Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/1 tsamba 7-8
  • Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtendere ndi Chisungiko Tsopano!
  • Mtendere ndi Chisungiko Padziko Lonse
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/1 tsamba 7-8

Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu

Chowonadi nchakuti, anthu sangathe konse kubweretsa mtendere weniweni, ndi wokhalitsa. Kulekeranji? Chifukwa chakuti anthu sindiwo akuswa mtendere enieniwo, ngakhale kuti nawonso ali ndi mbali m’liŵongo la mbiri yawo yokhathamira ndi mwazi. Wakuswa mtendere weniweni ali wamphamvu koposa anthu. Iye ndiye Satana Mdyerekezi, yemwe akulongosoledwa m’Baibulo kukhala “wonyenga wa dziko lonse.”​—Chibvumbulutso 12:9.

BAIBULO limati: ‘Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo [Satana].’ (1 Yohane 5:19) Chifukwa chake, kupeza mtendere weniweni ndi chisungiko chokhalitsa kuyenera kuloŵetsamo kuchotsedwapo kwa Satana pamodzi ndi dongosolo ladziko limene walipanga limene akulilamulira mowonekeratu. (Yerekezerani ndi Yesaya 48:22; Aroma 16:20.) Anthu sangathe kuchita chimenechi.

Pamenepa, kodi ndimotani mmene mtendere ndi chisungiko zingapezedwere? Mwa mphamvu ya Uyo amene ali wamphamvu zopanda polekezera kuposa Satana. Mulungu Wamphamvuyonse waika malire a nthaŵi ku ntchito za Satana pakati pa anthu. Pamene malire a nthaŵiyo adzafika, ‘chiwonongeko chadzidzidzi’ chidzafika pa dziko logona m’mphamvu ya Satana. (1 Atesalonika 5:3-7, NW) Umboni wonse umasonyeza kuti chimenechi chidzachitika posachedwapa.

Mtendere ndi Chisungiko Tsopano!

Komabe, bwanji ponena za tsopano? Mlingo wakutiwakuti wa mtendere weniweni ndi chisungiko uli wotheka ngakhale tsopano. Motani? Osati mmene atsogoleri achipembedzo ambiri ayesera, mwakudziloŵetsa m’ndale za dziko lino, koma, mmalomwake, mwakutsatira malamulo a Mulungu ndi uphungu wake.

Kodi njira yoteroyo imaperekadi mtendere? Inde, imatero. Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zayesa ndipo zapeza kuti kulidi kotheka kusangalala ndi mtendere weniweni limodzinso ndi mlingo wa chisungiko. Kutsatira malamulo a Mulungu monga momwe asonyezedwera m’Baibulo kwazitheketsa kugwirizana pamodzi monga gulu la mitundu yonse m’mtendere weniweni, mosasamala kanthu za fuko, mtundu, kapena chinenero chawo.​—Salmo 133:1.

Pomvera lamulo laumulungu, iwo mophiphiritsira ‘asula malupanga awo kukhala zolimira ndipo samaphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:2-4) Iwo amachimva chitetezo m’chikondi cha Mulungu ndipo ali ndi chidaliro chakuti abale awo auzimu amakhala ndi nkhaŵa yachisamaliro kulinga kwa iwo. (Aroma 8:28, 35-39; Afilipi 4:7) Ngati mukukaikira kuti kaya zimenezi nzowona, tikukupemphani kuwachezera pa Nyumba zawo Zaufumu ndikudziwonera nokha.

Mtendere ndi Chisungiko Padziko Lonse

Komabe, uku sindiko kukwaniritsidwa komalizira kwa lonjezo la Baibulo la mtendere weniweni ndi chisungiko. Kutalitali! Kwangokhala mbaliŵali ya chimene dzikoli lingakhale ngati aliyense atsatira malamulo a Mulungu. Posachedwapa mbaliŵali imeneyo idzakhala yeniyeni.

Mtumwi Paulo anati: “Pamene kuli kwakuti iwo [osatumikira Mulungu] akunena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ [akuganiza kuti pomalizira pake apeza mtendere ndi chisungiko m’njira yawoyawo] pamenepo chiwonongeko chadzidzidzi chidzaŵafikira modzidzimutsa.” (1 Atesalonika 5:3, NW) Mulungu adzawona kuti Satana wasokeretsa anthu kwa utali wokwanira. Tsopano idzakhala nthaŵi yakumchotsapo, pamodzi ndi dongosolo loipa la dzikoli lokhala m’mphamvu yake. Imeneyo idzakhala nthaŵi yakukwaniritsidwa kwa ulosi wa Danieli wakuti: ‘Masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.’​—Danieli 2:44.

Kodi zimenezi zidzakhala kachitidwe koipa ka Mulungu? Osati mpang’ono pomwe. Chiwonongeko chadzidzidzi chidzabwera kokha pa awo ochiyenerera malinga ndi chiweruzo cha Mulungu, miyezo ya Mulungu. Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Mlengi adzapereka chiŵeruzo cholungama m’nkhaniyi? Ndithudi tiyenera kusiya nkhaniyi mwachidaliro m’manja mwake! Ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo cha chiweruzo chake? Mwambi umati: ‘Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.’ (Miyambo 2:21, 22) Kodi munthu aliyense angachitire chisoni imfa ya woipa?

Popeza kuti wakuswa mtendere adzakhala atachotsedwapo, mtendere weniweni ndi chisungiko zidzakhala mkhalidwe wa anthu pa dziko lonse lapansi pansi pa ulamuliro wopindulitsa wa Ufumu wa Mulungu. ‘Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ (Yesaya 11:9) Kodi mukulikhulupirira lonjezo la Baibulo limeneli? Kodi muli ndi chidaliro kuti zinthuzi zidzachitika posachedwapa? Ngati muli ndi zikaikiro zirizonse, tikukulimbikitsani kuti musanthule nkhaniyi mwakuya. Kunena zowona, njira ya Mulungu ndiyo njira yokha imene munthu angachifikire chonulirapo cholakalakidwa kwa nthaŵi yaitalicho cha mtendere weniweni ndi chisungiko chowona.

[Zithunzi patsamba 8]

Anthu a Yehova amasangalala ndi mtendere weniweni ndi mlingo wabwino wa chisungiko lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena