Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 5/15 tsamba 9
  • Paulo Alimbana ndi Plato Ponena za Chiukiriro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Paulo Alimbana ndi Plato Ponena za Chiukiriro
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Plato
    Galamukani!—2013
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu cha Chiukiriro Ncholimba Motani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • ‘Imfa Idzathetsedwa’
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 5/15 tsamba 9

Paulo Alimbana ndi Plato Ponena za Chiukiriro

MTUMWI Paulo analemba za chiukiriro pa 1 Akorinto 15:35-58 ndi 2 Akorinto 5:1-10. Pakutero, kodi anatsatira malingaliro a Plato ndi anthanthi Achigiriki onena za moyo wosakhoza kufa, kapena kodi anagwirizana ndi chiphunzitso cha Yesu ndi Malemba ena onse?

Kabukhu ka Immortality of the Soul or Resurrection of the Individual: St. Paul’s View with Special Reference to Plato, kolembedwa mu 1974 ndipo kovomerezedwa ndi akibishopu wa Tchalitchi cha Greek Orthodox cha ku North ndi South America, kamapereka yankho lenileni. Atafotokoza mpangidwe wa chiukiriro m’malemba otchulidwa pamwambapo ndi chiyambukiro cha Chihelene panthaŵiyo, wolemba nkhaniyo anagamula motere:

“Plato anaphunzitsa kuti moyo umapitiriza kukhalako kosatha ndi kwamuyaya, popanda thupi. Kwa Plato moyo mwachibadwa ndipo pawokha uli wosakhoza kufa . . . Woyera Mtima Paulo sanaphunzitse lingaliro lotero ngakhale kutchula mpang’ono pomwe kuti anatero . . .

“Mtumwi Paulo sakunena za kusakhoza kufa kwa moyo kapena mzimu monga mbali zolekana ndi zosiyana koma za chiukiriro cha thupi lathunthu la munthu logwirizana ndi moyo ndi mzimu monga momwe zinakhalira pakuuka kwa Kristu. Lingaliro la Paulo lonena za mpangidwe umene anthu adzauka nawo silimanena za kutsitsimuka kwa matupi akufa kumanda.

“Lingaliro lake lonena za mpangidwe umene anthu adzauka nawo lingafotokozedwe bwinopo kukhala kusintha, kulengedwanso, ndi kupangidwanso, mwa mphamvu ya Mulungu, kwa munthu yense wathunthu, munthu mmodzimodziyo, umunthu wake, maganizo ndi thupi, munthu weniweni wa mikhalidwe yonse. Chiukiriro chathu cha mtsogolo chidzachitika osati monga choloŵa chathu chachibadwa, koma monga mphatso yaikulu ya Mulungu.”

Inde, kusakhoza kufa sindiko choloŵa chachibadwa cha munthu aliyense. Mmalomwake, ndimphatso yamtengo wapatali ndi yachisomo yochokera kwa Yehova kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Kristu kwa amene amapanga mpingo wodzozedwa Wachikristu.​—1 Akorinto 15:20, 57; Afilipi 3:14.

[Chithunzi patsamba 9]

Chithunzithunzi cha ku Vatican Museum

[Mawu a Chithunzi]

Plato, wanthanthi Wachigiriki

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena