelo.”
Tinasamuka mu February 1988. Uku nkumene tidakali, makilomita oposa 1,000 kutali ndi ana ndi mabwenzi athu. Tangotuluka kumene m’chisanu choipa m’zaka 20. Ndine mkulu mmodzi yekha mu mpingo wathu, chotero pali zambiri zochita. Komabe, tadalitsidwadi. Lokondweretsa mwapadera ndi gawo. Titagogoda pazitseko zawo, anthu amati: “Chonde lowani!” Maphunziro a Baibulo ngokhweka kuwayamba. Timalandira zinthu zosiyanasiyana monga zopereka pamene ndalama zisowa, ndipo tabwerapo kunyumba ndi sopo, zonunkhiritsa thupi, maleza, zovala za ana (kaamba ka zidzukulu zathu), ufa, ndiwo zamasamba, zipatso, yogurt, vinyo, ndipo ngakhale ice cream. Nthaŵi ina tinalandira mipando yamatabwa!
Chipatso Chomwe Chimabweretsa Mfupo Yolemera
Lerolino, pa msinkhu wa zaka 56, ndimasangalala nthaŵi zonse nditalingalira banja lathu. Anawa “sanabadwire m’chowonadi.” Iwo anabadwira m’banja Lachikristu, ndipo chowonadi chinafunikira kuloŵetsedwa m’maganizo ndi mitima yawo yaing’onoyo. Omwe anakwatira anatero “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; Deuteronomo 6:6, 7) Zowona, tinapanga zophophonya ndi zolakwa poweruza. Nthaŵi zina tinachita chisalungamo. Pa nthaŵi zina, ndinalephera kukhazikitsa chitsanzo chabwino kapena kunyalanyaza thayo langa monga tate ndi mwamuna. Pamene ndinazindikira chimene ndinachita, ndinapempha chikhululukiro kwa Yehova ndi kwa mkazi wanga kapena kwa ana anga, ndipo ndinakalamira kuwongolera cholakwacho.
Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwathu, banjalo—tsopano lowonjezereka ndi akamwini, apongozi, ndi zidzukulu—liri ndi asanu ndi mmodzi mu uminisitala wa nthaŵi zonse, anayi ndi akulu, ndipo mmodzi ndi mtumiki wotumikira. Onsewa kupatulapo adzukuluwo ngwobatizidwa. Ana atatu aang’ono omwe akali nafebe akukonzekera utumiki wa nthaŵi zonse monga ntchito yawo. Kodi ndi mfupo yaikulu iti imene munthu angayembekezere? Ndiri woyamikira kwa Yehova kaamba ka kutitsogoza kulerera anawa m’chilangizo chake. Tasangalatsidwa kuwawona akutsatirabe ziphunzitso zake. Ndipo ndimapemphera kuti ife, limodzi ndi iwo, sitidzapatuka konse panjira yamoyo.
[Bokosi patsamba 30]
Pamene anakula, ana athu nthaŵi zina anafotokoza chiyamikiro m’makalata cha njira imene tinawalerera. Nazi ndemanga zawo zina:
“Bambo, tsimikizirani kuti inu ndi Amayi munachita zabwino koposa kwa ife, ngakhale ngati munapangapo zophophonya—zimene zimachitika kwambiri tsopano kwa Carlos ndi ine posamalira mnyamata wathu Fabrício.”
Mwana wamkazi Alice, wazaka 33, mayi wa anyamata aŵiri.
“Tiyenera kuvomereza kuti inu munapanga kuyesayesa kogwirizana kutilera m’chilangizo cha Yehova. Ndipo tiri opindula kwambiri motani kuchokera ku icho!”
Mwana wamkazi Márcia, wazaka 27, ndi mwamuna wake, yemwe ali m’ntchito yadera.
“Ndimazindikira kuti mwaŵi umene ndiri nawo tsopano sukadakhala wothekera popanda thandizo lanu limene nonse aŵirinu munandipatsa kukhazikitsa maziko olimba auzimu ndi kukonda Yehova ndi utumiki wake.”
Mwana wamwamuna Maércio, wazaka 23, mpainiya wapadera.
“André, pindula mokwanira ndi kukhala pafupi ndi Bambo ndi zokumana nazo zawo. Usanyalanyaze konse uphungu wawo. Mudzakhala wokhoza kuthandizana. Ndiri wachimwemwe kuposa ndi kale lonse tsopano.”
Mwana wamwamuna Plínio, wazaka 20, ku Beteli.
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Foto: MOURA
[Mawu a Chithunzi patsamba 27]
Foto: CALINO