Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 11/15 tsamba 5-7
  • Mmene Mungayang’anizirane ndi Chitokoso Chamakhalidwe a Kukhala Waumphaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungayang’anizirane ndi Chitokoso Chamakhalidwe a Kukhala Waumphaŵi
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwona Mtima​—Kaimidwe ka Baibulo
  • Yankho: Kukhulupirira Mulungu
  • Kudalitsidwa Kaamba ka Kukhulupirira Mulungu
  • Posachedwapa, Sikudzakhalanso Mmphaŵi!
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Kuba kwa wosauka Nkololeka?
    Galamukani!—1997
  • Aumphaŵi Komabe Olemera Zingatheke Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Dziko Lopanda Umphawi Layandikira
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 11/15 tsamba 5-7

Mmene Mungayang’anizirane ndi Chitokoso Chamakhalidwe a Kukhala Waumphaŵi

“ANTHU ngaumphaŵi chifukwa chakuti ngaulesi,” anatero dokotala wina wa ku Afirika. “Mzinda ngwodzala ndi malova. Ngati iwo anafunadi ntchito, akanaipeza. Sipafunikira kukhala munthu aliyense waumphaŵi lerolino.”

Palibe kukaikira kuti anthu ena ngaulesi ndikuti ulesi ungatsogolere kuumphaŵi. Baibulo limati: ‘Tulo tapang’ono, kungowodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, m’kugona, ndipo umphaŵi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.’ (Miyambo 24:33, 34) Komabe, anthu aumphaŵi ambiri sialesi konse. Mwachitsanzo, lingalirani mwamuna amene analemba motere: ‘Kufikira nthaŵi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tiri amaliseche, tikhomedwa, tiribe pokhazikika.’ (1 Akorinto 4:11) Ulova wakufa nawo? Kutalitali. Mawuwo analembedwa ndi mtumwi Paulo. Iye anasankha kukhala ndi moyo wokhala ndi chuma chochepa kotero kuti angalondole bwino uminisitala Wachikristu. Kusauka kwake kwina kunachititsidwanso ndi mikhalidwe yomwe sanathe kuilamulira, monga ngati chizunzo chachipembedzo.

Lerolino, amphaŵi ambiri amdziko ndiwo minkhole ya mikhalidwe yomwe sakhoza kuilamulira​—mwinamwake kusaphunzira, kugwa kwa chuma chakwawoko, kapena kusakhazikika kwa ndale zadziko. Ena amagwira ntchito kuchokera m’mamawa mpaka mochedwa usiku ndipotu nkusabwerako ndi kanthu komwe. Chotero mwaŵi wa kupata chuma kupyolera m’njira zosawona mtima ungawoneke kukhala wokhumbirika, ngakhale woyenerera. Eya, ena angalingalire kuti Baibulo limalungamitsa mkhalidwe wa kupanduka kwapakanthaŵi! Ndiiko komwe, ilo limati: ‘Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala.’ Ndipo munthu wanzeru anapemphera motere: ‘Mundichotsere umphaŵi kuti ndingasauke ndikuba.’​—Miyambo 6:30; 30:8, 9.

Kuwona Mtima​—Kaimidwe ka Baibulo

Kodi malemba a Baibulowa amaperekadi chivomerezo chomveka cha kusawona mtimaku? Eya, tiyeni tiŵasanthule mawu ake apambuyo ndi patsogolo. Pambuyo povomereza kuti anthu sanyoza mbala imene imaba chifukwa cha njala, Miyambo 6:31 ikupitiriza motere: ‘Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kaŵiri; idzapereka chuma chonse cha m’nyumba yake.’ Kufotokoza m’mawu ena, mbala itagwidwa, iyo imayang’anizana ndi mlandu wonse walamulo. Iye amaulipirira upandu wakewo! Chotero, m’malo mwa kulimbikitsa umbala, mawu awa amachenjeza anthu aumphaŵi kuti umbala ungabalenso kutheredwa chuma kowonjezereka, kochititsa chisoni iwo eniwo ndi mabanja awo, ndi kutha kwaulemu wawo.

Koma bwanji ponena za pemphero la munthu wanzeruyo? Iye anapempha kuti asakhale waumphaŵi ndi ‘kukana Mulungu [wake.]’ (Miyambo 30:9) Inde, kusawona mtima kwa munthu yemwe amati amatumikira Yehova kungabweretse chitonzo padzina la Mulungu ndi pampingo wa anthu Ake. Mtumwi Paulo analemba motere: “Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?” Ngati anthu ena omwe anati ndi Akristu anaba, ichi chikapangitsa ‘dzina la Mulungu kuchitidwa mwano pakati pa amitundu.’​—Aroma 2:21, 24.

Chotero, pachifukwa chabwino, Baibulo limati: ‘Waumphaŵi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.’ (Miyambo 28:6) Ngakhale kuti mtumwi Paulo mwini yekhayo analibe zambiri nthaŵi zina, iye sanalekerere kapena kutembenukira ku kusawona mtima. Mmalo mwake, iye analemba motere: ‘Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.’​—Aefeso 4:28.

Yankho: Kukhulupirira Mulungu

Bwanji nanga za anthu amene akugwira ntchito mwakalavula gaga komatu osapeza zokwanira kusamalira mabanja awo? Kodi kusawona mtima kapena ngakhale umbala ungalungamitsidwe kwa iwo, makamaka ngati matenda agwera chiŵalo cha m’banjalo kapena zakugwa mwadzidzidzi zina? Anthu ena amaganiza motero. Nzika ina ya m’dziko la ku Afirika inati: “M’dziko mwathu, utakhala wowona mtima, sungakhale ndi moyo. Ngati ufuna kupulumuka, munthuwe ufunikira kukhalako ndi moyo wokhotakhota pang’ono.”

Komabe, mu Afirika monse anthu kaŵirikaŵiri amawona mawu akuti “Khulupirirani Mulungu” atalembedwa pamagalimoto aakulu, omatikidwa pamakoma, olembedwa m’mapulasitiki ndi kumatikidwa kumbuyo kwamagalimoto. Baibulo lokhalo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” (Miyambo 3:5) Kusawona mtima sikungagwirizane ndi kuchonderera kwa Baibulo. Koma kodi kukhulupirira Mulungu ndikodi yankho lopindulitsa ku chitokoso chamakhalidwe a kukhala waumphaŵi?

Monga mtumiki wa Mulungu, mtumwi Paulo anakumanapo ndi mavuto oterowo onga ‘njala ndi ludzu, m’masautso a chakudya kaŵirikaŵiri, m’chisanu ndi umaliseche.’ (2 Akorinto 11:27) Ndithudi, Paulo ayenera kukhala anadabwa kuti adzapulumuka nazo bwanji! Koma pambuyo pa zaka 25 za zokumana nazo Zachikristu, iye analemba kuti: ‘Ndadziŵa ngakhale kupeputsidwa, ndadziŵanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa. Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.’ (Afilipi 4:12, 13) Inde, Paulo anakhulupirira Mulungu.

Paulo anazindikira kuti malamulo amakhalidwe abwino Amalemba simawu anthano, opanda pake. Iwo ndimalangizo ochokera kwa Mulungu wamoyo wofunitsitsa kuthandiza ndi kuchilikiza ofunafuna kuŵagwiritsira ntchito. Mneneri wakale anati: “Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi iye.”​—2 Mbiri 16:9.

Kudalitsidwa Kaamba ka Kukhulupirira Mulungu

Kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kwa anthu ambiri kukhulupirira Mulungu? Mosakaikira chiri chifukwa chakuti chipembedzo chawo chalephera kuwapatsa chifukwa chokwanira cha kuchitira motero. Matchalitchi achititsa Mulungu kuzindikiridwa kukhala wopanda dzina, chinthu wamba, wosakhala munthu, wosatha kudziŵidwa ndi munthu. Koma kupyolera m’phunziro la Baibulo, Mboni za Yehova zafikira pakumdziŵa Mulungu, osati kukhala chinthu wamba, koma monga Munthu wokhala ndi dzina. (Salmo 83:18; Ahebri 9:24) Iwo aphunzira kuti iye ali nayo mikhalidwe yomupangitsa kukhala woyenerera kuti tim’khulupirire. Mwachitsanzo, mogwirizana ndi Eksodo 34:6, Yehova ndi ‘Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.’ Mboni zimakhulupirira Mulungu ndipo zimazindikira kuti ‘ndi wochuluka m’chowonadi.’ Chotero, iwo ali ndichidaliro chotheratu m’malonjezo ake a kubweretsa dziko latsopano lopanda umphaŵi wofa nawowu umene ukuvutitsa fuko lalikulu la anthu.​—2 Petro 3:13.

Chotero mamiliyoni ambiri a Mboni za Yehova atsimikizira kuti kukhulupirira Mulungu nkopindulitsa. Mwachitsanzo, Rosaline, Mboni yomwe imakhala mu Sierra Leone, amagwira ntchito mwamphamvu kuchokera 5 koloko m’mamawa mpaka usiku kwenikweni kuti adzipezere zakudya ndi zovala ndi ana ake asanu ndi mmodzi. Mkaziyu akuti: “Anthu ambiri amati nkosatheka kukhala wowona mtima, komatu ndimadziŵa kuti ichi sichowona. Nthaŵi zina ndimakhala nawo mavuto ndipo sindimadziŵa mmene adzathetsedwera. Koma ndimadziŵa kuti nditakhala wowona mtima, zinthu zonse zidzakhala zabwino kwa ine. Chotero ndimayesa zolimba kupeŵa kusamkondweretsa Yehova.”

Wolemba nkhani wina anati: “Munthu waumphaŵi wanjala amafunikira chiyembekezo . . . kuposa mkate.” Inde, kupanda chiyembekezo, kuthedwa nzeru, ndi kupanda chimwemwe kokhalirira ndizo matenda amene angakhale oŵaŵa kwambiri kuposa njala. Koma munthu wodziŵa ndi kukhulupirira Mulungu safunikira kuthedwa nzeru. “Ndimagwira ntchito zolimba tsopano,” akuwonjezera tero Rosaline, “koma ndiri ndi chisangalalo chifukwa chakuti ndimadziŵa kuti ikudza nthaŵi pamene sindidzafunikira kuvutika mwanjirayi. Nthaŵi ino ndimagwira ntchito kuti ndidzipezere zakudya mwinine ndi banja langa, koma m’dziko latsopano la Yehova, mudzakhala zakudya zamwana alilenji. Chotero ndiri nacho tsopano chiyembekezo ndi chisangalalo chimene ndinalibe ndisanadziŵe Yehova.”​—Yerekezerani ndi Yesaya 25:6; Chibvumbulutso 21:3, 4.

Zowonadi, okhulupirira Mulungu angakumanebe ndi kutsendereza kwachuma, monga mmene anachitira mtumwi Paulo. Koma iwo samafunikira kutembenukira kukuswa malamulo a Mulungu ndicholinga chakuti apulumuke m’zandalama. Wamasalmo Davide anati: ‘Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.’ (Salmo 37:25) Inde, Mulungu amasamala ndikudalitsa omwe amaika zikondwerero zake choyamba m’miyoyo yawo.​—Mateyu 6:25-33.

Chotero ngati ndinu mphaŵi, ‘musaleme pakuchita zabwino.’ (2 Atesalonika 3:13) Musatembenukire konse kukupotoza makhalidwe abwino. Pangani unansi ndi Mulungu ndikudalira pa iye kukuthandizani kuchita ndi mavuto ndi zotopetsa za moyo. Awo amene amatumikira Yehova ndikumkhulupirira kotheratu akuchondereredwa motere: ‘Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa iye nkhawa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.’​—1 Petro 5:6, 7.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

“Munthu waumphaŵi wanjala amafunikira chiyembekezo . . . kuposa mkate”

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova zimathandiza anthu kukhulupirira Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena