kodi Kuikidwiratu Kuyenera Kulamulira Moyo Wanu?
PANDANDANDAYO, munthu yekha amene sanakhulupirire choikidwiratu anali Yesu Kristu. Kodi lingaliro lake linali lotani?
Zolembera za mbiri yaumwini za m’zaka za zana loyamba zonena za Yesu (mabuku a Baibulo a Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane) zikusonyeza chikhulupiriro chake kukhala chakuti anthu paokha amayambukira mtsogolo mwawo, kungotanthauza zimene zimawachitikira.
Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti Mulungu “adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye” ndikuti munthu ‘wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.’ Mofananamo, pamene nzika za Yerusalemu zinanyalanyaza machenjezo amene akadapulumutsa miyoyo yawo, Yesu sanapatse mlandu kuikidwiratu kaamba ka zochita zawo. M’malomwake, iye anati: “Inu simunafuna ai.”—Mateyu 7:7-11; 23:37, 38; 24:13.
Tingazindikirenso kulingalira kwa Yesu mwa zimene ananena ponena za ngozi yakupha imene inachitika m’Yerusalemu, akumati: “Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m’Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m’Yerusalemu? Ndinena kwa inu, Iaitu.” (Luka 13:4, 5) Onani kuti Yesu sanati imfa ya amuna 18 amenewo inali yoikidwiratu, ndiponso sananene kuti iwo anafa chifukwa chakuti anali olakwa kwenikweni kuposa ena. M’malomwake, mosiyana ndi Afarisi a m’tsiku lake amene anayesera kugwirizanitsa chikhulupiriro cha kuikidwiratu ndi chiphunzitso cha chosankha chaufulu cha munthu, Yesu anaphunzitsa kuti munthu angayambukire mtsogolo mwake.
Atumwi a Yesu mofananamo anaphunzitsa kuti chipulumutso chiri chosankha chomwe onse angachifikire. Mtumwi Paulo analemba motere: ‘Wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso.’ Ndipo mtumwi Petro anati: ‘Lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nawo kufikira chipulumutso.’ (2 Timoteo 3:15; 1 Petro 2:2; onaninso Machitidwe 10:34, 35; 17:26, 27.) Encyclopædia of Religion and Ethics ya Hastings ikusonyeza kuti olemba a m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu, monga ngati Justin, Origen, ndi Irenaeus, ‘sanadziŵe chirichonse ponena za kulinganizidwiratu kwa kanthaŵi; iwo anaphunzitsa chifuniro chaufulu.’
Koma ngati ambiri chotero, kuphatikizapo Ayuda ambiri owazinga, anakhulupirira mipangidwe ya choikidwiratu, kodi nchifukwa ninji Yesu ndi Akristu oyambirira sanakhulupirire kuti kuikidwiratu kwa munthu nkokhazikitsidwiratu? Chifukwa chimodzi ndicho chakuti lingalirolo ladzazidwa ndi mavuto. Kungotchula aŵiri okha: Choikidwiratu nchosemphana ndi mikhalidwe ya Yehova Mulungu; chimatsutsidwa ndi zigomeko zokhazikitsidwa. Kuwonjezerapo, icho chingaike moyo wanu wapanopo ndi wamtsogolo pangozi. Kusanthula kosamalitsa kudzakusonyezani mmene ichi chiriri tero.
Matanthauzo a Choikidwiratu ndi Mikhalidwe ya Mulungu
Kumbuyoko m’zaka za zana lachitatu B.C.E., wanthanthi Zeno wa ku Citium anaphunzitsa ophunzira ake mu Atene “kuvomereza chiphunzitso cha Kuikidwiratu kukhala chobisika m’njira zina zake.” Komabe, tsiku lina, pambuyo pakuti Zeno anazindikira kuti kapolo wake anali ndi liŵongo lakuba, Zeno anayang’anizana mwachindunji ndi matanthauzo a nthanthi yakeyake. Anatero motani? Pamene iye anapanda mbalayo, kapoloyo anazaza nati: “Koma zinaikidwiratu kuti ndiyenera kuba.”
Kapolo wa Zeno anali ndi nsonga. Ngati inu mumakhulupirira kuti njira ya moyo ya munthu aliyense limagamulidwiratu pasadakhale, pamenepo kupatsa mlandu mbala kuli kofanana ndi kupatsa mlandu mbewu ya malalanje chifukwa chokhala mtengo wa malalanje. Ndiiko nkomwe, munthuyo ndi mbewuyo zonse zimangokula mogwirizana ndi programu. Nangano, kodi tanthauzo lenileni la kulingalira koteroko nlotani?
Eya, ngati apandu amangotsatira choikidwiratu chawo, pamenepo amene anakhazikitsa zochita zawozo ndiye waliŵongo la machitidwe awo. Kodi ameneyo angakhale yani? Malinga ndi kunena kwa akatswiri a kuikidwiratu, ndi Mulungu iyemwini. Mutalingaliranso mosamalitsa pang’ono, mudzapeza kuti Mulungu panopa ayenera kukhala Nakatande Woyambirira wa kuipa konse, chiwawa, ndi kutsendereza komwe kwakhala kukuchitidwa ndi munthu. Kodi mukuvomereza zimenezo?
Nkhani ya mu Nederlands Theologisch Tijdschrift (Magazine Achidutch a Zaumulungu) ikudziŵitsa kuti kulingalira kwa choikidwiratu koteroko “kumapatsa lingaliro la chithunzi cha Mulungu kuti, kwa Akristu okha, ngosafikirika.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti limasemphana ndi chithunzi cha Mulungu choperekedwa ndi olemba Baibulo ouziridwa. Mwachitsanzo, onani malemba ogwidwa mawu awa ochokera m’bukhu louziridwa la Masalmo: ‘Pakuti inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa.’ ‘Moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.’ ‘[Mfumu Yaumesiya yoikidwa ya Mulungu] idzaombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.’ (Salmo 5:4; 11:5; 72:14) Mwachiwonekere, matanthauzo a choikidwiratu ndi mikhalidwe ya Mulungu zimawombana.
Choikidwiratu ndi Nsonga
Koma bwanji ponena za masoka achilengedwe? Kodi iwo samaikidwiratu kuti achitike ndipo chotero kukhala osakhoza kuwasintha?
Kodi nsonga zimatinji? Tamverani zopeza za kufufuza kwa zochititsa masoka achilengedwe, monga momwe zasimbidwira ndi nyuzipepala Yachidutch yakuti NRC Handelsblad: “Kufikira lerolino, zivomezi, zigumula, zigumukire, ndi mphepo za mkuntho . . . zinkalingaliridwa kukhala zochitika zoipa za chilengedwe. Komabe, kulingalira kosamalitsa kukusonyeza kuti kuloŵerera kwa munthu kopambanitsa m’chilengedwe kwayambukira moipa luso la malo otizinga kudzichinjiriza lokha molimbana ndi masoka. Monga chotulukapo, masoka achilengedwe amapha miyoyo yambiri kuposa ndi kale lonse.”—Kanyenye ngwathu.
Zigumula za ku Bangladesh zotchulidwa m’nkhani yapitayo ndizo zinali kulingaliridwa. Asayansi tsopano akunena kuti “kuwonongedwa kwa madera aakulu a nkhalango za ku Nepal, Kumpoto kwa Indiya, ndi Bangladesh kwakhala chochititsa chachikulu m’zigumula zimene zakantha Bangladesh m’zaka zaposachedwapa.” (Magazine a Voice) Lipoti lina likunena kuti kulikha nkhalango kwawonjezera liŵiro la zigumula m’Bangladesh kuchokera pa chigumula chimodzi m’zaka 50 zirizonse kufika ku chimodzi m’zaka 4 zirizonse. Machitidwe ofananawo a kuloŵerera kwa munthu m’mbali zina za dziko anatsogoza ku zotulukapo zatsoka zofananazo—chilala, moto wa m’nkhalango, ndi zigumukire. Inde, zochita za anthu—osati kuikidwiratu kwachinsinsi—kaŵirikaŵiri zimachititsa kapena kukulitsa masoka achilengedwe.
Izi pokhala tero, zochita za munthu ziyeneranso kuchita zosiyana: kunyalanyaza masoka. Kodi mmenemo ndi mmene ziriri? Ndithudi. Tangolingalirani nsonga izi: UNICEF (United Nations Children’s Fund) ikusimba kuti kwa zaka zambiri mazana ambiri a ana mkati mwa Bangladesh anakhala akhungu. Kodi izi zinachititsidwa ndi kuikidwiratu kosasinthika? Kutalitali. Pambuyo pakuti antchito a UNICEF anakhutiritsa amayi kumadyetsa banja lawo osati mpunga wokha komanso zipatso ndi ndiwo zamasamba, matenda a masowo anayamba kutha mphamvu. Kufikira tsopano lino, kusintha kwa kadyedwe kumeneku kwapulumutsa ana mazana ambiri m’Bangladesh ku matenda a khungu.
Mofananamo, anthu amene samasuta amakhala ndi moyo, pa avareji, zaka zitatu kufika ku zinayi motalikirako kuposa amene amasuta. Okwera galimoto amene amavala malamba a mipando yake amakumana ndi ngozi zakupha zochepera kuposa amene samavala. Kunena zowona, zochita zanu—osati kuikidwiratu—nzimene zimayambukira moyo wanu.
Zotulukapo Zoipa za Choikidwiratu
Monga kwatchulidwa, choikidwiratu chingafupikitse moyo wanu. Motani? Pokambitsirana “zitsanzo za choikidwiratu zochititsa mantha kwambiri,” The Encyclopedia of Religion ikulongosola kuti: “Kuchokera pa Nkhondo Yadziko II timadziŵa za kuukira kwakudzipha ndi zida kwa ku Japani ndi kudzipha m’misasa ya SS (Schutzstaffel) mu ulamuliro wa Hitler povomereza ku lingaliro la cholinganizidwiratu (Schicksal) cholingaliridwa kukhala chamtengo kwenikweni kuposa miyoyo ya anthu.” Ndipo posachedwapa kwambiri, akudziŵitsa motero magwero amodzimodziwo, “kuukira kwakudzipha koyambitsidwa ndi chipembedzo pa chandamale cholingaliridwa kukhala chiwopsyezo ku Chisilamu . . . kunakhala pafupifupi chochitika cha tsiku ndi tsiku m’malipoti a nyuzipepala a ku Near East.” Asilikali achichepere zikwi zambiri, akutero malipoti oterowo, anapita ku nkhondo okhutira kuti “ngati sikunalembedwe kuti munthu asafe, iye sadzavutika ndi chivulazo.”
Komabe, ngakhale aphunzitsi olemekezedwa Achisilamu akutsutsa mkhalidwe wosasamala woterowo. Mwachitsanzo, caliph wina anati: “Munthu amene ali pamoto ayenera kugonjera ku chifuniro cha Mulungu; koma munthu amene saali pamoto safunikira kudziponya yekha pamotopo.” Momvetsa chisoni, asilikali ambiri sanachitepo kanthu mogwirizana ndi uphungu wa caliph. Mkati mwa nkhondo ya zaka zisanu ndi zitatu, Iran anavutika ndi imfa 400,000—imfa zochititsidwa ndi nkhondo zambiri kuposa zimene United States inali nazo mu Nkhondo Yadziko II! Mwachiwonekere, choikidwiratu chingafupikitse moyo wanu. Icho chingafikire pa kuika pangozi moyo wanu wa mtsogolo. Motani?
Popeza kuti wokhulupirira kuikidwiratu amakhulupirira kuti mtsogolo ndimosapeŵeka monga mmene kale lirili, iye angakhale ndi chikhotero cha mkhalidwe wovutitsa. Chikhotero chotani? Encyclopedia of Theology ikuyankha kuti: “Munthuyo . . . amadzimva kukhala wopanda thandizo, wopanda pake, mfundo yofutukuka m’zochitika zamayanjano zimene zimawoneka kukhala zosapeŵeka. Ichi chimayambitsa kusakangalika kumene moyamikira kumamatira pa kulongosola kwamalaulo kwakuti chirichonse chimadalira pa chinsinsi ndi pa ulamuliro wa kuikidwiratu.”
Kodi nchiyani chimene chimapanga kusakangalika kukhala kowopsya? Iko kaŵirikaŵiri kumatsogolera ku mkhalidwe wa kugonjetsedwa kopusa. Ichi chingatsekereze wokhulupirira kuikidwiratu ku kupanga kuyesayesa kapena ngakhale kuchitapo kanthu ku chiitano chosangalatsa cha Mulungu ichi: ‘Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi . . . Tcherani khutu lanu, mudze kwa ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo.’ (Yesaya 55:1-3) Ngati kukhulupirira kuikidwiratu kuchilikiza kulephera kwa ‘kudza’ ndi ‘kumvetsera,’ chidzatulukapo kuphonya mwaŵi wa ‘kukhala ndi moyo’ kosatha m’Paradaiso akudzayo wobwezeretsedwa pa dziko lapansi. Ndi mtengo wotani nanga wolipirira!
Chotero kodi muli pati? Ngati munakulira m’mudzi mmene malingaliro a kuikidwiratu ali maziko a kuganiza kwa anthu, mungakhale munavomereza chikhulupirirocho popanda kukaikira. Komabe, zitsutso zofotokozedwa m’nkhani ino zingakhale zakuthandizani kuwona kuti ku mlingo waukulu moyo wanu wa lerolino ndi wa mtsogolo umaumbidwa ndi zochita zanu.
Monga momwe mwawonera, kulingalira, nsonga, ndipo, pamwamba pa zonse, Malemba Opatulika amasonyeza kuti simuyenera kugonjera ku mkhalidwe wa kugonja kwakupha. M’malomwake, monga momwe Yesu anafulumizira kuti: “Vutikirani . . . kuloŵera pa khomo lopapatiza.” (Luka 13:24, The Emphatic Diaglott, kuŵerenga kwa lemba ndi lemba) Kodi iye anatanthauzanji? Akulongosola motere wochitira ndemanga Baibulo wina: “Liwu lakuti [kuvutikira] latengedwa ku maseŵera Achigiriki. M’mipikisano yawo . . . iwo ankakalamira, kapena kuvutikira, kapena kukupanga kuyesayesa ndi mphamvu zawo zonse kuti apeze chipambano.” M’malo mwakugonjera kwanu ku kulakidwa, Yesu anasonkhezera kuti muyenera kukalamira kaamba ka chipambano!
Chotero, chotsani kotheratu kusakangalika kopangitsidwa ndi kuikidwiratu. Loŵani mu mpikisano wa moyo monga mmene Mawu a Mulungu akufulumizira, ndipo musalole choikidwiratu kukuchedwetsani. (Onani 1 Akorinto 9:24-27.) Wonjezerani liŵiro mwakuvomereza mofulumira ku chiitano chouziridwa ichi: “Sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu.” Kodi mungapange motani chosankha chimenecho? Mwa ‘kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kumamatira Iye.’ Kuchita tero kungatsogolere ku chilakiko, popeza kuti Yehova adzatsimikizira kukhala ‘moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.’—Deuteronomo 30:19, 20.
[Chithunzi patsamba 7]
Mose sanalalikire kuikidwiratu koma anafulumiza kuti: “Sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo.”