Ndinadzichepetsa Ndipo Ndinapeza Chimwemwe
MU 1970, ndinali ndi zaka zakubadwa 23 ndipo wolakalaka ukumu. Ndinaikidwa kukhala kalaliki wamkulu kuntchito kwanga pa kalabu la magalimoto ku Ivrea, Italiya. Ndinatsimikiza mtima kukhala munthu wotchuka. Komabe ndinali wochita tondovi ndi woziya. Chifukwa ninji?
Mwamuna wanga anathera nthaŵi yake yochuluka kumabawa akutchova juga ndi mabwenzi ake, ndipo anandilekera kusenza mathayo ochuluka abanja. Unansi wathu unayamba kunyonyotsoka. Tinali kukanganirana zinthu zazing’onong’ono. Chifukwa cha chimenecho, maganizo anga anadzazidwa ndi malingaliro oipa.
Ndinkanena kuti, ‘Palibe munthu amene amakondwera nawe. Iwo amangofuna kukudyera masuku pamutu kaamba ka udindo wako.’ Ndinkadziuzanso kuti: ‘Mulungu sangakhaleko chifukwa chakuti ngati akadakhalako, iye sakadalola kuvutika kwakukulu ndi kuipa kochuluka chotero. Moyo ulibe tanthauzo lirilonse kusiyapo kuti ndiwo liŵiro lothamangira ku imfa.’ Sindinazindikire chifukwa chake zinthu zinali motero.
Kuyambika kwa Kusintha
Tsiku lina mu 1977, Mboni za Yehova ziŵiri zinagogoda pachitseko pathu. Mwamuna wanga, Giancarlo anaziitana kuloŵa m’nyumba, ndipo anakakhala kuchipinda chochezera kukakambitsirana. Cholinga cha mwamuna wanga chinali kuwasintha kukhala okhulupirira chisinthiko mofanana naye, koma iwo ndiwo amene anasintha kulingalira kwake!
Posakhalitsa Giancarlo anayamba kupanga masinthidwe m’moyo wake. Iye anayamba kukhala woleza mtima kwambiri, akumathera nthaŵi yochuluka ndi chisamaliro kwa ine ndi mwana wathu wamkazi. Iye anayesa kulankhula nane za zinthu zimene anali kuphunzira, koma ndinkathetsa kukambitsiranako mwaukali.
Ndiyeno tsiku lina pamene Mbonizo zinafika, ndinakhala pansi ndipo ndinamvetseradi. Iwo analankhula za mapeto a dongosolo lazinthu ndi za Ufumu wa Mulungu, dziko lapansi Laparadaiso, ndi kuukitsidwa kwa akufa. Ndinazizwa! Sindinathe kugona kwa mausiku atatu otsatira! Ndinafuna kuphunzira zambiri, koma kunyada kwanga kunandilepheretsa kufunsa mafunso mwamuna wanga. Ndiyeno tsiku lina anandiuza molimba mtima kuti: “Lero udzamvetsera. Ndiri ndi mayankho a mafunso ako onse.” Kenaka ananditsanulira chowonadi cha Baibulo.
Giancarlo anandiuza kuti dzina la Mlengi ndilo Yehova, ndikuti mkhalidwe Wake waukulu ndiwo chikondi, kuti Iye anatumiza Mwana Wake monga dipo kotero kuti tikakhale ndi moyo wosatha, ndi kuti pambuyo pake akawononga oipa pa Armagedo, Yesu Kristu akaukitsa akufa mkati mwa Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi. Iye ananena kuti oukitsidwawo akatukulidwira kuungwiro mwamaganizo ndi kuthupi ndipo akakhala ndi mwaŵi wakukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la Paradaiso.
Tsiku lotsatira, ndinatsagana ndi mwamuna wanga kumka ku Nyumba Yaufumu kwanthaŵi yoyamba. Pambuyo pake ndinamuuza kuti: “Anthu awa amakondana. Ndifuna kupitirizabe kudza kuno chifukwa chakuti iwo ngachimwemwedi.” Ndinayamba kufika pamisonkhano mokhazikika, ndi phunziro Labaibulo linachititsidwa nane. Ndinalingalira kwambiri za zimene ndinkaphunzira ndipo posakhalitsa ndinakhutira maganizo kuti ndapezadi anthu enieni a Mulungu. Mu January 1979, mwamuna wanga ndi ine tinasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova mwakubatizidwa.
Uminisitala Wanthaŵi Zonse
Pambuyo pake chaka chimenecho pa msonkhano wadera, panaperekedwa nkhani yolimbikitsa ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse. Ndinasonkhezeredwa kuyamba utumikiwo, ndipo ndinafikira Yehova m’pemphero ponena za nkhaniyo. Komano ndinakhala ndi pakati, ndipo makonzedwe anga anadodometsedwa. Mkati mwa zaka zinayi zotsatira, tinakhala ndi ana atatu. Aŵiri a iwo anadwala kwakayakaya, panthaŵi zosiyana. Mokondweretsa, onse anachira bwinobwino.
Tsopano ndinalingalira kuti sindingathenso kuzengeleza makonzedwe anga akuchita uminisitala wanthaŵi zonse. Ndinaleka ntchito yanga yakuthupi kuti ndisamalire bwino kwambiri mathayo anga monga mkazi ndi nakubala. Mwamuna wanga ndi ine tinapanga makonzedwe akudalira pa malipiro amodzi, zomwe zinatanthauza kulepa zinthu zosafunikira zonse. Komabe, Yehova anatidalitsa molemera, ndipo sanatitaye konse kukhala amphaŵi kapena osoŵa.
Mu 1984, mwana wanga wamkazi yemwe panthaŵiyo anali wazaka 15 ndipo anali atangobatizidwa kumene, anayamba uminisitala wanthaŵi zonse monga mpainiya. Panthaŵi imodzimodziyo, mwamuna wanga anaikidwa kukhala mkulu. Nanga ine? Ndikumalingalira kuti sindikathabe kuchita upainiya, ndinaika chonulirapo cha maola 30 pamwezi m’ntchito yolalikira. Ndinachifikira ndipo ndinati: ‘Ndachita bwino! Ukuchita zochuluka.’
Komabe, kachiŵirinso, kunyada kunakhala vuto langa. (Miyambo 16:18) Ndinapitiriza kulingalira kuti ndinkachita bwino ndipo sindinafunikire kupanga kupita patsogolo kwauzimu kwina kulikonse. Mkhalidwe wanga wauzimu unayamba kunyentchera, ndipo ndinayamba kutaikiridwa ndi mikhalidwe yabwino yomwe ndidapeza. Ndiyeno ndinalandira chilango chofunikira.
M’chaka cha 1985 oyang’anira oyendayenda aŵiri ndi akazi awo anali alendo athu pamene anali pakucheza kwawo kwanthaŵi zonse kochezetsa mpingo wathu. Kuwona Akristu odzichepetsa, odzimana ameneŵa kunandipangitsa kusinkhasinkha pankhaniyo. Ndinafufuza nkhani ya kudzichepetsa, ndikumagwiritsira ntchito mabukhu a Watch Tower Society. Ndinalingalira za kudzichepetsa kwakukulu kumene Yehova amasonyeza pochita nafe anthu ochimwa. (Salmo 18:35) Ndinadziŵa kuti ndinafunikira kusintha kulingalira kwanga.
Ndinachonderera Yehova kundithandiza kukulitsa kudzichepetsa kotero kuti ndimtumikire monga momwe anafunira ndi kunditsogolera kugwiritsira ntchito mphatso zomwe ndinali nazo kumlemekeza. Ndinalemba chofunsirira utumiki waupainiya, ndipo ndinayamba kumtumikira muutumiki wanthaŵi zonse mu March 1989.
Tsopano ndingathe kunena kuti ndiridi wachimwemwe ndikuti kudzichepetsa ndiko kwachititsa chimwemwe changa. Ndapeza chifuno chenicheni cha moyo—cha kuthandiza anthu osoŵa kuti adziwe kuti Yehova, Mulungu wowona, sali patali ndi omfunafuna iye.—Monga momwe yasimbidwira ndi Vera Brandolini.