Mafanizo—Mfungulo ya Kufikira Mitima
DAVIDE wakhala akuthaŵathaŵa kuti apulumutse moyo wake. Mdani wake ndi Sauli, mfumu yodzozedwa ya Israyeli. Komabe, Sauli ndimwamuna wokhala ndi udani waukulu kwa Davide, ndipo ali wodzala ndi kaduka. Chifukwa cha mbanda yake, mfumuyo tsopano yabwera ndi asirikali 3,000. Popeza kuti apambanidwa m’chiŵerengero, Davide ndi amuna ake abisala mkati mwenimweni mwa phanga m’chipululu.
Pamene Davide ndi amuna ake aunjikana pamodzi mumdima, pakuchitika zozizwitsa. Mfumu Sauli akuloŵa m’phanga limeneli kuti adzithandize. Davide ali ndi chida m’dzanja, akuŵenderera mdani wake wopanda thandizoyo. Koma zikuwadabwitsa amuna a Davide, kuti iye sakuipha mfumuyo. Iye wangodula mkawo wa mwinjiro wa Sauli. Pochita chisoni ngakhale ndi chimenechi, Davide akunena kuti: ‘Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.’—1 Samueli 24:1-6.
Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imapereka phunziro lalikulu ponena za ulemu kaamba ka ulamuliro wopatsidwa ndi Mulungu. Imafikiranso mtima, mwinamwake ngakhale mogwira mtima kuposa uphungu wachindunji. Imeneyo ndiyo mphamvu ya nkhani zolembedwa m’Mawu a Mulungu kaamba ka kutiphunzitsa.—Aroma 15:4.
Moyenerera, Mboni za Yehova zimayesayesa kuchita zoposa kungolankhula zenizeni polalikira mbiri yabwino, pochititsa maphunziro Abaibulo apanyumba, popereka nkhani Zamalemba, kapena pochitira umboni wamwamwaŵi. Izo zimayesa kufikira mitima mwakusimba zokumana nazo ndikugwiritsira ntchito mafanizo. Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki limafotokoza kuti: “Mafanizo amasonkhezera chikondwerero ndipo amagogomezera malingaliro ofunika. Iwo amasonkhezera mphamvu zoganiza za munthu ndipo amapangitsa kukhala kosavuta kwambiri kumvetsera malingaliro atsopano. [Mafanizo osankhidwa bwino amakopa malingaliro ndi kuwasonkhezera.] . . . Nthaŵi zina, fanizo lingathe kugwiritsiridwa ntchito kupeŵa maganizo oipitsidwa.”a—Tsamba 168.
M’bukhu lake lakuti Essentials of Public Speaking, Warren DuBois akunena kuti: “Ngati wolemba kapena wolankhula alongosola malingaliro ake kupyolera m’zochitika kapena mawu a anthu, ngakhale nkhani yosasangalatsa kwenikweni imatentha ndi kukoma.” Chotero, kupangitsa uthenga wokopa kale ndi wopatsa moyo kukhala wotentha ndi wokoma kuli kotsimikizirika kuthandiza aminisitala Achikristu kufikira mitima.
Mafanizo Amene Amaphunzitsa
Kodi ndimafanizo a mtundu wotani amene amagwira ntchito koposa? Kaŵirikaŵiri, ndiamene amazikidwa pa chinthu chimene omvetsera angachidziŵe mosavuta. Yesu Kristu anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’zimenezi. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu analankhula ponena za zinthu zofala monga mchere, nyali, ndi mbalame. (Mateyu 5:1–7:29) Mwachitsanzo, aliyense anali wozoloŵerana ndi nyali zimene zinayaka ndi mafuta a azitona ndi zimene nthaŵi zina zinaikidwa pa choikapo chake. Chifukwa chake, ophunzira a Yesu ayenera kukhala anazindikira kuti iwo anayenera kukhala owalitsa kuunika kwauzimu pamene anawauza kuti: ‘Sayatsa nyali, ndi kuivundikira m’mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m’nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa kumwamba.’ (Mateyu 5:15, 16) Mafanizo osavuta amene amayenerera nkhani adzathandiza aminisitala Achikristu kumveketsa malingaliro ndi ziphunzitso za Baibulo.
Mwinamwake mafanizo amphamvu koposa a Yesu ananena za anthu. Talingalirani olembedwa mu Luka mitu 15 ndi 16. Alembi ndi Afarisi adamsuliza Yesu chifukwa chakulandira ochimwa ndi osonkhetsa msonkho. Poyankha, iye anasimba nkhani zofokotoza anthu. Iye analankhula za mbusa amene anapeza nkhosa yake yotaika, mkazi amene anapeza kobiri lotaika, mwana woloŵerera amene anabwerera kunyumba, ndi mdindo wosalungama.
Mafanizo a zinthu ndi zokumana nazo zenizeni angakhale othandiza kwambiri kwa minisitala Wachikristu. Mwachitsanzo, onani mmene Alexander H. Macmillan, yemwe anayenda kwambiri monga wokamba nkhani zapoyera kwa zaka 60, analongosolera chowonadi cha Baibulo ponena za akufa. Patatsala nthaŵi yochepa kuti atate ake amwalire, omwe anakhulupirira kuti moyo sukhoza kufa, Macmillan anakambitsirana motere ndi atate wake:
“Atate anandifunsa funso lachindunji lakuti: ‘Mwananga, kodi ndidzakhala wosukidwa m’manda pamene ndidzakhala ndikuyembekezera ufumu wakumwamba kuyamba ntchito yake yakudzaza dziko lapansi ndi ungwiro?’
“Limenelo linali funso limene mwamuna wachichepere sakanatha kuliyankha mofulumira kuti akhutiritse wokalamba amene sanaganizirepo za nkhani imeneyo.
“Poyankha ndinawafunsa kuti: ‘Atate, kodi munagona tulo tabwino usiku wapita?’
“Iwo anayankha kuti, ‘Inde mwananga, ndinagonadi bwino pambuyo popatsidwa mibulu yogoneka ndi dokotala.’
“‘Kodi munasukidwa pamene mudali m’tulo?’
“‘Ayi, sindinatero. Ndikulakalaka kuti nkanamagona nthaŵi yonse, popeza kuti sindimamva kupweteka.’”
Ndiyeno A. H. Macmillan anaŵerengera atate ake Yobu 14:13-15 ndi 3:17-19 ndi kunena kuti: “Mwawonatu atate, akufa ali m’tulo ta imfa ndipo sadziŵa kanthu pamene ali mumkhalidwe umenewo, choncho ndimotani mmene angasukidwire?”
Ha, ndikaphunzitsidwe kogwira mtima kotani nanga! Ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, nanunso mukhoza kugwiritsira ntchito malemba ndi mafanizo kuti mukope maganizo ndi mtima.
Kupeza Mafanizo
Koma kodi nkuti kumene mungapeze mafanizo ogwira mtima kapena zokumana nazo zenizeni za m’moyo? Zambiri zingatengedwe m’nkhokwe yanu ya zokumana nazo zaumwini. Mwachitsanzo, kodi mumafuna kufotokoza mwafanizo madalitso a chikhulupiriro, mphamvu ya pemphero, kapena chisangalalo cha uminisitala? Ngati ndinu Mkristu wodzipereka, mwachidziŵikire mukhoza kusimba zochitika zosiyanasiyana m’moyo wanu. Mwina mukhoza kumva zokumana nazo zabwino pamisonkhano yampingo kapena polankhula ndi Akristu anzanu. Kapena mukhoza kuŵerenga chokumana nacho cholimbikitsa mu Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Kwenikweni, Watch Tower Publications Index imatsogoza ku zokumana nazo zolembedwa za padziko lonse.
Kodi ndimotani mmene mungasimbire chokumana nacho mogwira mtima? Chenicheni nchakuti, kukhala wokhoza kuwoneratu kumakuthandizani kugwira chisamaliro cha omvetsera anu. Mukhoza kuyamba chokumana nacho ndi mawu akuti: “Mpainiya wina anadziwonera yekha mmene Yehova amadalitsira amene amamkhulupirira.” Mwamsanga, omvetsera anu amazizwa kuti ndimadalitso otani amene mlengezi wa Ufumu wanthaŵi zonseyo anasangalala nawo. Khalani wotsimikiza kuwauza iwo.
Yesani kusimba chokumana nacho m’mawu anuanu. Perekani tsatanetsatane, pakuti kutero kumakhala ndi chisonkhezero ku nkhaniyo. Mwakupereka chithunzi chabwino cha mikhalidwe yoloŵetsedwamo, mukhoza kusonkhezera omvetsera anu mosavuta. Koma samalani kuti simuloŵeratu m’kusimba nkhani moti iwo nkulephera kuwona chifukwa chimene mukusimbira chochitikacho. Ndiponso, peŵani kuwonjezera, popeza kuti ngakhale ngati iko kungawonjezere kukondweretsa kwa nkhani yanu, kukhoza kudodometsa kudalirika kwanu. Kaamba ka chifukwa chofananacho, peŵani kusimba nkhani kapena zokumana nazo zamphekesera zimene simungazitsimikizire.
Kupangitsa Baibulo Kusimba Zenizeni
Zokumana nazo zophunzitsa koposa zimapezeka m’Baibulo lenilenilo. Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti mufuna kusonyeza wophunzira wa Baibulo kapena gulu kuti ana akhoza kutenga kaimidwe kumbali ya Yehova Mulungu. Mungasankhe kugwiritsira ntchito nkhani ya buthu losatchulidwa dzina limene linalankhula kwa mkazi wa Namani ponena za Elisa mneneri wa Yehova. Choyamba, ŵerengani nkhaniyo pa 2 Mafumu 5:1-5. Ndiyeno mukhoza kufunsa kuti: “Kodi muganiza kuti kunali kovuta motani kwa buthu limeneli kusunga umphumphu wake kwa Mulungu m’dziko la kulambira konama? Kodi sizinalire kulimba mtima kwa iye kuti akhoze kulankhula mokhutiritsa ponena za Yehova ndi mneneri wake?”
Kufufuza kwapasadakhale kukhoza kukuthandizani kupangitsa nkhaniyo kukhala yeniyeni. Mukhoza kupeza chidziŵitso chothandiza pansi pa NAAMAN, SYRIA, ndi ELISHA mu Watch Tower Publications Index. Zilozero za m’danga mu New World Translation of the Holy Scriptures zikhoza kukutsogolerani kuchokera ku nkhani ya mu 2 Mafumu kumka ku Salmo 148:12, 13, pamene timaŵerenga kuti: ‘Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndilokwezeka; Ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.’ Ha, nchilimbikitso chotani nanga kwa achichepere kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima!—Machitidwe 4:29-31.
Ngati ndinu minisitala Wachikristu, ‘perekani chisamaliro chosalekeza ku chiphunzitso chanu’ m’nkhani imeneyi. (1 Timoteo 4:16, NW) Musamangochinena chowonadi—chifotokozeni mwafanizo. Pangitsani nkhani za m’Baibulo kuwoneka m’chithunzi chamalingaliro ndikukhala zatanthauzo. Gwiritsirani ntchito zokumana nazo ndi mafanizo oyenerera. Izi ndizo njira zofikira mtima.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 29]
Mofanana ndi Yesu, aminisitala Achikristu amakono akhoza kugwiritsira ntchito mafanizo owonekera kuti apereke uthenga wawo ndi kufikira mitima