Lipoti la Olengeza Ufumu
Akulola Kuunika Kwawo Kuŵalira ku India
MBIRI yabwino ya Ufumu ikulalikidwa ku India ndi Mboni zachimwemwe zokwanira 11,524. (Mateyu 24:14) Olengeza Ufumu okwanira 1,066 amene anabatizidwa mkati mwa chaka chautumiki cha 1991, akulola kuunika kwawo kuwalira kwa ena. Onse anali osangalala chotani nanga kuwona anthu okwanira 28,866 akumafika pa phwando la Chikumbutso cha imfa ya Kristu!
◻ Poyamba ambiri amaphunzira chiyembekezo cha Ufumu kupyolera mu umboni wamwamwaŵi. Mwachitsanzo, Mboni ina inalankhula za Ufumu kwa antchito anzake, amenenso ali amisiri opala matabwa. Wantchito mnzake wina analabadira ndipo anayamba kulola kuunika kwake kuwalira pa banja lake ndi mabwenzi. Amenewa mwachimwemwe anapatsira ena uthenga Waufumuwo. Malinga ndi kunena kwa malipotiwo, m’zaka zochepekera zokha, ‘anthu oposa 30 analandira chowonadi.’ Yehova anamdalitsa iye pamodzi ndi abale ake atsopano auzimu chifukwa chakulola kuunika kwawo kuwala.
◻ Mbale wina wachichepere wa ku mpingo wina analola kuunika kwake kuwalira mwakuchitira umboni mwamwaŵi kwa ophunzira anzake pasukulu. Ena a iwo anakondwerera chiyembekezo cha Ufumu, ndipo kaŵirikaŵiri anawafotokozera Baibulo mpaka pakati pausiku. Mmodzi wa iwo, Mkatolika, anaima nji m’chowonadi mosasamala kanthu kuti anachenjezedwa ndi wansembe wake za zotulukapo zowopsa ngati akapitiriza kuyanjana ndi Mboni. Komabe, wophunzirayo anakhutiritsidwa kuti anali kuphunzira chowonadi cha Baibulo kwa Mbonizo, ndipo anapitiriza kulandira chidziŵitso. Pomalizira pake iye anabatizidwa ndipo tsopano akutumikia monga mtumiki wotumikira mumpingo. Iye amakondwera m’chiyembekezo chimene chimadza kupyolera m’kuunika kodabwitsa kwa chowonadi!—Aroma 12:12.
◻ Munthu wina amene anamvetsera kwa Mboni yachichepere imeneyi anali wophunzira wina wotchuka, wosakhulupirira mwa Mulungu, amene ankaseka onse amene anadzinenera kukhala okhulupirira Mulungu, koma tsiku lina anaphatikizidwa m’kukambitsiranako ndipo anafunsa mafunso ambiri. Iye anadabwa pamene analandira mayankho anzeru ku mafunso ake onse natsimikizira kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu. Iye anapita patsogolo m’chidziŵitso Chabaibulo ndipo pomalizira pake anabatizidwa. Atate wake Achihindu anamtsutsa kufikira pakumchotsa panyumba pawo. Komabe, kuima nji kwa mnyamatayu kaamba ka chowonadi kunafupidwa pamene abale ake aŵiri akuthupi ndi mabwenzi ake aŵiri anavomereza chowonadi ndipo anabatizidwa. Mmodzi wa abale ake akutumikira tsopano pa ofesi yanthambi ku India.
◻ Wophunzira wina wolinganiza zinthu anapezekaponso pakukambitsirana ndi Mboni yachichepereyo. Iye anali wosuta ndudu wosalekeza ndiponso wakumwa mowa mopambanitsa. Panthawi ina, anafuna kumenya ophunzira anzake aŵiri amene adaphunzira chowonadi kwa Mboniyo. Chifukwa cha kuvomereza chowonadi, iwo anakana kugwirizana ndi ophunzira pamene anachita sitalaka ndiponso anakana kupereka mwazi panthawi ya ndawala yopereka mwazi yotsogozedwa ndi wophunzira wolinganiza. Tsopano mwamuna wachichepere ameneyu ngwachimwemwe chifukwa chokhala Mboni ya Yehova yonyamula kuunika.
◻ M’zochitika zonsezi, wophunzira amene anayamba kulola kuunika kwake kuwala kwathandiza ausinkhu ake okwanira 15 kudzipatulira ndi kubatizidwa mwa kuchitira umboni kwa iwo mwamwaŵi.
Nkosangalatsa kuwona anthu ambiri m’dziko lalikululo akulandira chiyembekezo cha Baibulo cha dziko latsopano la Mulungu ndi kugwirizana ndi gulu lonse la abale apadziko lonse amene Yehova Mulungu akusonkhanitsa kuti adzakhale ndi moyo kosatha mu Ufumu wake.