Kututa Olambirawo
MTUMWI Yohane anapatsidwa masomphenya a zochitika zogwedeza dziko zimene zikachitika ‘m’tsiku la Ambuye.’ Anawona Ambuye Yesu Kristu wakumwamba akunka kunkhondo yachilungamo, yochitiridwa chithunzi ndi kavalo woyera—“wolakika kuti alakike.” Chinthu choyambirira chimene akuchita ndicho kuponyera pansi mdani wamkulu wa Mulungu, Satana, kumchotsa kumwamba ndi kumponyera kufupi ndi dziko lapansili. Satana akuchitapo kanthu mwakuloŵetsa anthu m’kuphana, njala, ndi matenda zosalingana ndi zina, zochitiridwa chithunzi ndi okwera pakavalo ophiphiritsira ndi akavalo awo—wofiira, wakuda, ndi wotumbuluka. (Chivumbulutso 1:10; 6:1-8; 12:9-12) Masoka ameneŵa anayamba kuchitika m’chaka cha 1914 ndipo awonjezeka chiyambire nthaŵiyo. Posachedwapa, adzafikitsidwa pachimake ndi chimene Yesu anachifotokoza kukhala ‘masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.’—Mateyu 24:3-8, 21.
Kodi zidzawayendera bwanji olambira Yehova panthaŵiyo? Chivumbulutso mutu 7, mavesi 1 mpaka 10, chimalankhula za magulu a angelo “akugwira” mphepo za chiwonongeko kufikira olambira ameneŵa atasonkhanitsidwa. Mkati mwa nyengo yoyambira 1914, omalizira a Israyeli wauzimu okhala padziko lapansi, okwanira 144,000, asonkhanitsidwa. Ndiyeno ‘tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ Khamu lalikulu limeneli lafika kale chiŵerengero cha mamiliyoni. Iwo akuima ovomerezedwa pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu chifukwa chakusonyeza chikhulupiriro m’mwazi woombola wa Yesu, amene anaphedwa ngati mwanawankhosa wopanda liŵongo. ‘Ndipo afuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’ Olambira achangu ameneŵa amapitirizabe kunena kuti “Idzani,” kwa ena, amene nawonso akusonkhanitsidwa kudzapulumuka ‘chisautso chachikulu.’—Chivumbulutso 7:14-17; 22:17.
“Ku Dziko Lonse Lapansi”
Ponena za olambira odzipereka ameneŵa, kunganenedwe kuti: ‘Liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi ndi ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.’ (Aroma 10:18) Ntchito yawo yolimba yadalitsidwa ndi zipatso zosangalatsa. Mwachitsanzo:
Mexico tsopano amachitira lipoti olambira Yehova okangalika okwanira 335,965, chiwonjezeko cha pafupifupi zikwi zana limodzi m’zaka zitatu zokha! Kodi nchifukwa ninji kuli kufutukuka kwakukulu koteroko? Nkhani yotsatirayi ingathandize kufotokoza. Mwamuna wachichepere wotchedwa Aurelio anali woyang’anira malo osungira ziŵiya zopatulika m’tchalitchi cha Katolika. Nthaŵi iriyonse imene Mboni za Yehova zinafika m’mudziwo, iye analiza mabelu a tchalitchi kulefula aliyense kuti asazimvetsere. M’kupita kwanthaŵi anagula Jerusalem Bible Yachikatolika nayamba kuliŵerenga, koma sanalimvetsetse. Ndiyeno tsiku lina anawona bwenzi lake litakwapatira kope la New World Translation. Aurelio anadzudzula bwenzi lakelo ndipo, akumaliuza kuti Baibulo lake linali lonyenga, ananka naye kunyumba kwake kukamsonyeza Baibulo “lenileni.” Bwenzi lakelo linati: “Taŵerenga Eksodo 20,” ndiyeno anachokapo.
Akumayambira ndi mutu 1, woyang’anira malo osungira ziŵiya zopatulikayo anaŵerenga Eksodo mpaka mutu 20, vesi 4 ndi 5. Anadabwa ndi zimene Baibulo lake la Katolika linanena pa mafano. Pambuyo pa Misa pa Sande yotsatira, iye anafikira wansembe ndi malemba onena za mafano. Poyamba wansembeyo anati iyemwini amangolemekeza mafano; samawalambira. Powona kuti ichi sichinakhutiritse Aurelio, wansembeyo anampatsa mlandu wophunzira ndi Mboni za Yehova. Aurelio anakana nawonjezera kuti, “Tsopano ndidzatero!”
Nthaŵi yotsatira imene Mbonizo zinabwera m’mudzimo, Aurelio anazifikira ndikuyamba kuphunzira nazo Baibulo. Iye anasiya kugwira ntchito m’tchalitchi ndipo m’miyezi itatu anayeneretsedwa kukhala ndi phande muuminisitala wapoyera ndi Mboni za Yehova. Nyumba yoyambirira imene anachezera inali ya wansembe uja, yemwe sanakhulupirire pamene anawona yemwe kale anali woyang’anira malo osungira ziŵiya zopatulikayo ali m’ntchito yolalikira Ufumu. Wansembeyo anamuwopseza kuti adzamchotsa m’tchalitchi, koma Aurelio anamuuza kuti zimenezo sizikafunika popeza kuti anachoka kale m’tchalitchi. Kachitidwe kake kolimba mtima kanalimbikitsa anthu ambiri a m’mudzimo omwe anali kuphunzira kale ndi Mboni za Yehova. Aurelio ndi ena 21 ochokera m’mudzimo anabatizidwa pamsonkhano wachigawo wotsatira. Kufutukukako kunali kofulumira kwakuti panthaŵiyi nkuti m’deralo muli mkulu mmodzi yekha wofunsa gululi mafunso a oyembekezera ubatizo.
‘Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi’
Palibe amene angathaŵe kulalikiridwa kwa Ufumuwo. Mkatolika Wachitaliyana ankakwiya nthaŵi iriyonse imene Mboni za Yehova zinamfikira. Chotero pamene kampani yake inamsamutsira ku Singapore, analingalira kuti tsopano sadzavutitsidwa nazo. Koma anadabwa kupeza kuti Mboni zinalikonso kumeneko. Choncho anagula agalu aŵiri owopsa kuti adzalume Mboni zotsatira zomwe zidzabwera. Pamene Mboni ziŵiri zinafika panyumba pake, agaluwo analumphira pabwalo. Pochita mantha, akaziwo anathaŵa kuti apulumutse miyoyo yawo, napita kumbali zosiyana pamphambano ya msewu. Pamene mmodzi wa agaluwo anafika pafupi, Mboni imodzi mothedwa nzeru inatulutsa mabrosha aŵiri m’chola chake ndikulonga kukamwa kotseguka kwa galuyo. Pomwepo, galuyo analeka kumthamangitsa, napotoloka, nabwerera kunyumba.
Mlungu wotsatira, Mboni ziŵiri zimenezi zinali kupanga ulendo wobwereza panyumba yakutsidya lina la khwalala. Mwini wa agalu uja anali m’dimba mwake, ndipo, modabwitsa, anawapatsa moni akaziwo nawaitanira kuloŵa m’nyumba mwake. Anawauza kuti sanalankhulepo ndi Mboni za Yehova kapena kuŵerenga chirichonse cha zofalitsidwa zawo. Koma anadabwa kupeza mabroshawo mkamwa mwa mmodzi wa agalu ake. Madzulo amenewo anaŵerenga mabroshawo ndipo anamsangalatsao. Ngakhale kuti anakhala Mkatolika kwa moyo wake wonse, iye anafotokoza chikhumbo chakuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.
Popeza kuti mwamunayo anasamutsidwiranso ku Italiya, makonzedwe anapangidwa kuti Mboni za Yehova zikaphunzire naye kumeneko. Pamene iye ndi mkazi wake anayamba kupezeka pamisonkhano, wansembe waderalo anawafikira ndi kuwawopseza. Pamene munthu wina anatentha dimba lawo, okwatiranawo anathetsa mayanjano onse ndi tchalitchi. Mwamunayu tsopano akuti: “Ndayamba kale kulalikira kwa ziŵalo zambiri za banja langa chifukwa ndikufuna kuti adziŵe kuti Yehova ndiye Mulungu yekha wowona.”
“Ku Malekezero a Dziko Lokhalamo Anthu”
Chokumana nacho china chochokera ku malekezero a dziko lapansi chikusonyeza mmene uthenga wa Ufumu umayamikiridwira ndi kuthandiza kusintha miyoyo. Pamene inali kupezekapo pakalasi lolangiza akazi apakati, Mboni ina mu Australia inakumana ndi mkazi yemwe anali ndi zizoloŵezi zambiri zoipa, ngakhale kukana kuleka kusuta panthaŵi imene anali ndi pakati. Mboniyo inavutika maganizo ndi mkhalidwe wake. Zinangochitika kuti anakhala ndi ana panthaŵi imodzi ndipo m’chipatala chimodzimodzicho, choncho anakhala ndi mpata wakulankhulana. Kunawonekera kuti mkaziyo anali ndi mavuto ambiri paubwana, ndipo tsopano ukwati wake unali pafupi kusweka. Chotero, pambuyo potuluka m’chipatala, Mboniyo inafikira mkaziyo niyamba kuphunzira naye Baibulo, kugwiritsira ntchito bukhu la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe.
Mwamuna wa mkaziyo ankapemphera kwa Mulungu kuti apeze chipembedzo chowona, nawonjezera mawu akuti: “Malinga ngati si Mboni za Yehova!” Komabe, pamene anapeza kuti mkazi wake anali kuphunzira ndi Mboni, anayamba kufunsa mafunso ndipo anaitanidwa kukhalapo paphunziropo. Anachita chimenechi, ndipo posakhalitsa anayamba kupezeka pamisonkhano yampingo. Tsopano, onse aŵiri mwamunayo ndi mkaziyo anabatizidwa, ndipo mwachiwonekere mkhalidwe wa ukwati wawo unawongokera mokulira.
Maphunziro Abaibulo apanyumba ozikidwa pa mabuku oterowo achititsa kusonkhanitsidwa kwa olambira ambiri atsopano. M’maiko ambiri kumene Mboni za Yehova zinalimbana ndi kugalukira boma, nkhondo yachiweniweni, kapena ziletso zaboma, ntchito ya phunziro Labaibulo lapanyumba inawonjezereka. Nkhondo yachiweniweni inamenyedwa kwa zaka zambiri mu Angola, ndipo Mboni zinavutika ndi chizunzo ndi zovuta zina. Kuchiyambi kwa chaka chatha, malipoti anasonyeza kuti, pa avareji, wofalitsa aliyense anali kuchititsa pafupifupi maphunziro Abaibulo apanyumba atatu, koma ofalitsawo anali ndi mabuku a Baibulo ochepa. Oyang’anira oyendayenda anali kuchezera gulu laling’ono tsiku lirilonse, kupanga makonzedwe a utumiki wakumunda masana ndi misonkhano madzulo alionse. Kunali kosangalatsa chotani nanga pamene kulimbanako kunatha ndipo matani 42 a mabuku a Baibulo ofunika kwambiriwo anafika kuchokera ku South Africa! Ndithudi, chikondi cha abale amenewo ‘chidzasefukira chiwonjezere, m’chidziŵitso, ndi kuzindikira konse,’ popeza tsopano ali okhoza “kutsimikizira zinthu zofunika koposa.” (Afilipi 1:9, 10, NW) Chiri chisonkhezero chotani nanga kwa awo amene ali ndi zothandizira kuphunzira Baibulo zambiri kugwiritsira ntchito makonzedwe amene Yehova akupereka mokoma mtima!—1 Timoteo 4:15, 16.
Chimwemwe cha olambira okhulupirika ameneŵa chimatikumbutsa za mawu a Yesu mu Ulaliki wa pa Phiri aŵa: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wa kumwamba uli wawo. . . . Achimwemwe ali awo amene azunzidwa kaamba ka chifukwa cha chilungamo, popeza kuti ufumu wa kumwamba uli wawo. . . . Kondwerani ndi kulumpha chifukwa cha chisangalalo, popeza kuti mphotho yanu iri yaikulu kumwamba.” (Mateyu 5:3-12, NW) Ha, ndikututa kotani nanga komwe kukuchitidwa mu Angola!
M’mbali zina za dziko, ziletso pa ntchito ya Mboni za Yehova zikuchepetsedwa kapena kuchotsedwa. Yesu anathirira ndemanga yotere m’tsiku lake: ‘Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.’ (Mateyu 9:37) Ha, ziri zowona motani nanga lerolino! Nthaŵi zonse pamakhala kufunika kwa antchito ambiri. Ndife achimwemwe kuti kulambira kwathu kumaphatikizapo kusonkhanitsa zotuta. Palibe chimwemwe china chachikulu chomwe chingapezeke padziko lapansi kuposa utumiki wathu wodzipatulira kwa Yehova Mulungu.
Komabe, kodi nchiyani chimene chimasonkhezera olambira Yehova kusonyeza chimwemwe ndi changu choterocho? Tidzawona.