Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/1 tsamba 15-19
  • Lemekezani Mwanayo, Mtsogoleri Wamkulu wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lemekezani Mwanayo, Mtsogoleri Wamkulu wa Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Zina Zomwe Ena Amanyozera Nazo Yesu
  • Zifukwa Zolemekezera Mwanayo
  • Zomwe Watichitira
  • Mmene Tingamlemekezere Mwanayo
  • Lemekezani Yehova—Chifukwa Ninji Ndipo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chitirani Ulemu Anthu Onse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chitirani Ena Ulemu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Tizipereka Ulemu kwa Oyenera Kulemekezedwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/1 tsamba 15-19

Lemekezani Mwanayo, Mtsogoleri Wamkulu wa Yehova

“Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.”​—YOHANE 5:23.

1. Kodi chikhulupiriro cha Chikristu Chadziko cha Utatu chimamunyoza bwanji Yesu?

LEROLINO anthu ambiri m’Chikristu Chadziko amati amalemekeza Yesu Kristu, komabe amachita zosiyana. Motani? Eya, anthu ambiri amati Yesu ndiye Mulungu Wamphamvuyonse, ndikuti Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse, anabwera padziko lapansi nakhala ndi moyo nafa monga munthu. Kunenaku kumapezeka m’chiphunzitso cha Utatu, chomwe ndicho chiphunzitso chachikulu cha Chikristu Chadziko. Koma ngati Utatu ngwabodza, ngati Yesu kwenikweni, ngwamng’ono ndipo wochepa kwa Mulungu, kodi kuwuika molakwa unansi wake ndi Mulungu kumeneku sikukapangitsa Yesu kusakhala wachimwemwe? Ndithudi, iye akalingalira kumuimira molakwika koteroko kukhala komnyoza iye limodzi ndi zonse zimene anaziphunzitsa.

2. Kodi Malemba amasonyeza momvekera motani kuti Yesu ngwamng’ono kwa Mulungu ndi wochepa kwa iye?

2 Chowonadi nchakuti, Yesu sananenepo kuti ndi Mulungu, koma anadzisonya mobwerezabwereza kukhala “Mwana wa Mulungu.” Ngakhale adani ake anachivomereza chimenechi. (Yohane 10:36; 19:7) Yesu nthaŵi zonse anali wodera nkhaŵa kukweza Atate ndikudzichepetsa mwiniyekha kwa Iye, monga momwe anavomerezera motere: ‘Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo. Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha . . . chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.’ Iye anabwerezanso, nati: ‘Chifukwa ndiri wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu.’ Iye anatinso: ‘Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu.’ (Yohane 5:19, 30; 7:28, 29; 8:42) Yesu sanalingalirepo kuti anali Mulungu kapena kuti anafanana naye. Chotero kuphunzitsa chinthu choterocho kumamunyoza Yesu.

Njira Zina Zomwe Ena Amanyozera Nazo Yesu

3. (a) Kodi ena m’Chikristu Chadziko amamnyoza Yesu mwa kukana chiyani? (b) Kodi ndiumboni wotani umene Yesu anaupereka ponena za kukhalapo kwake asanakhale munthu?

3 Modabwitsa, palinso ena m’Chikristu Chadziko lerolino amene amanyoza Yesu mwa kukana kuti iye sanakhaleko asanakhale munthu. Komabe, pokhapo titavomereza kuti Yesu anadzadi pansi pano kuchokera kumwamba mpomwe tingayambe kumlemekeza molondola. Yesu mwini mobwerezabwereza anati anakhalako asanakhale munthu. Iye anati: ‘Kulibe munthu anakwera kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.’ Pambuyo pake anati: ‘Mkate wamoyo wotsika kumwamba Ndine amene. . . . Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?’ Ndipo anatinso: ‘Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera kumwamba. . . . Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndiripo.’ (Yohane 3:13; 6:51, 62; 8:23, 58) Yesu anasonyanso kukukhalapo kwake asanakhale munthu m’pemphero lake kwa Atate wake wakumwamba pausiku wa kuperekedwa kwake.​—Yohane 17:5.

4. (a) Kodi anthu ambiri amamnyoza Yesu m’njira ina yowonjezereka iti? (b) Kodi ndiumboni wotani umene uyenera kukhala wokwanira kutsimikizira kuti Yesu anakhalakodi ndi moyo, ndipo nchifukwa ninji?

