Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 4/1 tsamba 26-29
  • Kuŵerengera Mtengo Wakusamukira ku Dziko Lokhupuka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuŵerengera Mtengo Wakusamukira ku Dziko Lokhupuka
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zenizeni za Moyo wa Kumaiko Akutali
  • Zipsinjo Zamakhalidwe
  • Makolo Amene Palibepo
  • Kudalira m’Makonzedwe a Mulungu
  • Kodi Ndisamukire Kudziko lina?
    Galamukani!—2000
  • ‘Kusamalira Nyumba ya Munthuwe’—Kuyang’anizana ndi Chitokosocho m’Maiko Omatukuka
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Ndingakhale Wopambana Motani Pamene Ndikukhala Kudziko Lina?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Ndingachite Chiyani Ngati Banja Lathu Ndi Losauka?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 4/1 tsamba 26-29

Kuŵerengera Mtengo Wakusamukira ku Dziko Lokhupuka

NCHOCHITIKA chozoloŵereka pamaofesi a oimira maiko akunja m’maiko onse otukuka kumene: kuwona nyumba yoyembekezerapo iri yodzaza ndi anthu omwe akuyembekezera kufunsidwa. Kudalira pakukambitsirana kwachiduleko koma kofunika kwambiri, zidzagamulidwa kaya iwo angalandire chiphaso chopitira ku dziko lotsungula Kumadzulo. Ambiri amakhulupirira kuti iyi idzakhala tikiti yowapangitsa kukhala okhupuka. “Ndakhala ndikugwira ntchito zolimba kwa zaka zinayi, ndipo sindinakhoze kugula ngakhale wailesi,” anadandaula motero wachichepere wina wa Kumadzulo kwa Afirika. “Ndikadakhala kuti ndidali ku Mangalande kapena ku United States, tsopano ndikadakhala ndi galimoto ndi nyumba yanga yanga.”

Sikovuta kumvetsetsa chifukwa chimene anthu ambiri m’maiko osauka, otukuka kumene aliri ndi malingaliro oterowo. Kwa iwo, ntchito nzovuta kupeza, ndipo malipiro ngotsika. Kukwera mitengo kwa zinthu kumakokolola ndalama zawo zosungidwa kubanki. Nyumba nzosapezekapezeka ndipo anthu amakhala mothithikana. Anthu amavala malaya olekedwa ndi okhala m’maiko achuma. Ambiri amadzimva kukhala okoledwa m’vuto la zandalama.

Ndipo Kumadzulo kokhupuka kumakodola chotani nanga! Mwamuna wachichepere wina wa ku Sierra Leone anati: “Ena amene apita kumaiko akutali amabwerako ndikumatisimbira nkhani zimene zimatisonkhezera kufuna kupita ndikukadziwonera tokha maiko otsungula. Iwo amati uyenera kugwira ntchito zolimba, komabe umapeza ndalama zochuluka kotero kuti utha kudzichirikiza wekha ndipo ngakhale kugula zinthu zosangalatsa, monga galimoto. Ndipo utabwerako ndi madola pafupifupi zikwi ziŵiri, ukhoza kuyamba bizinesi ndikukwatira.”

Mosadabwitsa, atumiki a Mulungu ena amalingalira mofananamo. Mlongo Wachiafirika anati: “Ife achichepere amene tiri m’gulu la Mulungu timamvetsera makambitsirano onena za mmene ena omwe anapita kumaiko akunja amapezera bwino kwambiri. Chotero nthaŵi zina ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi bwanji ponena za ine? Kodi bwanji ndikuvutika kunoku? Kodi ndipite kapena ndikhale?’”

Ngati mumakhala m’dziko losauka, mwinamwake mungazizwe kaya ngati kusamuka kukawongolera mkhalidwe wa moyo wanu. Komabe, kusamukira ku dziko lachilendo ndiko ntchito yovuta, sitepe lodula ndi lofunika kusamala kwenikweni. Iko kungaloŵetsemo kuphunzira chinenero chatsopano, kupeza maluso antchito atsopano, kusinthira ku mwambo watsopano wamakhalidwe, kupirira tsankho limene ambiri amalisonyeza kwa alendo, ndikuphunzira njira ya moyo yatsopano kotheratu. Chikhalirechobe, Akristu ambiri achita chimenecho mwachipambano ndipo akhaladi chuma chenicheni ku mipingo ya m’maiko awo atsopano, akutumikira monga ofalitsa, apainiya, akulu, ndi atumiki otumikira opereka chitsanzo chabwino.

Chinkana kuli choncho, sionse amene zinthu zawayendera bwino motero. Zovuta ndi kupanikiza kochititsidwa ndi kusamuka zatulukira m’kuvulaza ena mwauzimu. Mwachiwonekere, pamenepa, sitepe loterolo siliyenera kupangidwa popanda kulingalira mosamalitsa, mwapemphero. Baibulo limalangiza pa Miyambo 3:5, 6 kuti: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; Umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.’ Inde, mufuna kutsimikizira kuti mukuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. (Yakobo 4:13-15) Ndipo Yesu anapereka uphungu wogwira ntchito kukuthandizani kuchita chimenechi pamene anasonkhezera omvetsera ake ‘kuŵerengera mtengo.’ (Luka 14:28) Ichi chimaphatikizapo zoposa kulingalira zachuma. Chimatanthauza kulingalira zotaikiridwa zauzimu zothekera zimene kusamuka kungachititse.

Zenizeni za Moyo wa Kumaiko Akutali

Musanapite kwina kulikonse, muyenera kukhala ndi lingaliro lenileni, lotsimikizirika ponena za zimene muyembekezera kupeza pamene mufika kumaloko. Ngati nkotheka, pangani ulendo wokacheza choyamba ndikudziwonera mmene mikhalidwe iliri. Apo phuluzi, mudzafunikira kungodalira pazouzidwa ndi ena. Baibulo limachenjeza kuti: ‘Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.’​—Miyambo 14:15.

Ena apeza chidziŵitso chawo chonse chonena za moyo wa kumaiko Akumadzulo kuchokera ku ziwonetsero za akanema ndi wailesi yakanema. Motero iwo amakhulupirira kuti aliyense kumeneko ngwachuma, amayendetsa galimoto yatsopano, ndipo amakhala m’nyumba yokongola. Komabe, zenizeni nzosiyana kotheratu. Maiko ambiri okhupuka ali ndi umphaŵi waukulu, kusoŵa nyumba, ndi ulova. Ndipo ambiri a nzika zosaukiratu ndiwo obwera m’dzikomo chatsopano. Ofisala woimira boma pa ofesi yakazembe ya U.S. m’dziko lina losauka anati: “Anthu samalingalira mmene kuliri kovuta kukhazikika m’Amereka. Ena amalembera makalata kwawo namasimba mmene akupezera bwino​—mmene agulira magalimoto aŵiri ndi nyumba​—koma m’chenicheni iwo akuvutika zedi.”

Mkhalidwewo ngwofanana ndi kwina kulikonse. A Sahr Sorie ndimphunzitsi wa Kumadzulo kwa Afirika yemwe wakhala m’London ndikuphunzirira kumeneko. Iye anathirira ndemanga kuti: “Sikopepuka kusamuka m’Afirika ndikukakhala ku Mangalande. Osamukirako ambirimbiri amakhala ndi moyo waumphaŵi kwadzawoneni. Nkhope zawo zimasonyeza kuvutika kwawo. Ena amakupeza kukhala kovuta kupeza ngakhale 20 pence yoti atumire foni. Kaŵirikaŵiri amagaŵana chipinda chimodzi ndi ena ambiri, ali kokha ndi mbaula yaing’ono yamagetsi yowafunditsako. Iwo amakhoza kupeza ntchito zotsika zokha, ndipo ngakhale atatero sizitha kuwapezera ndalama zokwanira kulipira ngongole zawo. Awo ochoka mu Afirika kuthaŵa umphaŵi kaŵirikaŵiri amagwera m’kuvutika koipitsitsa m’miraga ya ku Yuropu.”

Zipsinjo zachuma zimene zimatsagana ndi kukhazikika m’dziko latsopano zikhoza kutsamwitsa uzimu wa munthu mosavuta. (Mateyu 13:22) Zowonadi, kugwira ntchito zolimba kumayamikiridwa m’Baibulo. (Miyambo 10:4; 13:4) Koma ambiri amene amapita kumaiko akutali amakakamizika kumagwira ntchito ziŵiri kapena zitatu kotero kuti apeze zonulirapo zawo zachuma​—kapena kuti angopeza zofunika m’moyo. Pamatsala nthaŵi yochepa yolambira Mulungu kapena pamakhala palibiretu iriyonse. Misonkhano Yachikristu, phunziro Labaibulo, ndikugaŵana chowonadi cha Baibulo ndi ena zimanyalanyazidwa. Mawu a Yesu Kristu amatsimikizira kukhala owona mowopsa: ‘Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.’​—Mateyu 6:24.

Zipsinjo Zamakhalidwe

Muyeneranso kulingalira za makhalidwe a dziko limene muyembekezera kupitako. Baibulo limatiuza kuti Loti anasankha kukakhala m’Boma la Yordano. M’lingaliro la zinthu zakuthupi, chosankha chake chinawoneka kukhala chanzeru, popeza kuti chinali chigawo chokhala “ndi madzi ambiri . . . , monga munda wa Yehova.” (Genesis 13:10) Komabe, anansi atsopano a Loti anali ‘oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova’​—achilakolako choipa chakugonana! (Genesis 13:13) Monga chotulukapo, ‘wolungama uja pokhala pakati pawo ndi kuwona ndi kumva zawo, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika.’​—2 Petro 2:8.

Mofananamo, lerolino kusamukira Kumadzulo kungachititse inu ndi banja lanu kuyang’anizana ndi zipsinjo zamakhalidwe ndi ziyeso zokulira kuposa mmene ziliri m’dziko lakwanu. Kuwonjezerapo, anthu achikulire sangamapatsidwe ulemu monga momwe anapatsidwira kwawo. Ulemu kwa makolo sungalimbikitsidwe. Anansi angakhale ndi chikondwerero chochepa mwa wina ndi mnzake. Kodi ndimotani mmene zipsinjo zoterozo zingakuyambukirireni ndi banja lanu? Ichi nchinthu chofunika kuchilingalira mwapemphero.

Makolo Amene Palibepo

Makolo ena asankha kusiya mabanja awo ndikupita okha kudziko lakutali. Cholinga chawo ndicho kutumizira banja lawo ndalama pamene akhazikika kapena kudzabwerera kwawo ndi ndalama zambirimbiri. Kodi makonzedwe oterowo nganzeru?

Malemba amapatsa makolo thayo lakupezera mabanja awo zosoŵa zakuthupi, ndipo m’zochitika zonkitsa, kholo lingakhale liribe chosankha kwenikweni koma kukagwira ntchito m’dziko lakutali kotero kuti akwaniritse thayolo. (1 Timoteo 5:8) Chikhalirechobe, makolo ngathayonso losamalira zosoŵa zauzimu za mabanja awo. Mawu a Mulungu amati: ‘Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW]’​—Aefeso 6:4.

Kodi tate angachite chimenechi mogwira mtima ngati amakhala kutali ndi banja lake kwa miyezi kapena zaka panthaŵi ina? Mwachiwonekere ayi. Chotero muyenera kulingalira ngati maubwino a zinthu zakuthupi alionse opezedwa ngoyenerera chiyambukiro chimene kusakhalapo kwanu kudzachititsa pa ana anu. Kuwonjezerapo, osamukira m’dziko kaŵirikaŵiri amapeza kuti sikopepuka konse kupeza “mwaŵi” umene anaulingalira. Ngati wosamukira m’dziko satha kulipirira banja kuti liloŵe m’dzikolo, kulekanako kungapitirizebe kwa zaka zambiri. Ichi nachonso, chingadzutse maupandu a makhalidwe. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:1-5.) Mwachisoni, ena okhala m’mikhalidwe yoyesa yoteroyo agonja ku chisembwere chakugonana.

Kudalira m’Makonzedwe a Mulungu

Pamene mikhalidwe ya chuma chadziko ikunyonyotsoka, ndibwino kukumbukira kuti atumiki a Mulungu sayenera kuopa kuti adzalekereredwa. Yesu anati: ‘Chifukwa chake musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.’​—Mateyu 6:31-33.

Mboni za Yehova lerolino zimatumikira zabwino za Ufumu wa Mulungu mwakulengeza mbiri yabwino mwachangu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) M’maiko osauka ambiri, muli kusoŵa kwakukulu kwa alaliki a Ufumu. Makamaka pali kusoŵa kwa akulu ndi atumiki otumikira. Mmalo mopita kudziko lokhupuka m’zachuma kumene kusoŵa sikwakukulu, ambiri asankha kutsala m’maiko akwawo. Kodi ndimotani mmene ena oterowo achitira?

Alethia, mkazi wa Kumadzulo kwa Afirika yemwe watumikira mu utumiki wanthaŵi zonse kwa zaka 30 m’dziko lakwawo, ananena izi: “Ndinali ndi mwaŵi wokakhala m’dziko lakutali. Chifukwa chimene sindinapitire nchakuti ndimakonda kukhala ndi anthu akwathu ndi achibale. Ndimasangalala kuwathandiza kuphunzira chowonadi kotero kuti tingatumikire Yehova pamodzi. Sindinasoŵe kalikonse mwakukhala kuno, ndipo sindichita chisoni pakanthu kalikonse.”

Winifred mofananamo akukhala m’dziko la mu Afirika. Mkhalidwe wa moyo kumeneko ukuŵerengeredwa kukhala pakati pa wotsika koposa m’dziko. Koma pambuyo pa zaka 42 muutumiki waupainiya wanthaŵi zonse, iye akuti: “Sikopepuka nthaŵi zonse kukhoza m’zandalama. Satana amayesayesa kuvutitsa zinthu, koma Yehova nthaŵi zonse wakhala akundigaŵira ndikusamalira zosoŵa zanga.”

M’nthaŵi zamakedzana Abrahamu ‘anakhazikika mtima kuti, chimene [Mulungu] analonjeza, analinayo mphamvu yakuchichita.’ (Aroma 4:21) Kodi nanunso ndinu wokhutiritsidwa kuti Yehova ngwokhoza kukwaniritsa lonjezo lake ndikukusamalirani ngati muika zabwino za Ufumu m’malo oyamba m’moyo wanu? Kodi mumavomerezana naye wamasalmo yemwe analemba kuti: ‘Chilamulo cha pakamwa [pa Mulungu] chindikomera koposa golidi ndi siliva zikwizikwi’? (Salmo 119:72) Kapena kodi mwina inuyo mukufunikira kugwiritsira ntchito mokwanira ndithu uphungu wa mtumwi Paulo? Pa 1 Timoteo 6:8 iye analemba kuti: ‘Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.’ Kodi chinthu chanzeru kuchita sichikakhala, kusafunafuna malo atsopano, koma kupangitsa amene mulimowo kukhala abwino koposa?

Mikhalidwe yazachuma m’maiko ambiri ingachititse mavuto oopsa kwa Akristu. Chotero, ngati banja lasankha kusamuka, pambuyo polingalira mfundo zonse zoloŵetsedwamo, palibe chifukwa chakuti ena akhale osuliza. (Agalatiya 6:5) Otsalawo angapitirizebe kupempha thandizo la Yehova kuti apirire mavuto amene dongosolo lino limawadzetsa, pamene akusangalala ndi madalitso auzimu amene Mulungu amawapatsa. Kumbukirani, posachedwapa kupanda chilungamo ndi zoipa zadziko lino zidzachotsedwa pansi pa Ufumu wa Mulungu. Pamenepo zidzakhala monga momwe wamasalmo ananenera kuti: ‘Muoloŵetsa dzanja lanu [Yehova], nimukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’​—Salmo 145:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena