Kalamirani Kufikira Chonulirapocho!
Mfundo Zazikulu Kuchokera mu Afilipi
MTUMWI Paulo anafuna kuti Akristu a ku Filipi apitirizebe kukalamira kufikira chonulirapo cha mphotho ya moyo wosatha. Chotero, anaŵalembera iwo pafupifupi 60 kapena 61 C.E., mkati mwa kuikidwa m’ndende kwake koyamba m’Roma. Kalata yake inatumizidwa ku mpingo umene iye anaukhazikitsa zaka khumi kuchiyambiyambi mu Filipi, mzinda woyambitsidwa ndi Philip wa ku Macedon (atate wa Alexander Wamkulu). Pofika zaka za zana loyamba C.E., uwo unakhala ‘mudzi wa ku Makedoniya, waukulu wa m’dzikomo,’ womwe tsopano uli mbali yakumpoto ya Girisi ndi kum’mwera kwa Yugoslavia.—Machitidwe 16:11, 12.
Akhulupiriri a ku Filipi adali osauka koma ooloŵa manja. Mobwerezabwereza, iwo anatumiza chinachake kukakwaniritsa zosoŵa za Paulo. (Afilipi 4:14-17) Koma kalata yake siinali kokha kalata yothokoza. Iyo inaperekanso chilimbikitso, kusonyeza chikondi, ndikupereka uphungu.
Mikhalidwe Yachikristu Njowonekera
Kalata ya Paulo inayamba ndi umboni wa chikondi chake kaamba ka akhulupiriri a ku Filipi. (1:1-30) Iye anathokoza Yehova chifukwa cha zopereka zawo zopititsira patsogolo mbiri yabwino ndikupemphera kuti chikondi chawo chichuluke. Paulo anali wosangalala kuti kuikidwa m’ndende kwake kunaŵapangitsa iwo kusonyeza ‘kulimbika mtima koposa kulankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.’ Iye analakalaka kukhala ndi Kristu koma analingalira kuti angawatumikirebe. Paulo anafunanso kuti iwo apitirizebe ‘kugwirira pamodzi . . . chikhulupiriro cha uthenga wabwino.’
Potsatira panadza uphungu wa khalidwe ndi mayendedwe. (2:1-30) Afilipi analimbikitsidwa kusonyeza chikondwerero chaumwini mwa ena ndikusonyeza kudzichepetsa kofanana ndi kwa Kristu. Iwo ‘ankawala monga mauniko a dziko lapansi’ ndipo anasonkhezeredwa ‘kugwira zolimba mawu a moyo.’ Paulo ankayembekezera kutumiza Timoteo kwa iwo ndipo adali ndichidaliro kuti iyemwini akabwera posachedwa. Pofuna kuwatsimikizira za Epafrodito, yemwe adadwala kwambiri, Paulo ankawatumizira mtumiki wokhulupirikayu.
Pitirizani Kukalamira Kufikira Chonulirapocho
Kenaka mtumwiyo anawasonyeza Afilipi kumene angaike chidaliro chawo pamene akupitiriza kukalamira kufikira chonulirapocho. (3:1-21) Chiyenera kuikidwa mwa Yesu Kristu, osati m’thupi kapena m’mdulidwe monga mmene ena ankachitira. Paulo analingalira ziyeneretso zake zakuthupi kukhala zapadzala chifukwa cha ‘mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu.’ Mtumwiyo anali ‘kulondola kufikira chonulirapo cha mphotho ya chiitano cha kumwamba cha Mulungu mwa njira ya Kristu Yesu’ ndipo analimbikitsa Afilipi kukhala amaganizo omwewo.
Kugwiritsira ntchito uphungu womalizira wa Paulo kukathandiza Afilipi kuyang’anira chonulirapo ndi mphotho. (4:1-23) Iye anawafulumiza iwo kupereka nkhaŵa zawo kwa Mulungu m’pemphero ndikudzaza maganizo awo ndi zinthu zabwino. Paulo anaŵayamikiranso chifukwa cha kuoloŵa manja kwawo ndikumaliza ndi moni ndichikhumbo chakuti chisomo cha Ambuye Yesu Kristu chikhale ndi mzimu umene anausonyeza.
Kalata ya Paulo kwa Afilipi imachilikiza kuoloŵa manja, chikondi, ndi kudzichepetsa. Imalimbikitsa chidaliro mwa Kristu ndipemphero la mtima wonse kwa Mulungu. Ndipo mawu a Paulo amathandizadi Mboni za Yehova kupitiriza kukalamira kufikira chonulirapo cha mphotho ya moyo wosatha.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]
Kufikira Chonulirapocho: “Kuiwala zinthu za pambuyo ndi kumatansira patsogolo ku zinthu za patsogolo,” analemba motero Paulo, “Ine ndiri kumalondola kufikira ku chonulirapo cha mphotho ya chiitano cha kumwamba cha Mulungu mwa njira ya Kristu Yesu.” (Afilipi 3:13, 14, NW) Mtumwiyo ankayesetsa mofanana ndi munthu amene ali pampikisano. Iye sanataye nthaŵi ndi kuyesayesa kuyang’ana m’mbuyo koma anakalamira kufikira chonulirapo chake—mofanana ndi wothamanga amene amatansira kudutsa mzera wothera liŵiro. Kwa Paulo ndi Akristu ena odzozedwa, mphothoyo inali moyo wakumwamba mwa chiukiriro pambuyo pakumaliza moyo wawo wokhulupirika kwa Mulungu wapadziko lapansi. Kaya ziyembekezo zathu nzakumwamba kapena padziko lapansi, tiyeni tisungebe umphumphu wathu kwa Yehova ndikukalamira kufikira chonulirapocho monga Mboni zake.—2 Timoteo 4:7.