Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 6/1 tsamba 21-23
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Alandira Mphatso ya Utumiki Waumishonale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Alandira Mphatso ya Utumiki Waumishonale
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Atenga Njira ya Moyo Yofupa
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Nyumba Yatsopano Kaamba ka Sukulu ya Mishonale ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 6/1 tsamba 21-23

Omaliza Maphunziro a Gileadi Alandira Mphatso ya Utumiki Waumishonale

PA MARCH 1, 1992, ziŵalo 22 za kalasi la 92 lomaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower analandira mphatso​—inde, mphatso ya utumiki waumishonale. Polankhula kwa kalasilo, Lloyd Barry wa Bungwe Lolamulira ananena kuti: “Talandiranitu mphatso yodabwitsa imeneyo ndi chimwemwe chachikulu, ndipo igwiritsireni ntchito kudzetsa chimwemwe pa ena.”

Alendo oitanidwa ndiponso ziŵalo za Beteli onse pamodzi okwanira 4,662 anasonkhana m’Nyumba Yosonkhanira ku Jersey City, mu New Jersey, paprogramu yomaliza maphunziro. Enanso okwanira 970 ku malo a Watchtower Society ku Wallkill, New York mu Brooklyn, ndi ku Patterson ankamvetsera pa mafoni olunzanitsidwa. Onsewo anamvetsera motchera khutu pamene omaliza maphunziro anapatsidwa uphungu wotsazikana umene ukawathandiza kulemekeza ndi kusamalira mphatso yautumiki waumishonale ndi kuigwiritsira ntchito mwanzeru.

Programuyo inayamba ndi kuimba kwachisangalalo nyimbo nambala 155, yakuti “‘Welcome One Another’!” Pambuyo pake, onse anachita chidwi pamene Frederick W. Franz, prezidenti wa Sukulu ya Gileadi wa zaka 98, anapereka pemphero logwira mtima. Ndiyeno, tcheyamani, Carey Barber chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, analonjera onse opezeka paprogramu yomaliza maphunziroyo naati: “Sipanakhalepo chifuno choposa cha lerolino cha amishonale a Gileadi.” Atatero, anapereka ndandanda ya nkhani zazifupi koma zothandiza zomwe zikaperekedwa.

Curtis Johnson chiŵalo cha Komiti ya Nyumba ya Beteli anakamba nkhani yoyamba ya mutu wakuti “Samalirani Bwino Munda Wanu.” Mbale Johnson anafotokoza kuti pamene amishonale atsopanoŵa afika ku magawo awo, aliyense wa iwo adzakhala ndi munda wauzimu woulima. (1 Akorinto 3:9) Anthu a Yehova padziko lonse ali munda wauzimu akubala chilungamo ndi chitamando pamaso pa mitundu yonse. (Yesaya 61:11) Wokambayo anagogomezera kuti ‘Chipambano chanu m’gawo lanu laumishonale chidzadalira kwenikweni pammene mumasamalirira munda wanu wauzimuwo.’ Kodi nchiyani chikawathandiza kusamalira bwino munda wawo wauzimu? ‘Yehova akhoza kukhala linga lachitetezo lochinga munda wanu wauzimu. Ngati ndinu wofunitsitsa kukulitsa ntchito zabwino, yandikanani naye nthaŵi zonse m’pemphero, ndiyeno chitani mogwirizana ndi mapemphero anu.’

Wotsatira anali Lloyd Barry yemwe anakamba nkhani yakuti “Kodwerani mwa Ambuye Nthaŵi Zonse.” (Afilipi 4:4) Pokhala anachitapo ntchito yaumishonale kwa zaka zoposa 25 mu Japani, anali ndi malingaliro ogwira ntchito othandizira omaliza maphunzirowo kuwona mmene angasangalalire ndi mphatso ya utumiki waumishonale. Iye anati: ‘Mudzapeza kuti chimwemwe chanu muutumiki wa Mulungu chidzakuthandizani kulaka zipsinjo zambiri ndipo ngakhale mavuto ena akuthupi amene mudzakumana nawo.’ (Miyambo 17:22) Iye anakumbutsa omaliza maphunzirowo kuti akhoza kuyang’anizana ndi mikhalidwe ndi zochitika zomwe zingasiyane kotheratu ndi zimene anazoloŵera. Angafunikire kuphunzira chinenero chatsopano. ‘Mudzafunikira kuyesayesa mwamphamvu kuti muphunzire chinenero chatsopano. Koma mutakhoza kulankhula ndi anthu mosavuta m’chinenero chawo, chimwemwe chanu chidzawonjezereka.’

Ndiyeno panabwera Eldor Timm, chiŵalo cha Komiti ya Fakitale, yemwe anakamba nkhani yakuti “Sumikani Maso Anu pa Mphotho.” Mphotho yotani imeneyo? Moyo wosatha! Kuti tiipate tiyenera kusumikapo maso athu. Wokambayo anafotokoza mbali zina zofanana ndi zosiyana pakati pa Akristu ochita makani okapeza moyo ndi anthu ochita makani othamanga a m’zaka za zana loyamba. Mofanana ndi othamangawo, Akristu ayenera kuyeseza zolimba, kusunga malamulo, ndi kuvula zolemetsa. Koma mosiyana ndi othamanga m’lingaliro lenileni, Akristu amachita makani a moyo wonse ndi kufunafuna mphotho ya moyo wosatha. Mmalo mwakuti pakhale wopambana mmodzi yekha, onse ochita makaniwo kwa moyo wonse kufikira mapeto adzalandira mphotho. Mbale Timm anamaliza ndi mawu akuti: ‘Kuti tipate mphotho ya moyo, tiyenera kukhala pamtendere ndi Yehova, Wopereka mphothoyo. Ndipo kuti tikhale pamtendere ndi Yehova, tiyenera kukhala pamtendere ndi abale athu.’

Milton Henschel chiŵalo cha Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yakuti “Mwa Chitonthozo cha Malemba, Tikhale ndi Chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Wokambayo anayamba ndi mawu akuti: ‘Kwa miyezi isanu yapitayo, mwakhala otanganitsidwa ndi Baibulo. Mwayandikana nalo kwenikweni. Ndipo mwakhala ndi chiyembekezo cholimba. Pamene mukupita ku magawo anu, chonde kumbukirani chimene chapangitsa chiyembekezo chanu kukhala cholimba motero. Nchifukwa chakuti mwayandikana kwambiri ndi Malemba.’ Kuti apereke chitsanzo cha nkhani ya m’Baibulo yosonkhezera chiyembekezo, wokamba nkhaniyo anasonya ku lemba la Oweruza mitu 6 mpaka 8, limene limafotokoza mmene Gideoni anapatsidwira ntchito yomasula Aisrayeli kwa Amidyani oponderezawo. Atafotokoza nkhaniyo ndi tanthauzo lake m’tsiku lathu anati: ‘Pamene mukhala ndi mwaŵi wakuyandikana ndi Malemba ndi kulingalira pazinthuzi, zimakupatsaninso mphamvu. Inde, zimakulimbikitsani.’

Onse ankayembekezera mwachidwi kumva uphungu wotsazikana umene aphunzitsi akulu aŵiri a sukuluyo akapereka kwa ophunzirawo. Jack Redford ndiye anayamba ndi nkhani yakuti “Chitani Chinthu Choyenera.” Anakumbutsa omaliza maphunzirowo kuti: ‘Ku Gileadi munaphunzitsidwa bwino lomwe chimene chiri choyenera malinga ndi Malemba. Tsopano mukupita ku magawo aumishonale ovutirapo. Ndipo tikudziŵa kuti mwina mudzayang’anizana ndi mavuto aakulu m’ntchito yanu. Mosasamala kanthu ndi zimenezi, ndi malingaliro anu enieniwo, tidziŵa kuti mukhoza kuchita choyenera.’ Kodi chidzakuthandizani nchiyani? Choyamba, muyenera kukhala ndi lingaliro labwino ponena za ena. Wokambayo anati: ‘Musayembekezere ungwiro mwa munthu wopanda ungwiro.’ Kukhala ndi lingaliro loyenera la mikhalidwe yovuta kukhozanso kukuthandizani. ‘Tonsefe timakhala ndi nthaŵi zabwino ndi zovuta,’ iye anatero. ‘Aliyense amakhoza kuchita ndi nthaŵi zabwino. Koma kupirira kwanu ndi kupitiriza muutumiki waumishonale kudzadalira pammene mumachitira ndi nthaŵi zovuta.’​—Yakobo 1:2-4.

Wosunga kaundula wa sukulu, Ulysses Glass, anasankha mutu wakuti “Kodi Mtsogolo Muli Chiyembekezo Chotani?” Ndi liwu lachifundo, analimbikitsa omaliza maphunzirowo kusunga chiyembekezo chawo chiri choŵala. (Miyambo 13:12) ‘Chiyambi cha kutaika kwa chiyembekezo nthaŵi zina sichingadziŵike konse,’ anafotokoza motero. ‘Mikhalidwe ikhoza kutitangwanitsa ndikusamalira zinthu zathu zokha mmalo mwa unansi wathu ndi Mulungu. Tikhoza kudwala kapena kuvutika ndi malingaliro chifukwa cha mmene ena amatichitira. Ena angakhale ndi zinthu zakuthupi zochuluka kutiposa kapena uminisitala ungamawayendere bwino, ndipo tingachite kaduka mwanjira inayake. Ngati tilola zinthu zoterezo kutikulira pang’onopang’ono, mwamsanga chiyembekezo cha Ufumu chidzazimiririka mumtima ndi maganizo athu, ndipo tingalepheredi kupirira m’makani okapeza moyo.’ Kodi tiyenera kuchitanji? ‘Tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga ngati titi tidzutsenso chiyembekezo chathu. Tiyenera kutangwanitsa malingaliro athu ndi ziyembekezo zotsimikizirika za Mulungu ndi kusumika maganizo athu onse pa Ufumu wa Mulungu kukhala weniweni. Ndipo tiyenera kuyambiranso kulankhulana ndi Yehova, popeza kuti zimenezi zidzatipatsa chimwemwe.’

Karl Klein, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira anapereka nkhani yaikulu ya dzoma lomaliza maphunzirolo. Mutu wake unali wakuti “Kodi Nkukhaliranji Odzichepetsa?” Ndipo kodi yankho la funso limeneli nlotani? ‘Chifukwa chakuti nkoyenera ndi kolungama, kuli kanthu kanzeru ndi kosonyeza chikondi kukachita,’ anafotokoza motero m’mawu ake oyamba. Omvetsera anachita chidwi pamene anafotokoza zitsanzo zinayi za anthu odzichepetsa omwe tiyenera kuwatsanzira: (1) Yehova Mulungu, yemwe anadzichepetsadi pochita ndi Abrahamu ndi Mose (Genesis 18:22-33; Numeri 14:11-21; Aefeso 5:1); (2) Yesu Kristu, yemwe ‘anadzichepetsa nakhala womvera kufikira imfa pamtengo wozunzirapo’ (Afilipi 2:5-8; 1 Petro 2:21); (3) mtumwi Paulo, yemwe ‘anakhala kapolo wa Ambuye ndi mtima wodzichepetsa kwakukulu’ (Machitidwe 20:18, 19; 1 Akorinto 11:1); ndi (4) ‘otitsogolera,’ monga prezidenti woyamba wa Sosaite, Mbale Russell, yemwe analemba kuti: “Ntchito imene chakomera Ambuye kugwiritsira ntchito maluso athu modzichepetsa yakhala ntchito, osati kwenikweni yakuyambitsa, koma kukonzanso, kupanga masinthidwe, kugwirizanitsa.” (Ahebri 13:7) Mbale Klein anafotokoza zifukwa zina zamphamvu zimene tiyenera kukhalira odzichepetsa. Ndithudi, kulabadira uphungu wakukhala odzichepetsa kudzathandiza omaliza maphunzirowo kugwiritsira ntchito mwanzeru mphatso ya utumiki waumishonale!

Pambuyo pa mawu amenewo, tcheyamani anapereka malonje ochokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi. Ndiyeno nthaŵi inafika yakuti omaliza maphunzirowo alandire madiploma awo. Ophunzirawo anachokera ku maiko asanu ndi aŵiri​—Canada, Finland, Falansa, Mauritius, Netherlands, Sweden, ndi United States. Koma anagaŵiridwa ku maiko 11​—Bolivia, Estonia, Grenada, Guatemala, Honduras, Hungary, Mauritius, Peru, Togo, Turkey, ndi Venezuela.

Pambuyo pakupuma, programu yamasana inayamba ndi chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda lotsogozedwa ndi Joel Adams, chiŵalo cha Komiti ya Dipatimenti Yautumiki. Pambuyo pake, omaliza maphunzirowo anaseŵera zina za zokumana nazo zautumiki wakumunda zimene anasangalala nazo mkati mwa nyengo ya sukuluyo. Pomalizira, panali drama yakuti Kodi Nkulemekezeranji Dongosolo Lateokratiki? yolimbikitsa omvetsera onse, kuphatikizapo omaliza maphunzirowo.

Ndithudi, omaliza maphunziroŵa anapita ku magawo awo achilendo ndi uphungu ndi chilimbikitso zimene zikawathandiza kugwiritsira ntchito mphatso yautumiki waumishonale kudzetsa chimwemwe osati pa iwo okha komanso kwa ena.

[Tchati patsamba 22]

Ziŵerengero za Kalasi

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 7

Chiŵerengero cha maiko kumene anaga- ŵiridwa: 11

Chiwonkhetso cha ophunzira: 22

Avareji ya msinkhu: 33.4

Avareji ya zaka m’chowonadi: 16.7

Avareji ya zaka muuminisitala wa nthaŵi zonse: 11.8

[Chithunzi patsamba 23]

Kalasi la 92 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kumanzere kumka kulamanja mum’zera uliwonse.

(1) Chan Chin Wah, M.; Bouancheaux, N.; Chapman, B.; Östberg, A.; Cole, L.; Jackson, K.; Meerwijk, A. (2) Smith, J.; Wollin, K.; Chapman, R.; Gabour, N.; Chan Chin Wah, J.; Smith, C.; Edvik, L. (3) Bouancheaux, E.; Östberg, S.; Cole, K.; Jackson, R.; Gabour, S.; Edvik, V.; Meerwijk, R.; Wollin, G.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena