Achichepere—Kodi Mudzapambana Chiyeso cha Kukhulupirika Kwachikristu?
“SUYENERA kuwona mayendedwe oipa kukhala kusakhulupirika. Ukungosanguluka basi. Zowona, umadziŵa kuti ngati makolo ako kapena akulu adziŵa, zikaŵakwiitsa ndi kuchititsa mavuto ochuluka. Koma pamene ukusanguluka, ungoyenera kuziiŵala zimenezo.”
Mnyamata yemwe wangogwidwa mawuyo ankachita dama mseri. Iye anakhala ndi moyo wapaŵiri, akumanyenga makolo ake ndi mpingo Wachikristu. Iye sanazindikire panthaŵiyo kuti anali kulephera chiyeso cha kukhulupirika Kwachikristu.
Zikwi zambiri za Akristu achichepere alephera ziyeso zofananazo za kukhulupirika. Ndipo nzosadabwitsa! Eya, Satana Mdyerekezi ‘akuchita nkhondo’ ndi anthu a Mulungu, kuchita zonse zimene angathe kuswa umphumphu wawo. (Chibvumbulutso 12:17) Iye makamaka wapanga achichepere chandamale cha “machitachita [ake] amachenjera.” (Aefeso 6:11, Kingdom Interlinear) Chotero kukhala wokhulupirika kumafuna kuyesayesa kwenikweni ndi kutsimikiza mtima.
Koma kodi kukhulupirika nchiyani? Mu Malemba Achihebri, liwu loyambirira lachinenerocho la “kukhulupirika” limasonyeza unansi wachikondi ndi munthu wokhala ndi cholinga m’malingaliro. (Salmo 18:25) Silimafotokoza chomangira chosalimba chimene chingasweke mosavuta koma unansi umene umakhala wokhazikika kufikira cholinga chake mogwirizana ndi munthuyo chitakwaniritsidwa. Mu Malemba Achigiriki, liwu loyambirira la chinenerocho la “kukhulupirika” liri ndi lingaliro la chiyero, chilungamo, kapena ulemu.
Chotero kukhulupirika kumaphatikizapo unansi wabwino ndi Mulungu. Aefeso 4:24 amatiuza kuti ‘nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa . . . m’chilungamo ndi m’chiyero cha chowonadi.’ Kodi mukufuna kukhala wokhulupirika kwa Yehova? Pamenepo muyenera kukulitsa unansi wokhulupirika ndi iye, chomangira chosakhoza kusweka, kutsimikiza mtima kumkondweretsa m’zochita zanu zonse. Muyenera kumamatira ku miyezo yolungama ya Yehova—mosasamala kanthu za mmene kungakhalire kokhumbirika kuchita mosiyana!
Zitsenderezo za Kukhala Wosakhulupirika
Moyamikirika, achichepere ambiri pakati pa Mboni za Yehova akuyesayesa kukhala okhulupirika, ndipo monga chotulukapo, amasangalala ndi chikumbumtima choyera. Komabe mtumwi Paulo analosera kuti mkati mwa “masiku otsiriza,” kusakhulupirika kukasonyezedwa ndi anthu mwachisawawa. (2 Timoteo 3:1, 2) Mochititsa chisoni, Akristu achichepere ena alola dziko iri losakhulupirika ‘kuŵapanikiza m’chikombole chake.’ (Aroma 12:2, Phillips) Kodi ndimotani mmene Satana wachitira zimenezi?
Chitsenderezo cha mabwenzi ndicho chiŵiya champhamvu cha Satana. Anthu ambiri amafuna kulingaliridwa bwino ndi ena, ndipo Satana amadziŵa bwino kugwiritsira ntchito chikhumbo chachibadwa chimenechi. Pofuna kuwonedwa abwino, Akristu achichepere ena aloŵa m’makambitsirano osayenera, mkhalidwe wachisembwere, kusuta, kuledzera—ngakhale kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa—zonsezi kufuna kukhala olandiridwa ndi mabwenzi awo.
Satana amafuna kuti ife ‘tidzisungire mogwirizana ndi zikhumbo za thupi lathu, tikumachita zinthu zofunidwa ndi thupi.’ (Aefeso 2:3, NW) Iye amadziŵa bwino mmene chikhumbo cha kugonana chimakhalira champhamvu mkati mwa “unamwali.” (1 Akorinto 7:36) Ndipo iye amafuna kuti mugonje ku zikhumbo zimenezo. Akristu achichepere ena mosadziŵa amaseŵerera m’manja mwake mwakuŵerenga mabuku, kuwonerera akanema, ndi mavideo zosonyeza maliseche kapena mwakuchita phyotophyoto. Kaŵirikaŵiri, zinthu zimenezi pambuyo pake, zimatsogolera kumachitachita oipitsitsa a kusakhulupirika. Kodi dziko la Satana ‘lakupanikizani m’chikombole chake’ m’mbali zina za izi?
Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri
Pamene kuli kwakuti kuchita choipa chachikulu chonga ngati dama mwaiko kokha ndinkhani yowopsa, achichepere ena amakulitsa mavuto awo. Iwo ali ngati “anthu opanda chowonadi,” otchulidwa m’Salmo 26:4, (NW) “amene amabisa zimene ali.” Achichepere otero amakhala ndi moyo wapaŵiri, kuchita m’njira ina pamene ali ndi makolo awo kapena Akristu ena achikulire ndi m’njira ina pamene ali ndi mabwenzi awo.
Komabe, kukhala ndi moyo wapaŵiri nkudzigonjetsa ndipo nkowopsa. Machitachita oipa osalamuliridwa nthaŵi zambiri amatsogolera ku machitachita ena oipitsitsa. Ndipo pamene kuli kwakuti chikumbumtima cha wina chingavutitsidwe poyamba, pamene wina aumirira kuchita zoipa, mpamene chikumbumtima chake chimalephera kuchitapo kanthu pa choipacho. Munthuyo m’lingaliro lenileni ‘angaleke kumva kupweteka’ kwa kuchita choipacho.—Aefeso 4:19, Kingdom Interlinear.
Panthaŵiyi kumakhala kovuta kwambiri kuulula choipa chake ndi kupeza chithandizo. Makamaka ichi chimakhala motero ngati Akristu achichepere ena akuphatikizidwa m’choipacho. Kaŵirikaŵiri pamakhala lingaliro la kukhulupirika kolakwika. Wachichepere wogwidwa mawu pachiyambi anafotokoza kuti: “Umazindikira chimene ukuchichita, ndipo umadziŵa kuti nchoipa. Kuti anthu ena ophatikizidwamo asaloŵe m’vuto, umavomereza kusauza aliyense.”
Koma pamene kuli kwakuti munthu ‘angabise zimene iye ali’ kwa makolo ake kapena ku mpingo, iye sangabisale kwa Yehova. ‘Palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.’ (Ahebri 4:13) Baibulo limatitsimikizira kuti: ‘Wobisa machimo ake sadzawona mwaŵi.’ (Miyambo 28:13) M’kupita kwanthaŵi choipacho chidzavumbulidwa. Munthu sanganyenge Yehova. Miyambo 3:7 imati: “Usadziyese wekha wanzeru; Opa Yehova, nupatuke pazoipa.” Kumbukiraninso kuti, “maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.”—Miyambo 15:3.
Wachichepere wotchulidwa papitapoyo, limodzinso ndi ena ophatikizidwa m’kuchita zoipa mseri, anapezedwa, ndipo iye ndi anzake anachotsedwa mumpingo Wachikristu. Pambuyo pake iwo anachira mwauzimu nabwezeretsedwanso. Chikhalirechobe, ndinjira yoipa chotani nanga yophunzirira tanthauzo la kukhulupirika!
‘Kuweruzana’ ndi Mulungu
Nanga bwanji ngati wina wasonyeza kale kusakhulupirika m’njira ina, mwinamwake mwakuchita choipa? Nkosavuta kudzipusitsa ndi kukana kufunika kwa kuwongolera nkhanizo. Wachichepere wina yemwe anachita dama mseri anati: “Ndinawonjezera uminisitala wanga wakumunda, ndikumalingalira kuti izi mwa njira ina zikaiŵalitsa choipacho.” Mtundu wopanduka wa Israyeli mofananamo unayesa kukondweretsa Yehova ndi nsembe. Koma Yehova anakana kudzipereka kwachinyengo koteroko. Iye anaŵalimbikitsa kuti: ‘Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa.’ Yehova akalandira nsembe zawo kokha iwo ‘ataweruzana naye.’ Zimenezo nzowonanso lerolino kwa aliyense yemwe angaloŵetsedwe m’kuchita choipa.—Yesaya 1:11, 15-18.
Munthu sangakhoze kuweruzana ndi Yehova mwakungodziŵitsa bwenzi lake. Chowona nchakuti, sinthaŵi zonse kuti mabwenzi amapereka chithandizo chabwino koposa, popeza kuti iwonso kaŵirikaŵiri samakhala ndi kuzoloŵera kokwanira m’moyo. Chofunika koposa, iwo sangakhululukire tchimo lanu. Mulungu yekha ndiye angatero. Chotero “tsanulirani mitima yanu” kwa iye mwa kuwaulula. (Salmo 62:8) Chinkana kuti mungachite manyazi ndi mkhalidwe wanu, tsimikizirani kuti Yehova ‘amakhululukira koposa.’—Yesaya 55:7.
Inu mudzafunikira chithandizo chowonjezereka. “Adziŵitseni makolo anu, adziŵitseni mofulumira akulu—pachiyambi penipeni,” Mkristu wachichepere yemwe anapindula ndi chithandizo chotero akulimbikitsa motero. Inde, makolo anu mwachiwonekere ali okhoza kukuthandizani. ‘Apatseni mtima wanu,’ kuŵadziŵitsa ukulu wonse wa mavuto anu. (Miyambo 23:26) Iwo angalinganize kuti inuyo mulandire chithandizo chowonjezereka kuchokera kwa akulu mumpingo pamene kuli kofunikira.—Yakobo 5:14, 15.
Kusonyeza Kukhulupirika Kowona—Motani?
Ndithudi, ndibwino koposa kusagweramo konse m’mkhalidwe wosakhulupirika. Salmo 18:25 limatiuza kuti: ‘Pa wachifundo [Yehova] mukhala wachifundo; pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.’ Yehova amadalitsa molemera awo omwe mokhulupirika amasunga miyezo yapamwamba ya makhalidwe.
Komabe, pali njira zina mmene kukhulupirika kwanu kungayesedwere. Mwachitsanzo, bwanji ngati bwenzi lanu latenga njira yopanduka. Kodi mudzalola kukhulupirika kwanu kolakwika kwa bwenzi lanulo kutsamwitsa kukhulupirika kwanu kwa Yehova? Chofunika kuchita ndikufikira bwenzilo ndi kulilimbikitsa kuulula nkhaniyo kwa makolo ake kapena kwa akulu. Liuzeni bwenzi lanulo kuti ngati silidzatero mkati mwa nyengo ya nthaŵi yoyenerera, inuyo mudzatero. Miyambo 27:5 imati: ‘Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.’ Mwakuthandiza bwenzi lanu m’njira imeneyi, mumasonyeza osati kokha kuwona kwa ubwenzi wanu komanso kuya kwa kukhulupirika kwanu kwa Yehova.
Mulimonse mmene chiyeso chingakhalire, nyonga yosonyezera kukhulupirika imachokera m’kukhala ndi unansi wolimba waumwini ndi Yehova. Pemphero latanthauzo ndi phunziro lakhama laumwini nzofunika ngati titi tisangalale ndi unansi wotero. Mokondweretsa, achichepere onse olakwa otchulidwa pachiyambi anavomereza kuti mapemphero awo ndi kuchita phunziro laumwini zinangokhala zizoloŵezi wamba—ndipo m’kupita kwanthaŵi zinalekeka. Yehova analeka kukhala weniweni kwa iwo, ndipo makhalidwe onyansa anatsatirapo. Kodi inu mukulimbitsa unansi wanu ndi Yehova, mwa pemphero ndi phunziro laumwini, kuti mukhalebe okhulupirika?
Zowonadi, nthaŵi zina mungalingalire kuti mwina mukuphonya kusanguluka. “Nthaŵi zina kumawoneka ngati kuti anthu akudziko akusanguluka,” anatero mkazi wina wachichepere. “Koma pamene muloŵerera mumkhalidwewo, mungakhoze kuwona kuti suli kusanguluka konse.” Iye analankhula chimene anakumana nacho, pokhala ataloŵa m’chisembwere chakugonana, chotulukapo kutenga pathupi ndi kutaya mimba. “Kukhala m’chowonadi ndichitetezo,” iye tsopano akutero—phunziro limene anaphunzira mwa njira yoipa. Salmo 119:165 limatikumbutsa kuti ‘akukonda chilamulo [cha Mulungu] ali nawo mtendere wambiri.’
Chotero, chitani changu kukhala wokhulupirika. Gwirani ntchito kukulitsa unansi wokhalitsa ndi Yehova. Danani nacho choipa ndipo mamatirani ku chabwino. (Aroma 12:9) Salmo 97:10 limatiuza kuti: ‘Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; aŵalanditsa m’manja mwa oipa.’ Inde, monga Mkristu wachichepere, mudzapindula ndi chitetezo cha Yehova ndi kusangalala ndi moyo wamuyaya ngati mupambana chiyeso cha kukhulupirika Kwachikristu.