Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera Kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Chimene Chilamulo cha Mose Chimatanthauza kwa Inu
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Chilamulo cha Kristu
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Ife Tiri Pansi pa Malamulo Khumi?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi ‘chabwino’ chimene Paulo sanathe kuchichita, chotchulidwa pa Aroma 7:19 chinali chiyani?

Kwenikweni, Paulo anali kutanthauza kulephera kwake kwakuchita zinthu zabwino zonse zofotokozedwa m’Chilamulo cha Mose. Zimenezo zinali zosatheka kwa Paulo ndi ena onse, kuphatikizapo ifeyo, chifukwa cha kupanda ungwiro ndi kuchimwa. Koma sitifunikira kutaya mtima. Nsembe ya Kristu inatsegula njira ya kukhululukidwa ndi Mulungu ndi kukhala ndi unansi wabwino ndi Iye.

Pa Aroma 7:19 timaŵerenga kuti: ‘Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.’ Mawu apatsogolo ndi apambuyo amasonyeza kuti Paulo kwenikweni ankalankhula za ‘chabwino’ m’lingaliro la zimene zinanenedwa m’Chilamulo. M’vesi 7 iye adati: ‘Kodi chilamulo chiri uchimo? Msatero ayi. Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire.’ Inde, Chilamulo chinasonyeza poyera kuti poti analephera kuchisunga mokwanira, anthu onse anali ochimwa.

Paulo anapitiriza kutchula kuti iye ‘kale anali wamoyo popanda chilamulo.’ Kodi nliti pamene zimenezo zinali choncho? Eya, pamene iye adali m’chuuno mwa Abrahamu Yehova asanapereke Chilamulocho. (Aroma 7:9; yerekezerani ndi Ahebri 7:9, 10.) Ngakhale kuti Abrahamu anali wopanda ungwiro, Chilamulo chinali chisanaperekedwe, chotero iye sanakumbutsidwe za kuchimwa kwake mwakulephera kusunga malamulo ake ambirimbiri. Kodi chimenechi chimatanthauza kuti pamene Chilamulo chinaperekedwa ndi kusonyeza kupanda ungwiro kwa munthu, icho chinapereka zotulukapo zoipa? Ayi. Paulo anapitiriza kuti: ‘Chotero chilamulo chiri choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.’​—Aroma 7:12.

Onani kuti Paulo analongosola Chilamulo kukhala ‘choyera’ ndi ‘chabwino.’ M’mavesi otsatira, anafotokoza kuti ‘chabwino’​—Chilamulocho​—chinasonyeza poyera kuti iye anali wochimwa, ndipo tchimo limeneli linamyeneretsa imfa. Paulo analemba kuti: ‘Chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m’kati mwanga ndiwo.’​—Aroma 7:13-20.

Pamenepa, m’mawu apambuyo ndi apatsogolo ameneŵa, Paulo sanali kulankhula za ubwino wachisawawa, kapena machitidwe wamba akukoma mtima. (Yerekezerani ndi Machitidwe 9:36; Aroma 13:3.) Iye makamaka anali kunena za kuchita (kapena kusachita) zinthu zimene zinali zogwirizana ndi Chilamulo chabwino cha Mulungu. Poyamba adali wokangalika m’chipembedzo Chachiyuda ndipo​—pomyerekeza ndi ena​—iye anali “wosalakwa.” Komabe, ngakhale kuti m’maganizo mwake anali kapolo wachikumbumtima ku Chilamulo chabwino chimenecho, iye sanachilabadire mokwanira. (Afilipi 3:4-6) Chilamulo chinasonyeza miyezo yolungama ya Mulungu, kusonyeza mtumwiyo kuti m’thupi lake iye adaali kapolo ku lamulo la uchimo motero anayenerera imfa. Komabe, Paulo anali woyamikira kuti mwa nsembe ya Kristu analengezedwa wolungama​—womasulidwa ku lamulo la uchimo ndi mphoto yake yoyenerera, chilango cha imfa.​—Aroma 7:25.

Akristu lerolino sali pansi pa Chilamulo cha Mose, chifukwa chakuti icho chinakhomeredwa pa mtengo wozunzirapo. (Aroma 7:4-6; Akolose 2:14, NW) Komabe, tichita bwino kuzindikira kuti icho sichinali chilamulo chothodwetsa chosafunika kuchilingalira konse. Ayi, kwakukulukulu Chilamulocho chinali chabwino. Motero tiyenera kuŵerenga mabuku a m’Baibulo okhala ndi Chilamulocho ndi kuphunzira zimene chinafunikiritsa Aisrayeli. Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zidzakhala zikuchita chimenecho posachedwapa, mwakuwerenga kwawo Baibulo kwa mlungu ndi mlungu.

Pamene tikuŵerenga Chilamulo, tiyenera kulingalira pa miyezo yabwino yokhala kumbuyo kwa malamulo ake osiyanasiyana ndi pa mapindu amene anthu a Mulungu anapeza pamene anayesayesa kutsatira malamulo abwino amenewo. Tiyenera kuzindikiranso kuti, ndife opanda ungwiro, motero sititha kutsatira ndendende ubwino umene timaphunzira m’Mawu a Mulungu. Koma pamene tikulimbana ndi lamulo la uchimo, tikhoza kusangalala ndi chiyembekezo cha kuwonjoledwa kupyolera mwa kugwiritsiridwa ntchito kwa nsembe ya Kristu kulinga kwa ife.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena