Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi banja Lachikristu liyenera kuchitanji ngati mwana wawo ayenera kumapita kusukulu kumene maphunziro achipembedzo ali okakamiza?
Makolo Achikristu samafuna kuti ana awo aphunzitsidwe chipembedzo chonyenga. Koma pangakhale mikhalidwe imene ana sangakane kukhala m’kalasi mmene akuphunzitsa chipembedzo, ngakhale kuti sangakhale ndi phande m’machitachita kapena madzoma achipembedzo chonyenga.
Abrahamu bwenzi la Mulungu anapereka chitsanzo chabwino ponena za kuphunzitsa ana zachipembedzo. Iye analerera ana ake m’Kanani, kumene anali ozingidwa ndi zolakwa zachipembedzo ndi machitachita “opatulika” onyansa. (Yerekezerani ndi Eksodo 34:11-15; Levitiko 18:21-30; Deuteronomo 7:1-5, 25, 26; 18:9-14.) Komabe, iye anali magwero a maphunziro achipembedzo kwa banja lake. Mulungu anali ndichidaliro kuti Abrahamu ‘akalamulira ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo.’—Genesis 18:19.
Monga wachichepere, Yesu nayenso anapindula ndi malangizo abanja ndi ampingo a kulambira kowona. Chotero, iye ‘anakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.’—Luka 2:52.
M’mbali zambiri padziko lapansi, achichepere Achikristu amalandira malangizo akudziko kusukulu za onse. Sizonse zimene zimaphunzitsidwa kumeneko zimene ziri zogwirizana kotheratu ndi chowonadi cha Baibulo ndi zenizeni zotsimikizirika. Mwachitsanzo, mibadwo yambiri ya achichepere Achikristu anapezekapo pamakalasi a sayansi ndi biology monga mbali ya kuphunzira kwawo kwanthaŵi zonse. Chotero ambiri a iwo adziŵa nthanthi zofala za chisinthiko ndi malingaliro olinganako onena za kuyambika “kwachibadwa” kwa moyo padziko lapansi.
Komabe, kudziŵako sikunapangitse achichepere Achikristu ameneŵa kumamatira ku chisinthiko chopanda umulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti panyumba ndi ku misonkhano Yachikristu, iwo anali atalandira kale chidziŵitso cholongosoka chozikidwa pa Mawu ouziridwa a Mulungu, chomwe chinathandiza kuzoloŵeretsa ‘zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:14) Makolo ambiri anaphunzira ndi ana awo kufotokozedwa kolinganizika kwa chisinthiko m’bukhu lolimbitsa chikhulupiriro la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?a Pokhala okonzekera motero, ana opita kusukulu ameneŵa sanavomereze malangizo achisinthiko a m’kalasi kukhala ofunika kukhulupiriridwa. Komabe anali okhoza kusonyeza m’mayankho awo ndi m’mayeso kuti anali kumvetsera ndikuti akhoza kuphunzira tsatanetsatane woperekedwayo. Ena anali ndi mwaŵi wakufotokoza malongosoledwe osiyana mogwirizana ndi mfundo zoperekedwa m’Baibulo ndi Mlengi wa anthu.—1 Petro 3:15.
Komabe, bwanji nanga za nthaŵi yakalasi yoperekedwa kuphunzira za chipembedzo chotchuka chakumaloko kapena ngakhale chipembedzo mwachisawawa?
Nkosatheka kuti maphunziro oterowo angaperekedwe mwauchete, monga mawu wamba. Mphunzitsiyo angakhale ali wa chipembedzo chimenecho ndipo chotero angayese kusonkhezera maganizo ndi mitima ya ophunzira. Chotero Mboni za Yehova zimakonda kuti ana awo apatulidwe m’makalasi olangiza zachipembedzo. Ichi chingatheketse ana awo kugwiritsira ntchito nthaŵi yasukulu mopindulitsa kwambiri kumaliza maasainimenti a makalasi ena kapena kuphunzira mulaibulale yasukulu.
Komabe, m’malo ena mapempho oterowo anakanidwa; sukuluyo kapena ngakhale akuluakulu akudziko angafune kuti ana onse apezekepo ndikumaliza kosi yachipembedzo kotero kuti akamalize maphunziro. Banja lirilonse liyenera kusankha palokha zimene likachita m’chochitika choterocho.
Atumiki ena a Mulungu mosadzifunira okha anakhala m’mikhalidwe imene anafunikira kupirira kuyang’anana ndi ziphunzitso kapena machitachita achipembedzo pamene anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu wowona. Mwachidziŵikire ndimo mmene zinaliri kwa Mose. Iye analeredwa monga mdzukulu wa Farao wa ku Igupto, ndipo “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto.” (Machitidwe 7:20-22) Mwinamwake zimenezo zinaphatikizapo kumlingo wakutiwakuti zikhulupiriro ndi machitachita achipembedzo ofala m’Igupto. Koma Mose anachinjirizidwa ndi malangizo apamwamba omwe mwachidziŵikire analandira ku banja lake ndipo mwina kwa Ahebri ena.—Eksodo 2:6-15; Ahebri 11:23-26.
Talingaliraninso chitsanzo cha Ahebri achichepere atatu, mabwenzi a Danieli, omwe analandira malangizo apadera m’Babulo ndipo anaikidwa kukhala antchito aboma. (Danieli 1:6, 7) Iwo analibe ufulu wakuchita kapena kukana chimene anafuna. Panthaŵi ina Mfumu Nebukadinezara analamula kuti asonkhane ndi nduna zina pa chifano chagolidi chimene anachiimika m’chigwa cha Dura, kumene machitidwe a kupembedza kwautundu akachitikira. Kodi Ahebri atatuwo anachita motani? Tingatsimikize kuti akanakonda kusapitako, koma zimenezo zinali zosatheka.b Komabe anamamatira ku zikhulupiriro zawo kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Zikumbumtima zawo zaumulungu zinawalola kukhalapo pamene anakana kwamtu wagalu kutengamo mbali, kapena kukhalamo ndi phande mwaumwini, m’kachitidwe kalikonse kachipembedzo chonyenga.—Danieli 3:1-18.
Pamene kuli kokakamiza kuti ophunzira onse akhalepo pakalasi lachipembedzo ndipo mwinamwake ndi kuphunzira kuti akapambane mayeso, ana ochokera m’mabanja a Akristu owona angapezekepo, monga momwe anachitira atatu aja pomvera lamulo la Nebukadinezara. Koma achichepere Achikristu akaika Mulungu pamalo oyamba. Iwo sakafunikira kutsutsa ndemanga yolakwa iriyonse kapena kachitidwe kosakhala kamalemba kalikonse kochitidwa ndi ena, monga momwe Ahebri atatuwo sanayese kudodometsa pamene ena anagwadira chifano chagolidicho. Komabe, achichepere Achikristu sakakhala ndi phande m’machitachita akulambira, mapemphero aunyinji, nyimbo zachipembedzo, ndi zina zoterozo.
Achichepere ameneŵa ayenera kuyesetsa nthaŵi zina kuphunzira chidziŵitso chomangirira kuchokera mu ‘malembo opatulika, okhoza kuwapatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.’ (2 Timoteo 3:15) Mwakulankhulana ndi ana awo, makolo ayenera kusanthula mosalekeza zinthu zophunziridwa m’kalasi. Izi zikathandiza Akristu achikulirewo kuwona zimene zifunikira kuwongoleredwa kapena kumveketsedwa kuchokera m’Baibulo kotero kuti ana awo sakusokonezeka kapena kusokeretsedwa.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Baibulo silimatchula kuti Danieli analipo pa chigwa cha Dura. Mwinamwake iye analoledwa kusapitako chifukwa cha udindo wake wapamwamba m’boma.