Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/1 tsamba 20-23
  • Njira ya Yehova Ndiyo Yabwino Koposa Yokhalira ndi Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya Yehova Ndiyo Yabwino Koposa Yokhalira ndi Moyo
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Choloŵa Chachikristu
  • Zikumbukiro Zakale
  • Sukulu ndi Chosankha Chachikulu
  • Upainiya ndi Utumiki wa pa Beteli
  • Kusunga Uchete
  • Mwaŵi Wosiyanasiyana Wautumiki
  • Moyo Wofupa Kwambiri
  • Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Moyo Wolemeretsa, Wofupa mu Utumiki wa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kufooka Kwanga Kwachititsa Kuti Mphamvu za Mulungu Zionekere
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Moyo Wanga m’Gulu Lotsogozedwa ndi Mzimu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/1 tsamba 20-23

Njira ya Yehova Ndiyo Yabwino Koposa Yokhalira ndi Moyo

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI ERKKI KANKAANPÄÄ

KUYAMBIRA panthaŵi imene ndinali mwana, chonulirapo changa chinali chakutumikira panthambi ya Mboni za Yehova ya Finland, yotchedwa Beteli. Choncho pamene woyang’anira woyendayenda anandifunsa chilimwe cha 1941 kuti, “Kodi ndimakonzedwe otani a mtsogolo amene uli nawo?” Ndinayankha kuti: “Nthaŵi zonse ndimafuna kupita ku Beteli.”

“Zingakhale bwino utangowaiŵala malotowo; sudzaitanidwa konse,” anatero. Poyamba ndinalefulidwa kwambiri, komano ndinasankha kungosiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova. Patapita miyezi ingapo, ndinalandira kalata yondiitana kukatumikira pa Beteli.

Ndinali mkamudzi wamanyazi wazaka 17 pamene ndinagogoda pachitseko cha ofesi yanthambi ku Helsinki mwakuliza belu patsiku lozizira kwambiri, loŵala kwambiri m’November 1941. Posapita nthaŵi Kaarlo Harteva, woyang’anira nthambi, anandilandira. Panthaŵiyo nthambiyi inali kuyang’anira Mboni zokwanira 1,135 mu Finland.

Choloŵa Chachikristu

Mu 1914 atate anagula kope la The Divine Plan of the Ages lofalitsidwa ndi Watch Tower. Komabe, nkhondo yadziko yoyamba inaulika mwadzidzidzi pambuyo pa zimenezo, ndipo sanapeze mpata wakuliŵerenga.

Kumenyera ufulu wa dziko kwa Finland kunadzetsa mavuto. Magulu amphamvu aŵiri​—otchedwa Achiyera ndi Ofiira​—anapangidwa. Achiyera anali ochirikiza chikapitolizimu ndi apakati, pamene kuli kwakuti la Ofiira anali antchito. Atate anayesayesa kukhala auchete, osaphatikana m’njira iriyonse ndi magulu aŵiriwo. Komabe, magulu aŵiriwo anawaika pandandanda ya okaikiridwa.

Monga momwe zinakhalira, Atate anaweruzidwa kuphedwa, choyamba ndi gulu la Achiyera ndiyeno ndi Ofiira. Panthaŵi ina mwamuna wina anaphedwa mwambanda ndipo wochita mbandayo sanagwidwe. Choncho anyamata khumi, kuphatikizapo atate, anapatsidwa chiweruzo cha imfa. Mmodzi wa aphunzitsi a atate, yemwe anali chiŵalo cha bungwe lopereka chiweruzo, ananena kuti iwo amasulidwe, ndipo anamasulidwa. Achichepere asanu ndi anayi otsalawo ananyongedwa.

Pachochitika china Atate anamasulidwanso ku chiweruzo cha imfa. Zitachitika zimenezo iwo anasankha kubisala kotheratu! Iwo ndi mbale wawo anakumba phanga, m’mene ankakhala kufikira nkhondo itatha. Kuti akhale ndi moyo, mbale wawo wamng’ono anawaperekera chakudya ndi madzi.

Nkhondoyo itatha mu 1918, Atate anakwatira namanga nyumba pafupi ndi phangalo. Pambuyo pake ndinalidziŵa bwino phangalo, pakuti ndikumene ndinali kuseŵerera. Atate anandiuza kuti anali kupemphera kwambiri pamene anabisala pansi pa nthakapo. Analonjeza Mulungu kuti ngati iwo akaphunzira momtumikirira Iye, akatero.

Mwamsanga pambuyo pokwatira, Atate anasankha kutenga kanthu kena kokaŵerenga paulendo wa bizinesi. M’chipinda chosungira katundu, anapezamo The Divine Plan of the Ages, bukhu limene analigula zaka zapitazo. Anatsegula pamutu wakuti “The Day of Jehovah” (Tsiku la Yehova) nauŵerenga. Analankhula paokha mobwerezabwereza nati: ‘Ichi ndicho chowonadi, ichi ndicho chowonadi.’ Atatsika kuchokera m’chipinda chosungira katundu, anauza amayi nati: “Ndachipeza chipembedzo chowona.”

Mwamsanga pambuyo pake Atate anayamba kulalikira kwa ena zinthu zimene analikuphunzira, choyamba analankhula kwa achibale awo ndi anansi. Ndiyeno anayamba kukamba nkhani zapoyera. Mosapita nthaŵi ena m’deralo anagwirizana nawo. Atagwirizana ndi Ophunzira Baibulo, monga momwe Mboni za Yehova zinkatchedwera panthaŵiyo, Atate anabatizidwa mu 1923. Pamene anafe tinabadwa​—kukhala anayi pomalizira pake​—Atate sananyalanyaze kutiphunzitsa. Kwenikweni, mpingo utapangidwa, tinafunikira kupezeka pamisonkhano yonse.

Zikumbukiro Zakale

Chikumbukiro changa chakale ndicho msonkhano umene unalinganizidwa mumpingo wakwathu mu 1929, pamene ndinali ndi zaka zisanu. Anthu ochuluka anasonkhana kuchokera m’mipingo yapafupi, ndipo woimira ofesi yanthambi nayenso analipo. M’masiku amenewo kudalitsa ana pamisonkhano kunali chizoloŵezi, kwenikweni muno mu Finland. Choncho mbale wochokera ku Beteli anadalitsa ana, monga momwe Yesu anachitira muuminisitala wake. Sindinaiŵale konse zimenezo.​—Marko 10:16.

Chikumbukiro china chakale ndicho kulandiridwa kwa dzina la Mboni za Yehova mu 1931. Atate, pozindikira ukulu wa chochitikacho, anaikako nzeru poŵerengera mpingo chilengezo chokhudza dzina latsopanolo.

Ndikumbukira kuti kale kwambiri, ndinkapitira limodzi ndi atate m’ntchito yolalikira. Poyamba, ndinkamvetsera kwa iwo, koma mkupita kwa nthaŵi ndinkaichita ndekha ntchitoyo. Mu 1935, pamene woyang’anira woyendayenda anatichezetsa, ndinapita kwa anansi athu onse ndi kuwaitanira kumsonkhano. Ndinawagaŵiranso timabuku, ndipo anthu ena anatilandira.

Sukulu ndi Chosankha Chachikulu

Ana anayife tinali tokha pasukulu amene tinali ndi makolo omwe anali Mboni, ndipo tinkasekedwa chifukwa chosagwirizana ndi achichepere ena m’mikhalidwe imene sinali Yachikristu. Ngakhale kuti anzanga akusukulu anayesa kundinyengerera kuti ndisute fodya, sindinatero. Monyodola ankatitchanso Araselo (Russell anali prezidenti woyamba wa Watch Tower Society) kapena Aharteva (Harteva panthaŵiyo anali woyang’anira nthambi ya Finland). Ndine wokondwa kunena kuti mkupita kwa nthaŵi achichepere ena amene ankatinyodola anakhala Mboni.

Aphunzitsi anga anandilimbikitsa kuwonjezera maphunziro anga, ndipo nthaŵi ina ndinalingalira zakukhala injiniya. Komano kunali msonkhano wa Mboni za Yehova ku Pori m’ngululu ya 1939, umene unakhala posinthira m’moyo wanga. Aŵirife mbale wanga wamng’ono, Tuomo, ndi ineyo tinadzipatulira kwa Yehova ndi kuphiphiritsira zimenezi mwa ubatizo wam’madzi pamsonkhanowo, pa May 28, 1939. Ndiyeno, chakuchiyambi kwa September, Nkhondo Yadziko ya II inaulika.

Mikhalidwe m’Yuropu inasintha mofulumira. Unansi pakati pa Finland ndi Soviet Union unavuta. Atate anagogomezera kuti Armagedo inali pafupi natilimbikitsa kuchita upainiya. Chotero, mu December 1940, mbale wanga ndi ineyo tinayamba kuchita upainiya kumpoto kwa Finland.

Upainiya ndi Utumiki wa pa Beteli

Pamene tinkachita upainiya, tinkakhala ndi Yrjö Kallio nthaŵi zambiri. Anali mbale yemwe anakhala Wophunzira Baibulo mu Pennsylvania ku United States pafupifupi zaka 30 kumbuyoko. Yrjö anali wokoma mtima kwambiri, ndipo anachita kalikonse kutipatsa malo abwino okhala. Mbale wake wakuthupi, Kyösti Kallio, anali prezidenti wa Finland kuyambira mu 1937 mpaka 1940. Yrjö anatiuza kuti anachitira umboni mosamalitsa kwa mbale wake, kumlongosolera kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha boma labwino ndi mtendere wachikhalire padziko lonse.

Mkupita kwa nthaŵi, chikhumbo changa chakukhala chiŵalo cha banja la Beteli chinakula. Mwachimwemwe, mosasamala kanthu ndi chenjezo la woyang’anira woyendayenda lotsutsa ziyembekezo zanga zomwe ndinalinganiza, ndinaitanidwa kukatumikira pa Beteli. Ntchito yanga yoyamba ndinali mnthumwantumwa. Komabe, posapita nthaŵi ndinasinthidwira m’fakitale. M’menemo ndinagwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana, kuphatikizapo m’kachipinda kathu kosindikizira ndi m’Dipatimenti Yamtokoma.

Kusunga Uchete

Mu 1942, pausinkhu wazaka 18, ndinaitanidwa kukagwira ntchito yausirikali. Popeza kuti ndinakana kulembedwa, ndinkafunsidwa mafunso kwanthaŵi yaitali, kaŵiri nditalozedwa mfuti. Nthaŵi zina ndinapandidwa. Ndiponso, panthaŵi yakundifunsa, ankandiika m’chipinda chozizira kwambiri chopanda mbaula m’ndendemo.

Pomalizira pake, mu January 1943, nthaŵi inafika yakuti ine ndi Mboni zina tipatsidwe chilango. Ofisala wa asirikali amene anatifunsa anafuna kuti timangidwe kwa zosachepera zaka khumi. Mtsogoleri wachipembedzo wa asirikali anafuna kuti chilangocho chikhale choposerapo, mwakulemba m’kalata yake kuti ‘chilango cha imfa kapena kutumiza amdyera kuŵiri ameneŵa ku Russia monga azondi ouluka ndi mapalatchuti [zochititsa imfa kwenikweni], zikakhala zowayenera.’

Kuzenga mlandu kongoyerekezera kunalinganizidwa. Ndinaitanidwa ndi khoti ndi kupatsidwa chilango cha imfa. Komabe, kumeneku kunali kuyesayesa kwina kofuna kundiwopsa, popeza kuti pambuyo pake patsiku limodzimodzilo ndinaitanidwanso ndi khoti ndi kupatsidwa chilango cha zaka zitatu ndi theka m’ndende yokhaulitsira. Ndinachita apilu, ndipo chilangocho chinachepetsedwa kukhala zaka ziŵiri.

M’ndendemo, chakudya chinali chosoŵa, ndipo munali ziwopsezo zoipa za akaidi ena. Ogonana ofanana ziŵalo anandiukira kaŵiri, koma mwamwaŵi ndinakhoza kuthaŵa. Mmodzi wa iwo anandiwopseza kuti akandipha ngati sindinavomereze zofuna zake. Koma monga momwe ndinachitira m’mayesero anga onse, ndinaitanira pa Yehova, ndipo anandithandiza. Kunena zowona, chiwopsezo cha mkaidiyo sichinali maseŵera, pakuti anali ataphapo kale munthu wina. Atamasulidwa, mwamunayo anachitanso mbanda ndipo anaikidwanso m’ndende.

Mosakaikira ndinaikidwa kukhala mkaidi wathayo chifukwa chakuti Mboni za Yehova nzodziŵika kukhala zokhulupirika. Ntchito yanga inali kugaŵira akaidi ena phoso lachakudya, ndipo ndinkaloledwa kuyenda mwaufulu m’mabwalo a ndende. Chifukwa chake, sindinangokhala ndi chakudya chondikwanira koma ndinasamaliranso abale anga Achikristu kuwona kuti anadya bwino. Mbale wina ananenepadi ali m’ndende, chinthu chosachitikachitika makamaka polingalira za kusoŵa kwa chakudya!

Ndinamasulidwa m’ndendemo m’September 1944, tsiku limene Mbale Harteva nayenso anamasulidwa. Kumasulidwa kwanga kunatanthauza kuyambiranso utumiki wa pa Beteli. Ndinalingalira kuti, ‘Kugwira ntchito pa Beteli kwa maola 16 patsiku nkwabwino kwambiri kuposa moyo wa m’ndende.’ Sindinapeŵepo ntchito chiyambire pamenepo!

Mwaŵi Wosiyanasiyana Wautumiki

Chakumapeto kwa 1944, ndinakumana ndi Margit, mpainiya wachichepere wokongola zedi, yemwe anavomera nditamfunsira, ndipo tinakwatirana pa February 9, 1946. M’chaka choyamba cha ukwati wathu, ndinatumikira pa Beteli pamene kuli kwakuti Margit anagwira ntchito ku Helsinki monga mpainiya. Ndiyeno mu January 1947 tinagaŵiridwa ntchito yadera.

M’ntchito yoyendayendayo, tinkakhala ndi mabanja osiyanasiyana nthaŵi zambiri ndi kugona nawo m’chipinda chimodzi. Tinadziŵa kuti anatipatsa zinthu zabwino zimene anakhoza, ndipo sitinadandaule. M’masikuwo madera anali aang’ono, ndipo mipingo ina inalibiretu Mboni zobatizidwa!

Mu 1948 tinaitanidwa kukatumikira pa Beteli. Patapita zaka ziŵiri Wallace Endres anadza ku Finland kuchokera ku United States, ndipo mosataya nthaŵi anaikidwa monga woyang’anira nthambi. Anatilimbikitsa mwachikondi kupitiriza kuphunzira Chingelezi, ndipo tinatero. Chotero, tinaitanidwa kuloŵa kalasi ya amishonale ya 19 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, imene inayamba mu February 1952 ku South Lansing, New York.

Titamaliza maphunzirowo tinagaŵiridwa kubwerera ku Finland. Komabe, tisanachoke ku United States, ndinaphunzitsidwa ntchito yoyendetsa makina osindikizira pamalikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.

Titabwerera ku Finland, tinagaŵiridwa ntchito yoyendayenda, komano mu 1955 tinaitanidwanso kunthambi ya Finland. M’chakacho ndinakhala woyang’anira fakitale, ndipo pambuyo pa zaka ziŵiri, mu 1957, ndinaikidwa kukhala woyang’anira nthambi. Chiyambire 1976, ndakhala ndikutumikira monga mgwirizanitsi wa Komiti Yanthambi ya Finland.

Mwachimwemwe, atate ŵanga ndi amayi anakhala okhulupirika kwa Yehova mpaka imfa yawo. Mkupita kwa nthaŵi, achibale a Atate oposa zana limodzi anakhala Mboni. Ndipo mpaka lero, mbale wanga ndi achemwali ndi mabanja awo onse akutumikira Yehova, mchemwali wanga mmodzi ndimpainiya.

Moyo Wofupa Kwambiri

Zaka zapitazo zakhala ndi ntchito yowonjezereka, koma ntchitoyo, pokhala ya Mulungu, yakhala yolemeretsa ndi yofupa ndithu. (1 Akorinto 3:6-9) Sikuti moyo wanga wonse wakhala wamtendere nthaŵi zonse. Ndinakumananso ndi mavuto ndi zopinga. Kale ndikali wachichepere, ndinazindikira kuti munthuwe uyenera kuphunzira kudzilanga wekha. Nthaŵi zonse sungachite zinthu ndendende mmene ufunira. Kaŵirikaŵiri ndinkawongoleredwa, ndipo pang’onopang’ono ndinaphunzira njira yolungama yokhalira ndi moyo.

Mwachitsanzo, mayesero ndi umphaŵi zomwe zinandigwera mkati mwa nkhondo zinandiphunzitsa kukhala ndi moyo ndi zofunika kwenikweni zokha. Ndinaphunzira kuzindikira ngati kanthu kena kanali kofunikadi kapena ayi. Ndikali nacho chizoloŵezi chodzifunsa ndekha ngati ndimafunikiradi chinthu chakutichakuti kapena ayi. Ndiyeno nditazindikira kuti sichofunika kwenikweni, sindimagula.

Chitsogozo choperekedwa ndi Yehova kupyolera m’gulu lake nchowonekeratu. Ndakhala ndi chimwemwe chakuwona chiŵerengero cha Mboni za Yehova chikukula m’zaka zimene ndakhala m’nthambi ya Finland kuchokera pa 1,135 mpaka kuposa 18,000! Ndithudi, ndawona kuti ntchito yanga yadalitsidwa, koma ndidziŵa kuti yadalitsidwa chifukwa chakuti ntchitoyo nja Yehova, osati zathu. (1 Akorinto 3:6, 7) Pamene ndinali wachichepere ndinasankha njira ya Yehova, ndipo yakhaladi yabwino koposa yokhalira ndi moyo.

[Chithunzi patsamba 23]

Erkki Kankaanpää lerolino, ndi Margit mkazi wake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena