Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 12/1 tsamba 21
  • Kulalikira Mbiri Yabwino ‘Kumalekezero Ake a Dziko’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira Mbiri Yabwino ‘Kumalekezero Ake a Dziko’
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • M’nkhalango ya Amazon Muli Zamoyo Zambiri
    Galamukani!—2010
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 12/1 tsamba 21

Ripoti la Olengeza Ufumu

Kulalikira Mbiri Yabwino ‘Kumalekezero Ake a Dziko’

“NDIPO mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Anatero Yesu kwa ophunzira ake nthaŵi pang’ono asanafe. Mwamsanga pambuyo pa chiukiriro chake, iye ananenanso kuti: ‘Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.’ (Mateyu 24:14, NW; Machitidwe 1:8) Lerolino, maulosi ameneŵa akukwaniritsidwa m’maiko oposa 200, kuphatikizapo dziko la Peru, Kum’mwera kwa Amereka.

Mboni zoposa 32,000 zikulalikira mbiri yabwino m’dziko lokongola limenelo, ndipo gawo lawo limaphatikizapodi ena a malekezero ake a dziko: mapiri aatali a Andes, omafika utali wa pakati pa mamita 4,000 ndi 4,500, ndiponso nkhalango yotentha ya Amazon, kumene anthu angafikiridwe kokha ndi mabwato. Nthambi ya Peru ikusimba motere:

◻ “M’madera ankhalango, tagaŵira apainiya apadera asanu ndi atatu ku mabwato aŵiri aang’ono otchedwa lanchas. Mabwato aang’ono ameneŵa amayandama pamadzi mwakuya mamita 0.3 okha, choncho chakhala chotheka kufutukulira kulalikira kwa mbiri yabwino kumadera ambiri atsopano pamitsinje yaing’onoyo. Pakali pano, abale amene akugwiritsira ntchito mabwato ameneŵa agawira magazini, mabuku, ndi Mabaibulo mazana zikwi zambiri m’Chigwa cha Amazon cha ku Peru. Monga chotulukapo chachindunji, mipingo inayi yatsopano yakhazikitsidwa, limodzinso ndi magulu akutali asanu amene amachitira lipoti ntchito ndikuchita misonkhano. Kukuyembekezeredwa kuti magulu ameneŵa adzakhala mipingo posachedwapa.”

◻ Tauni ina ya m’nkhalango inakula pafupi ndi malo opopera a paipi yamafuta ya Trans-Andes, imene imanyamula mafuta kuchokera m’nkhalango yonseyo kunka ku mapiri a Andes aitaliwo mpaka kugombe lakumadzulo. Chifukwa cha anthu ogwira ntchito papaipi yamafutayo, tauni imeneyi idali ndi mabawa 20 ndipo inadziŵika kukhala malo omwera mowa ndikusangalala. Komabe, pambuyo pakuti apainiya apaderawo anapereka umboni wokwanira, ambiri anavomereza uthenga Waufumu, ndipo tsopano m’taunimo mwatsala mabawa anayi okha! Mkati mwa kuchezera kwaposachedwapa kwa woyang’anira dera, anthu 189 anabwera ku nkhani yapoyera. M’taunimo tsopano muli gulu la ofalitsa 7, ndipo anthu oposa 45 amapezeka pamisonkhano yonse. Posachedwapa, ndi dalitso la Yehova, lidzakhala mpingo.

◻ Mu umodzi wa mipingo 221 ya mu Lima, mzinda waukulu wa Peru, mwamuna wa zaka 29 zakubadwa akusimba mmene anapezera chowonadi. Pokhala ataleka sukulu pa msinkhu wa zaka 13, iye anagwirizana ndi gulu la anyamata ovutitsa nayamba ntchito yomenyana, kumwa mankhwala ogodomalitsa, ndikuchita chisembwere. Pambuyo pa zaka ziŵiri za utumiki wankhondo wokakamiza, iye anayamba kukhala ndi mavuto amaganizo. Kenaka, mu 1983, mlongo wodzichepetsa, wosadzikweza anakumana naye muuminisitala wake wa kunyumba ndi nyumba. Kwa nthaŵi yoyamba, iye anamva za dziko latsopano lachikondi ndi mtendere. Phunziro Labaibulo linayambidwa, ndipo ndithandizo lachikondi kuchokera ku mpingo ndi nyonga ya Yehova, iye anakhoza kulaka mikhalidwe yake yoipa. Mu 1986 anabatizidwa ndipo tsopano akutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo.

Zowonadi, mawu a Yesu akuti Ufumu udzalalikidwa ‘kumalekezero ake a dziko’ akukwaniritsidwa m’Peru ndi zotulukapo zozizwitsa, kupindulitsa anthu ambiri m’dzikolo amene ali ndi njala ndi ludzu la chowonadi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena