Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 5/1 tsamba 26-29
  • Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso—Gawo 2

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso—Gawo 2
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutenga Thayo
  • Kukonzekeretsedwa Kaamba ka Kulekanitsidwa
  • Sukulu Yakabisira
  • Mapindu a Sukuluyo
  • Okangalika Muuminisitala
  • Akuluakulu Aboma Akutilondalondabe
  • Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso—Gawo 3
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu
    Galamukani!—1998
  • Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 5/1 tsamba 26-29

Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso​—Gawo 2

MKATI mwa Nkhondo Yadziko ya II, pachomangira cha lamba langa la yunifomu yausirikali Wachinazi panalembedwa kuti “Mulungu Ali Nafe.” Kwa ine chimenechi chinali chimodzi cha zisonyezero za kudziloŵetsa kwa matchalitchi m’nkhondo ndi kukhetsa mwazi. Chinandinyansa kwabasi. Chotero pamene Mboni za Yehova ziŵiri zinakambitsirana nane mu Limbach-Oberfrohna, Jeremani Wakum’maŵa, ndinachida kwambiri chipembedzo ndipo ndinakhala wosakhulupirira kukhalako kwa Mulungu ndi kukhala wokhulupirira nthanthi yachisinthiko.

“Musaganize kuti ndidzakhala Mkristu,” ndinauza tero Mboni zomwe zinandifikira. Koma zigomeko zawo zinandikhutiritsa kuti Mulungu aliko. Pokhala ndi chilakolako chofuna kudziŵa, ndinagula Baibulo ndipo mkupita kwanthaŵi ndinayamba kuliphunzira nawo. Zimenezo zinachitika m’ngululu ya 1953, pamene ntchito ya Mboni mu Jeremani Wakum’maŵa inaletsedwa kale ndi boma la Komyunizimu kwa zaka pafupifupi zitatu.

The Watchtower ya August 15, 1953, inafotokoza mkhalidwe wa Mboni za Yehova panthaŵiyo kuti: “Ngakhale kuti amazondedwa ndi kuwopsezedwa nthaŵi zonse, ngakhale kuti sangayenderane popanda choyamba kutsimikizira kuti sakulondoledwa, ngakhale kuti kupezedwa ndi mabuku a Watchtower kumatanthauza zaka ziŵiri kapena zitatu m’ndende monga mlandu wa ‘kufalitsa mabuku osonkhezera chiwembu’, ndipo ngakhale kuti mazanamazana a abale ofikapo, omwe ankatsogolera, ali m’ndende, atumiki a Yehova akupitirizabe kulalikira mu Jeremani Wakum’maŵa.”

Mu 1955, ine ndi mkazi wanga Regina tinakapezeka pamsonkhano wamitundu yonse wa Mboni za Yehova ku Nuremberg, Jeremani Wakumadzulo, ndipo chaka chotsatira tonse aŵirife tinabatizidwa ku Berlin Wakumadzulo. Izi ndithudi zinachitika Khoma la Berlin lisanamangidwe mu 1961, kulekanitsa kotheratu Jeremani Wakum’maŵa ndi Berlin Wakumadzulo. Koma ngakhale nthaŵi imene ndinali ndisanabatizidwebe, umphumphu wanga kwa Yehova Mulungu unaikidwa pachiyeso.

Kutenga Thayo

Mpingo wa Mboni za Yehova umene tinayamba kupitako mu Limbach-Oberfrohna unafunikira winawake womakatenga mabuku a Baibulo ku Berlin Wakumadzulo. Tidali ndi bizinesi yaing’ono ndi ana aŵiri achichepere, koma kutumikira Yehova kunakhala kale cholinga chathu m’moyo. Tinakonzakonza galimoto lathu lakale, moti nkukhoza kubisamo mabuku okwanira 60. Kukhala wamtengatenga kunali ntchito yowopsa, koma inandiphunzitsa kudalira Yehova.

Kudutsa ndi galimoto kuchokera ku Berlin Wakum’maŵa kumka ku chigawo Chakumadzulo sikunali nkhani yosavuta, ndipo kaŵirikaŵiri ndinadabwa mmene tinakhozera kuchita chimenecho. Titafika m’chigawo chosaletsedwa, tinatenga mabuku ndi kuwabisa m’galimoto tisanadutsenso malire kubwerera ku Jeremani Wakum’maŵa.

