Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
YEHOVA ndiye Mulungu amene amayankha mapemphero. Kwenikwenidi, Mawu ake, Baibulo, amamutcha kukhala “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Iye ali wofunitsitsa kuyankha mapemphero. Koma kodi ndimapemphero ayani amene iye amawayankhadi?
Mulungu amayankha mapemphero a anthu omwe amamkondweretsa. Iwo ali ndi kaimidwe kamaganizo kaulemu ka wamasalmo yemwe anati: ‘Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba inu, Mulungu. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo.’ (Salmo 42:1, 2) Komabe, kodi pali umboni wotani wakuti Yehova amayankha mapemphero a olambira ake owona?
Umboni Wakuti Mulungu Amayankha Mapemphero
Baibulo liri ndi cholembedwa chachikulu chotsimikizira kuti Yehova amayankha mapemphero a atumiki ake okhulupirika. Mwachitsanzo, pamene Mfumu Yehosafati wa Yuda anapempherera chilanditso, Mulungu anayankha pemphero lake nampatsa chilakiko mwakuchititsa adani ake kuphana okhaokha. (2 Mbiri 20:1-26) Mofananamo pamene Mfumu Hezekiya anayang’anizana ndi gulu lankhondo lamphamvu, modzichepetsa anapempha chithandizo kwa Mulungu. Hezekiya anawona chipulumutso cha Yehova pamene mngelo anakantha Asuri okwanira 185,000 usiku umodzi.—Yesaya 37:14-20, 36-38.
Kodi nchifukwa ninji Mulungu anayankha mapemphero amenewo? M’zochitika zonse ziŵiri, mafumuwo anachonderera kuti kulephera nkhondoyo kukanyazitsa dzina la Yehova. (2 Mbiri 20:6-9; Yesaya 37:17-20) Iwo anali odera nkhaŵa ndi dzina lake. “Cholinga chachikulu cha pemphero sindicho ubwino wokha wa wopemphayo koma ulemu wa dzina la Mulungu,” imatero The International Standard Bible Encyclopedia. Chotero, atumiki okhulupirika a Yehova angakhale otsimikizira kuti iye adzawathandiza ‘chifukwa cha dzina lake.’ Cholembedwa chotsimikizira kuti mapemphero otero ayankhidwa chimapereka chidaliro kwa anthu a Mulungu chakuti iye amamva mapemphero awo.—Salmo 91:14, 15; 106:8; Miyambo 18:10.
Komabe, ngakhale ngati chochitika chikuloŵetsamo dzina la Yehova, Mulungu amasankha kaya kuyankha mapemphero ena kapena ayi. Iye angakhale ndi zifukwa zabwino zosayankhira mapemphero ena. Ngati timalingalira kuti mapemphero athu sakumvedwa, nkwabwino kulingalira chifukwa chake zingakhalire tero.
Chifukwa Chake Mapemphero Ena Samayankhidwa
‘Pochulukitsa mapemphero anu ine sindidzamva,’ Yehova nthaŵi ina anauza Aisrayeli motero. Posonyeza chifukwa chake, iye anapitiriza kuti: “Manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Kodi ndimotani mmene wina angakhalire ndimwaŵi wakumvedwa pamene amanyalanyaza lamulo la Yehova? Mwambi wa m’Baibulo umapereka yankho lomvekera bwino, kumati: ‘Wopeŵetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.’—Miyambo 28:9.
Baibulo limapereka chifukwa china chimene mapemphero ena samamvedwa, pamene limati: ‘Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.’ (Yakobo 4:3) Ayi, Yehova sadzayankha mapemphero ofuna kukhutiritsa zilakolako zoipa. Tiyeneranso kukumbukira kuti Mulungu samalamulidwa ndi anthu. Iye ali Amene amasankha mmene adzayankhira mapemphero athu.
Mapemphero otsimikizira kuyankhidwa ndi aja omwe amapita kwa Mulungu kuchokera mumtima wabwino, wokhala ndi cholinga choyenera, ndipo mwanjira yake yoikika—kupyolera mwa Yesu Kristu. (Yohane 14:6, 14) Komabe ngakhale aja amene mapemphero awo amafitsa ziyeneretso zoterozo nthaŵi zina amalingalira kuti sakumvedwa. Kodi nchifukwa ninji Mulungu sakayankha nthaŵi yomweyo mapemphero ena a atumiki ake?
