Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/1 tsamba 4-7
  • Kuyamikira Mphatso Yamtengo Wapatali ya Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyamikira Mphatso Yamtengo Wapatali ya Moyo
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusintha Nkotheka!
  • Chopereka cha Mulungu cha Moyo Wosatha
  • Kulemekeza Mphatso ya Moyo
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • N’chifukwa Chiyani Mphatso Imene Mulungu Watipatsa Ndi Yamtengo Wapatali?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Tiziyamikira Mphatso ya Moyo Imene Mulungu Anatipatsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/1 tsamba 4-7

Kuyamikira Mphatso Yamtengo Wapatali ya Moyo

MOYO​—ndichuma chamtengo wapatali chotani nanga! Popanda uwo sitingachite kalikonse. Pamene utaika, sungabwezeretsedwe mwanjira iriyonse yaumunthu. Ngati moyo wathu ukhala paupandu, timachita chirichonse chimene tingathe kuti tiupulumutse. Eya, ena apempha ngakhale chithandizo choposa chaumunthu pamene ali m’vuto!

Tikukumbutsidwa zankhani ya m’Baibulo ya chombo chimene chinakumana ndi namondwe wamphamvu panyanja. Pamene chinatsala pang’ono kusweka, “amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m’nyanja akatundu anali m’chombo kuchipepuza.”​—Yona 1:4-6, 14; yerekezerani ndi Machitidwe 27:18, 19.

Amalinyerowo sanazengereze kutaya katundu wawo wabwino koposa poyesayesa kupulumutsa miyoyo yawo. Tikhoza kubwezeretsa chuma chakuthupi​—koma osati moyo. Ndipo chifukwa chakuti mwachibadwa timakonda miyoyo yathu, timapeŵa ngozi. Timadyetsa, kuveka, ndi kusamalira matupi athu. Ndipo tikadwala timafunafuna chithandizo chamankhwala.

Komabe, Mpatsi wa moyo amafuna zambiri kwa ife koposa kungotsatira nzeru zachibadwa zodzitetezera. Ndiiko komwe, moyo uli mphatso yosagulika, ndipo imachokera kwa Munthu wolemekezeka koposa m’chilengedwe chonse. Chifukwa chakukhala ndi chiyamikiro chowona mtima kaamba ka mphatsoyo ndi Mpatsi wake, kodi sitiyenera kusamalira moyo? Ndipo kodi zimenezo sizikaphatikizapo kusamalira miyoyo ya ena?

Pamenepo, sikuyenera kutidabwitsa kuti Chilamulo chimene Yehova Mulungu anapereka kwa mtundu wa Israyeli chinaphatikizapo malamulo olinganizidwa kutetezera miyoyo ndi thanzi la ena. (Eksodo 21:29; Deuteronomo 22:8) Mofananamo, Akristu lerolino ayenera kukhala ndi nkhaŵa ponena za chisungiko chakuthupi. Mwachitsanzo, ngati muli ndi ana m’nyumba mwanu, mosasamala kodi mumasiya pofikirika zinthu zonga mkanda, mapini, singano, kapena zinthu zina zosongoka zimene zingachititse kuvulala kwakukulu kwa mwana amene amaseŵera nazo kapena kuzimeza mosadziŵa kanthu? Kodi makemikolo aupandu ndi mankhwala zimasungidwa pamene ana sangazifikire? Ngati madzi ataika pansi, kodi mumafulumira kuwapukuta kuchinjiriza ngozi? Kodi mumakonzetsa mwamsanga ziwiya zogwiritsira ntchito magetsi zowonongeka? Kodi galimoto lanu limakonzedwa mokhazikika? Kodi ndinu woyendetsa galimoto wabwino? Ngati mumayamikiradi mtengo wapatali wa moyo, mudzasonkhezeredwa kutenga njira zanzeru zotetezera m’mbali zimenezi ndi zina.

Komabe, nzachisoni kunena kuti, ena amachita ngakhale ndi miyoyo yawo yeniyeniyo mosasamala. Mwachitsanzo, kodi ndani lerolino amene samadziŵa kuti kusuta fodya kumawononga thanzi? Komabe, mamiliyoni ambiri amakhala akapolo ku chizoloŵezicho, pamene thanzi lawo limawonongeka nthaŵi iriyonse pamene asuta utsi wakuphawo. Ena amagwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa maganizo, ndiponso ena zakumwa zoledzeretsa, zonsezo modziwononga. AIDS ndinthenda yakupha imene iribe mankhwala odziŵika oyichiritsira. Koma ambiri akanapeŵa kuwatenga matendawo ngati akanakana chisembwere, mitundu ina yakugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, ndi kuthiriridwa mwazi. Ndikupanda chiyamikiro cha moyo kwatsoka chotani nanga!​—Aroma 1:26, 27; 2 Akorinto 7:1.

Kusintha Nkotheka!

Awo amene amayamikira Mlengi wawo Wamkulu, Yehova, ali ndi chifukwa champhamvu chowonera moyo kukhala wamtengo wapatali. Moyo ndiwo mphatso yake yopatulika. Chotero, iwo ali ofunitsitsa kupanga masinthidwe aliwonse ofunika kuti ausamalire monga mphatso yaumulungu. Lingalirani chokumana nacho cha Kwaku, mphunzitsi wa ku Ghana. Iye anali chidakwa chosasamala, akuwononga moyo wake.

Kwaku akukumbukira kuti: “Ndinayesa kukakamiza mkazi wanga kundilemekeza, zimene kaŵirikaŵiri zinaputa mikangano yaikulu ndi kumenyana, makamaka pamene ndinali woledzera. Chifukwa chakumwerekera ndi moŵa, kaŵirikaŵiri ndinali wopanda ndalama, ndipo kaŵirikaŵiri ndinalephera kupereka ndalama zochirikizira banja. Momvekera bwino, zimenezi zinakwiyitsa mkazi wanga kwambiri. Nthaŵi zonse pamene ndinasoŵa ndalama (ndipo zimenezi zinachitika kaŵirikaŵiri), ndinachita chirichonse chimene ndikatha kuchirikiza chizoloŵezi changacho. Nthaŵi ina ndinankitsa kwambiri kotero kuti ndinagwiritsira ntchito ndalama zimene ndinasonkhanitsa kwa ana a m’kalasi langa zolembetsera kulemba mayeso. Ndinamka kukachezerera kuumwa ndi kumagulira anzanga akumwa nawo. Posapita nthaŵi tsiku linafika lakuyang’anizana ndi zotulukapo za zochita zangazo. Hedimasitala wanga akadapanda kuloŵereramo mwamsanga, ndikanachotsedwa ntchito.

“Moyo wanga unali utasokonezeka kwambiri. Ndinali wamanyazi, koma posapita nthaŵi anandichoka. Ndiyeno ndinayamba kukulitsa malingaliro akudzipha chifukwa ndinalingalira kuti moyo unandilephera. Komabe, sindinathe kuleka kumwerekera kwanga ndi moŵako. Koma pamene tsiku lina m’bawa ndinadziloŵetsa m’ndewu ndipo ndinabayidwa, ndinazindikira kuti kukonda moŵa kwangako tsiku lina kudzandiphetsa.

“M’nthaŵi yonseyo, Mboni za Yehova zinali kufika panyumba pathu nthaŵi ndi nthaŵi, kuyesayesa kutichititsa kukondweretsedwa ndi Baibulo. Mkazi wanga ndi ine nthaŵi zonse tinali kuzizemba chifukwa tinalingalira kuti zinali zosautsa. Komabe, panthaŵi ina, ndinasankha kuzimvetsera chifukwa ndinazichitira chisoni. Posapita nthaŵi phunziro la Baibulo linanditsegula maso ndipo ndinadziŵa chiyembekezo chodabwitsa cha kukhala ndi moyo kosatha m’dongosolo latsopano la Mulungu. Pamene ndinaphunzira Baibulo mowonjezereka mothandizidwa ndi Mboni za Yehova, ndipamenenso kuyamikira kwanga Yehova kunakula monga Mpatsi wathu wa moyo ndi mphatso yake ya moyo, ndipo ndipamenenso ndinasangalala kwambiri ndi kugwira ntchito kwa uphungu wa Baibulo. Zimenezi zinandilimbikitsanso kuyeretsa moyo wanga. Zimenezi sizinali zosavuta, popeza kuti ndinafunikira kupitirizabe kukana [moŵa] ndi kupeŵa anzanga akale. Yehova, Wakumva pemphero, anawona kutsimikiza kwa mtima wanga ndipo anandimva.a

“Mkazi wanga, ngakhale kuti sali mmodzi wa Mboni za Yehova, tsopano amandilemekeza ndi chipembedzo changa chifukwa cha kusintha kwakukulu kumene akukuwona m’moyo wanga ndi muunansi wathu waukwati. Anansi athu safunikiranso kulanditsa ndewu pakati pa mkazi wanga ndi ine. Ndimakonda mtendere wamaganizo umene ndiri nawo tsopano. Ndithudi, kuyamikira Yehova Mulungu monga Mpatsi wa Moyo, kukhala ndi lingaliro lake la mtengo wapatali wa moyo, ndi kumvera malangizo ake a kakhalidwe ndiyo njira yokha yopindulitsa ya moyo.”

Chopereka cha Mulungu cha Moyo Wosatha

Anthu zikwi zambiri, mofanana ndi Kwaku, athandizidwa ndi Mboni za Yehova ‘kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwachifuniro cha Mulungu m’chilungamo ndi m’chiyero cha chowonadi.’ (Aefeso 4:24) Iwo afikira pakuyamikira osati kokha moyo wawo umene ali nawo tsopano komanso chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’paradaiso wapadziko lapansi. Baibulo limalonjeza kuti m’Paradaiso ameneyo wopangidwa ndi Mulungu, palibe wokhala padziko amene adzamvanso kuwawa kopitiriza kwa njala, chifukwa chakuti “Yehova wamakamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona.”​—Yesaya 25:6.

Pakali pano, moyo, ngakhale kuti uli mphatso yabwino koposa, uli wakanthaŵi chabe. Aliyense akuyang’anizana ndi imfa, ndipo imfa ndinkhonya yosautsa chotani nanga! Kuwona wina amene mumakonda akuzimiririka kuchoka pakati pa amoyo ndi kuloŵa m’kutonthola kwa manda nkopweteka kwambiri. Koma mu Ufumu wa Mulungu, wolamuliridwa ndi Kristu, lonjezo la Yehovalo lidzakwaniritsidwa: “Sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

Panthaŵiyo mphatso ya moyo idzafutukulidwa mwanjira yodabwitsa. Opulumuka chisautso chachikulu padziko lapansi lino adzakhala ndi mwaŵi wakuloŵa moyo wachikwanekwane. Ndiyeno, mwa chiukiriro, kubwezeretsa ku moyo, Yehova Mulungu adzabwezeretsa mphatso yake yamtengo wapatali kwa awo ogona mu imfa. (Yohane 5:24, 28, 29) Izi zidzatanthauza kubweranso kwa akufa okondedwa ndi amuna akale owopa Mulungu!

Kodi zonsezi nzabwino kopambanitsa kotero kuti nkovuta kuzikhulupirira? Ayi, “chifukwa palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”​—Luka 1:37; yerekezerani ndi Yobu 42:2.

Ndiponso, Yehova Mulungu iyemwini wapatsa anthu chitsimikiziro chakuti zonsezi zidzachitika. Motani? Mwakupereka nsembe wapamtima wake, Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu, kutiwombola ku uchimo ndi imfa. Aroma 8:32 amatitsimikizira kuti: “Iye [Yehova Mulungu] amene sanatimana Mwana wake wa iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?” Baibulo limatiuza kuti zimenezi zidzaphatikizapo kuchotsera mtundu wa anthu makhalidwe oipa ndi mitundu yonse ya chisalungamo, upandu, ndi chiwawa. (Yesaya 11:9) Moyo sudzalingaliridwanso wopanda mtengo.

Ngakhale patsopano lino, pansi pamikhalidwe yakupanda ungwiro, moyo ukhoza kukhala wosangalatsa kwambiri. Kodi ndani amene samakondwa ndi kununkhira kwabwino kwa chakudya, kuzizirira kwa kamphepo kayaziyazi patsiku lotentha, mawonekedwe okongola a phiri lalitali, kuloŵa kwadzuŵa kofiirira bwino, kuyenda kwatawatawa kwa madzi a mfuleni, mawonekedwe okopa mtima a maluŵa amitundumitundu, mamvekedwe a nyimbo yogwira mtima, kapena kuimba kwa mbalame. Taimani kwakamphindi. Ganizani, kodi kudzakhala motani kusangalala ndi zinthu zoterozo kwamuyaya?

Pamenepo, kodi nkwanzeru kutaya mwaŵi wamtengo wapatali wakukhala ndi moyo kosatha chifukwa cha chisangalalo chakanthaŵi chimene njira ya moyo yopanda nzeru ndi yadyera ingapereke? (Yerekezerani ndi Ahebri 11:25.) Mwanzeru, Baibulo limatifulumiza ‘kuti nthaŵi yotsalira tisakhalenso ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.’ (1 Petro 4:2) Tikukulimbikitsani ndi mtima wonse, inde, kukufulumizani, kuchita zimenezo mwakuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kugwiritsira ntchito zimene mumaphunzira. (Yohane 13:17) Chotero mudzaloŵa unansi wabwino ndi Yehova, Mulungu wodzala ubwino ndi chifundo, amene angakufupeni moyo wamuyaya!

[Mawu a M’munsi]

a Kuchira ku uchidakwa ndiko ntchito yovuta, kaŵirikaŵiri yomafunikira chithandizo cha akatswiri. Wonani magazini athu ena, Galamukani! wa June 8, 1992, kaamba ka chidziŵitso chothandiza pa nkhaniyi.

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi njira ya moyo wanu imasonyeza kuyamikira moyo?

[Chithunzi patsamba 7]

Dziko latsopano la Mulungu lidzatilola kupeza zisangalalo za moyo wamuyaya!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena