Baibulo Kodi Nlochokera kwa Mulungu?
YEHOVA, Mulungu wa mphamvu zopanda malire ndi ulamuliro, alidi ndi kuyenera kwa kulankhula ndi zolengedwa zake zaumunthu m’njira iriyonse imene angafunire. Ngati angasankhe kulankhula kupyolera m’mawu olembedwa, iye angafunikirenso kusunga uthenga wake kwa mibadwo mibadwo. Kodi mmenemu ndimmene zakhalira ndi Baibulo?
Pafupifupi zaka 1,500 Kristu asanadze, pamene Baibulo linayamba kulembedwa, padali zolembedwa zina zambiri zachipembedzo. Komabe, zonsezi zinaleka kugwiritsiridiwa ntchito ndipo m’kupita kwanthaŵi zinazimiririka. Zina zafukulidwa ndi akatswiri a za m’mabwinja ndipo tsopano ndizinthu zakale zongosonyezedwa m’malo osungira zinthu zamakedzana. Kumbali ina, mbali za Baibulo zomwe zinalembedwa zaka zoposa zikwi zitatu zapitazo sizinaiŵalidwe konse, ndipo makope ake apulumuka kufikira m’tsiku lathu. Izi nzozizwitsa, makamaka polingalira za udani womwe unachitidwa motsutsana ndi Baibulo m’mbiri yonse. Palibe bukhu lina lirilonse lomwe lakhala chandamale cha chitsutso chankhanza ndi udani waukulu motero. Kuŵerenga kapena kufalitsa Baibulo kunabweretsa chilango cha faindi, kuponyedwa m’ndende, chizunzo chankhanza, ndipo kaŵirikaŵiri imfa.
Kodi ndimotani mmene bukhu wamba likanapulumukira pansi pa mikhalidwe yoteroyo? Baibulo ilo lokha limatiuza kuti: ‘Mawu a Mulungu akhala chikhalire.’ (1 Petro 1:25) Kukhalitsa ndi kusakhoza kuwonongedwa kwa Baibulo zimatithandiza kulizindikira monga Mawu opatulika a Mulungu.
Kuwonjezerapo, tiyenera kuyembekezera kuti uthenga wa Mulungu wonka kwa anthu uyenera kupezekapo padziko lonse. Kodi ndimmene ziriri ndi Baibulo? Inde ndithudi! Palibe bukhu lina lirilonse m’mbiri limene lafika pafupi ndi Baibulo m’chimenechi. Kugaŵiridwa kwa Baibulo kukuyerekezeredwa pa chiŵerengero cha 3,000,000,000. Ndiponso, palibe bukhu lina limene latembenuzidwira m’zinenero zambiri chotero. Baibulo lingaŵerengedwe tsopano, lathunthu kapena mbali yake, m’malirime osiyanasiyana oposa 1,900. American Bible Society ikusimba kuti ilo tsopano limapezeka ku 98 peresenti ya anthu okhala padziko lonse. The New Encyclopædia Britannica imalitcha Baibulo kukhala “mwinamwake unyinji wa mabuku okhala ndi chisonkhezero chachikulu koposa m’mbiri ya anthu.” Motero, kulilongosola kukhala bukhu lalikulu koposa padziko lapansi sikunyada.
Kugwirizana kwa mkati kwa Baibulo kuyambira kuchiyambi mpaka kumapeto kuli umboni wamphamvu wakuti linauziridwadi ndi Mulungu. Kodi kukakhala kwanzeru kuyembekeza kuti zolembedwa za anthu 40 osiyanasiyana pa nyengo ya zaka zoposa 1,600 zingatsimikizire kukhala zogwirizana ndi kukhala ndi mutu umodzi waukulu? Ichi chikakhala chosatheka ngati chikanachitika mwamwaŵi kapena pansi pa chitsogozo cha anthu. Komabe, ziridi tero ndi mabuku 66 opanga Baibulo. Kokha munthu waluntha loposa la anthu wamba, wokhala ndi moyo wautali ndiye amene angapangitse chinthu chozizwitsa choterocho.
Si Mbiri Wamba
Mbiri yakale yomwe iri m’Baibulo njozizwitsa. Koma uthenga wochokera kwa Mulungu wongokhala ndi zolembedwa za mbiri yakale ungakhale ndi phindu lochepa kwa ife. Tikufunikira chitsogozo ndi nzeru yeniyeni, ndipo zimenezo zingapezedwenso m’Baibulo. Mwachitsanzo, Baibulo limatilimbikitsa kukulitsa ‘chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ukoma, chikhulupiriro, chifatso, chiletso’—nkhani zomwe zafotokozedwa mokwanira m’masamba ake. (Galatiya 5:22, 23; Akolose 3:12-14) Baibulo limavomereza kukangalika, ukhondo, kuwona mtima, kukhulupirika muukwati, ulemu ndi chikondi kwa anthu anzathu; ndipo liri ndi uphungu wochuluka wonena za khalidwe la anthu m’banja ndi m’chitaganya.
Pamene wagwiritsiridwa ntchito, uphungu wa Baibulo umawonekera kukhaladi wopindulitsa. Umatimasula ku umbuli ndi kukhulupirira malaulo. (Yohane 8:32) Nzeru yake yeniyeni njosayerekezeka. Mosakaikira, ilo liridi ndi nzeru yaumulungu.
Kunena kwakuti ‘mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita’ kumagwirizana kotheratu ndi njira imene Baibulo limasinthiradi anthu. (Ahebri 4:12) Anthu mamiliyoni ambiri lerolino alaka zikhoterero zaumunthu zovulaza ndipo asintha njira yawo yamoyo yakale yachiwonongeko kukhala abwinopo chifukwa cholabadira miyezo ya Baibulo.—Aefeso 4:22.
Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene miyezo ya Baibulo yanyalanyazidwa? Chotulukapo chimakhala kupanda chimwemwe ndi chisoni, nkhondo, umphaŵi, matenda opatsirana mwakugonana, ndi mabanja osweka. Zinthu zoterozo ziyenera kuyembekezeredwadi chifukwa chakuti kunyalanyaza Baibulo Lopatulika kumatanthauza kukana chitsogozo cha Mulungu, amene analenga munthu ndipo wodziŵa zosoŵa zake.
Baibulo limaloseranso za mtsogolo, chinthu chimene anthu sangathe kuchita. Kubuka kwa maulamuliro adziko kuyambira ya Babulo kupyola zaka mazana ambiri mpaka m’tsiku lathu kunalengezedwa mwaulosi m’Baibulo. (Danieli, mitu 2, 7, 8) Kuwonjezerapo, pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, m’Baibulo munaphatikizidwa malongosoledwe olongosoka a mikhalidwe yadziko m’zaka za zana lino la 20. (Mateyu, mitu 24, 25; Marko, mutu 13; Luka, mutu 21; 2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4; Chibvumbulutso 6:1-8) Ndandanda yaitali ya maulosi a Baibulo okwaniritsidwa imatitsimikizira kuti ziyembekezo za mtsogolo mwachimwemwe zofotokozedwa m’masamba ake nzenizeni.
Thayo Lathu
Wonsewu ndi umboni wokhutiritsa wakuti Mulungu walankhuladi ndi anthu. Zowonadi, Mulungu anapereka uthenga wake kupyolera mwa anthu opanda ungwiro. Komatu chimenechi sichifukwa chokhulupirira kuti Baibulo silowona kusiyana ndi mmene ukanakhalira uthenga wapakamwa wochokera kwa Mulungu, kapena woperekedwa kupyolera mwa angelo, kapena wolembedwa kumwamba mozizwitsa kenaka nkuperekedwa kwa anthu padziko lapansi.
Komabe, kuvomereza magwero opatulika, kapena aumulungu a Baibulo kumaika thayo pa ife. Moyenerera Yehova amatiyembekezera kuŵerenga Mawu ake mokhazikika. (Salmo 1:1, 2) Kuŵerenga Baibulo kobala zipatso kumafuna kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wabwino. Munthuyo ayenera kukumbukira kuti Baibulo siliyenera kuŵerengedwa monga ngati kuti ndi bukhu wamba. Munthu ayenera kuliwona osati ‘monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu.’—1 Atesalonika 2:13.
Zinthu zina m’Baibulo zingakhale zovuta kuzimvetsetsa. Koma kupyolera m’kuŵerenga kobwerezabwereza, munthu amafikira pakumvetsetsa ndikupeza chithunzi chokwanira cha chifuniro cha Mulungu ndi zolinga zake. (Ahebri 5:14) Mwinamwake simunakhutiritsidwe kwenikweni kuti Baibulo ndi Mawu opatulika a Mulungu. Koma, kunena zowona, kodi mungasonyeze motani chikhulupiriro kapena kupanda chikhulupiriro m’Baibulo ngati simunaliphunzire mosamalitsa?
Mosasamala kanthu za kukaikira kwamakono ponena za magwero ake aumulungu, kulisanthula mosamalitsa Baibulo Lopatulika, kwapangitsa anthu ambiri olingalira kufuula mawu a mtumwi Paulo akuti: ‘Mulungu akhale wowona, ndimo anthu onse akhale onama’!—Aroma 3:4.
[Chithunzi patsamba 4]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Baibulo limapezeka tsopano ku 98 peresenti ya anthu okhala padziko lonse
Palibe bukhu lina lirilonse m’mbiri lomwe lafika pafupi ndi chiŵerengero cha kugaŵiridwa kwa Baibulo choyerekezeredwa kukhala 3,000,000,000. The New Encyclopædia Britannica ikulitcha “mwinamwake unyinji wa mabuku okhala ndi chisonkhezero chachikulu koposa m’mbiri ya anthu”
[Zithunzi patsamba 4]
Baibulo lapulumuka, pamene kuli kwakuti zolembedwa zina zachipembedzo zangokhala zinthu zakale za m’malo osungira zinthu zamakedzana
Pamwamba: Mbiri ya ku Asuri yonena za Chigumula
Kulamanja: Mapemphero opita kwa mulungu Wachiigupto Ra
[Mawu a Chithunzi]
Zonse ziŵiri: Mwachilolezo cha Trustees of The British Museum
[Chithunzi patsamba 5]
Lolembedwa ndi anthu osiyanasiyana okwanira 40 pa nyengo ya zaka 1,600, Baibulo limatsatira mutu umodzi waukulu kuyambira kuchiyambi mpaka kumapeto. Kokha munthu waluntha loposa la anthu wamba, wokhala ndi moyo wautali ndiye amene angapangitse chinthu chozizwitsa choterocho
[Chithunzi patsamba 5]
Kubuka kwa maulamuliro adziko kuyambira ya Babulo kupyola zaka mazana ambiri mpaka m’tsiku lathu kunalengezedwa mwaulosi m’Baibulo. (Danieli 2, 7, 8)
Kulamanja: Kaisara Augustus
[Mawu a Chithunzi]
Museo della Civiltà Romana, Roma
[Chithunzi patsamba 6]
Pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, Baibulo linaneneratu molongosoka za mikhalidwe yadziko yalerolino. (Mateyu 24, 25; Marko 13; Luka 21; 2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4; Chibvumbulutso 6:1-8) Kulongosoka kosalakwa kwa ulosi wa Baibulo kumatitsimikizira kuti lonjezo la Mulungu la dziko lapansi laparadaiso lidzakwaniritsidwadi
[Mawu a Chithunzi]
Reuters/Bettmann Newsphotos