Kodi Mumalidziŵa Bwino Motani Baibulo?
‘Bukhu la Tomasi? Ndithudi, limenelo lirimo m’Baibulo. Koma bukhu la Yona mulibemo. Kumene anabadwira Kristu? Oo, kumeneko ndi ku Yerusalemu—kapena kodi kunali ku Nazarete? Sindiri wotsimikiza kwenikweni kaya ngati bukhu la Yesaya liri m’mbali yoyamba kapena yachiŵiri ya Baibulo. Chiŵerengero cha atumwi? Sindikudziŵa kwenikweni.’
“ZOPEZEDWA zimenezi sizikanakhala zodabwitsa ngati zidasonkhanitsidwa kuchokera pakati pa anthu osakhala Akristu okha,” akutero magazini a Christianity Today. “Chodabwitsa—ndiponso chovutitsa maganizo—ndicho kuchuluka kwa umbuli Wamalemba kopezeka pakati pa Akristu obadwanso.”
Mwachitsanzo, 22 peresenti ya Akristu wamba ofufuzidwawo analingalira kuti liripodi bukhu la Tomasi m’Baibulo, pamene 13 peresenti sanali otsimikiza. Ponena za Yona, 27 peresenti ananena kuti mulibemo m’Baibulo, ndipo 12 peresenti sanadziŵe chirichonse. Maperesenti asanu ndi imodzi sanathe konse kulota kumene Kristu anabadwira, pamene 16 peresenti anatchula Yerusalemu, ndipo 8 peresenti anati kunali ku Nazarete. Anthu okwanira 13 peresenti yathunthu sanadziŵe konse kumene bukhu la Yesaya lingapezeke m’Baibulo, pamene 11 peresenti analiika m’Malemba Achikristu Achigiriki (“Chipangano Chatsopano”). Ndipo pamene kuli kwakuti ambiri anadziŵa kuti panali atumwi 12, 12 peresenti anapereka ziŵerengero zina, kuchokera pa 2 kufika ku oposa 20, ndipo 10 peresenti sanadziŵe kalikonse.
Funso limene linapereka vuto lalikulu linali lakuti kaya mawu akuti “Mulungu amathandiza anthu odzithandiza okha” anali m’Baibulo kapena ayi. Kokha 38 peresenti ya “Akristu” ofufuzidwawo anadziŵa kuti sakanapezeka kulikonse m’Baibulo, pamene chiŵerengero chachikulu ndithu, 42 peresenti, analingalira kuti anali mawu ogwidwa kuchokera m’Baibulo. Otsalawo sanadziŵe.
“Kodi nchifukwa ninji pali umbuli wochuluka chotero ponena za Baibulo?” ikufunsa motero Christianity Today. “Mwachidziŵikire kwenikweni, zikuchitika chifukwa cha kusaŵerenga Baibulo. Theka la nzika za ku Amereka zonse silimaŵerenga Baibulo. Unyinji wa Akristu onse obadwanso amaŵerenga Baibulo kamodzi kapena kaŵiri pamlungu, kapena osaliŵerenga konse. Nzosadabwitsa kuti Akristu ambiri amadziŵa zochepa ponena za Malemba!”