Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 9/1 tsamba 8-9
  • Chilangizo Chowonjezereka Chotsazika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilangizo Chowonjezereka Chotsazika
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • “Limbani Mtima Ndaligonjetsa Dziko”
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kukonzekeretsa Atumwi Kaamba ka Kuchoka Kwake
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Chilangizo Chotsazikira
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Yesu Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 9/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Chilangizo Chowonjezereka Chotsazika

YESU ndi atumwiwo akukonzekera kuchoka m’chipinda chapamwamba. “Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe,” iye akupitiriza motero. Ndiyeno akupereka chenjezo lochititsa kakasi lakuti: “Adzakutulutsani m’masunagoge; koma ikudza nthaŵi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.”

Atumwiwo mwachiwonekere akuvutitsidwa maganizo kwambiri ndi chenjezo limeneli. Ngakhale kuti Yesu poyamba ananena kuti dziko likawada iwo, sananene kuti iwo akaphedwa. “Izi sindinanena kwa inu kuyambira pachiyambi,” Yesu akufotokoza, “chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.” Komabe, nkwabwino chotani nanga kuwakonzekeretsa pasadakhale ndi mawu ameneŵa asanachoke!

“Koma tsopano,” Yesu akupitiriza, “ndimuka kwa iye wondituma ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa ine, mumka kuti?” Poyamba madzulowo, iwo anafunsa kumene anali kupita, koma tsopano iwo akhwethemuka maganizo kwambiri ndi zimene iye wawauza kotero kuti akulephera kufunsanso ponena za zimenezi. Monga momwe Yesu akunenera: “Koma chifukwa ndalankhula izi ndi inu chisoni chadzala mumtima mwanu.” Atumwiwo ngachisoni osati kokha chifukwa chakuti amva kuti adzavutika ndi chizunzo chowopsa ndikuphedwa komanso chifukwa chakuti Mbuye wawo akuwasiya.

Chotero Yesu akufotokoza kuti: “Kuyenera kwa inu kuti ndichoke ine; pakuti ngati sindichoka, nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.” Yesu angakhale m’malo amodzi okha panthaŵi imodzi, koma pamene ali kumwamba, angatume wothandiza, mzimu woyera wa Mulungu, kwa otsatira ake kulikonse kumene angakhale padziko lapansi. Chotero kuchoka kwa Yesu kudzakhala kopindulitsa.

Mzimu woyera, Yesu akutero, “adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruzo.” Tchimo la dziko, la kulephera kwake kusonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, lidzavumbulidwa. Ndiponso, umboni wokhutiritsa wa chilungamo cha Yesu udzasonyezedwa ndi kukwera kwake kumka kwa Atate wake. Ndipo kulephera kwa Satana ndi dziko lake loipa kuti aswe umphumphu wa Yesu kuli umboni wokhutiritsa wakuti wolamulira wa dziko waweruziridwa ku imfa.

“Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu,” Yesu akupitiriza, “koma simungathe kuzisenza tsopano lino.” Chotero Yesu akulonjeza kuti pamene atsanulira mzimu woyera, umene uli mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito, udzawatsogolera kumvetsetsa zinthu izi mogwirizana ndi luntha lawo lakuzizindikira.

Atumwiwo akulephera kumvetsetsa makamaka kuti Yesu adzafa ndiponso kuwonekera kwa iwo pambuyo pakuutsidwa kwake. Chotero iwo akufunsana: “Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, kanthaŵi ndipo simundiwona; ndiponso kanthaŵi, ndipo mudzandiwona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate?”

Yesu akuzindikira kuti iwo akufuna kumfunsa, chotero akufotokoza kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuula maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.” Masana otsatira, pamene Yesu akuphedwa, atsogoleri achipembedzo akudziko akusangalala, koma ophunzirawo akuchita chisoni. Komabe, chisoni chawo chisandulika chimwemwe, pamene Yesu aukitsidwa! Ndipo chisangalalo chawo chikupitirizabe pamene awapatsa mphamvu pa Pentekoste kukhala mboni zake mwakutsanulira mzimu woyera wa Mulungu pa iwo!

Poyerekezera mkhalidwe wa atumwiwo ndi wa mkazi panthaŵi ya zoŵaŵa zake zakubala, Yesu akuti: “Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthaŵi yake.” Koma monga momwedi iye samakumbukiranso chisautso chake mwana wake atabadwa, Yesu akunena kuti: “Inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuwonaninso [nditaukitsidwa], ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.”

Podzafika nthaŵiyi, atumwiwo sanapemphapo kanthu m’dzina la Yesu. Koma tsopano iye akuti: “Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa. . . . Pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda ine, ndikhulupirira kuti ine ndinatuluka kwa Atate. Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.”

Mawu a Yesu ali chilimbikitso chachikulu kwa atumwiwo. “Mwa ichi tikhulupirira kuti munatuluka kwa Mulungu,” iwo akutero.

“Kodi mukhulupirira tsopano?” Yesu akufunsa. “Onani ikudza nthaŵi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake zayekha, ndipo mudzandisiya ine pandekha.” Muli monse mmene zingawonekere kukhala sosakhulupirika, izi zikuchitika muusikuwo kusanache!

“Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa ine mukakhale nawo mtendere,” Yesu akumaliza motero. “M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.” Yesu analilaka dziko mwakukwaniritsa chifuniro cha Mulungu mokhulupirika mosasamala kanthu za chirichonse chimene Satana ndi dziko lake anayesayesa kuchita kuti aswe umphumphu wake. Yohane 16:1-33; 13:36.

▪ Kodi ndichenjezo la Yesu lotani limene likuvutitsa maganizo atumwi ake?

▪ Kodi nchifukwa ninji atumwiwo alephera kumfunsa Yesu ponena za kumene anali kupita?

▪ Kodi atumwiwo makamaka akulephera kumvetsetsa chiyani?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuchitira fanizo kuti mkhalidwe wa atumwiwo wachisoni udzasandulika chimwemwe?

▪ Kodi Yesu akunena kuti atumwiwo adzachitanji posachedwa?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akulakira dziko?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena