Kodi Mtundu wa Anthu Ukufunikiradi Mesiya?
“DZIKO LIKUFUNIKIRA MESIYA, IKUTERO NDUNA YA BOMA”
Mutuwo unali mu The Financial Post ya ku Toronto, Canada, mu 1980. Nduna yogwidwa mauwoyo inali Aurelio Peccei, pulezidenti ndi woyambitsa gulu lotchuka loyang’anira mavuto a chitaganya lotchedwa Club of Rome. Malinga nkunena kwa Post, Peccei anakhulupirira kuti “mtsogoleri wachisomo—wa sayansi, wa ndale zadziko, kapena wa chipembedzo—ndiye angakhale njira yokha yopulumukira dziko ku zipsinjo za chitaganya ndi zamalonda zimene zikuwopseza kuwononga kutsungula.” Kodi muganiza bwanji? Kodi dzikoli liridi mumkhalidwe wowopsa kwakuti mtundu wa anthu ufunikiradi Mesiya? Talingalirani limodzi lokha la mavuto amene dzikoli likuyang’anizana nawo—njala.
MASO aakulu aŵiri, ofiira akukuyang’anani pachithunzithunzi cha nyuzipepala kapena magazini. Ali maso a mwana, mtsikana wamng’ono wosafika ngakhale zaka zisanu. Koma maso ameneŵa sioseketsa kwa inu. Mwa iwo mulibe chikondwerero chija chaubwana, mulibe lingaliro lakudabwa kwachimwemwe, mulibe chidaliro chopanda nkhaŵa. Mmalomwake, ngodzala nkhaŵa yopweteka mtima, kulobodoka ndi kufooka, njala yopanda nayo chiyembekezo. Mwanayo akufa ndi njala. Moyo wake chikhalire wakhala wanjala ndi kusautsika basi.
Mwinamwake, mofanana ndi ambiri, simumafuna kuwonetsetsa zithunzi zoterozo, chotero mwamsanga mutembenukira ku tsamba lina. Sindiye kuti simusamalira, koma kuti mukumva kukhala wogwiritsidwa mwala chifukwa mukuwona kuti nthaŵi yatha kale kwa mtsikanayu. Ziŵalo zowonda ndi mimba yofufuma ziri zizindikiro zakuti thupi lake layamba kale kunyozololoka. Panthaŵi imene mukuwona chithunzithunzi chake, mwinamwake ayenera kukhala anafa kale. Zoipirapo, mukudziŵa kuti mkhalidwe wake suli kokha wa apo ndi apo.
Kodi vutolo nlalikulu motani? Eya, kodi mungayerekezere ana mamiliyoni 14? Ambirife sitingatero; chiŵerengerocho nchachikulu kwambiri kuchiyerekezera. Pamenepa, tayerekezerani sitediyamu yokwana kukhala anthu 40,000. Tsopano yerekezerani kuti yadzazidwa thothotho ndi ana—mmizera yonse, m’mindandanda yonse, ngati nyanja ya nkhope zokhazokha. Ngakhale zimenezo nzosamvetsetseka kuziyerekezera. Komabe, kukafunikira masitediyamu oterowo 350 odzaza ndi ana kuti afikire mamiliyoni 14. Malinga nkunena kwa UNICEF (United Nations Children’s Fund), ndicho chiŵerengero chowopsa cha ana ochepera pa zaka zisanu amene amafa chaka chirichonse chifukwa cha kusadya chakudya chathanzi chokwanira ndi matenda otetezereka mosavuta m’maiko osatukuka. Zimenezi zimakwanira sitediyamu imodzi yodzala ndi ana amene akufa tsiku lirilonse! Wonjezerani pamenepa chiŵerengero cha akulu amene ali ndi njala, ndipo mudzapeza chiŵerengero cha dziko lonse cha anthu mamiliyoni chikwi chimodzi imodzi amene sakudya chakudya chathanzi chokwanira nthaŵizonse.
Nchifukwa Ninji Kuli Njala Yotere?
Pulaneti lathu pakali pano limatulutsa chakudya chambiri choposa chimene anthu amadya tsopano, ndipo likhozabe kutulutsa chochulukirapo. Komabe, pamphindi iriyonse, ana 26 amafa chifukwa chakusowa chakudya chathanzi ndi matenda. Pamphindi imodzimodziyo, dziko limawononga pafupifupi $US2,000,000 kukonzekera nkhondo. Kodi mungayerekezere zimene ndalama zonsezo—kapena mbali yaing’ono ya ndalamazo—ingachite kwa ana 26 amenewo?
Mwachiwonekere, njala yadziko lonse singanenedwe kukhala ikuchititsidwa kokha ndi kupereŵera kwa chakudya kapena ndalama. Vutolo nlalikulu koposa. Monga momwe Jorge E. Hardoy, pulofesa wa ku Argentina anafotokozera kuti “dziko lonse lathunthu likusoŵa luso lakugaŵira chitonthozo, mphamvu, nthaŵi, zofunikira ndi chidziŵitso kwa awo amene amafunikira kwambiri zinthu zimenezi.” Inde, vutolo siliri ndi zinthu zothandizira munthu, koma munthu mwiniyo. Umbombo ndi dyera zikuwonekera kukhala zikulamulira mphamvu ya anthu m’chitaganya. Mbali imodzi mwa zisanu ya chiŵerengero cha dziko lapansi ali ampondamatiki amene amasangalala koposa kuŵirikiza nthaŵi 60 ndi zinthu zambiri ndi mautumiki koposa mmene imachitira mbali imodzi mwa zisanu ya aumphaŵi.
Zowona, ena mowona mtima akuyesa kupititsa chakudya kwa anjala, koma zoyesayesa zawo zimalepheretsedwa ndi zochitika zosapeŵeka. Njala kaŵirikaŵiri imakantha maiko amene akumenyana nkhondo za chiweniweni kapena chipanduko, ndipo sikwachilendo kuwona gulu loukira likutsekereza zakudya kusafikira osoŵa. Mbali zonse ziŵiri zimawopa kuti mwakulola chakudya kufika kwa anthu wamba ovutika ndi njala m’dera la mdani, akakhala akudyetsa adani awo. Maboma amagwiritsira ntchito njala monga chida cha ndale zadziko.
Kodi Palibe Njira Yothetsera?
Mwatsoka, vuto la mamiliyoni ovutika ndi njala sindilo lokha limene likukantha munthu wa makono. Kuwononga komakulakula ndi kuipitsa malo athu okhala, mliri wopitirira wa nkhondo umene ukuwononga mamiliyoni a anthu, mliri wachiwawa chaupandu umene umadzetsa mantha ndi kusakhulupirirana kulikonse, ndi kululuzika kwa makhalidwe kumene kukuwonekera kukhala koyambitsa zovuta zonsezi—mavuto onseŵa apadziko lonse amagwirizana, titero kunena kwake, ndi kutsimikizira chowonadi chosapeŵeka—munthu sangathe kudzilamulira yekha mwachipambano.
Mosakaikira, ndicho chifukwa chake anthu ambiri ataya mtima ponena za kuwona chothetsera mavuto onse a dziko. Ena amalingalira monga momwe anachitira Aurelio Peccei, katswiri wa ku Italiya wotchulidwa poyambirirapo. Ngati kuti kudzakhale chothetsera, iwo atero, chiyenera kuchokera ku magwero—achilendo—mwinamwake ngakhale osakhala aumunthu. Motero lingaliro la mesiya liri ndi kukopa kwamphamvu. Koma kodi nkoyenereradi kuyembekezera mesiya? Kapena kodi chiyembekezo choterocho ndiloto chabe lokhumbira?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Cover photos: Top: U.S. Naval Observatory photo; Bottom: NASA photo
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
WHO photo by P. Almasy
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
WHO photo by P. Almasy
U.S. Navy photo