Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/1 tsamba 25-29
  • Monga Mkazi Wamasiye, Ndinapeza Chitonthozo Chenicheni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Monga Mkazi Wamasiye, Ndinapeza Chitonthozo Chenicheni
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzira Chowonadi cha Baibulo
  • Kugaŵana Chidziŵitso Chopezedwa Chatsopano
  • Kuchitira Umboni m’Khwalala
  • Ndinalimbikitsidwa Kulaka Mantha
  • Kulimbikitsidwa ndi Kudalitsidwa
  • Kulinganiza Mathayo
  • Chitonthozo cha Moyo Wonse
  • Kulimbitsa Chikhulupiro mwa Kuphunzira Baibulo ku India
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kuyandikira kwa Mulungu Kunandithandiza Kulaka
    Galamukani!—1993
  • Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kulera Ana Eyiti M’njira za Yehova Inali Ntchito Yovuta Komanso Yosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2006
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/1 tsamba 25-29

Monga Mkazi Wamasiye, Ndinapeza Chitonthozo Chenicheni

Monga momwe yasimbidwira ndi Lily Arthur

Minisitala wachichepere wa Mboni za Yehova ankafikira nyumba ndi nyumba m’chigawo cha Ootacamund, mu India. Mwamwambo akazi sanatsegulire chitseko mlendo woteroyo. Pambuyo pa maola angapo, atatopa ndi kukhumudwa, iye anatembenuka kuti abwerere kunyumba. Koma anaima, akumadzimva kukhala wokakamizika kufikira khomo lotsatira. Talingalirani zomwe zinachitika, monga momwe zalongosoledwera ndi mkazi yemwe anamtsegulira chitseko.

MWANA wanga wamkazi wamiyezi iŵiri ali m’manja mwanga ndi mwana wanga wamwamuna wa miyezi 22 ali kumbali kwanga, ndinatsegula chitseko mofulumira ndikuwona mlendo ali chiriri. Usiku wapitawo ndinavutitsidwa maganizo kwambiri. Ndikumafuna chitonthozo, ndinapemphera motere: “Atate wakumwamba, chonde nditonthozeni ndi Mawu anu.” Tsopano, modabwitsidwa, mlendoyo analongosola kuti: “Ndakubweretserani uthenga wa chitonthozo ndi chiyembekezo wochokera m’Mawu a Mulungu.” Ndinalingalira kuti ayenera kukhala mneneri wotumizidwa ndi Mulungu. Koma kodi ndimkhalidwe wotani womwe unandipangitsa kupereka pemphero langa lofuna thandizo?

Kuphunzira Chowonadi cha Baibulo

Ndinabadwa mu 1922 m’mudzi wa Gudalur m’Mapiri okongola a Nilgiri kum’mwera kwa India. Amayi anga anamwalira pamene ndinali ndi zaka zitatu zakubadwa. Pambuyo pake, Atate, omwe anali mtsogoleri wachipembedzo wa Chiprotesitanti, anakwatiranso. Mwamsanga titangodziŵa kulankhula, Atate anaphunzitsa achimwene ndi achemwali anga ndi ine kupemphera. Pamsinkhu wa zaka zinayi, pamene Atate ankakhala padesiki pawo tsiku ndi tsiku kumaŵerenga Baibulo, ine ndinkakhala pansi kuŵerenga Baibulo langa.

Pamene ndinakula, ndinakhala mphunzitsi. Kenaka, pamene ndinafika msinkhu wa zaka 21, atate anga anakonza za ukwati wanga. Mwamuna wanga ndi ine tinadalitsidwa ndi mwana wamwamuna, Sunder, ndipo pambuyo pake ndi mwana wamkazi, Rathna. Komabe, pafupifupi nthaŵi imene Rathna anabadwa, mwamuna wanga anadwala kwambiri, ndipo mwamsanga pambuyo pake anamwalira. Mwadzidzidzi, ndinakhala mkazi wamasiye pamsinkhu wa zaka 24, ndi thayo losamalira ana aang’ono aŵiri.

Pambuyo pa zimenezo ndinampempha Mulungu kuti anditonthoze ndi Mawu ake, ndipo linali tsiku lotsatira pamene minisitala wa Mboni za Yehova anafika. Ndinamuitana kuloŵa m’nyumba ndipo ndinalandira bukhu la “Mulungu Akhale Woona.” Usiku umenewo pamene ndinkaliŵerenga, ndinapitiriza kuwona dzina lakuti Yehova, lomwe kwa ine linali lachilendo. Pambuyo pake minisitalayo anabwerera nandisonyeza m’Baibulo kuti ilo ndi dzina la Mulungu.

Posakhalitsa ndinaphunziranso kuti ziphunzitso zonga ngati Utatu ndi moto wa helo nzosazikidwa pa Baibulo. Chitonthozo ndi chiyembekezo zinadza pa ine pamene ndinaphunzira kuti pansi pa Ufumu wa Mulungu dziko lapansi lidzakhala paradaiso ndikuti akufa okondedwa adzabwerera m’chiukiriro. Chofunika koposa, ndinayamba kudziŵa ndi kukonda Mulungu wowona, Yehova, amene anamva pemphero langa ndikundithandiza.

Kugaŵana Chidziŵitso Chopezedwa Chatsopano

Ndinayamba kuzizwa mmene ndinaphonyera kuŵerenga mavesi a Baibulo okhala ndi dzina la Mulungu amenewo. Ndipo kodi nchifukwa ninji sindinawone chiyembekezo chomvekera cha moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi m’kuŵerenga kwanga kwaumwini Baibulo? Ndinkaphunzitsa pasukulu Yachiprotesitanti yotsogozedwa ndi amishonale, choncho ndinasonyeza mavesi a Baibulowo kwa mtsogoleri wa sukuluyo. (Eksodo 6:3; Salmo 37:29; 83:18; Yesaya 11:6-9; Chibvumbulutso 21:3, 4) Ndinanena kuti zikuwoneka kuti mwanjira inayake tinawanyalanyaza iwo. Koma ndinadabwitsidwa kuwona kuti sanakondwere.

Kenaka ndinalembera kalata mphunzitsi wamkulu yemwe ankakhala m’tauni ina, ndikumagwira mawu mavesi a Baibulo ameneŵa. Ndinapempha mwaŵi wakulankhula naye. Iye anayankha kuti bambo wake, mtsogoleri wachipembedzo wotchuka kwambiri wochokera ku Mangalande, adzakambitsirana nane nkhaniyo. Mchimwene wa mphunzitsi wamkuluyo anali bishopu wotchuka.

Ndinakonzekera nsonga zonse ndi malemba ndipo ndinatenga bukhu langa la “Mulungu Akhale Woona” ndi ana anga kunka ku tauni yotsatirayo. Motenthedwa maganizo ndinafotokoza amene Yehova ali, kuti kulibeko Utatu, ndi zinthu zina zomwe ndinaphunzira. Iwo anamvetsera kwakanthaŵi koma sananene kanthu. Kenaka mtsogoleri wachipembedzo wochokera ku Mangalandeyo anati: “Ndidzakupempherera.” Kenaka anandipempherera nandithamangitsa.

Kuchitira Umboni m’Khwalala

Tsiku lina minisitala wa Mboni za Yehova anandiitana kukachita umboni wa m’khwalala ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndinamuuza kuti chimenechi ndichinthu chomwe sindikachita konse. Mudziŵa, m’India anthu angaganize zoipa kwambiri ponena za mkazi woima m’khwalala kapena kupita kukhomo ndi khomo. Chingabweretse chitonzo pa mbiri yabwino ya mkaziyo ndiponso pa banja lake. Popeza kuti ndinakonda ndi kulemekeza kwambiri bambo anga, sindinafune kubweretsa chitonzo pa iwo.

Koma minisitalayo anandisonyeza vesi la Baibulo limene limati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga, kuti ndimuyankhe iye wonditonza ine.” (Miyambo 27:11, King James Version) Iye anati: “Umakondweretsa mtima wa Yehova mwakusonyeza poyera kuti uli kumbali yake ndi Ufumu wake.” Ndikumakhumba kukondweretsa mtima wa Yehova kuposa china chirichonse, ndinatenga chola chamagazini ndikunka naye m’ntchito yochitira umboni wa m’khwalala. Ngakhale tsopano sindikudziŵa mmene ndinachitira. Mmenemo munali mu 1946, pafupifupi miyezi inayi pambuyo pofikiridwa.

Ndinalimbikitsidwa Kulaka Mantha

Mu 1947, ndinavomera ntchito yophunzitsa kunja kwa Madras, kugombe la Kum’mawa kwa India, ndipo ndinasamukira kumeneko ndi anawo. Gulu laling’ono la Mboni za Yehova zokwanira zisanu ndi zitatu zinkakumana mokhazikika m’tauniyo. Kuti tikapezekepo pa misonkhano imeneyo, tinafunikira kuyenda mtunda wa mamailosi 16. Mu India panthaŵiyo, kaŵirikaŵiri akazi sankayenda okha. Iwo ankadalira pa amuna kuwatenga iwo. Sindinadziŵe kukwera basi, kugula tiketi, ndi kutsika basi, ndi zina zotero. Ndinalingalira kuti ndifunikira kutumikira Yehova, koma motani? Chotero ndinapemphera motere: “Yehova Mulungu, sindingathe kukhala osakutumikirani. Koma nzosatheka kwa ine monga mkazi Wachimwenye kupita kunyumba ndi nyumba.”

Ndinayembekeza kuti Yehova akandilola kumwalira kuti andimasule ku kusemphana maganizo kumeneku. Komabe, ndinasankha kuŵerenga chinachake m’Baibulo. Zinangochitika kuti ndinatsegula bukhu la Yeremiya, pamene pamati: ‘Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza. Usawope nkhope zawo; chifukwa ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe.’​—Yeremiya 1:7, 8.

Ndinalingalira kuti Yehova ankalankhuladi kwa ine. Chotero ndinalimba mtima ndipo panthaŵi yomweyo ndinapita pamakina anga ndikusoka chola chonyamuliramo magazini. Pambuyo pa pemphero lowona mtima, ndinapita ndekha kunyumba ndi nyumba, kugaŵira mabuku anga onse, ndipo ndinayambitsa phunziro Labaibulo tsiku lomwelo. Ndinakhala wotsimikiza mtima kumpatsa Yehova malo oyamba m’moyo mwanga, ndipo ndinaika chikhulupiriro ndi chidaliro changa chonse mwa iye. Ntchito yolalikira poyera inakhala mbali yokhazikika ya moyo wanga mosasamala kanthu za chitonzo. Mosasamala kanthu za chitsutso, ntchito yanga inasangalatsa anthu ena.

Ichi chinachitiridwa fanizo pamene mwana wanga wamkazi ndi ine tinapita kunyumba ndi nyumba m’Madras zaka zambiri pambuyo pake. Mwamuna Wachihindu, woweruza wa ku Bwalo Lalikulu Lamilandu, asakudziŵa msinkhu wanga, anati: “Ndadziŵa magazini ameneŵa kuyambira usanabadwe! Zaka makumi atatu zapitazo, mkazi wina ankaimirira nthaŵi zonse pa Mount Road ndikuwagaŵira.” Iye ankafuna sabusikripishoni.

Panyumba ina Brahman Wachihindu, nduna yoleka kugwira ntchito, anatiitana kuloŵa m’nyumba nati: “Zaka zambiri-mbiri zapitazo mkazi wina ankagaŵira Nsanja ya Olonda pa Mount Road. Ndidzatenga chomwe ukugaŵira chifukwa cha iye.” Ndinafunikira kumwetulira chifukwa ndinadziŵa kuti mkazi yemwe onse aŵiriwo anasonyakoyo ndinali ine.

Kulimbikitsidwa ndi Kudalitsidwa

Munali mu October 1947 pamene ndinachitira chithunzi kudzipereka kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wam’madzi. Panthaŵiyo ndinali Mboni yokha yachikazi yolankhula Tamil m’dziko lonselo, koma tsopano akazi ambiri a fuko la Tamil ndi Mboni za Yehova zokhulupirika, zokangalika kumeneko.

Pambuyo pobatizidwa, chitsutso chinabwera kuchokera kumbali zonse. Mchimwene wanga analemba kuti: “Wataya makhalidwe ovomerezeka onse ndi ulemu.” Ndinalandiranso chitsutso pasukulu pomwe ndinkagwira ntchito ndi m’mudzi. Koma ndinamamatirabe zolimba kwa Yehova mwakupitiriza kupemphera kosaleka. Nditauka pakati pausiku, ndinkayatsa nyali ndikumaphunzira.

Pamene ndinalimbikitsidwa, ndinakhala m’malo abwino akutonthoza ndi kuthandiza ena. Mkazi wina wokalamba Wachihindu amene ndinaphunzira naye anachilimika kulambira Yehova. Pamene anamwalira, mkazi wina m’banjalo anati: “Chomwe chinatikondweretsa kwambiri chinali kukhala kwake wokhulupirika kwa Mulungu amene anasankha kumlambira kufikira kumapeto.”

Mkazi wina amene ndinaphunzira naye sankamwetulira konse. Nthaŵi zonse nkhope yake inasonyeza kuda nkhaŵa ndi chisoni. Koma pambuyo pomphunzitsa ponena za Yehova, ndinamlimbikitsa kupemphera kwa iye, popeza kuti amadziŵa mavuto athu ndipo amatisamalira. Mlungu wotsatira nkhope yake inali yokondwera. Inali nthaŵi yanga yoyamba kumuwona akumwetulira. “Ndakhala ndikupemphera kwa Yehova,” iye analongosola tero, “ndipo ndiri ndi mtendere wa maganizo ndi mtima.” Iye anapereka moyo wake kwa Yehova ndikukhalabe wokhulupirika mosasamala kanthu za mavuto ambiri.

Kulinganiza Mathayo

Pokhala ndi ana aang’ono aŵiri ofunikira chisamaliro, ndinalingalira kuti chikhumbo changa chakutumikira Yehova nthaŵi zonse monga mpainiya sichikakwaniritsidwa konse. Komano mbali yatsopano ya utumiki inatseguka pamene winawake anafunikira kutembenuzira mabuku a Baibulo m’chinenero cha Tamil. Ndi thandizo la Yehova ndinakhoza kusamalira thayo limenelo ndipo, panthaŵi imodzimodziyo, kugwira ntchito yakuthupi monga mphunzitsi, kusamalira ana, kuchita ntchito yanga yapanyumba, kupezekapo pamisonkhano yonse, ndikukhala ndi phande muutumiki wakumunda. Pomalizira pake, pamene anawo anakula, ndinakhala mpainiya wapadera, mwaŵi womwe ndasangalala nawo kwa zaka 33 zapitazi.

Ngakhale pamene Sunder ndi Rathna anali amsinkhu wauchichepere, ndinayesera kukhomereza mwa iwo chikondi cha Yehova ndichikhumbo chakuika nthaŵi zonse zikondwerero zake poyamba m’mbali iriyonse ya miyoyo yawo. Iwo anadziŵa kuti munthu woyamba kulankhula naye pamene auka anali Yehova ndikuti iye anali munthu womalizira kulankhula naye asanagone. Ndipo anadziŵa kuti kukonzekera misonkhano Yachikristu ndi utumiki wakumunda siziyenera kunyalanyazidwa chifukwa cha homuweki yakusukulu. Pamene ndinawalimbikitsa kuchita zimene angathe m’ntchito yawo yakusukulu, sindinaumirire konse kuti ayenera kupeza gredi yapamwamba, ndikumawopa kuti angatenge chimenecho kukhala chinthu chofunika koposa m’moyo wawo.

Pambuyo pakubatizidwa kwawo, iwo anagwiritsira ntchito nthaŵi ya tchuthi cha sukulu kuchita upainiya. Ndinalimbikitsa Rathna kukhala wolimba mtima, osati wamantha ndi wamanyazi monga mmene ndinaliri. Pambuyo pomaliza sukulu yake yasekondale ndi maphunziro a zamalonda, iye anayamba upainiya, ndipo pambuyo pake anakhala mpainiya wapadera. Kenaka, anakwatiwa ndi woyang’anira woyendayenda, Richard Gabriel, yemwe tsopano akutumikira monga mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi ya Watch Tower Society mu India. Iwo limodzi ndi mwana wawo wamkazi, Abigail, amagwira ntchito nthaŵi zonse panthambi ya India, ndipo mwana wawo wamwamuna wamng’ono, Andrew, ndi wofalitsa wa mbiri yabwino.

Komabe, pamsinkhu wa zaka 18, Sunder anaswa mtima wanga, pamene analeka kuyanjana ndi Mboni za Yehova. Zaka zotsatira zinali zowawitsa kwa ine. Ndinapitiriza kuchonderera Yehova kuti akhululuke zophophonya zirizonse zomwe ndinapanga pomulera iye ndikumpangitsa Sunder kulingalira bwino kuti abwerere. Koma, m’kupita kwa nthaŵi, ndinataya chiyembekezo chonse. Kenaka tsiku lina pambuyo pa zaka 13 iye anabwera kudzandiuza kuti: “Amayi, musadandaule, ndidzakhala bwino.”

Mwamsanga pambuyo pa chimenecho, Sunder anapanga zoyesayesa zapadera kukhala wachikulire mwauzimu. Iye anapita patsogolo kufikira pansonga yakuikiziridwa kuyang’anira mpingo wa Mboni za Yehova. Pambuyo pake analeka ntchito yake yokhala ndi malipiro abwino kuti akhale mpainiya. Tsopano iye ndi mkazi wake, Esther, akutumikira pamodzi m’ntchito imeneyi mu Bangalore kumbali yakum’mwera kwa India.

Chitonthozo cha Moyo Wonse

Kaŵirikaŵiri ndimathokoza Yehova chifukwa chondilola kupyola kuvutika ndi mavuto m’zaka zonsezi. Popanda zokumana nazo zoterozo sindikanakhala ndi mwaŵi wamtengo wake wakulaŵa kuukulu woterowo ukoma wa Yehova, chifundo chake, ndi kusonyezedwa kwa chisamaliro ndi chikondi chake. (Yakobo 5:11) Nzokondweretsa kuŵerenga m’Baibulo ponena za chisamaliro ndi kudera nkhaŵa kwa Yehova kaamba ka “mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.” (Deuteronomo 24:19-21) Koma siziri kanthu polinganiza ndi chitonthozo ndi chikondwerero chakukumanadi ndi chisamaliro ndi kudera nkhaŵa kwake.

Ndaphunzira kuika chikhulupiriro ndi chidaliro chotheratu mwa Yehova, osati kuchirikizika pa luntha langa, koma m’njira zanga zonse kumlemekeza. (Salmo 43:5; Miyambo 3:5, 6) Monga mkazi wamasiye wachichepere, ndinapemphera kwa Mulungu kaamba ka chitonthozo kuchokera m’Mawu ake. Tsopano, pamsinkhu wa zaka 68, ndinganenedi kuti mwakumvetsetsa Baibulo ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake, ndapeza chitonthozo chosayerekezeka.

[Chithunzi patsamba 26]

Lily Arthur ndi ziŵalo za banja lake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena