Chimwemwe Chowona Potumikira Yehova
‘Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chiri pa Yehova, Mulungu wake.’—SALMO 146:5.
1, 2. Kodi anthu anenanji za kumasulira liwu lakuti chimwemwe, ndipo kodi chimwemwe chimatanthauzanji kwa anthu ambiri lerolino?
KODI chimwemwe nchiyani? Akatswiri omasulira mawu, anthanthi, ndi akatswiri a maphunziro azaumulungu akhala akuyesayesa kumasulira liwulo kwa zaka mazana ambiri. Koma alephera kupereka mamasulidwe amene amavomerezedwa ndi onse. Encyclopædia Britannica ikuvomereza kuti: “‘Chimwemwe’ ndi limodzi la mawu osokoneza kwambiri.” Mwachiwonekere chimwemwe chimatanthauza zinthu zosiyana kwa anthu osiyana, kudalira pa mmene amauwonera moyo.
2 Kwa anthu ambiri chimwemwe chimadalira pa kukhala ndi thanzi labwino, chuma chakuthupi, ndi unansi wosangalatsa. Komabe, pali anthu amene ali nazo zonsezo koma ngwopanda chimwemwe. Kwa amuna ndi akazi odzipereka kwa Yehova Mulungu, Baibulo limapereka lingaliro la chimwemwe lomwe nlosiyana kotheratu ndi lingaliro la onse.
Lingaliro Losiyana la Chimwemwe
3, 4. (a) Kodi Yesu anatcha yani kukhala achimwemwe? (b) Kodi tingawonenji pa mfundo zodzetsa chimwemwe zimene Yesu anatchula?
3 Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu Kristu sananene kuti chimwemwe chimadalira pa thanzi labwino, chuma chakuthupi, ndi zina zotero. Iye anatcha kukhala achimwemwe amene ali “ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu” (NW) ndi awo ‘akumva njala ndi ludzu la chilungamo.’ Yogwirizana ndi mfundo ziŵiri zimenezi zofunikira kaamba ka chimwemwe chowona ili ndemanga ya Yesu yowoneka ngati yodzitsutsa yakuti: ‘Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.’ (Mateyu 5:3-6) Mwachidziŵikire, Yesu sanali kunena kuti anthu akakhala achimwemwe pamene wokondedwa wawo wafa. Mmalomwake, ankalankhula za awo amene amachita chisoni chifukwa cha mkhalidwe wawo wochimwa ndi zotulukapo zake.
4 Mtumwi Paulo analankhula za cholengedwa cha anthu chikubuula ndi uchimo pamaziko a chiyembekezo chakuti ‘chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi.’ (Aroma 8:21, 22) Anthu amene amavomereza makonzedwe a kukhululuka machimo amene Yehova wapereka kudzera m’nsembe ya dipo ya Kristu ndi amene akuchita chifuniro cha Mulungu amasangalatsidwadi ndipo amakhala achimwemwe. (Aroma 4:6-8) Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anatchanso kukhala achimwemwe ‘akufatsa,’ ‘akuchitira chifundo,’ “oyera mtima,” ndi ‘akuchita mtendere.’ Iye anapereka chitsimikizo chakuti ngakhale azunzidwa, ofatsa amenewo sadzataya chimwemwe chawo. (Mateyu 5:5-11) Kuli kokondweretsa kuwona kuti mfundo zolemekezeka zodzetsa chimwemwe zimenezi zimaika olemera ndi osauka pamalo amodzi.
Maziko a Chimwemwe Chenicheni
5. Kodi chimwemwe cha anthu odzipereka a Mulungu chimadalira pa chiyani?
5 Magwero a chimwemwe chowona sakupezeka m’chuma chakuthupi. Mfumu yanzeru Solomo inati: ‘Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.’ (Miyambo 10:22) Kwa zolengedwa zimene zimavomereza uchifumu wa chilengedwe chonse wa Yehova, chimwemwe nthaŵi zonse chimabwera ndi dalitso la Mulungu. Munthu wodzipereka amene ali nalo ndipo amalandira dalitso la Yehova amakhaladi wachimwemwe. Titachilingalira monga momwe limanenera Baibulo, chimwemwe chimaphatikizapo kukhala wokwanira, chikhutiro, ndi kukondweretsedwa muutumiki wa Yehova.
6. Kodi anthu a Yehova afunikira chiyani kuti akhaledi achimwemwe?
6 Chimwemwe chowona chimadalira pa unansi wabwino ndi Yehova. Chimadalira pa kukonda Mulungu ndi kukhala wokhulupirika kwa iye. Atumiki odzipereka a Yehova amavomereza ndi mtima wonse mawu aŵa a Paulo: ‘Palibe mmodzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha . . . tikhalira [Yehova, NW] moyo . . . tikhala ake a [Yehova].’ (Aroma 14:7, 8) Chotero, chimwemwe chowona sichingapezedwe popanda kumvera Yehova ndi kugonjera mosangalala ku chifuniro chake. Yesu anati: ‘Odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.’—Luka 11:28.
Mfundo Zopangitsa Chimwemwe Zosinthasintha
7, 8. (a) Kodi mfundo zodzetsa chimwemwe zingaikidwe m’magulu otani? (b) Kodi tinganenenji za ukwati ndi kubala ana?
7 Mfundo zopangitsa chimwemwe zomwe zatchulidwazo zingatchedwe “zazikulu,” kapena “zosasintha,” chifukwa chakuti nzofunika kwa atumiki odzipereka a Yehova nthaŵi zonse. Kuwonjezerapo, pali zimene tingazitche zosinthasintha, mfundo zimene zingapangitse chimwemwe panthaŵi ina koma sizingatero panthaŵi ina. M’nthaŵi za makolo akale ndi nyengo za Chikristu chisanakhale, ukwati ndi kubala ana zinalingaliridwa kukhala zofunika koposa zodzetsa chimwemwe. Izi zikusonyezedwa m’kuchonderera kwa Rakele kwa Yakobo kuti: “Ndipatse ana ndingafe.” (Genesis 30:1) Kaimidwe kamaganizo kameneka ponena za kubala ana kanayenerana ndi chifuno cha Yehova cha nyengo imeneyo.—Genesis 13:14-16; 22:17.
8 Ukwati ndi kubala ana zinalingaliridwa kukhala madalitso operekedwa ndi Mulungu kwa anthu a Yehova a nthaŵi zakale. Komabe, zimenezi zinabweretsa chisoni ndi mikhalidwe ina m’nyengo zamavuto m’mbiri yawo. (Yerekezerani Salmo 127, 128 ndi Yeremiya 6:12; 11:22; Maliro 2:19; 4:4, 5.) Choncho, nkowonekeratu kuti ukwati ndi kubala ana simfundo zobweretsa chimwemwe zachikhalire.
Kukhala Wachimwemwe Popanda Ukwati M’nthaŵi Zakale
9. Kodi nchifukwa ninji mwana wamkazi wa Yefita anathokozedwa chaka ndi chaka?
9 Atumiki ambiri a Mulungu apeza chimwemwe chowona popanda ukwati. Polemekeza lumbiro la atate ŵake, mwana wamkazi wa Yefita anakhala mbeta. Kwa kanthaŵi, iye ndi asungwana anzake analirira unamwali wake. Koma iye anakhala ndi chimwemwe chotani nanga potumikira kwanthaŵi zonse m’nyumba ya Yehova, mwinamwake pakati pa ‘akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako’! (Eksodo 38:8) Iye anathokozedwa chaka ndi chaka chifukwa cha zimenezi.—Oweruza 11:37-40.
10. Kodi Yehova anafuna kuti Yeremiya achite chiyani, ndipo kodi kukuwoneka kuti anali ndi moyo wopanda chimwemwe chifukwa cha zimenezo?
10 Chifukwa cha nthaŵi zovuta zimene mneneri Yeremiya anakhalamo, Mulungu anafuna kuti apeŵe kukwatira ndi kulera ana. (Yeremiya 16:1-4) Koma Yeremiya anatsimikiziradi kuwona kwa mawu a Mulungu: ‘Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova.’ (Yeremiya 17:7) Kwa zaka zonse zoposa 40 za utumiki wake wolosera, Yeremiya anatumikira Mulungu mokhulupirika monga mbeta. Malinga ndi zimene timadziŵa, iye sanakwatire konse ndipo analibe ana. Komabe, ndani angakaikire kuti Yeremiya anali wachimwemwe, mofanana ndi otsalira okhulupirika Achiyuda amene ‘anasonkhanira pa zokoma za Yehova’?—Yeremiya 31:12.
11. Kodi pali zitsanzo zotani Zamalemba za atumiki okhulupirika a Yehova amene anali achimwemwe ngakhale kuti analibe anzawo amuukwati?
11 Anthu ena ambiri atumikira Yehova mwachimwemwe popanda mnzawo wamuukwati. Iwo anali mbeta, akazi amasiye, kapena amuna amasiye. Pakati pawo panali mneneri wamkazi wotchedwa Ana; mwinamwake Dorika, kapena Tabita; mtumwi Paulo; ndi chitsanzo chachikulu koposa cha onse—Yesu Kristu.
Mbeta Koma Achimwemwe Lerolino
12. Kodi atumiki ena odzipereka, achimwemwe a Yehova apeza mpata wochitanji lerolino, ndipo chifukwa ninji?
12 Lerolino, Mboni za Yehova zikwi zambiri zikutumikira Mulungu mokhulupirika popanda mnzawo wamuukwati. Ena akhala okhoza kulandira chiitano cha Yesu chakuti: ‘Amene angathe kulandira ichi [mphatso ya umbeta] achilandire.’ Iwo achita zimenezi ‘chifukwa cha ufumu wa kumwamba.’ (Mateyu 19:11, 12) Kutanthauza kuti, agwiritsira ntchito ufulu wawo wopatsidwa ndi Mulungu mwakupereka nthaŵi yochuluka ndi nyonga kuchilikiza zabwino za Ufumu. Ambiri a iwo akutumikira monga apainiya, amishonale, kapena ziŵalo za banja la Beteli pa malikulu a dziko lonse a Watch Tower Society kapena pa imodzi ya nthambi zake.
13. Kodi nzitsanzo ziti zimene zimasonyeza kuti Mkristu akhoza kukhala mbeta koma wachimwemwe?
13 Mlongo wina wokalamba anapatsa nkhani ya moyo wake mutu wosangalatsa wakuti “Mbeta ndi Wachimwemwe Monga Mpainiya.” (Nsanja ya Olonda, September 15, 1985, masamba 24-7) Mlongo wina, mbeta, amene anathera zaka zoposa 50 akutumikira pa Beteli anati: “Ndiri wokhutira kwambiri ndi moyo wanga ndi ntchito yanga. Ndiri wotanganitsidwa kwambiri tsopano koposa kalelonse m’ntchito imene ndikukonda kwambiri. Ndiribe zonong’onezera bondo. Ndikapanganso chosankha chimodzimodzicho.”—Nsanja ya Olonda, December 15, 1982, tsamba 18.
14, 15. (a) Malinga ndi mtumwi Paulo, kodi chofunika nchiyani kuti munthu akhale mbeta? (b) Kodi nchifukwa ninji Paulo akunena kuti munthu wosakwatira achita “bwino koposa” ndipo amakhala “wokondwera koposa”?
14 Onani liwulo “chosankha.” Paulo analemba kuti: “Ngati wina atsimikiza mumtima mwake, popanda chikakamizo, koma ali nawo ulamuliro pa chifuniro chake ndipo wapanga chosankha chimenechi mumtima mwake, kusunga unamwali wake, adzachita bwino. Chotero iye amene apereka unamwali wake muukwati achita bwino, koma iye amene saupereka muukwati achita bwino koposa.” (1 Akorinto 7:37, 38, NW) Nchifukwa ninji achita “bwino koposa”? Paulo analongosola kuti: ‘Ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; . . . Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye . . . Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; . . . kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.’—1 Akorinto 7:32-35.
15 Kodi ‘kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa’ ndi cholinga cha ‘kukondweretsa Ambuye’ kumadzetsa chimwemwe? Mwachiwonekere Paulo analingalira motero. Polankhula za mkazi wamasiye Wachikristu, iye anati: ‘Ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri nawo mzimu wa Mulungu.’—1 Akorinto 7:39, 40.
Maubwino a Mkhalidwe Wosakwatira
16. Kodi ndimaubwino ena otani amene Mboni zosakwatira za Yehova zimakhala nawo?
16 Kaya Mkristu ali mbeta chifukwa cha chosankha chaumwini kapena mokakamizidwa ndi mikhalidwe, mkhalidwe wosakwatira umabweretsa maubwino aumwini ambiri. Kaŵirikaŵiri mbeta zimakhala ndi nthaŵi yochuluka yakuphunzira Mawu a Mulungu ndi kusinkhasinkha pa iwo. Ngati agwiritsira ntchito mkhalidwewu mwaubwino, uzimu wawo umazama. Pokhala opanda mnzawo wamuukwati wofotokozerana naye mavuto awo, ambiri amaphunzira kudalira kotheratu pa Yehova ndikufuna chitsogozo chake m’zinthu zonse. (Salmo 37:5) Izi zimathandiza kubweretsa unansi wathithithi ndi Yehova.
17, 18. (a) Kodi atumiki osakwatira a Yehova ali ndi mwaŵi wotani wakufutukula utumiki wakumunda? (b) Kodi ndimotani mmene atumiki ena osakwatira a Yehova afotokozera chimwemwe chawo?
17 Akristu osakwatira amakhala ndi mwaŵi wakufutukula utumiki wawo wakumunda kutamanda Yehova. Maphunziro apadera omwe akuperekedwa tsopano pa Sukulu Yamaphunziro Autumiki nga abale omwe ndimbeta kapena amasiye okha. Alongo omwe ndimbeta nawonso amakhala omasuka kwambiri kutenga mwaŵi muutumiki wa Mulungu. Mlongo wokalamba wotchulidwa poyambirirayo anadzipereka mwaufulu kukatumikira m’dziko la ku Afirika pamene, malinga ndi kunena kwake, anali “mkazi wofooka pang’ono wazaka zoposa 50 zakubadwa.” Ndipo anakhala kumeneko, ngakhale m’nthaŵi yachiletso, pamene amishonale onse anathamangitsidwa. Adakali kutumikira kumeneko monga mpainiya, ngakhale kuti tsopano ali ndi zaka zoposa 80. Kodi ali ndi chimwemwe? M’nkhani ya moyo wake analemba kuti: “Ndinali wokhoza kugwiritsira ntchito ufulu wapaderawo ndi kusacholowana zimene umbeta umapereka kukhala wotanganitsidwa muuminisitala, ndipo ichi chandibweretsera chimwemwe chachikulu. . . . M’kupita kwa zaka unansi wanga ndi Yehova wakhala wozamirapo. Monga mkazi amene ali mbeta m’dziko la Afirika, ndamuona Yehova kukhala Mchinjirizi.”
18 Apaderanso ali mawu a mbale yemwe anatumikira pa malikulu a Watch Tower Society kwa zaka makumi ambiri. Iye anali wachimwemwe, ngakhale kuti sanakwatirepo ndipo ngakhale kuti anali ndi chiyembekezo chakumwamba chopanda chiyembekezo cha kukwatira. Pamsinkhu wa zaka 79, analemba kuti: “Tsiku lirilonse ndimapempha Atate wathu wakumwamba wachikondi m’pemphero kaamba ka thandizo ndi nzeru kuti ndikhalebe wathanzi mwauzimu ndi mwakuthupi ndikuti ndikhale wanyonga kotero kuti ndipitirize kuchita chifuniro chake chopatulika. M’zaka makumi anayi mphambu zisanu ndi zinayi zapitazi zomwe ndakhala muutumiki wa Yehova ndakhaladi ndi moyo wachimwemwe, wopatsa mphotho ndi wodalitsidwa. Ndipo ndi chifundo chokoma mtima cha Yehova ndikuyang’ana kutsogolo kupitiriza utumiki ku ulemu ndi ulemerero wake ndi kudalitsa anthu ake. . . . Chimwemwe cha Yehova chimandithandiza kupitiriza kulimbana nayo nkhondo ya chikhulupiriro, kuyang’ana kutsogolo kunthaŵi imene adani a Yehova sadzakhalaponso ndipo dziko lonse lapansi litadzazidwa ndi ulemerero wake.”—Numeri 14:21; Nehemiya 8:10; The Watchtower, November 15, 1968, masamba 699-702.
Kodi Chimwemwe Chowona Chimadalira pa Chiyani?
19. Kodi chimwemwe chathu nthaŵi zonse chidzadalira pa chiyani?
19 Unansi wathu wapadera ndi Yehova, chiyanjo chake, ndi dalitso lake—zimenezi ndizo mfundo zimene zidzatibweretsera chimwemwe chowona kwamuyaya. Polingalira bwino zinthu zimene zimabweretsa chimwemwe chowona, ngakhale atumiki okwatira a Yehova amazindikira kuti ukwati wawo suli chinthu chofunika koposa m’miyoyo yawo. Iwo amalabadira uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: ‘Koma ichi nditi, abale, yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe.’ (1 Akorinto 7:29) Izi sizikutanthauza kunyalanyaza akazi awo. Amuna ofikapo Achikristu amaika utumiki wa Yehova patsogolo, ndipo ngakhalenso akazi awo opembedza, achikondi, ndi ochilikiza, ena alidi muutumiki wanthaŵi zonse pamodzi ndi amuna awo.—Miyambo 31:10-12, 28; Mateyu 6:33.
20. Kodi ndikaimidwe kamaganizo kotani kamene Akristu ambiri amakhala nako ponena za mwaŵi wawo wa ukwati?
20 Abale okwatira omwe ndi oyang’anira oyendayenda, odzipereka mwaufulu a pa Beteli, akulu mumpingo—ndithudi, Akristu onse okwatira amene amaika zabwino za Ufumu patsogolo—‘sachititsa nalo dziko’; amagwirira ntchito pakulinganiza mwaŵi wawo wa ukwati ndi moyo wawo wodzipereka ku utumiki wa Yehova. (1 Akorinto 7:31) Komabe, ngachimwemwe. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chochititsa chenicheni cha chimwemwe chawo sindicho ukwati wawo koma utumiki wawo kwa Yehova. Ndipo amuna ndi akazi okwatira okhulupirika ambiri—inde, ndiponso ana awo—ngachimwemwe kuti zinthu ziri motero.
21, 22. (a) Malinga nkunena kwa Yeremiya 9:23, 24, kodi nchiyani chomwe chiyenera kutidzaza ndi chimwemwe? (b) Kodi ndimfundo zotani zodzetsa chimwemwe zimene zatchulidwa pa Miyambo 3:13-18?
21 Mneneri Yeremiya analemba kuti: ‘Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m’nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m’mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m’chuma chake; koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziŵa ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi, pakuti m’menemo ndikondwerera, ati Yehova.’—Yeremiya 9:23, 24.
22 Kaya ndife mbeta kapena okwatira, magwero athu aakulu koposa a chimwemwe ayenera kukhala chidziŵitso chathu cha Yehova ndi chikhutiro chakuti tiri ndi dalitso lake chifukwa chakuti tikuchita chifuniro chake. Timakhalanso achimwemwe kudziŵa zimene zimapangitsa mapindu enieni, zinthu zimene Yehova amakondwera nazo. Mfumu yomwe inakwatira akazi ambiri, Solomo, sinalingalire ukwati kukhala mfungulo yokha ya chimwemwe. Iye anati: ‘Wodala ndi wopeza nzeru, ndi wowona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere. Njira zake ziri zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.’—Miyambo 3:13-18.
23, 24. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti atumiki onse okhulupirika a Yehova adzakhala achimwemwe m’dongosolo latsopano la zinthu?
23 Tiyeni tonsefe amene ndife okwatira tipeze chimwemwe chamuyaya pochita chifuniro cha Mulungu. Ndipo abale ndi alongo athu onse okondedwa omwe asankha kukhala mbeta kapena akakamizidwa ndi mikhalidwe apirire ziyeso zawo ndi kupeza chimwemwe ndi chikhutiro m’kutumikira Yehova tsopano ndi kuumuyaya wonse. (Luka 18:29, 30; 2 Petro 3:11-13) M’dongosolo lazinthu la Mulungu likudzalo, “mabuku” adzatsegulidwa. (Chivumbulutso 20:12) Mabukuwa adzakhala ndi malamulo ndi zitsogozo zatsopano zosangalatsa.
24 Ndithudi, tingakhale ndichidaliro kuti “Mulungu [wathu] wachimwemwe” watisungira zinthu zabwino koposa zimene zidzakwaniritsa chimwemwe chathu. (1 Timoteo 1:11, NW) Mulungu adzapitiriza ‘kuoloŵetsa dzanja lake ndikukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.’ (Salmo 145:16) Nkosadabwitsa kuti chimwemwe chowona chilipo ndipo nthaŵi zonse chidzakhalapo potumikira Yehova.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi chimwemwe cha atumiki odzipereka a Yehova chimadalira pa chiyani?
◻ M’nthaŵi za Baibulo, kodi ndani anali ena a atumiki achimwemwe osakwatira a Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji Paulo anavomereza umbeta, ndipo ndimotani mmene Akristu ena aupezera kukhala moyo wachimwemwe?
◻ Kodi nthaŵi zonse chimwemwe chathu chidzadalira pa chiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala achidaliro kuti okhulupirika onse adzakhala achimwemwe m’dongosolo latsopano la zinthu?
[Chithunzi patsamba 16]
Alongo ambiri omwe ndimbeta akutumikira Yehova mwachimwemwe monga aminisitala anthaŵi zonse
[Chithunzi patsamba 18]
Kutumikira zabwino za Yehova ndiko magwero aakulu a chimwemwe