Yehova amadziŵa nthaŵi yabwino koposa yakuyankha mapemphero. Ngakhale kuti mnyamata angafune njinga, atate wake sangamgulire kufikira mwanayo atakula kwakuti akhoza kuyendetsa bwino. Zimenezi zingakhale zowona ndi mapemphero a aja amene amakonda Mulungu. Podziŵa zimene ziri zabwino koposa kwa iwo, iye amapereka zimene ziri zofunika panthaŵi yoyenera koposa.
Komabe, atumiki a Yehova samalandira zonse zimene angazipempherere. Pokhala opanda ungwiro, iwo angafune zinthu zomwe sizingakhale zabwino kwa iwo. Atate wawo wakumwamba wachikondi sakawapatsa chirichonse chovulaza, popeza ali Mpatsi wa ‘mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chirichonse changwiro.’ (Yakobo 1:17) Mofananamo, Mulungu sakhoza kupereka chinthu chimene chiri chosafunika m’lingaliro lake. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 12:7-10.) Iye amayankha mapemphero mogwirizana ndi chifuniro chake ndi chifuno kaamba ka anthu ake.—1 Yohane 5:14, 15.
Yesu “Anamvedwa Moyanjidwa”
Yesu Kristu anali munthu wopemphera. (Mateyu 6:9-13; Yohane 17:1-26) Iye anali ndi chidaliro chotheratu chakuti Atate wake wakumwamba akamva ndi kuyankha mapemphero ake. Panthaŵi ina Yesu anati: ‘Atate . . . ndadziŵa ine kuti mumandimva ine nthaŵi zonse.’ (Yohane 11:41, 42) Koma kodi Yesu sanagwiritsidwe mwala pamapeto amoyo wake wapadziko lapansi? Kodi iye sanalire mofuula kuti: ‘Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiiranji ine?’—Mateyu 27:46.
Pamene Yesu ananena mawu amenewo, iye mwachiwonekere anali kukwaniritsa ulosi wonena za imfa yake. (Salmo 22:1) M’lingaliro lokhala ndi malire, Yesu angakhale anatanthauzanso kuti Yehova anachotsa chitetezo chake ndi kulola Mwana wake kufa imfa yoŵaŵa ndi yochititsa manyazi kotero kuti ayese umphumphu wake kotheratu. Kupenda zochitika patsiku lomalizira la moyo wapadziko lapansi wa Yesu kumasonyeza kuti Mulungu anamva mapemphero ake.
Usiku umene anagwidwa, Yesu anapemphera m’munda wa Getsemane. Kwanthaŵi zitatu iye anachonderera kuti: ‘Atate, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire ine; koma simonga ndifuna ine, koma inu.’ (Mateyu 26:39, 42, 44) Yesu sanali kuzengereza kupereka moyo wake monga dipo la anthu okhulupirika. Ayi, koma iye mwachiwonekere anali wodera nkhaŵa kwambiri ndi kuthekera kwa kusalemekeza Atate wake okondeka koposa mwakufera pa mtengo wozunzirapo monga wamwano wotembereredwa. Kodi Yehova anamva pemphero la Yesu?
Zaka zambiri pambuyo pake, mtumwi Paulo analemba kuti: ‘M’masiku a thupi lake [Kristu, NW] anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo [anamvedwa moyanjidwa, NW] popeza anaopa Mulungu.’ (Ahebri 5:7; Luka 22:42, 44) Inde, pausiku woŵaŵitsa imfa yake isanachitike, Yesu “anamvedwa moyanjidwa.” Koma kodi ndimotani?
Yehova anatumiza mngelo yemwe ‘anamuwonekera [Yesu] namlimbitsa iye.’ (Luka 22:43) Polimbitsidwa motero, Yesu anali wokhoza kuyang’anizana ndi imfa pa mtengo wozunzirapo. Mwachiwonekere, Yehova anampatsa chitsimikizo chakuti imfa yake pa mtengopo sikadzetsa chitonzo pa dzina laumulungu koma kuti m’kupita kwanthaŵi ikagwiritsiridwa ntchito kuliyeretsa. Ndithudi, imfa ya Yesu pa mtengo wozunzirapo inatsegula njira kwa Ayuda, amene anali otembereredwa pansi pa Chilamulo, kuti apulumutsidwe ku chiweruzo cha imfa.—Agalatiya 3:11-13.
Masiku atatu pambuyo pake, Yehova anamuukitsa Yesu ndi kumchotsera chinenezo chirichonse chothekera cha kuchitira mwano mwakumkwezera pamalo okwezeka kumwamba. (Afilipi 2:7-11) Ha, ndinjira yodabwitsa chotani nanga yoyankhira pemphero la Yesu lonena za ‘chikho ichi’! Pemphero limenelo linayankhidwa m’njira ya Yehova. Ndipo Yesu anasangalala ndi madalitso abwino chifukwa chakuti anauza Atate wake wakumwamba kuti: ‘Koma sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.’—Luka 22:42.
Mmene Yehova Amayankhira Mapemphero Lerolino
Mofanana ndi Yesu, aja omwe amafuna kukondweretsa Yehova lerolino ayenera nthaŵi zonse kupempha kuti chifuniro cha Mulungu chichitike. Iwo ayenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzayankha mapemphero awo mwanjira imene idzaŵapindulitsa koposa. Kwenikwenidi, iye ‘adzachita koposaposatu zonse zimene azipempha, kapena aziganiza.’—Aefeso 3:20.
Mkazi wachichepere Wachikristu amene ankakhala ndi makolo ake osakhulupirira anawona chowonadi cha lembali. M’kalata yochokera ku Watch Tower Society, anapemphedwa kulingalira mwapemphero kuthekera kwa kulandira ntchito yapadera yaumishonale. Ngakhale kuti chikhumbo chake chinali chakukhala kunyumba kuthandiza makolo ake kukhala Akristu, iye anapempha Mulungu m’pemphero kuti: “Kodi chifuniro chanu nchiyani? Kodi ndicho kulandira chiitano ichi mosasamala kanthu za kutsutsa kwa makolo anga, kapena kodi ndicho kuthandiza makolo anga mwakupitiriza kukhala nawo?” Nthaŵi iriyonse pamene anapemphera, chikumbumtima chake chinamuuza kulandira chiitanocho. Iye anaganiza kuti limenelo linali yankho lochokera kwa Yehova.
Mulungu anamlimbikitsa mkaziyu kumamatira ku chosankha chake. Pamene anapemphedwa kupita ku Chisumbu cha Awaji, ku Japani, makolo ake anadabwa ndipo anakulitsa chitsutso chawo. Komabe, pokhala osakhoza kumtsimikizira kusintha malingaliro ake, amayi wake anasankha kuphunzira Baibulo kokha kuti awone chifukwa chake mwana wawo wamkazi anapanga chosankha chimenecho. Miyezi itatu pambuyo pake makolo akewo anamchezera. Powona mmene anasamaliridwira bwino ndi Mboni zina za Yehova, atate wake anakondweretsedwa kwambiri nalira pamene anatsala okha. Posakhalitsa nawonso anayamba kuphunzira Baibulo. M’kupita kwanthaŵi makolo a mkazi wachichepereyu anabatizidwa nayamba kutumikira Yehova mokhulupirika. Kodi Yehova Mulungu sanadalitse mkazi Wachikristu ameneyu koposaposatu?
Mapemphero Awo Amayankhidwa
Kodi mukukumbukira mawu a mkazi wotchulidwa kuchiyambi kwa nkhani yapitayo? Iye sanadzimve kuti mapemphero ake amayankhidwa. Komabe, pambuyo pake anazindikira kuti Mulungu anali kuyankha mapemphero ake. Mkaziyu anasunga cholembedwa cha mfundo zazikulu za mapemphero ake. Tsiku lina iye anayang’ana m’bukhu lamanotsi nawona kuti Yehova anamva mapemphero ake ambiri, ngakhale ena amene mkaziyo anawaiŵala! Chotero iye anadziŵa kuti Mulungu ankamsamalira ndi kuyankha mapemphero ake m’njira yachifundo imene inampindulitsa koposa.
Ngati mukulingalira kuti mapemphero anu sakuyankhidwa, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndiri ndi unansi waumwini ndi Yehova, “Wakumva pemphero”? Ngati ayi, kodi ndikuchita chirichonse kuti ndiphunzire ponena za iye ndi kukhala mmodzi wa atumiki ake odzipereka?’ Iye amayankha mapemphero a aja amene amamkonda ndi kuchita chifuniro chake. Iwo ‘amalimbika chilimbikire m’kupemphera’ ndipo amamvedwa moyanjidwa, monga momwe zinaliri ndi Yesu. (Aroma 12:12) Chotero, “tsanulirani mitima yanu” kwa Yehova ndipo chitani chifuniro chake. (Salmo 62:8) Pamenepo mapemphero anu adzamvedwa.
Lerolino, mamiliyoni a anthu akupempherera chinthu chinachake chapadera. Inde, ndipo mapemphero awo akumvedwa. Tiyeni tiwone chifukwa chake tingakhale otsimikiza kuti mapemphero otero adzayankhidwa.