Lipoti la Olengeza Ufumu
Yehova Afupa Wachichepere Wokhulupirika
ACHICHEPERE okhulupirika ali amtengo wapatali pamaso pa Yehova. Chokumana nacho chotsatirachi cha mnyamata wokhulupirika chiyenera kusonkhezera achichepere ena kusunga umphumphu wawo m’kutumikira kwawo Yehova.
Ku Argentina, mnyamata wina wazaka 11 ndi mphwake anaphunzira bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi agogo ŵawo ŵakazi. Posapita nthaŵi, makolo awo anyamatawo anayamba kutsutsa, ndipo anawaletsa kupita kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu. Kwanthaŵi yakutiyakuti, kotero kuti akapezeke kumisonkhano, anyamatawo ankatulukira pazenera la m’chipinda chosambira, nalumphira pabwalo, kenako nkukwera mpanda ndi kulumphira m’bwalo la anansi tero basi mphaka kufika pa Nyumba Yaufumu. Ndiyeno munthu wina anauza amayi ŵawo kuti iwo ankapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Amayiwo anawopseza kuwapanda anawo, ndipo zimenezi zinachititsa mantha mnyamata wamng’ono, choncho analeka kuphunzira. Koma wamkuluyo analimbikira. Kwa zaka zisanu anatha kupezeka pamisonkhono makolo ake osadziŵa.
Pamene anafika zaka 16, anafuna kuyamba maphunziro pasukulu yasekondale, maphunziro amene munalibe m’tawuni limene ankakhala. Kukhala kutali ndi kwawo kukampatsa ufulu wowonjezereka wakulondola chowonadi. Makolo ake adamlola kupita, ndipo zonse zidayenda bwino kwa miyezi itatu. Kenako mphunzitsi wamkulu wasukuluyo anadziŵitsa makolo ake kuti mwana wawo ankakana kuchita sawatcha ku mbendera kapena kuyimba nyimbo yafuko. Pamaso pa mphunzitsi wamkulu, makolo ake, mlembi, loya, ndi maprofesa ena khumi, mnyamatayo anakhoza kupereka umboni wabwino koposa pachifukwa chimene chikumbumtima chake sichidamlolere kuchita zinthu zimenezo. (Eksodo 20:4, 5) Makolowo anakwiya kwambiri. Amayi akewo adatenga kamfuti ka m’malaya kuti akawombere agogo ŵake ŵakazi, amene anati ndiwo adali ndi thayo. Koma sanathe kuwapeza ali okha.
Pambuyo pake, atapangidwa nzeru ndi bwenzi la banja lawo ndi kuvomerezedwa ndi mphunzitsi wamkulu wa sukuluyo, makolowo anasankha kuika mwanayo m’chipatala cha amisala, akuganiza kuti kumchiritsa maganizo kudzampangitsa kutaya chikhulupiriro chake. Ogwira ntchito m’chipatalacho anatenga mnyamatayo pamtunda wa makilomita 100 m’galimoto ndipo anambaya jekeseni za mankhwala a insulin ochulukitsitsa ndi mankhwala ena kufikira atakomoka. Atagalamuka, anasokonezeka kotheratu, osatha kuzindikira aliyense, ndipo anataya pang’ono nzeru yakukumbukira. Pambuyo pa kufufuza kosamalitsa adokotalawo sanampeze ndi matenda aliwonse amaganizo. Koma chipatalacho chinapitirizabe kumampatsa mankhwala. Nzeru zitabweramo, mnyamatayo anapemphera mosalekeza kwa Yehova kuti asamsiye nampempha kumpatsa nyonga yakupirira nayo. Yehova adamtetezeradi, ndipo mkupita kwanthaŵi anatulutsidwa m’chipatala.
Panthaŵi ina mphunzitsi wamkulu wasukuluyo anafunsa mnyamatayo ngati anali wokonzekera kutaya chikhulupiriro chake. Pamene iye adakana, mphunzitsi wamkuluyo anauza makolowo kuti ambwezere kuchipatala chifukwa chakuti msala wake unakula kuposa pakale. Makolowo anampereka kunyumba yosungirako amsala nawuza mayi woyang’anira malowo kusamlola kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Pamene makolowo adachoka, mnyamatayo anadabwa chotani nanga! Eni malowo osungirako amsala anali Mboni za Yehova! Pomalizira pake makolo anamleketsa kulandiranso mankhwala amsala, nakhutiritsidwa kuti adokotala adawanyenga. Panthaŵiyo Khoti Lalikulu la Argentina lidalamula kuti ana a Mboni za Yehova sanafunikirenso kuchotsedwa pasukulu chifukwa cha kusachita sawatcha ku mbendera.
Kodi mayesero amenewa adampindulitsa mnyamatayu? Inde. Iye akuti: “Ndinakhoza kupereka umboni wochuluka kwa adokotala, maprofesa, anzanga apasukulu, makolo, ndi achibale, kwenikweni, ku mzinda wonse. Makolo anga akhalako ofeŵa tsopano ndipo ali ndi lingaliro labwinopo la Mboni. Tsopano, pamene ndiyang’ana kumbuyo ku ubwana wanga, ndimawona mmene Mulungu wathu amasamalira modabwitsa munthu amene akhalabe wokhulupirika kwa iye. Ziridi monga momwe wamasalmo adanenera pa Salmo 27:10 kuti: ‘Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.’”
Wachichepereyu tsopano ali ndi zaka 23, wokwatira, ndipo wokangalika kwambiri muutumiki wa Yehova. Ndithudi, mphamvu ya Yehova yochirikiza njopanda malire.—Salmo 55:22.