Nthaŵi ina, tinali titangomaliza kubisa mabuku pamene munthu wosadziŵika anatuluka m’nyumba. “Inu apo,” anafuula motero. Mtima wanga unaphonya kugunda. Kodi ankatiwona? “Ndibwino kuti nthaŵi ina mukapite kwina. Galimoto la wailesi la apolisi a Jeremani Wakum’maŵa limaima pangodya paja, adzakugwirani.” Ndinafoya ndi chitonthozo. Tinadutsa malire popanda vuto, ndipo anayife m’galimotolo tinaimba njira yonse pobwerera kwathu.

Kukonzekeretsedwa Kaamba ka Kulekanitsidwa

M’ma 1950, abale mu Jeremani Wakum’maŵa anadalira pa abale a Kumadzulo kaamba ka mabuku ndi chitsogozo. Koma mu 1960 panakhala masinthidwe amene anathandiza Mboni iriyonse mu Jeremani Wakum’maŵa kukhala yogwirizana ndi Mboni zinzake m’dera lakwawo. Ndiyeno mu June 1961, kalasi loyamba la Sukulu Yautumiki Waufumu ya akulu inachitidwa mu Berlin. Ndinaloŵa kosi yoyamba imeneyi ya milungu inayi. Pambuyo pa milungu isanu ndi umodzi yeniyeni, tinalekanitsidwa mwadzidzidzi ndi Kumadzulo pamene Khoma la Berlin linamangidwa. Ntchito yathu tsopano sinali kokha yochitidwa mwakabisira komanso yolekanitsidwa.

Ena anawopa kuti ntchito ya Mboni za Yehova mu Jeremani Wakum’maŵa idzabwerera kumbuyo ndi kulekeka kotheratu. Komabe, kulinganizanso gulu komwe kunayamba kumbuyoko pasanapite chaka kunatithandiza kusunga chigwirizano chathu chauzimu ndi nyonga. Ndiponso, maphunzirowo operekedwa kwa akulu omwe analoŵa kalasi loyamba la Sukulu Yautumiki Waufumu anawakonzekeretsa kupereka maphunzirowo kwa akulu enanso. Chotero Yehova anatikonzekeretsa kaamba ka kulekanitsidwa kwathu, monga momwe anatikonzekeretsadi kaamba ka chiletso mu 1950 ndi misonkhano yachigawo ya mu 1949.

Pokhala olekanitsidwa kotheratu ndi Kumadzulo, zinawonekeratu kuti tinayenera kuchita zoyesayesa zathu kuti gulu likhalebe likupita patsogolo. Tinalembera abale athu Achikristu ku Berlin Wakumadzulo ndi kupangana nawo zakukumana pamsewu waukulu Kum’maŵa umene apaulendo ochokera Kumadzulo analoledwa kuyendamo. Tinanamizira kuferedwa galimoto pamalo amene tinapangana kukumanapo. Pambuyo pa mphindi zingapo, abalewo anafika natibweretsera mabuku a Baibulo. Mwamwaŵi, iwo anabweretsanso bukhu langa la Sukulu Yautumiki Waufumu, manotsi omwe ndidalemba, ndi Baibulo zimene ndinasiya m’Berlin kuwopera kugwidwa. Ndinakondwa chotani nanga kuzipezanso! Sindinazindikire kwenikweni kuti zinthuzi zikakhala zofunikira kwambiri m’zaka zingapo zotsatirapo.

Sukulu Yakabisira

Masiku oŵerengeka pambuyo pake, tinalangizidwa kupanga makonzedwe a makalasi a Sukulu Yautumiki Waufumu m’madera onse a Jeremani Wakum’maŵa. Aphunzitsi anayi anaikidwa, kuphatikizapo ineyo. Koma kwa ine inawoneka kukhala ntchito yosatheka kuphunzitsa akulu onsewo pamene ntchito inali pansi pachiletso. Kuti tibise zimene tinkachita, ndinapereka lingaliro lokachita makalasiwo monga tchuthi chokagona kumsasa.

Kalasi lirilonse linali ndi ophunzira anayi ndi ine monga mphunzitsi, kuphatikizapo mbale wachisanu ndi chimodzi yemwe anali wophika. Akazi ndi ana nawonso analiko. Chotero tonse pamodzi tinali gulu la anthu okwanira kuchokera pa 15 mpaka 20. Malo anthaŵi zonse ochitirako tchuthi chogona konko anali osatheka kuchitirako, chotero ine ndi banja langa tinapita kukafunafuna malo oyenerera.

Panthaŵi ina, pamene tinkadutsa m’mudzi wina, tidawona kanjira kopita ku nkhalango yamitengo yokhala kutali ndi misewu yaikulu. Anawoneka kukhala malo oyenera, chotero ndinakawonana ndi meya. “Tikufunafuna malo kumene ine ndi mabanja ena tingachitire tchuthi kwa milungu ingapo,” ndinafotokoza motero. “Tifuna kukhala patokha kumene ana akhoza kudziseŵerera. Kodi mungatilole kugwiritsira ntchito nkhalango ija kuja?” Iye analola, chotero tinapanga makonzedwe.

Pamalopo, tinakhazikitsa mahema ndi karavani yanga mozungulira kotero kuti malo apakati akhale osawonekera kunja. Karavaniyo ndiyo inakhala chipinda chophunzirira. Tinakumana m’menemo ndikuphunzira zozama kwa maola 8 patsiku kwa masiku 14. Pamalo osawonekera kunja apakatiwo panali mipando ndi thebulo, zolinganizidwiratu kuti mwina pangafike anthu mwadzidzidzi. Ndipo ankafikadi! Panthaŵi zoterozo tinayamikiradi chichirikizo chachikondi cha mabanja athu.

Tikakhala m’kalasi, mabanja athu ankayang’anira kunjako. Tsiku lina, meyayo, yemwe analinso mlembi wa Chipani cha Komyunizimu, anawonedwa akubwera m’kanjira kobwera ku nkhalango kumene tinali. Mlonda anasinika switchi imene inalumikizidwa ndi nsambo ku belu la alamu lokhala m’karavaniyo. Mwamsanga tinatuluka m’karavanimo ndikukakhala pamipando yokonzedwa kale pathebulopo ndi kuyamba kutchova juga. Panalinso botolo la vinyo kuti ziwonekedi kukhala zenizeni. Meyayo anatichezera mwaubwenzi ndi kubwerera kunyumba osakhala ndi chikaikiro chirichonse cha zimene zinali kuchitika.

Makalasi a Sukulu Yautumiki Waufumu anachitidwa m’dziko lonselo kuchokera m’ngululu ya 1962 mpaka kumapeto kwa 1965. Maphunziro ozama amene anaperekedwa, amene anaphatikizapo malangizo a mmene tingachitire ndi mkhalidwe wathu mu Jeremani Wakum’maŵa, anakonzekeretsa akulu kaamba ka uyang’aniro wa ntchito yolalikira. Kuti apezeke pamakalasiwo, akuluwo sanangopereka tchuthi chawo koma anadziikanso paupandu wakuponyedwa m’ndende.

Mapindu a Sukuluyo

Akuluakulu aboma anali kupenda mosamalitsa ntchito zathu, ndipo kumapeto kwa 1965, pambuyo pakuti akulu ambiri anamaliza sukuluyo, anayesa kupha ntchito ya gulu lathu. Anagwira Mboni 15 zolingaliridwa kukhala zotsogolera m’ntchitoyo. Chinali chiwembu chokonzedwa bwino lomwe, ndipo chinafika m’mbali zonse za dzikolo. Apanso, ambiri analingalira kuti ntchito ya Mbonizo ikafafanizidwa. Koma ndi chithandizo cha Yehova tinasintha kagwiridwe kathu ka ntchito malinga ndi mkhalidwewo ndi kupitiriza monga poyamba.

Chimene kwenikweni chinatheketsa zimenezi ndimaphunziro amene akulu anawalandira pa Sukulu Yautumiki Waufumu ndi unansi wodalirana wosasweka umene anaumanga mwa mayanjano amene anasangalala nawo panthaŵi yamakalasi ameneŵa. Motero, gulu linasonyeza kulimba kwake. Kunali kofunika chotani nanga kuti tinatsatira mosamalitsa malangizo a gulu!​—Yesaya 48:17.

Zinakhala zowonekeratu m’miyezo yotsatira kuti chiwembu cha akuluakulu aboma chinalephera kudodometsa kotheratu ntchito yathu. Posapita nthaŵi, tinakhoza kuyambiranso makalasi a Sukulu Yautumiki Waufumu. Pamene akuluakulu anawona nyonga yathu yakudzukanso, anakakamizika kusintha machenjera awo. Ha, chidali chipambano chotani nanga kwa Yehova!

Okangalika Muuminisitala

Panthaŵiyo magulu athu a Phunziro Labukhu Lampingo anali ndi anthu pafupifupi asanu okha. Aliyense wa ife analandira mabuku Abaibulo kupyolera m’makonzedwe a phunziro labukhu ameneŵa, ndipo ntchito yolalikira inagwirizanitsidwa kuchokera m’timagulu tamaphunziro timeneti. Ineyo ndi Regina tinali ndi madalitso a Yehova kuchokera pachiyambi akupeza anthu ambiri ofuna kuphunzira Baibulo.

Utumiki wa kunyumba ndi nyumba unasinthidwa pang’ono kuti tisadziŵidwe ndi kugwidwa. Tinkati tikafikira malo amodzi, tinalumpha nyumba zingapo tisanagogode pa ina. Panyumba ina dona wina anandiitanira m’nyumba ndi Regina. Tinali kukambitsirana naye nkhani ya m’Malemba pamene mwana wake wamwamuna analoŵa. Kunena kwake kunali kosapita m’mbali mpang’ono ponse.

“Kodi mudamuwonapo Mulungu wanu?” anafunsa tero. “Muyenera kudziŵa zimenezo, ine ndikhulupirira zimene ndimawona basi. Zinazo nzachabechabe.”

“Sindikhulupirira zimenezo,” ndinayankha tero. “Kodi ubongo wako udauwonapo? Koma zonse zimene umachita zimasonyeza kuti uli nawo.”

Regina ndi ine tinapereka zitsanzo za zinthu zina zimene timavomereza popanda kuziwona, monga ngati magetsi. Mnyamatayo anatchera khutu, ndipo tinayamba naye phunziro Labaibulo lapanyumba pamodzi ndi amayi ake. Onse aŵiriwo anakhala Mboni. Kwenikweni, anthu 14 amene ine ndi mkazi wanga tinaphunzira nawo anakhala Mboni. Theka la chiŵerengero chimenecho tinakumana nawo pamaulendo athu akunyumba ndi nyumba, ndipo enawo tinakumana nawo muulaliki wamwamwaŵi.

Tinali kuti titangoyamba kutsogoza phunziro Labaibulo lapanyumba mokhazikika ndi kuwona munthuyo kukhala wodalirika, tinkamuitanira kumisonkhano yathu. Komabe, mfundo yaikulu koposa imene tinasamala inali yakuti mwina wophunzirayo akadodometsa chisungiko cha anthu a Mulungu. Chotero, panali kupita chaka kapena kuposapo tisanaitanire wophunzira Baibulo ku misonkhano, ndipo nthaŵi zina kukatenga nthaŵi yotalikirapo. Ndikukumbukira mwamuna wina amene anali ndi malo apamwamba; anali wotchuka kwa akuluakulu a Chipani cha Komyunizimu. Iye anakhala ndi phunziro Labaibulo kwa zaka zisanu ndi zinayi asanaloledwe kupezeka pamisonkhano! Lerolino mwamunayu ndimbale wathu Wachikristu.

Akuluakulu Aboma Akutilondalondabe

Pambuyo pa 1965 sitinayang’anizanenso ndi kugwidwa kwa anthu ambiri panthaŵi imodzi, koma sitinakhalebe pamtendere. Akuluakulu anatifufuzabe mwakhama. M’nthaŵi imeneyi ndinaloŵetsedwa kwambiri m’kuyendetsa ntchito ya gulu lathu, choncho akuluakulu aboma anaika chisamaliro chapadera pa ine. Nthaŵi zambiri anadzanditenga kukandifunsa mafunso ku polisi. “Basi ufulu wako sudzauwonanso,” iwo amatero. “Uku ukupitaku nkundende.” Koma nthaŵi zonse ankandibweza pomalizira pake.

Mu 1972 akuluakulu aŵiri anandifikira ndipo anathokoza gulu lathu mosadziŵa. Iwo anakhalapo akumvetsera pa phunziro lathu lampingo la Nsanja ya Olonda. “Nkhaniyo inali yokwiitsa kwambiri,” anatsutsa motero. Iwo analidi odera nkhaŵa ndi zimene ena angalingalire ponena za nthanthi ya Chikomyunizimu ngati anaŵerenga nkhani yophunziridwayo. “Ndiiko komwe,” iwo anatero, “Nsanja ya Olonda imagaŵiridwa paunyinji wa mamiliyoni asanu kapena asanu ndi imodzi, ndipo imaŵerengedwa m’maiko osatukuka. Sirili pepala wamba lopanda ntchito.” Ndinati mumtima, ‘Wanena zowona!’

Pofika mu 1972 tinali pansi pachiletso kwa zaka 22, ndipo Yehova anatitsogolera mwachikondi ndi mwanzeru. Tinatsatira malangizo ake mosamalitsa, koma padaakali zaka 18 kutsogolo kuti Mboni mu Jeremani Wakum’maŵa ziloledwe mwalamulo. Ndife oyamikira chotani nanga tsopano pokhala ndi ufulu wodabwitsa wotitheketsa kusangalala m’kulambira Mulungu wathu, Yehova!​—Monga momwe yasimbidwira ndi Helmut Martin.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena