Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/15 tsamba 8-13
  • Yehova Amakhululukira Koposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amakhululukira Koposa
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Machimo Ena Osakhululukidwa
  • Machimo Awo Anali Osakhululukidwa
  • Machimo Awo Anakhululukidwa
  • Zifukwa za Kudalira Chikhululukiro cha Mulungu
  • Chithandizo Chochokera kwa Amuna Achikulire
  • Mulungu Amapatsa Mphamvu
  • Kodi Mwachimwira Mzimu Woyera?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Ndi Tchimo Liti Limene Munthu Sangakhululukidwe?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Pali Tchimo Limene Silingakhululukidwe?
    Galamukani!—2003
  • Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/15 tsamba 8-13

Yehova Amakhululukira Koposa

“Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; . . . pakuti iye adzakhululukira koposa.”​—YESAYA 55:7.

1. Kodi awo okhululukiridwa ndi Yehova amakhala ndi dalitso lotani tsopano?

YEHOVA amakhululukira ochimwa olapa ndi kuwatheketsa tsopano kusangalala ndi mtendere wa maganizo m’paradaiso wauzimu. Zimenezi ziri choncho chifukwa chakuti amakwaniritsa zofunika izi: “Funani Yehova popezeka iye, itanani iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti iye adzakhululukira koposa.”​—Yesaya 55:6, 7.

2. (a) Kodi ‘kufuna Yehova’ ndi ‘kubwerera kwa iye,’ kumatanthauzanji malinga nkunena kwa Yesaya 55:6, 7? (b) Kodi nchifukwa chiyani akapolo Achiyuda mu Babulo anafunikira kubwerera kwa Yehova, ndipo kodi chinachitika nchiyani kwa ena a iwo?

2 “Kufuna Yehova” ndi kuitanira pa iye ndi kuyanjidwa, munthu woipa ayenera kusiya njira zake zoipa ndi malingaliro alionse akuchitira ena zoipa. Kufunika kwa “kubwerera kwa Yehova” kumasonyeza kuti woipayo anasiya Mulungu, amene poyamba anali naye unansi wathithithi. Zinali choncho ndi anthu okhala mu Yuda, amene pomalizira pake kusakhulupirika kwawo kwa Mulungu kunawatengera ku ukapolo m’Babulo. Ayuda okhala muukapolo anafunikira kubwerera kwa Yehova mwakulapa ntchito zoipa zimene zinawapangitsa kutengeredwa ku ndende ya ku Babulo ndi zaka 70 zonenedweratu za kupasuka kwa mudzi wawo. Mu 537 B.C.E., dzikolo linakhalidwanso ndi Ayuda otsalira owopa Mulungu omasulidwa ku Babulo ndi lamulo la boma. (Ezara 1:1-8; Danieli 9:1-4) Kubwezeretsedwako kunali ndi ziyambukiro zazikulu chotani nanga kwakuti dziko la Yuda linayerekezeredwa ndi Paradaiso wa Edene.​—Ezekieli 36:33-36.

3. Kodi ndimotani mmene otsalira a Israyeli wauzimu akhalira ndi chokumana nacho chofanana ndi cha akapolo owopa Mulungu amene anabwerera ku Yuda?

3 Aisrayeli auzimu akhala ndi chokumana nacho chofanana ndi cha Ayuda owopa Mulungu amene anabwerera ku Yuda pambuyo pa ukapolo ku Babulo. (Agalatiya 6:16) Otsalira a Israyeli wauzimu anasintha njira zawo ndi malingaliro awo itangotha Nkhondo Yadziko I. Chaka cha 1919 chinali mapeto a ukapolo wawo wakusakhala ndi chiyanjo chonse cha Mulungu mu ulamuliro wa Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Chifukwa chakuti analapa machimo awo ophatikizapo kuwopa munthu ndi kusachita ntchito mu utumiki wa Yehova, anawamasula kuchoka ku Babulo Wamkulu, kuwabweretsa ku mudzi wawo wabwino wauzimu, ndi kuwayambitsanso ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu. Paradaiso wauzimu wasefukira pakati pa anthu a Mulungu kuyambira panthaŵiyo, kukulemekeza dzina lake loyera. (Yesaya 55:8-13) Pamenepa, m’chochitika chenicheni chamakedzana ndi chamakono chophiphiritsira, tiri ndi umboni wowonekera bwino wakuti chikhululukiro chaumulungu chimadzetsa madalitso ndi kuti Yehova amakhululukiradi koposa olapawo.

4. Kodi atumiki a Yehova ena ali ndi mantha otani?

4 Chifukwa chake, Atumiki a Yehova amakono angadalire chikhululukiro chake. Komabe, ena a iwo ali okhwethemulidwa ndi zochimwa zawo zakale, ndipo malingaliro oipa amawalefula. Amadzilingalira kukhala osayenera kukhala m’paradaiso wauzimu. Kunena zowona, ena amawopa kuti anachita tchimo losakhululukidwa ndipo sadzakhululukidwa konse ndi Yehova. Kodi nzotero?

Machimo Ena Osakhululukidwa

5. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti machimo ena ali osakhululukidwa?

5 Machimo ena ngosakhululukidwa. Yesu Kristu anati: “Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa mzimu woyera sichidzakhululukidwa.” (Mateyu 12:31) Chotero pamenepa, wochitira mwano mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, sadzakhululukiridwa. Mtumwi Paulo anasonya ku tchimo lotero pamene analemba kuti: “Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, . . . koma anagwa m’chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.”​—Ahebri 6:4-6.

6. Kodi nchiyani chimapangitsa tchimo kukhala lokhululukidwa kapena losakhululukidwa?

6 Mulungu yekha ndiye amadziŵa ngati munthu wachita tchimo losakhululukidwa. Komabe, Paulo anadziŵitsa za nkhaniyi pamene analemba kuti: “Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziŵitso cha chowonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina kowopsa kwa chiweruziro.” (Ahebri 10:26, 27) Munthu wodzigangira amachita zinthu mwadala, kapena ali “wouma khosi ndipo kaŵirikaŵiri amaumirira pa malingaliro akeake.” (Webster’s New Collegiate Dictionary) Aliyense wopitiriza kuchita tchimo modzigangira ndi mouma khosi pambuyo pakuzindikira chowonadi sakhululukiridwa. Chotero, chimene chimapangitsa tchimo kukhala lokhululukidwa kapena losakhululukidwa kwenikweni sitchimolo mwa ilo lokha, koma mkhalidwe wa mtima, kudzigangira kumene kumaphatikizidwapo. Kumbali ina, kodi nchiyani mwachiwonekere chimene chiri nkhani pamene Mkristu wochimwa avutika maganizo kwambiri kaamba ka uchimo wake? Mwinamwake nkhaŵa yake yaikulu imasonyeza kuti iye sanachite tchimo losakhululukidwa.

Machimo Awo Anali Osakhululukidwa

7. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti otsutsa Yesu ena achipembedzo anachita tchimo losakhululukidwa?

7 Atsogoleri achipembedzo Achiyuda ena amene anatsutsa Yesu anachimwa mwadala, ndipo motero anachita tchimo losakhululukidwa. Ngakhale kuti anawona mzimu woyera wa Mulungu ukugwira ntchito mwa Yesu pamene anachita zabwino ndi kuchita zozizwitsa, akuluakulu achipembedzo amenewo anati mphamvu zake zinachokera kwa Beelzebule, kapena Satana Mdyerekezi. Anachimwa akudziŵa bwino lomwe za kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu. Motero, anachita tchimo losakhululukidwa, chifukwa Yesu anati: “Koma amene aliyense anganenere mzimu woyera zoipa sadzakhululukidwa nthaŵi ino kapena irinkudzayo.”​—Mateyu 12:22-32.

8. Kodi nchifukwa ninji tchimo la Yudasi Isikariote linali losakhululukidwa?

8 Tchimo la Yudasi Isikariote nalonso linali losakhululukidwa. Kupereka kwake Yesu kunali kwadala, akumafikitsa pachimake njira yake yonyenga ndi yosawona mtima mwadala. Mwachitsanzo, pamene Yudasi anawona Mariya akudzoza Yesu mafuta a mtengo wapatali, iye anafunsa kuti: “Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi malupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?” Mtumwi Yohane anawonjezera kuti: “Koma [Yudasi] ananena ichi sichifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.” Mwamsanga pambuyo pake, Yudasi anapereka Yesu ndi ndalama zasiliva 30. (Yohane 12:1-6; Mateyu 26:6-16) Ndithudi, Yudasi anamva chisoni ndipo anadzipha. (Mateyu 27:1-5) Koma iye sanakhululukiridwe, popeza kuti kuchita kwake kwadala, njira yadyera yosalapa ndi ntchito zake zonyenga zinasonyeza kuchimwira kwake mzimu woyera. Kunali koyenerera kotani nanga kuti Yesu anatcha Yudasi “mwana wachitayiko”!​—Yohane 17:12; Marko 3:29; 14:21.

Machimo Awo Anakhululukidwa

9. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anakhululuka machimo a Davide ogwirizanitsidwa ndi Batisheba?

9 Machimo adala amasiyana kotheratu ndi zolakwa zimene zimakhululukidwa ndi Mulungu. Tawonani chitsanzo cha Mfumu Davide ya Israyeli. Iye anachita chigololo ndi Batisheba, mkazi wa Uriya, ndipo pambuyo pake anauza Yoabu kuchita chiwembu chakuti Uriya aphedwe m’nkhondo. (2 Samueli 11:1-27) Nchifukwa ninji Mulungu anachitira chifundo Davide? Kwakukulukulu chifukwa cha pangano la Ufumu komanso chifukwa cha chifundo cha Davide ndi kulapa kwake kowona mtima.​—1 Samueli 24:4-7; 2 Samueli 7:12; 12:13.

10. Ngakhale kuti Petro anachita tchimo lowopsa, nchifukwa ninji Mulungu anamkhululukira?

10 Talingaliraninso mtumwi Petro. Anachita tchimo lowopsa mwakubwerezabwereza kukana Yesu. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anakhululukira Petro? Mosiyana ndi Yudasi Isikariote, Petro anakhala wowona mtima muutumiki wa Mulungu ndi Kristu. Tchimo la mtumwiyu linali chifukwa cha kufooka kwa thupi, ndipo analapadi ndi ‘kulira moŵaŵa mtima.’​—Mateyu 26:69-75.

11. Kodi “kulapa” mungakufotokoze bwanji, ndipo kodi munthu ayenera kuchitanji ngati iye walapadi?

11 Zitsanzo zotchulidwazo zimasonyeza kuti ngakhale munthu amene wachita tchimo lowopsa angapeze chikhululukiro cha Yehova Mulungu. Koma kodi ndi kaimidwe kotani kamaganizo kamene kafunikira kuti munthu akhululukiridwe? Kulapa kowona nkofunika ngati Mkristu wolakwa ati akhululukiridwe ndi Mulungu. Kulapa kumatanthauza “kutembenuka ku uchimo chifukwa cha kupwetekedwa mtima ndi zinthu zoipa zimene zinachitidwa kale” kapena “kumva chisoni kapena kumva manyazi ndi zimene munthuwe wachita kapena zimene wapewa kuchita.” (Webster’s Third New International Dictionary) Munthu wolapa mowona mtima akasonyeza kumva chisoni pachitonzo chirichonse, chisoni, kapena mavuto amene tchimo lake linadzetsa pa dzina la Yehova ndi gulu lake. Wochimwa wolapa akawonetsanso zipatso zoyenerera kulapa, kuchita ntchito zogwirizana ndi kulapa. (Mateyu 3:8; Machitidwe 26:20) Mwachitsanzo, ngati iye anabera munthu wina, ayenera kutenga njira yoyenerera kubwezera chotaikacho. (Luka 19:8) Mkristu wolapa woteroyo ali ndi zifukwa zabwino za Malemba zakudalira kuti Yehova adzamkhululukira koposa. Kodi zimenezi nchiyani?

Zifukwa za Kudalira Chikhululukiro cha Mulungu

12. Kodi lemba la Salmo 25:11 limasonyeza kuti munthu wolapa angapempherere chikhululukiro pa maziko otani?

12 Wochimwa wolapa mwachidaliro angapempherere chikhululukiro pa maziko a dzina la Yehova. Davide anapempha kuti: “Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.” (Salmo 25:11) Pemphero lotero, limodzi ndi kulapa kwa chitonzo chimene wochimwayo wadzetsa pa dzina la Mulungu, liyenera kukhalanso monga chopinga ku tchimo lalikulu m’tsogolo.

13. Kodi pemphero limachita mbali yanji m’chikhululukiro chaumulungu?

13 Yehova Mulungu amayankha mapemphero ochoka mumtima a atumiki ake olakwa koma olapa. Mwachitsanzo, Yehova sanatseke makutu ake kwa Davide, amene anapemphera kuchokera mumtima pambuyo pakuzindikira kuwopsa kwa machimo ake ophatikizapo Batisheba. Kwenikweni, mawu a Davide mu Salmo 51 amafotokoza mapembedzero ake ambiri. Iye anapempha kuti: “Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima woseka ndi wolapa.”​—Salmo 51:1, 2, 17.

14. Kodi Malemba amapereka chitsimikiziro chotani kuti Mulungu amakhululukira awo amene amaika chikhulupiriro m’nsembe yadipo ya Yesu?

14 Mulungu amakhululukira awo amene amasonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu. Paulo analemba kuti: “Tiri ndi mawomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.” (Aefeso 1:7) Mofanana ndi tanthauzo limeneli, mtumwi Yohane analemba kuti: “Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.”​—1 Yohane 2:1, 2.

15. Kodi wochimwa wolapa ayenera kuchitanji kuti apitirize kukhala ndi chifundo cha Mulungu?

15 Chifundo cha Yehova chimapatsa wochimwa wolapa maziko a chidaliro kuti iye angakhululukiridwe. Nehemiya ananena kuti: “Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo.” (Nehemiya 9:17; yerekezerani ndi Eksodo 34:6, 7.) Ndithudi, kuti apitirize kusangalala ndi chifundo chaumulungu, wochimwayo ayenera kuyesayesa kusunga lamulo la Mulungu. Monga momwe wamasalmo ananenera, “nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa. Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.”​—Salmo 119:77, 156.

16. Kodi nchitonthozo chanji chimene chiripo nchenicheni chakuti Yehova amalingalira mkhalidwe wathu wochimwa?

16 Chenicheni chakuti Yehova amalingalira mkhalidwe wathu wochimwa chimapatsanso chitonthozo wochimwa wolapayo ndi chifukwa cha kupemphera ndi chidaliro kuti Mulungu adzamkhululukira. (Salmo 51:5; Aroma 5:12) Wamasalmo Davide anapereka chitsimikiziro chotonthoza pamene analengeza kuti: “[Yehova Mulungu] sanachitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuwopa iye. Monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:10-14) Inde, Atate wathu wakumwamba alidi wachifundo koposa ndi wokoma mtima kuposa kholo laumunthu.

17. Kodi mbiri ya munthu yakale ya utumiki wokhulupirika kwa Mulungu iri ndi mbali yanji pachikhululukiro?

17 Wochimwa wolapa angapempherere chikhululukiro ndi chidaliro chakuti Yehova sadzanyalanyaza mbiri yake yautumiki wokhulupirika wapapitapo. Nehemiya sanali kupembedzera chikhululukiro cha tchimo lake, koma anati: “Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.” (Nehemiya 13:31) Mkristu wolapa angapeze chitonthozo m’mawu awa: “Pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachiwonetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

Chithandizo Chochokera kwa Amuna Achikulire

18. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati tchimo la Mkristu lampangitsa kukhala wodwala mwauzimu?

18 Bwanji ngati Mkristu akudzimva kukhala wosayenerera kukhalabe m’paradaiso wauzimu kapena sakutha kupemphera chifukwa tchimo lake lampangitsa kudwala mwauzimu? “Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la [Yehova, NW],” analemba motero wophunzira Yakobo. “Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo [Yehova, NW] adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.” Inde, akulu ampingo angapemphere mogwira mtima ndi wokhulupirira mnzathu wolapa ndi chiyembekezo chakumbwezeretsera thanzi lake lauzimu labwino.​—Yakobo 5:14-16.

19. Ngati munthu wachotsedwa, kodi ayenera kuchitanji kuti akhululukiridwe ndi kubwezeretsedwa?

19 Ngakhale ngati komiti yachiweruzo yachotsa wochimwa wosalapa, sikukutanthauza kuti iye wachita tchimo losakhululukidwa. Komabe, kuti akhululukiridwe ndi kubwezeretsedwa, ayenera kumvera malamulo a Mulungu modzichepetsa, kutulutsa zipatso zogwirizana ndi kulapako, ndipo kulembera akulu pempho la kubwezeretsedwa. Pambuyo pakuchotsedwa kwa wochita chigololo mu mpingo m’Korinto wakale, Paulo analemba kuti: “Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira; kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo angamizidwe ndi chisoni chochulukacho. Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.”​—2 Akorinto 2:6-8; 1 Akorinto 5:1-13.

Mulungu Amapatsa Mphamvu

20, 21. Kodi nchiyani chingathandize munthu amene akudera nkhaŵa ponena za kuti mwina anachita tchimo losakhululukidwa?

20 Ngati zinthu zonga thanzi lofooka kapena kupsinjika maganizo zikupangitsa munthu kuvutika mtima kuti anachita tchimo losakhululukidwa, kupeza mpumulo wabwino ndi kugona kungathandize. Komabe, makamaka muyenera kukumbukira mawu a Petro akuti: ‘Tayani pa [Mulungu] nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.’ Ndipo musalole nkomwe Satana kukukhwethemulani, chifukwa Petro akupitiriza kuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire; ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵawa zomwezo zirimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko. Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, . . . adzafikitsa inu opanda chirema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.”​—1 Petro 5:6-10.

21 Chotero ngati muli wachisoni koma wamantha kuti munachita tchimo losakhululukidwa, kumbukirani kuti njira za Yehova nzanzeru, zolungama ndi zachikondi. Chifukwa chake, pempherani kwa iye m’chikhulupiriro. Pitirizani kudya chakudya chauzimu chimene amagaŵira kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Sonkhanani ndi okhulupirira anzanu ndi kukhala ndi phande muuminisitala Wachikristu mokhazikika. Zimenezi zidzalimbikitsa chikhulupiriro chanu ndipo zidzakumasulani ku mantha akuti mwina Mulungu sanakhululuke tchimo lanu.

22. Kodi tidzapendanso chiyani?

22 Okhala m’paradaiso wauzimu angatonthozedwe ndi chidziŵitso chakuti Yehova amakhululukira koposa. Komabe, moyo wawo lerolino suli wopanda ziyeso. Mwinamwake ali opsinjika maganizo chifukwa cha imfa ya wokondedwa kapena bwenzi lokondedwa likudwala kwambiri. Monga momwe tidzawonera, m’mikhalidwe imeneyi ina, Yehova amathandiza ndi kutsogolera anthu ake ndi mzimu wake woyera.

Kodi Mayankho Anu Ngotani?

◻ Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti Yehova ‘amakhululukira koposa’?

◻ Kodi nditchimo lotani limene lilibe chikhululukiro?

◻ Kodi machimo a munthu amakhululukidwa pa mikhalidwe yotani?

◻ Kodi nchifukwa ninji ochimwa olapa angadalire chikhululukiro cha Mulungu?

◻ Kodi nchithandizo chotani chimene chiripo kaamba ka ochimwa olapa?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mumadziŵa chifukwa chake Davide ndi Petro anakhululukiridwa koma Yudasi Isikariote sanatero?

[Chithunzi patsamba 12]

Chithandizo cha akulu ampingo chingachite zazikulu kuthandiza Mkristu mwauzimu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena