Kodi Mumakumbukira?
Kodi munalingalirapo mosamalitsa makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati nditero, mwinamwake mudzakupeza kukhala kosangalatsa kukumbukira zotsatirazi:
◻ Kodi ndimotani mmene cholembedwa cha Baibulo cha nkhondo za Yehova chimatipatsira chidaliro poyang’anizana ndi ‘chisautso chachikulu’? (Mateyu 24:21)
Pokhala wolamulira wa nthaŵi zonse, Yehova wasonyeza kuti angaganize kuposa adani ake ndi kuyendetsa zinthu kuti apulumutse anthu ake.—8/15, tsamba 27.
◻ Kodi makolo ayenera kukhala ofunitsitsa kuchita chiyani kuti asungitse kulankhulana pakati pawo ndi ana awo?
Makolo ayenera kuthera nthaŵi ndi ana awo. Ndiponso, ayenera kukhala ofunitsitsa kudzimana kaamba ka kukula kwamaganizo, kwakuthupi, ndi kwauzimu kwa ana awo.—9/1, tsamba 22.
◻ Kodi kusandulika kwa Yesu kuli ndi tanthauzo lanji kwa ife lerolino? (Marko 9:2-4)
Kusandulikako kungakulitse chikhulupiriro m’mawu aulosi a Yehova ndipo kungalimbitse chikhulupiriro chathu mwa Yesu Kristu monga Mwana wa Mulungu ndi Mesiya wolonjezedwa. Kungakhwimitsenso chikhulupiriro chathu m’kuuka kwa Yesu ku moyo wauzimu ndi kuwonjezera chikhulupiriro chathu m’boma la Mulungu.—9/15, tsamba 23.
◻ Kodi mawu akuti “kwakanthaŵi” pa Yesaya 11:6, (NW) amatanthauzanji?
Kumasulira kosamalitsa kwa vesili kumasonyeza kuti mmbulu ndi mwanawankhosa sizidzakhalira pamodzi mosalekeza m’dziko latsopano. Kuli kothekera kuti nyama zoterozo zidzakhalabe ndi malo okhala osiyana ndipo chotero zimakhala pansi pa magulu a ‘nyama zoŵeta ndi zakuthengo’ monga momwe zinaliri m’Paradaiso woyambirira. (Genesis 1:24, NW) Komabe, nyama zidzakhala pamtendere ina ndi inzake, kukhoza kukhalira pamodzi popanda vuto.—9/15, tsamba 31.
◻ Kodi mfungulo ya Chikristu chenicheni nchiyani?
Chikondi ndicho mfungulo ya Chikristu chenicheni. Chikhulupiriro, ntchito, ndi mayanjano abwino ziri zofunikanso, koma popanda chikondi phindu lawo silimazindikiridwa. Izi ziri choncho chifukwa chakuti kwakukulukulu Yehova ali Mulungu wachikondi. (1 Akorinto 13:1-3; 1 Yohane 4:8)—10/1, tsamba 20.
◻ Kodi mawu akuti “mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira” pa Mlaliki 3:2 amachilikiza lingaliro lakuti Mulungu anaikiratu nthaŵi yathu yakufa?
Ayi. Solomo anali kungofotokoza zungulirezungulire wosalekeza wa moyo ndi imfa amene amakantha anthu opanda ungwiro. Mlaliki 7:17 amalongosola kuti: “Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?” Kodi uphungu umenewu ukakhala ndi tanthauzo lanji ngati nthaŵi ya imfa ya munthu inaikidwiratu?—10/15, masamba 5-6.
◻ Kodi nchiyani chimene chimatsutsa lingaliro lakuti mtumwi Petro anali bishopu woyamba wa Roma?
Palibe umboni wakuti Petro anachezera konse mzinda wa Roma; ndiponso Petro sanadzitche kukhala woposa aliyense wa atumwi a Kristu. (2 Petro 1:1)—10/15, tsamba 8.
◻ Kodi nkoyenera kuti Akristu atumize maluŵa kumaliro?
Ngati kuli kodziŵika bwino lomwe kuti mwambo (kapena chopangidwa, monga ngati mtanda) chiri ndi tanthauzo lachipembedzo m’dera lanu, chiyenera kupeŵedwa. Chotero Akristu sangatumize maluŵa mumpangidwe wa mtanda kapena kuwagwiritsira ntchito m’njira ina iriyonse yomwe iri ndi tanthauzo lachipembedzo chonyenga. Komabe, m’maiko ambiri panthaŵi ino, chizoloŵezi chopereka maluŵa chosagwirizanitsidwa ndi chipembedzo chiri chofala. Akristu ena atumiza maluŵa kudzetsa chimwemwe pa chochitika chachisoni ndi kusonyeza chifundo ndi nkhaŵa.—10/15, tsamba 31.
◻ Kodi mamasuliridwe ovomerezedwa amamveketsa chiyani ponena za Utatu?
Amamveketsa kuti chiphunzitso cha Utatu sichiri lingaliro lokhweka. M’malomwake, chiri mpambo wa malingaliro ocholoŵana osiyana amene anasonkhanitsidwa pamodzi m’zaka mazana ambiri ndipo analukanalukana. Akatswiri ambiri, kuphatikizapo okhulupirira Utatu, amavomereza kuti kwenikwenidi Baibulo liribe chiphunzitso cha Utatu.—11/1, masamba 21-2.
◻ Kodi nchifukwa ninji 29 C.E. liri deti lofunika m’mbiri ya Baibulo?
Chifukwa chakuti mwakuphatikiza mawu otsimikizirika Abaibulo ndi kuika deti la ulamuliro wa Tiberiyo, ophunzira Baibulo angaŵerengere kuti uminisitala wa Yohane unayamba m’ngululu ya 29 C.E. ndikuti miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake, m’phukuto ya 29 C.E., Yohane anabatiza Yesu.—11/15, tsamba 31.
◻ Kodi liwu lakuti “kulambira” linatanthauzanji kwa anthu olankhula Chihebri, ndipo kodi limagwira ntchito motani kwa Mboni za Yehova lerolino?
Liwu Lachihebri lolingana ndi liwu lakuti “kulambira” lingatembenuzidwe kukhala “utumiki.” Chotero, m’kuganiza Kwachihebri, kulambira kunatanthauza utumiki. Zimenezi ndizo zimene limatanthauza kwa anthu a Yehova lerolino, chotero chizindikiro chofunika koposa cha chipembedzo chowona ndicho utumiki waumulungu wakulalikira.—12/1, tsamba 19.