Kodi Nchiyani Chachitikira chibadwa cha Anthu?
“Kodi nchifukwa ninji tiri ndi nkhanza pa ana masiku ano? Kodi nchifukwa ninji tiri ndi nkhanza pa nyama? Kodi nchifukwa ninji tiri ndi chiwawa? . . . Kodi nchifukwa ninji anthu amachita uchigaŵenga? Kodi nchifukwa ninji anthu amagwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa? . . . Kodi chifukwa ninji kuli kwakuti pamene mulinazo zonse zofunika, anthu ena amatembenukira pazinthu zofunikazo, kumene kumadodometsa kutsungula konse?”
MAFUNSOWO anafunsidwa mofuula ndi nduna yaikulu yaboma la Briteni. Mwinamwake inuyo mwafunsa mafunso ofananawo nthaŵi zambiri. Kodi mwapeza mayankho alionse okhutiritsa?
Polingalira zamtsogolo pamafunsowa, nduna yabomayo inati: “Kwa zaka zambiri pamene ndinali m’ndale ndipo wachichepere, ndiri ndi ziyembekezo zanga zonse ndi maloto ndi zikhumbo, kunawonekera kwa ine ndi kwa amsinkhu wanga ambiri kuti ngati tikafikira nthaŵi pamene tikakhala ndi nyumba zabwino, maphunziro abwino, ndi moyo wabwinopo, pamenepo zonse zikakhazikika ndipo tikayenera kukhala ndi mtsogolo mwabwinopo ndimosavuta. Tsopano tikudziŵa kuti siziri choncho. Tikuyang’anizana ndi mavuto enieni a chibadwa cha anthu.”—Kanyenye ngwathu.
Chibadwa cha anthu chingalongosoledwe kukhala “choloŵanecholoŵane wa malingaliro aakulu ndi makhalidwe a anthu.” Mwachiwonekere, malingaliro ndi makhalidwe owombana angabutse mavuto pamlingo wa munthu payekha, mtundu, kapena ngakhale pamitundu yonse. Komabe kodi kwenikweni chibadwa cha anthu chiyenera kupatsidwa mlandu ku ukulu wotani kaamba ka zikhoterero zowopsa zalerolino za chiwawa, uchigaŵenga, kuyendetsa mankhwala ogodomalitsa, ndi zina zotero?
Kodi chibadwa cha anthu ndicho chiyenera kupatsidwa mlandu wonse kaamba ka mikhalidwe imene imawopseza “kudodometsa kutsungula konse”? Kapena kodi pali zochititsa zina zimene tiyenera kuzilingalira kuti tifotokoze chifukwa chimene anthu amagwera mosavuta m’machitachita oluluzika, adyera pamene kuli kwakuti akhoza kulondola mikhalidwe yapamwamba, yolemekezeka? Tiyeni tiwone.