4 Ena m’Chikristu Chadziko amapitadi patali mwa kukana kuti Yesu sanali munthu wam’mbiri, nati sanakhalepo ndi moyo monga munthu. Ngati iye sanakhalepo ndi moyo, sipakafunikira kukambirana chifukwa ndi mmene tiyenera kumlemekezera. Komabe mboni zowona ndi maso zochuluka zosungidwa m’Malemba ziyenera kukhala umboni wokwanira kuvomereza mosakaikira kuti Yesu anakhalakodi ndi moyo padziko lapansi. (Yohane 21:25) Ichi chiri mwachiwonekere chowona popeza kuti Akristu oyambirira anaphunzitsa kaŵirikaŵiri ponena za Yesu mwakuika pangozi moyo ndi ufulu wawo weniweniwo. (Machitidwe 12:1-4; Chibvumbulutso 1:9) Komabe, pambali pa zimene ophunzira ake analemba ponena za iye, kodi kukhalapo kwa Yesu kungasonyezedwe?

5, 6. Kodi nchiyani chimene umboni wam’mbiri, kusatchula Malemba, umasonyeza ponena za kukhalako kwenikweni kwa Yesu Kristu?

5 The New Encyclopædia Britannica (1987) ikuti: “Mbiri yolembedwa apa ndi apo imatsimikizira kuti m’masiku amakedzana ngakhale adani a Chikristu sanaikaikire konse mbiri ya Yesu.” Kodi zina za mbiri zolembedwazi ndizo ziti? Mogwirizana ndi katswiri Wachiyuda Joseph Klausner, pali umboni wa zolembera zoyambirira za Talmud. (Jesus of Nazareth, tsamba 20) Palinso umboni wa katswiri wa mbiri yakale Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba wotchedwa Josephus. Mwachitsanzo, iye akufotokoza kuponyedwa miyala kwa Yakobo, namutchula kukhala “mbale wa Yesu amene anatchedwa Kristu.”​—Jewish Antiquities, XX, [ix, 1].

6 Kuwonjezera apa, palinso umboni woyambirira wa akatswiri a mbiri yakale Achiroma, makamaka wa Tacitus wotchuka. Iye analemba kuchiyambiyambi m’zaka za zana lachiŵiri ponena za “gulu lodedwa kaamba ka zoipa zawo, lotchedwa Akristu motchuka. Christus [Kristu], komwe dzinalo [Chikristu] linachokera, anavutika ndi chilango choipitsitsa m’kulamulira kwa Tiberiyo m’manja mwa mmodzi wa olamulira athu.” (The Annals, XV, XLIV) Kulingalira umboni wakuti Yesu anali munthu wa m’mbiri kukhala wokhutiritsa, katswiri wotchuka wanthanthi Wachifrench wa m’zaka za zana la 18, Jean-Jacques Rousseau, anachitira umboni motere: “Mbiri ya Socrates, imene palibe munthu angathe kuikaikira, njosatsimikiziridwa bwino monga mmene iliri ya Yesu Kristu.”

Zifukwa Zolemekezera Mwanayo

7. (a) Kodi ndiumboni wa Malemba uti umene umatilamula kulemekeza Yesu Kristu? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova walemekezeranso Mwana wake?

7 Tsopano tafika pachifukwa cholemekezera Yesu Kristu. Mfundo yakuti atsatiri ake akulamulidwa kumlemekeza ingawonedwe m’mawu ake opezeka pa Yohane 5:22, 23 awa: ‘Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana; kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.’ Kuyambira pa kuukitsidwa kwa Kristu, Yehova walemekeza Mwana wake kumlingo wokuliradi, ‘namveka korona waulemerero ndi ulemu chifukwa cha kulawa imfa.’ (Ahebri 2:9; 1 Petro 3:22) Kwakukulukulu, tiri nazo zifukwa za kulemekezera Yesu ponse paŵiri chifukwa cha munthu amene iye ali ndi chifukwa cha zimene wachita.

