Mlungu Umene Unasintha Dziko
“Wolemekezeka ndiye wakudza m’dzina la [Yehova, NW]!”—MATEYU 21:9.
1. Kodi ndimagulu aŵiri osiyana ati amene anayambukiridwa ndi zochitika za mu August wathawu?
“MASIKU ATATU OVUTITSA AMENE ANAGWEDEZA DZIKO.” Mu August 1991, mitu yankhani zanyuzi monga umenewu inagogomezera chenicheni chakuti dziko likhoza kuponyedwa m’chisokonezo chachikulu m’masiku ochepa okha. Ndithudi, masiku akumapeto kwa August anali ndi zochitika zoyambukira osati anthu akudziko okha komanso gulu limene Yesu anati: “Sakhala a dziko lapansi.” Gululi lerolino limatchedwa Mboni za Yehova.—Yohane 17:14.
2, 3. (a) Kodi ufulu unagogomezeredwa motani mu Zagreb mosasamala kanthu za chiwopsezo cha nkhondo? (b) Kodi chikhulupiriro chachikulu chinadzetsa mfupo yotani ku Odessa?
2 Msonkhano wamitundu wa Mboni za Yehova woyamba kuchitikira mu Yugoslavia unalinganizidwa kukhalako pa August 16 mpaka 18. Monga momwe zinakhalira, unali msonkhano waukulu woyamba wa anthu a Yehova wochitikira m’dziko lokhala pachiwopsezo chakuulika kwa nkhondo yachiŵeniŵeni. Mboni za m’dzikolo, pamodzi ndi antchito odzifunira ochokera kumaiko apafupi, adagwira ntchito yakalavulagaga kwa miyezi iŵiri kukonza bwalo lampira wachitanyu la HAŠK Građanski mu Zagreb. Malowo anayera mochititsa kaso, oyenereradi Msonkhano wa “Okonda Ufulu Waumulungu.” Zikwi zambiri za nthumwi za mitundu yonse zinakonzekera kukapezekako, kuphatikizapo zokwanira 600 zochokera ku United States. Pamene chiwopsezo cha nkhondo yachiŵeniŵeni chinakula, panakhala kunena kwakuti: “Aku Amereka sadzabwera.” Koma anabweradi, limodzinso ndi nthumwi zochokera kumaiko ena ambiri. Anayembekezera kukhala ndi chiŵerengero cha opezekapo 10,000, koma panali anthu 14,684 patsiku lothera m’bwalomo! Onse anadalitsidwa kwambiri chifukwa chakuti sanaleke ‘kusonkhana kwawo pamodzi.’—Ahebri 10:25.
3 Kwa masiku atatu pambuyo pa msonkhano wa ku Zagreb, panachitika chiŵembu chofuna kulanda boma mu Soviet Union chimene chinalephera. Panthaŵiyo, okonda ufulu waumulungu ankachita zomalizira m’ntchito yokonzekera msonkhano wawo ku Odessa mu Ukraine. Kodi msonkhanowo ukachitidwa? Ndi chikhulupiriro chachikulu abalewo anachita ntchito zomalizira m’kukonzanso bwalolo, ndipo nthumwi zinkafikabe. Monga ngati chozizwitsa, chiŵembucho chinatha. Msonkhano wosangalatsa unachitidwa pa August 24, 25, ndi opezekapo 12,115 ndi 1,943—imene inali 16 peresenti ya chiŵerengero chapamwamba—omwe anabatizidwa! Mboni zatsopano zimenezi, pamodzi ndi osunga umphumphu kwanthaŵi yaitali, anasangalala kuti anabwera kumsonkhanowo ndi chidaliro chotheratu pa Yehova.—Miyambo 3:5, 6.
4. Kodi ndichitsanzo chotani choperekedwa ndi Yesu chimene Mboni za Kum’maŵa kwa Yuropu zachitsatira?
4 Mboni zokhulupirika zimenezi zinatsanzira njira ya Chitsanzo chathu, Yesu Kristu. Iye sananyalanyaze konse kupita kumapwando olamulidwa ndi Yehova, ngakhale pamene Ayuda anafuna kumupha. Pamene anakwera ku Yerusalemu ku Paskha wake womalizira, iwo anaimirira m’kachisi, nafunsana kuti: “Muyesa bwanji inu, sadzadza kuphwando kodi?” (Yohane 11:56) Koma iye anadzadi! Izi zinayambitsa mlungu umene unasintha mbiri ya anthu. Tiyeni tsopano tipende zina za zochitika zazikulu za mlungu umenewo—Nisani 8 mpaka 14 pa kalenda Yachiyuda.
Nisani 8
5. Kodi Yesu anadziŵa ponena za chiyani pamene ankapita ku Betaniya pa Nisani 8, 33 C.E.?
5 Patsikuli Yesu ndi ophunzira ake apita ku Betaniya. Kumeneko, Yesu adzagonako masiku asanu ndi limodzi kunyumba kwa bwenzi lake lapamtima Lazaro, amene posachedwa adamuukitsa kwa akufa. Betaniya ali pafupi ndi Yerusalemu. Mwamtseri, Yesu wawuza kale ophunzira ake kuti: ‘Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.’ (Mateyu 20:18, 19) Yesu akudziŵa bwino lomwe kuti tsopano adzayang’anizana ndi mayesero osautsa. Komabe, pamene nthaŵiyo ya kuyesedwa kwakukulu ifika, iye saleka konse kutumikira abale ake. Nafenso tikhaletu nawo ‘mtima . . . umene unalinso mwa Kristu Yesu.’—Afilipi 2:1-5; 1 Yohane 3:16.
Nisani 9
6. Madzulo pa Nisani 9, kodi Mariya anachitanji, ndipo Yesu ananenanji kwa Yudase?
6 Dzuŵa litaloŵa, pamene Nisani 9 iyamba, Yesu akudya chakudya m’nyumba ya Simoni yemwe kale anali wakhate. Ndikunoko kumene mlongo wa Lazaro Mariya athira mafuta onunkhira amtengo wake wapatali pamutu pa Yesu ndi kumiyendo naipukuta modzichepetsa ndi tsitsi lake. Pamene Yudase atsutsa zimenezi, Yesu akuti: ‘Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga.’ Pakumva kuti Ayuda ambiri akupita ku Betaniya ndipo akukhulupirira Yesu, ansembe akulu apangana zakupha iye ndi Lazaro.—Yohane 12:1-7.
7. M’maŵa pa Nisani 9, kodi dzina la Yehova linalemekezedwa motani, ndipo nchiyani chimene Yesu ananenera?
7 M’mamaŵa, Yesu atenga ulendo wopita ku Yerusalemu. Makamu apita kukakomana naye, akuzunguza makhwatha akanjedza ndi kufuula kuti: ‘Hosana; wolemekezeka iye wakudza m’dzina la [Yehova, NW], ndiye Mfumu ya Israyeli.’ Ndiyeno Yesu akwaniritsa ulosi wa pa Zekariya 9:9 mwakukwera pa bulu popita kumzindawo. Pamene afika pafupi ndi Yerusalemu, aulirira mzindawo, kulosera kuti Aroma adzaumangira tsasa ndi kuuwononga kotheratu—ulosi umene ukakwaniritsidwa mosalephera zaka 37 pambuyo pake. (Ichi chimasonyezanso tsoka limene lidzagwera Chikristu Chadziko, chimene chapanduka ndi kutsatira chitsanzo cha Yerusalemu wamakedzana.) Olamulira Achiyuda sakumfuna Yesu kukhala mfumu yawo. Afuula mwaukali nati: ‘Onani dziko litsata pambuyo pake pa iye.’—Yohane 12:13, 19.
Nisani 10
8. Pa Nisani 10, kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera ulemu waukulu kaamba ka nyumba yolambiriramo Yehova, ndipo nchiyani chinatsatirapo?
8 Yesu apitanso kukachisi. Kachiŵiri, iye apitikitsamo amalonda aumbombo ndi osintha ndalama. Mzimu wamalonda—‘chikondi cha pa ndalama’—suyenera kuchitikira m’nyumba yolambirira Yehova! (1 Timoteo 6:9, 10) Yesu alipafupi kufa. Anena zakudzala mbewu kuchitira fanizo zimenezi. Mbewu yoyamba ifa, koma imera nikhala phesi limene libala mbewu zambiri. Mofananamo, imfa ya Yesu idzadzetsa moyo wosatha kwa makamu amene amasonyeza chikhulupiriro mwa iye. Atavutika m’maganizo ndi kuyandikira kwa imfa yake, Yesu apemphera kuti dzina la Atate wake lilemekezedwe mwa zimenezo. Monga yankho, liwu la Mulungu libangula kuchokera kumwamba ndipo onse okhalapo alimva nliti: ‘Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.’—Yohane 12:27, 28.
Nisani 11—Tsiku la Zochitika
9. (a) M’maŵa patsiku la Nisani 11, kodi Yesu anagwiritsira ntchito motani mafanizo kutsutsa Ayuda ampatuko? (b) Mogwirizana ndi fanizo la Yesu, kodi ndani amene aphonya mwaŵi waukulu?
9 Yesu ndi ophunzira ake atulukanso mu Betaniya kaamba ka tsiku lathunthu lotangwanitsa. Yesu agwiritsira ntchito mafanizo atatu kusonyeza kulakwa kwa Chiyuda champatuko. Iye watemberera mkuyu wosabala, ndipo mkhalidwe wake wofotawo tsopano usonyeza mtundu Wachiyuda wosakhulupirika ndi wosabala zipatso. Poloŵa m’kachisi, afotokoza mmene alimi achabe a munda wampesa aphera ngakhale mwana wa mbuye wawo amene ndiye woloŵa nyumba—kuchitira chithunzi kukana kwa Ayuda choikiziridwa chawo chochokera kwa Yehova, kumene kudzawonekeratu poyera mwakupha kwawo Yesu. Iye alongosola phwando laukwati lolinganizidwa ndi mfumu—Yehova—amene alendo ake oitanidwawo (Ayuda) adzikhululukira mwadyera kuti asapezekeko. Motero, chiitanocho chiperekedwa kwa akunja—Amitundu—nabwera ena a iwo. Koma mwamuna wopezedwa wopanda chovala chaukwati aponyedwa kunja. Iye achitira chithunzi Akristu onyenga a Chikristu Chadziko. Ayuda ambiri a m’tsiku la Yesu anaitanidwa ‘koma osankhidwa ndiwo oŵerengeka’ odzakhala pakati pa a 144,000 osindikizidwa chizindikiro omwe alandira Ufumu wakumwamba.—Mateyu 22:14; Chivumbulutso 7:4.
10-12. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu anawatsutsa atsogoleri achipembedzo Achiyuda, ndipo kodi iye anawadzudzula ndi mawu amphamvu otani onyenga amenewo? (b) Kodi chiweruzo chinaperekedwa motani pa Ayuda ampatuko pomalizira pake?
10 Atsogoleri achipembedzo onyenga Achiyuda afunafuna njira yoti amkole Yesu ndi mawu, koma iye ayankha mafunso awo amachenjera ndi kuwavumbula pamaso pa anthu. Ha, Ayuda achipembedzo opandukawo ati! Ndipo Yesu akuwatsutsa kotheratu chotani nanga! Iwo asusukira malo apamwamba, malaya apadera, ndi maina aulemu, monga “Rabi” ndi ‘Bambo,’ mofanana ndi atsogoleri achipembedzo ambiri a m’tsiku lathu. Yesu akupereka lamulo lakhalidwe lakuti: ‘Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.’—Mateyu 23:12.
11 Yesu awatsutsa mwamphamvu atsogoleri achipembedzo amenewo. Kasanu ndi kaŵiri iye awadzudzula nati: “Tsoka inu,” akuwatcha atsogoleri akhungu ndi onyenga. Ndipo nthaŵi iriyonse iye apereka chifukwa chimene awatsutsira. Iwo atsekereza ena kuloŵa Ufumu wakumwamba. Pamene atchera msampha munthu wotembenuzidwira ku Chiyuda, iye amakhala mkole wa Gehena moŵirikiza kaŵiri, mwachiwonekere wokhala kale pamzera wachiwonongeko chifukwa cha machimo ake akale aakulu kapena kugontha kwamaganizo. “Inu opusa, ndi akhungu” atero Yesu, popeza kuti Afarisi aika mtima pa golidi wa kachisi mmalo mwa kusungitsa kulambira koyera kumeneko. Iwo anyalanyaza chiweruzo cholungama, chifundo, ndi kukhulupirika pamene akupereka chachikumi cha mbewu zonunkhira, tsabola, ndi chitowe, namasiya nkhani zazikulu za Chilamulo. Kusamba kwadzoma sikudzayeretsa konse chidetso chawo chamkati—kokha mtima woyeretsedwa mwakusonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu yobwerayo ndiwo ungakwaniritse zimenezo. Chinyengo chawo chamkati ndi kusayeruzika kumawombana ndi mkhalidwe wawo wakunja uliwonse monga “manda opaka njereza.”—Mateyu 23:13-29.
12 Indedi, nditsoka kwa Afarisi, amene alidi “ana a iwo amene anapha aneneri” akale! Alidi njoka, ana a mamba, oweruziridwa ku Gehena, pakuti adzapha osati Yesu yekha komanso awo amene iye awatuma. Ichi ndicho chiweruzo chidzaperekedwa “pa mbadwo uwu wamakono.” M’kukwaniritsidwa kwake, Yerusalemu anawonongedwa kotheratu zaka 37 pambuyo pake.—Mateyu 23:30-36.
13. Kodi mawu a Yesu pazopereka zapakachisi akugwira ntchito pamikhalidwe yotani lerolino?
13 Asanachoke pakachisi, Yesu alankhula mothokoza mkazi wamasiye wosoŵa amene aponya timakobiri tiŵiri—‘za moyo wake, zonse anali nazo.’ Zosiyanadi ndi olemera aumbombo, amene akuponyamo zopereka zachiphamaso! Mofanana ndi mkazi wamasiye wosoŵayo, Mboni za Yehova lerolino mofunitsitsa zimapereka nthaŵi, nyonga, ndi ndalama kotero kuti zichirikize ndi kufutukula ntchito yadziko lonse ya Ufumu. Nzosiyana chotani nanga ndi alaliki a pa TV onyengawo amene aswera nkhosa zawo masuku pamutu ndi kudzikundikira okha chuma chadzawoneni!—Luka 20:45–21:4.
Pamene Nisani 11 Ifika Kumapeto Kwake
14. Kodi nchisoni chotani chimene Yesu anasonyeza, ndipo ndimotani mmene anayankhira mafunso owonjezereka a ophunzira ake?
14 Yesu alirira Yerusalemu ndi anthu ake nati: ‘Simudzandiwonaso ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa iye amene akudza m’dzina la [Yehova, NW].’ (Mateyu 23:37-39) Pambuyo pake, ali chikhalire pa Phiri la Azitona, ophunzira a Yesu apamtima afunsa zimenezi, ndipo powayankha Yesu afotokoza chizindikiro chimene chidzasonyeza kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu ndi chimaliziro cha dongosolo lazinthu loipa la Satana.—Mateyu 24:1–25:46; Marko 13:1-37; Luka 21:5-36.
15. Kodi nchizindikiro chotani chimene Yesu anachipereka ponena za nthaŵi yakukhalapo kwake yakupereka chiweruzo, ndipo kodi chinayamba liti kukwaniritsidwa?
15 Ponena za chiweruzo cha Yehova chimene chidzaperekedwa pa kachisi posachedwapa, Yesu akusonyeza kuti icho chikuchitira chithunzi zochitika zatsoka zamtsogolo pachimaliziro cha dongosolo lonse lazinthu. Nthaŵi yakukhalapo kwake imeneyo idzadziŵika ndi kuulika kwa nkhondo yaikulu imene sinachitikepo, limodzinso ndi kusoŵa kwa chakudya, zivomezi, ndi miliri, pamodzi ndi kusoŵeka kwa chikondi ndi kusayeruzika. Ha, zakhala zowona chotani nanga zimenezi m’zaka za zana lathu la 20 chiyambire 1914!
16, 17. Kodi nzochitika zadziko zotani zimene Yesu anafotokoza, ndipo kodi Akristu ayenera kuchitanji ponena za ulosiwo?
16 Chimake chidzakhala ‘masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.’ Popeza kuti chimenechi chidzakhala chosakaza mofanana ndi Chigumula cha m’tsiku la Nowa, Yesu akuchenjeza zakumwerekera m’zolondola zadziko. ‘Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.’ Tiyenera kukhala achimwemwe chotani nanga kuti Ambuyeyo waika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wodzozedwa kuti apereke chenjezo ndi kugaŵira chakudya chauzimu chokwanira cha nthaŵi ino yakukhalapo kwake!—Mateyu 24:21, 42, 45-47.
17 M’zaka za zana lathu la 20, tawona ‘padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru . . . anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.’ Koma Yesu akutiuza kuti: ‘Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.’ Ndipo atichenjeza nati: ‘Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndikuti tsikulo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.’ Ndikokha mwakukhala ogalamuka mpamene tingakhalebe ovomerezedwa pamaso pa Yesu, “Mwana wa munthu,” m’nthaŵi yakukhalapo kwake.—Luka 21:25-28, 34-36.
18. Kodi ndiuphungu wotani umene tingatengepo pa mafanizo a Yesu a anamwali khumi ndi matalente?
18 Pomaliza kufotokoza kwake kowoneratu zochitika za m’tsiku lathu, Yesu apereka mafanizo atatu. Choyamba, m’fanizo la anamwali khumi, iye agogomezeranso kufunika kwa “kudikira.” Kenako, m’fanizo la akapolo ndi matalente, asonyeza mmene kukhala wachangu kukufupidwira mwakuitanidwa ‘kuloŵa m’chikondwero cha Ambuye.’ Akristu odzozedwa, omwe akuchitiridwa chithunzi m’mafanizo ameneŵa, limodzi ndi nkhosa zina akhoza kupeza chilimbikitso chachikulu m’mawu opereka chithunzi chabwino ameneŵa.—Mateyu 25:1-30.
19, 20. Kodi ndiunansi wamakono wathithithi wotani umene ukusonyezedwa m’fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi?
19 Fanizo lachitatu likusonya ku nthaŵi yakukhalapo kwa Yesu m’mphamvu ya Ufumu pamene akhala pampando wake wachifumu waulemerero kumwamba. Ndinthaŵi yakuweruza mitundu ndi yakulekanitsa anthu a padziko lapansi m’magulu aŵiri, lina la anthu ofatsa onga nkhosa ndi linalo, la oumakhosi onga mbuzi. Nkhosazo zimachita zopambana kusonyeza kuchirikiza kwawo abale a Mfumuyo—otsalira odzozedwa padziko lapansi panthaŵi ino ya mapeto adziko. Nkhosa zimenezi zikufupidwa ndi moyo wosatha, pamene kuli kwakuti mbuzi zosayamikirazo zikupita kuchiwonongeko chosatha.—Mateyu 25:31-46.
20 Ha, ndiunasi wathithithi wotani nanga umene tikuwona pakati pa nkhosa zina ndi abale a Mfumuyo panthaŵi ino yachimaliziro cha dongosolo la zinthu! Ngakhale kuti otsalira odzozedwa anasenza okha mtolo waukulu wa ntchitoyo kuchiyambi kwa kukhalapo kwa Mfumuyo, mamiliyoni a nkhosa zina zachangu tsopano akupanga 99.8 peresenti ya atumiki a Mulungu padziko lapansi. (Yohane 10:16) Ndipo nawonso asonyeza kukhala ofunitsitsa kupirira ‘njala, ludzu, umaliseche, matenda, ndi ndende’ monga atsamwali a odzozedwawo osunga umphumphu.a
Nisani 12
21. Kodi nchiyani chimene chinapita patsogolo pa Nisani 12, ndipo motani?
21 Chiwembu chakupha Yesu chikupita patsogolo. Yudase wakawonana ndi ansembe akulu ku kachisi, navomereza kupereka Yesu pa ndalama zasiliva 30. Ngakhale chimenechi chidaloseredwa.—Zekariya 11:12.
Nisani 13
22. Kodi ndimakonzedwe otani omwe anapangidwa pa Nisani 13?
22 Yesu, amene apitiriza kukhala m’Betaniya, mwachiwonekere kaamba ka kupemphera ndi kusinkhasinkha, atumiza ophunzira ake ku Yerusalemu kukapeza munthu “wangana.” M’nyumba ya munthuyo, m’chipinda chachikulu chapamwamba, iwo akonza Paskha. (Mateyu 26:17-19) Pamene dzuŵa lichoma pa Nisani 13, Yesu awatsatira kumeneko kukachita nawo phwando lopambana onse m’mbiri. Kodi nchiyani tsopano chidzachitika pa Nisani 14? Nkhani yathu yotsatira idzanena.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani yotsatira iyenera kutithandiza kumvetsetsa bwino lomwe unansi wathithithi pakati pa kagulu ka nkhosa ka odzozedwa ndi nkhosa zina.
Kodi Mungafotokoze Motani Mwachidule?
◻ Kodi ndikuchereza ndi kuwoloŵa manja kotani kumene ena anakusonyeza kwa Yesu pamasiku a Nisani 8 mpaka 10?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu anavumbulira atsogoleri achipembedzo onyenga pa Nisani 11?
◻ Kodi ndiulosi waukulu wotani umene Yesu anapereka, ndipo kodi ukukwaniritsidwa motani lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene zinthu zinayandikirira kuchimake pa Nisani 12 ndi 13?
[Chithunzi patsamba 12]
Yesu athokoza mkazi wamasiye wosoŵa yemwe anapereka timakobiri tiŵiri—zonse anali nazo