8. Kodi ndi kaamba ka mfundo zapadera ziti zonena za Yesu Kristu zimene iye akuyenerera ulemu?

8 Yesu Kristu amayenerera kulemekezedwa chifukwa chakuti iye, monga Logosi, kapena Mawu, ngwolankhulira wa Yehova wabwino koposa. Kuchokera m’Malemba nkwachiwonekere kuti dzina laulemulakuti ‘Mawu’ limaloza kwa Yesu asanadze padziko lapansi limodzinso ndi pambuyo pa kukwera kwake kumwamba. (Yohane 1:1; Chibvumbulutso 19:13) Pa Chibvumbulutso 3:14 iye akulankhula za iyemwini kukhala ‘woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.’ Iye sali kokha ‘woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse’ koma monga “Mwana wobadwa yekha” ndiyekhayo amene analengedwa mwachindunji ndi Yehova Mulungu. (Akolose 1:15; Yohane 3:16) Kuwonjezerapo, ‘zonse zinalengedwa kupyolera mwa iye, ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.’ (Yohane 1:3) Chotero, pamene tiŵerenga pa Genesis 1:26 kuti Mulungu anati, ‘Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu,’ ‘ti’ ameneyo akuphatikizapo Logosi, kapena Mawu. Motsimikizirika, chenicheni chakuti Yesu m’kukhalapo kwake asanakhale munthu adali ndi mwaŵi wodabwitsa wa kukhalamo ndi phande ndi Yehova Mulungu polenga chimampangitsa kukhala woyenerera ulemu waukulu.

9. Kodi nchifukwa ninji tikutsimikizira kuti Yesu ndiye Mikayeli mngelo wamkulu, ndipo kodi ndimotani mmene Mikayeli analemekezera Yehova m’chigwirizano ndi thupi la Mose?

9 Yesu Kristu amayenereranso ulemu chifukwa chakuti ndimkulu wa angelo a Yehova, kapena mngelo wamkulu. Kodi chitsimikizochi tachifikira motani? Eya, liwu lapatsogololo lakuti “wamkulu,” kutanthauza “mfumu” kapena “kalonga,” likusonyeza kuti pali mngelo wamkulu mmodzi yekha. Mawu a Mulungu amalankhula za iye pamene asonya kwa Ambuye Yesu Kristu woukitsidwayo. Tikuŵerenga motere: ‘Ambuye adzatsika kumwamba mwiniyekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Kristu adzayamba kuuka.’ (1 Atesalonika 4:16) Mngelo wamkuluyu ali ndidzina, monga momwe tikuŵerengera pa Yuda 9 kuti: ‘Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi Mdyerekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Yehova akudzudzule.’ Mwakusatsogolera Yehova kuyesa kudzetsera Mdyerekezi chiweruzo, Yesu mwakuteroko analemekeza Atate wake wakumwamba.

10. (a) Kodi ndimotani mmene Mikayeli amatsogolera m’kumenyera nkhondo Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi Mikayeli anasamalira thayo lotani m’chigwirizano ndi mtundu wa Israyeli?

10 Mikayeli mngelo wamkulu amamenyera nkhondo Ufumu wa Mulungu, akumatsogolera kuyeretsa kumwamba mwakuchotsako Satana ndi makamu a ziŵanda zake. (Chibvumbulutso 12:7-10) Ndipo mneneri Danieli anati iye ‘akutumikira ana a Mulungu.’ (Danieli 12:1, NW) Chotero, zikumveka ngati kuti Mikayeli ndiye adali ‘mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israyeli’ ndikuti ndiye anagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kuloŵetsa anthu ake m’Dziko Lolonjezedwa. Mulungu analamulira kuti: ‘Musamalire iye, ndi kumvera mawu ake; musamwawitsa mtima . . . popeza dzina langa liri m’mtima mwake.’ (Eksodo 14:19; 23:20, 21) Mosakaikira mngelo wamkulu wa Yehova ayenera kukhala anali wodera nkhaŵa kwambiri ndi anthu a dzina lenileni la Mulungu. Moyenerera kwenikweni ndiye anathandizira mngelo wina amene anatumizidwa kukatonthoza mneneri Danieli, komano anatsekerezedwa njira ndi chiŵanda champhamvu. (Danieli 10:13) Chotero kungakhale kwanzeru kutsimikizira kuti mngelo amene anawononga asilikali ankhondo a Sanakeribu okwanira 185,000 sanalinso wina koma Mikayeli mngelo wamkulu.​—Yesaya 37:36.

11. Kodi Yesu akuyenerera kulemekezedwa kaamba ka kukhala atalondola njira yotani ya moyo padziko lapansi?

11 Yesu Kristu samayenerera kulemekezedwa kokha kaamba ka chimene iye ali koma iye amayenereranso kuti timchitire ulemu chifukwa cha zimene wachita. Mwachitsanzo, ndimunthu yekha amene anakhala nawo moyo wangwiro. Adamu ndi Hava analengedwa angwiro, koma ungwiro wawo sunakhalitse. Komabe, Yesu Kristu anakhalabe ‘wokhulupirika, wopanda chilema, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa’ mosasamala kanthu za zirizonse zimene Mdyerekezi anabweretsa pa iye mwa kumuyesa kapena kumuzunza. M’zonsezo ‘sanachita tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo.’ Iye anawatokosa moyenerera omtsutsa achipembedzo kuti: ‘Ndani mwa inu anditsutsa ine za tchimo?’ Panalibe ndi mmodzi yense wa iwo adatukula dzanja! (Ahebri 7:26; 1 Petro 2:22; Yohane 8:46) Ndipo chifukwa cha kusunga kwake umphumphu wosachimwa, Yesu anayeretsa Atate wake wakumwamba kukhala Mfumu ya chilengedwe chonse yoyenerera ndipo anatsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza lamkunkhuniza.​—Miyambo 27:11.

12. (a) Kodi Yesu anali munthu wamtundu wanji, ndipo kodi iye anachita chiyani ndi kuvutika motani kaamba ka ena? (b) Kodi nchifukwa ninji munganene kuti Yesu amayenerera ulemu chifukwa cha zimene anachita ndi zimene anavutika nazo?

12 Yesu Kristu amayenerera ulemu wathu, osati kokha chifukwa chakuti anakhala ndi moyo wangwiro, wosachimwa komanso chifukwa chakuti anali munthu wabwino, munthu wopanda dyera, wodzipereka nsembe. (Yerekezerani ndi Aroma 5:7.) Iye anatumikira zosoŵa zauzimu ndi zakuthupi za anthu popanda kutopa. Ha, iye anasonyeza changu cha nyumba ya Atate wake chotani nanga, ndipo anali woleza mtima chotani nanga pochita ndi ophunzira ake! Iye anali wofunitsitsa kuvutika chotani nanga pochita chifuniro cha Atate wake! Pansautso yake m’munda wa Getsemane, Baibulo likuti: ‘Ndipo pokhala iye m’chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu; ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.’ Inde, Iye ‘anapereka mapemphero ndi mapembedzero . . . ndi kulira kwakukulu ndi misozi.’ (Luka 22:44; Ahebri 5:7) Mneneri Yesaya ananenera molunjika chotani nanga ponena za nsautso yake pa Yesaya 53:3-7!

13. Kodi Yesu anatikhazikitsira chitsanzo chabwino chotani cholemekeza Atate wake wakumwamba?

13 Yesu amafunikiranso ulemu wathu chifukwa cha chitsanzo chabwino chimene iye anatikhazikitsira polemekeza Atate wake wakumwamba. Iye anathadi kunena bwino kuti: “Ndilemekeza Atate wanga.” (Yohane 8:49) Paliponse iye analemekeza Yehova Mulungu m’mawu ndi ntchito zake. Chotero, pamene anachiritsa mwamuna wina, cholembedwa cha Baibulo sichimati anthu analemekeza Yesu, koma kuti “analemekeza Mulungu.” (Marko 2:12) Chotero, pamapeto pauminisitala wake wapadziko lapansi, Yesu anatha kunena molondola m’pemphero kwa Atate wake wakumwamba kuti: ‘Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m’mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.’​—Yohane 17:4.

Zomwe Watichitira

14. Kodi imfa ya Yesu inatikwaniritsiranji chomwe chimamuyeneretsa kulemekezedwa?

14 Ndipo Yesu Kristu amayenerera ulemu wathu mokulira chotani nanga chifukwa cha zonse zimene watikwaniritsira! Iye anafera machimo athu kotero kuti tiyanjanitsidwe ndi Yehova Mulungu. Yesu ponena za mwiniyekha anati: ‘Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Chotero, imfa yake inatheketsa zonse zimene Ufumu udzatikwaniritsira anthufe: moyo wosafa kumwamba kaamba ka a 144,000 omwe amapanga mkwatibwi wake ndi moyo wosatha m’paradaiso ya padziko lapansi kwa mamiliyoni ena amene atsimikizira chikhulupiriro chawo ndikukhala omvera pansi pa chiyeso.​—Salmo 37:29; Chibvumbulutso 14:1-3; 21:3, 4.

15. Kodi nchitsanzo chimodzi chiti chimene Yesu anavumbulira umunthu wa Atate wake kwa ife?

15 Yesu Kristu akuyenereranso kulemekezedwa chifukwa chakuti, monga m’Phunzitsi Wamkulu, iye wativumbulira mwangwiro chifuniro cha Atate wake ndi umunthu wake. Mwachitsanzo, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, iye anasonya kuubwino wa Atate wake mwa kuwalitsira dzuŵa ndi kuvumbitsira mvula pa oipa ndi abwino mofananamo ndipo kenaka anati: ‘Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wakumwamba ali wangwiro.’​—Mateyu 5:44-48.

16. Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anafotokozera mwachidule njira ya Yesu yoyenerera kumchitira ulemu?

16 Mtumwi Paulo anafotokoza mwachidule njira ya Yesu yoyenerera kuchitiridwa ulemu pamene analemba kuti: ‘Ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, [iye] sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtengo wozunzira.’​—Afilipi 2:5-8.

Mmene Tingamlemekezere Mwanayo

17, 18. Kodi ndim’njira zosiyanasiyana zotani mmene tingamchitire ulemu Yesu Kristu?

17 Popeza kuti Yesu Kristu mosakaikira amayenerera kuti timchitire ulemu, funso lomwe tingafunse nlakuti: Kodi tingamlemekeze motani Mwanayo? Timatero mwakusonyeza chikhulupiriro m’nsembe yake ya dipo, ndipo chikhulupirirocho timachitsimikizira mwa kutenga masitepe ofunikira kulapa, kutembenuka, kudzipereka, ndi kubatizidwa. Mwakudza kwa Yehova m’pemphero m’dzina la Yesu, timalemekeza Yesu. Timamlemekezanso pamene tilabadira mawu ake awa: ‘Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtengo wake wozunzirapo, nanditsate ine.’ (Mateyu 16:24) Timamlemekeza Yesu Kristu pamene tilabadira malangizo ake a kufuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo timamlemekeza pamene tilabadira lamulo lake la kukhalamo ndi phande m’ntchito yopanga ophunzira. Ndiponso, timamlemekeza Yesu pamene tisonyeza chikondi cha paubale chimene adati chikazindikiritsa atsatiri ake owona onse.​—Mateyu 6:33; 28:19, 20; Yohane 13:34, 35.

18 Kuwonjezera apa, timabweretsanso ulemu kwa Mwanayo mwakunyamula dzina lake, tikumadzitcha Akristu, ndipo kenaka ndikukhala mogwirizana ndi dzinalo mwa makhalidwe athu abwino. (Machitidwe 11:26; 1 Petro 2:11, 12) Mtumwi Petro anati tiyenera kutsatira mapazi a Yesu mwathithithi. (1 Petro 2:21) Chotero mwakumutsanzira m’makhalidwe athu onse, timamlemekezanso. Ndipo motsimikizirika, pamene chaka ndi chaka tichita phwando la Chikumbutso cha imfa ya Kristu, timamchitira ulemu wapadera.​—1 Akorinto 11:23-26.

19, 20. (a) Kodi Yesu akusungira atsatiri ake mphotho zotani kaamba ka kumulemekeza, tsopano ndi mtsogolo? (b) Kodi nchidaliro chotani chomwe tingakhale nacho mwa Mwanayo?

19 Kodi Yesu ali ndi mfupo zotani kwa ophunzira ake kaamba ka kutsatira njira imene imamulemekeza? Iye anati: ‘Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi irinkudza, moyo wosatha.’​—Marko 10:29, 30.

20 Choncho, ngati tidzimana chifukwa cha Yesu, iye adzatsimikizira kuti tafupidwa. Yesu akutitsimikizira kuti: ‘Chifukwa chake yense amene adzavomereza ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wakumwamba.’ (Mateyu 10:32) Chotero monga mmene Atate wakumwamba amalemekezera omulemekeza, ife tingakhale achidaliro kuti Mwana wobadwa yekha wa Yehova adzatsanzira Atate wake pankhaniyi, monga mmene Mwanayu amachitira m’nkhani zina.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ndimotani mmene ambiri m’Chikristu Chadziko amanyozera Mwanayo?

◻ Kodi ndiumboni wotani umene Yesu anapereka ponena za kukhalapo kwake asanakhale munthu?

◻ Kodi ndizifukwa zina ziti zimene tiri nazo zolemekezera Yesu?

◻ Kodi ndinjira zina ziti zimene tingalemekeze nazo Yesu?

◻ Kodi kulemekeza Yesu Kristu kumatulukapo madalitso otani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena