Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 10/15 tsamba 8-13
  • Makonzedwe a Yehova Achikondi a Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makonzedwe a Yehova Achikondi a Banja
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Banja m’Nthaŵi za m’Baibulo
  • Mbali ya Amuna Achikristu
  • Akazi Achikristu Ochirikiza
  • Ana Oyamikira
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Malangizo Anzeru kwa Okwatirana
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu Monga Mwamuna
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 10/15 tsamba 8-13

Makonzedwe a Yehova Achikondi a Banja

“Chifukwa cha ichi ndipinda mawondo anga kwa Atate, amene kuchokera kwa iye [banja, NW] lonse la m’mwamba ndi dziko lapansi alitcha dzina.”​—AEFESO 3:14, 15.

1, 2. (a) Kodi ndicholinga chotani chimene Yehova analengera banja? (b) Kodi ndimbali yotani imene banja liyenera kukhala nayo m’makonzedwe a Yehova lerolino?

YEHOVA analenga chimangidwe cha banja. Mwa ilo, anachita zoposa kungokhutiritsa chikhumbo cha munthu cha unansi, chichirikizo, kapena chikondi. (Genesis 2:18) Banja linali njira mwa imene chifuniro chaulemerero cha Mulungu cha kudzaza dziko lapansi chikakwaniritsidwa. Iye anauza okwatirana oyambirirawo kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Mkhalidwe wachikondi ndi wachisamaliro wa m’banja ukakhaladi wopindulitsa kwa miyandamiyanda ya ana omwe akabadwa kwa Adamu ndi Hava ndi mbadwa zawo.

2 Komabe, okwatirana oyambirira amenewo anasankha njira yakusamvera​—yokhala ndi zotulukapo zatsoka kwa iwo eni ndi ana awo. (Aroma 5:12) Chotero moyo wa banja lerolino ngwosokonezedwa kusiyana ndi chimene Mulungu anafuna kuti ukhale. Chikhalirechobe, banja likupitirizabe kukhala ndi malo ofunika kwambiri m’makonzedwe a Yehova, likumakhala maziko a chitaganya Chachikristu. Sitikunena zimenezi mwakusayamikira ntchito yabwino imene ikuchitidwa ndi Akristu ambiri pakati pathu amene ndimbeta. Mmalomwake, tikuyamikiranso chithandizo chachikulu chimene mabanja nawonso akuchipereka pamkhalidwe wabwino wauzimu wa gulu Lachikristu lonse. Mabanja olimba amamanga mipingo yolimba. Komabe, kodi ndimotani mmene banja lanu lingapitire patsogolo pamene likuyang’anizana ndi zovuta za lerolino? Kupeza yankho, tiyeni tipendetu zimene Baibulo limanena pamakonzedwe abanja.

Banja m’Nthaŵi za m’Baibulo

3. Kodi ndimbali zotani zimene mwamuna ndi mkazi anachita m’banja la makolo akale?

3 Onse aŵiri Adamu ndi Hava anakana makonzedwe a umutu wa Mulungu. Koma amuna achikhulupiriro, monga Nowa, Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yobu, moyenerera anatenga malo awo, monga mitu yabanja. (Ahebri 7:4) Banja la makolo akale linali ngati kaboma, atate akumakhala mtsogoleri wachipembedzo, mlangizi, ndi woweruza. (Genesis 8:20; 18:19) Akazinso anali ndi mbali yofunika, akumatumikira osati monga akapolo koma monga oyang’anira nyumba othandiza.

4. Kodi ndimotani mmene moyo wa banja unasinthira pansi pa Chilamulo cha Mose, koma kodi ndimbali yotani imene makolo anapitiriza kuchita?

4 Pamene Israyeli anakhala mtundu mu 1513 B.C.E., lamulo labanja linakhala pansi pa Chilamulo cha mtundu choperekedwa kupyolera mwa Mose. (Eksodo 24:3-8) Mphamvu yakupanga chosankha, kuphatikizapo pankhani zochita ndi moyo ndi imfa, tsopano inapatsidwa kwa oweruza oikidwa. (Eksodo 18:13-26) Ansembe Achilevi anatenga mathayo akupereka nsembe m’kulambira. (Levitiko 1:2-5) Komabe, atate anapitirizabe kuchita mbali yaikulu. Mose anafulumiza atate kuti: “Mawu aŵa ndi kuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo mudziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula aŵa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Amayi anali ndi chisonkhezero chachikulu. Miyambo 1:8 inalamula achichepere kuti: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” Inde, pansi pa ulamuliro wa mwamuna wake, mkazi Wachihebri anapanga​—ndi kusungitsa​—lamulo la banja. Iye anayenera kupatsidwa ulemu ndi ana ake ngakhale atakalamba.​—Miyambo 23:22.

5. Kodi Chilamulo cha Mose chinalongosola motani malo a ana m’makonzedwe a banja?

5 Malo a ana analongosoledwanso bwino ndi Chilamulo cha Mulungu. Deuteronomo 5:16 inati: “Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.” Kusalemekeza makolo kunali mlandu wowopsa koposa m’Chilamulo cha Mose. (Eksodo 21:15, 17) “Aliyense wakutemberera atate wake kapena amayi wake,” chinatero Chilamulocho, “azimupha ndithu.” (Levitiko 20:9) Kupandukira makolo kunali kupandukira Mulungu weniweniyo.

Mbali ya Amuna Achikristu

6, 7. Kodi nchifukwa ninji mawu a Paulo pa Aefeso 5:23-29 akuwonekera kukhala anali achilendo ndi osalandirika kwa oŵerenga a m’zaka za zana loyamba?

6 Chikristu chinapereka chidziŵitso chowonjezereka pamakonzedwe a banja, makamaka mbali ya mwamuna. Kunja kwa mpingo Wachikristu, kunali kofala kwa amuna m’zaka za zana loyamba kuchitira akazi awo mwanjira yaukali ndi yotsendereza. Akazi anamanidwa zoyenerera zazikulu ndi ulemu wawo. The Expositor’s Bible limanena kuti: “Mgiriki wophunzitsidwa bwino mwambo anawona mkazi kukhala wombalira ana basi. Mkazi analibe mphamvu iriyonse pachilakolako chake cha kugonana. Chikondi sichinali mbali ya ukwati. . . . Mkazi wonga kapoloyo analibe zoyenerera. Thupi lake linali la mwiniwake kuligwiritsira ntchito paliponse pamene anafunira.”

7 Mumkhalidwe woterowo, Paulo analemba mawuŵa pa Aefeso 5:23-29: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW] ali yekha mpulumutsi wa thupilo. . . . Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda [mpingo, NW], nadzipereka yekha m’malo mwake; . . . amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga.” Kwa oŵerenga a m’zaka za zana loyamba, mawuŵa anali achilendo osalandirika. The Expositor’s Bible ikunena kuti: “Palibe m’Chikristu chimene chinawonekera kukhala chachilendo ndi chotsendereza, poyerekezera ndi makhalidwe olekerera apanthaŵiyo, kuposa lingaliro Lachikristu la ukwati. . . . [Ilo] linayambitsa nyengo yatsopano kwa mtundu wa anthu.”

8, 9. Kodi amuna ali ndi maganizo oipa ofala otani kulinga kwa akazi, ndipo nchifukwa ninji kuli kofunika kuti amuna Achikristu akanize malingaliro oterowo?

8 Uphungu wa Baibulo kwa amuna uli wosalandirika ndi lerolinonso. Mosasamala kanthu ndi zonenedwa zonse za kufunika kwa kupatsa ufulu akazi, akazi akuwonedwabe ndi amuna ambiri monga ongokhutiritsira chikhumbo chakugonana. Pokhulupirira nthanthi yakuti kwenikweni akazi amakonda kutsenderezedwa, kulamuliridwa, kapena kuvutitsidwa, amuna ambiri amachitira nkhanza akazi awo mwakuthupi ndi mwamaganizo. Kukakhala konyazitsa chotani nanga kwa mwamuna Wachikristu kunyengedwa ndi malingaliro akudziko ndi kuchitira mkazi wake mwankhanza! “Mwamuna wanga anali mtumiki wotumikira ndipo anali kupereka nkhani zapoyera,” akutero mkazi wina Wachikristu. Komabe akuulula kuti, “Ndinali mkhole wa kumenyedwa monga mkazi.” Mwachiwonekere, machitidwe oterowo anali osemphana ndi makonzedwe a Mulungu. Mwamunayo anali mmodzi wa oŵerengeka kwambiri; anafunikira kufuna chithandizo chakuletsa mkwiyo wake ngati anafuna kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu.​—Agalatiya 5:19-21.

9 Amuna akulamulidwa ndi Mulungu kukonda akazi awo monga matupi awo. Kukana kuchita zimenezo ndiko kupandukira makonzedwe enieniwo a Mulungu ndipo kukhoza kulepheretsa unansi wa munthuwe ndi Mulungu. Mawu a mtumwi Petro ngomvekera bwino: “Amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, . . . kuti mapemphero anu angaletsedwe.” (1 Petro 3:7) Kuchitira mkazi mwaukali kungakhalenso ndi chiyambukiro chovulaza pamkhalidwe wake wauzimu ndi wa ana ake.

10. Kodi ndinjira zina zotani zimene amuna angachitire umutu wawo m’njira yofanana ndi ya Kristu?

10 Amuna inu, mabanja anu adzakhala achipambano pansi pa umutu wanu ngati muuchita m’njira yonga ya Kristu. Kristu sanali waukali kapena wankhanza. Mosiyana, iye anati: “Phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” (Mateyu 11:29) Kodi banja lanu lingakuneneni kukhala wotero? Kristu anachitira ophunzira ake monga mabwenzi ndipo anawakhulupirira. (Yohane 15:15) Kodi mumapatsa mkazi wanu ulemu wofananawo? Baibulo linati ponena za “mkazi wangwiro”: “Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira.” (Miyambo 31:10, 11) Zimenezo zimatanthauza kumlola kukhala ndi ufulu wakutiwakuti wakuchita ndi kusankha zinthu, osati kummanga ndi ziletso zosayenera. Ndiponso, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kunena zakukhosi kwawo ndi malingaliro. (Mateyu 9:28; 16:13-15) Kodi ndimmene mumachitira kwa mkazi wanu? Kapena kodi mumawona kusagwirizana kowona mtima pakanthu kena kukhala chitokoso pa ulamuliro wanu? Mwakulingalira zoganiza za mkazi wanu mmalo mwakuzinyalanyaza, mumakulitsa kulemekeza kwake umutu wanu.

11. (a) Kodi ndimotani mmene atate angasamalire zosoŵa zauzimu za ana awo? (b) Kodi nchifukwa ninji akulu ndi atumiki otumikira ayenera kupereka chitsanzo chabwino m’kusamalira mabanja awo?

11 Ngati ndinu atate, mufunikiranso kutsogolera m’kusamalira zosoŵa zauzimu, zamaganizo, ndi zakuthupi za ana anu. Zimenezo zimaphatikizapo kukhala ndi dongosolo labwino la zochita zauzimu za banja lanu: kugwira nawo ntchito muutumiki wakumunda, kuchititsa phunziro Labaibulo lapanyumba, kukambitsirana lemba latsiku. Mokondweretsa, Baibulo limasonyeza kuti mkulu kapena mtumiki wotumikira ayenera kukhala “woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha.” Chotero, amuna otumikira m’maudindo ameneŵa ayenera kukhala mitu yabanja yopereka chitsanzo chabwino. Pamene kuli kwakuti ayenera kusenza mtolo wolemera wa mathayo ampingo, ayenera kuika banja la iwo eni pamalo oyamba. Paulo anasonyeza chifukwa chake kuti: “Ngati munthu sadziŵa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji mpingo wa Mulungu?”​—1 Timoteo 3:4, 5, 12.

Akazi Achikristu Ochirikiza

12. Kodi mkazi amachita mbali yanji m’makonzedwe Achikristu?

12 Kodi ndinu mkazi Wachikristu? Pamenepo muyenera nanunso kuchita mbali yofunika m’makonzedwe a banja. Akazi Achikristu akufulumizidwa kuti “akonde amuna awo, akonde ana awo, akhale odziletsa, odekha, ochita m’nyumba mwawo, okoma, akumvera amuna a iwo okha.” (Tito 2:4, 5) Chotero muyenera kuyesayesa kukhala mkazi wachitsanzo chabwino, mukumasunga nyumba kukhala yaukhondo ndi yosangalatsa kwa banja lanu. Ntchito yapanyumba nthaŵi zina ingakhale yotopetsa, koma siyonyazitsa kapena yosaphula kanthu. Monga mkazi, ‘mumaweruzira nyumba’ ndipo mungakhale ndi ufulu waukulu mwakutero. (1 Timoteo 5:14) Mwachitsanzo, “mkazi wangwiro” uja anagula zinthu zapanyumba, anagula munda, ndipo ngakhale kupeza ndalama mwakuchita kabizinesi. Nzosadabwitsa kuti mwamuna wake anamtama! (Miyambo, chaputala 31) Mwachiwonekere, zochita zayekha zimenezo zinachitidwa mwakusalumpha malangizo opatsidwa ndi mwamuna wake monga mutu wake.

13. (a) Kodi nchifukwa ninji kugonjera kungakhale kovuta kwa akazi ena? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kwabwino kwa akazi Achikristu kugonjera kwa amuna awo?

13 Komabe, kugonjera kwa mwamuna wanu kungakhale kovutirapo nthaŵi zina. Siamuna onse amene amayenerera ndi kupeza ulemu. Ndipo inuyo mungakhale waluso kwambiri ponena za kusamalira ndalama, kukonzekera, kapena kulinganiza zinthu. Mwina mungakhale ndi ntchito yakuthupi yabwino ndipo mumathandizira kwambiri kupeza ndalama zapanyumba. Kapena mwina kale munakhalapo ndi vuto la kutsenderezedwa ndi mwamuna ndipo mukukupeza kukhala kovuta kugonjera kwa mwamuna. Komabe, kusonyeza “ulemu waukulu,” kapena “kuwopa,” mwamuna wanu kumasonyeza ulemu wanu wa umutu wa Mulungu. (Aefeso 5:33, Kingdom Interlinear; 1 Akorinto 11:3) Kugonjera nkofunikanso kwambiri kuti banja lanu likhale ndi chipambano; kumakuthandizani kupeŵa kuchititsa zitsenderezo ndi mavuto osafunikira pabanja lanu.

14. Kodi mkazi angachitenji pamene sakuvomereza chosankha cha mwamuna wake?

14 Komabe, kodi zimenezi zimatanthauza kuti muyenera kukhala chete pamene muwona kuti mwamuna wanu akupanga chosankha chimene chikuwombana ndi zabwino za banja lanu? Osati kwenikweni. Sara mkazi wa Abrahamu, sanakhale chete pamene anazindikira chiwopsezo pakakhalidwe kabwino ka mwana wake, Isake. (Genesis 21:8-10) Mofananamo, mungawone kuti muyenera kupereka malingaliro anu nthaŵi zina. Ngati muchita zimenezi mwanjira yaulemu “panthaŵi yake,” mwamuna Wachikristu wowopa Mulungu adzamvetsera. (Miyambo 25:11) Koma ngati lingaliro lanu silikutsatiridwa ndipo palibe kulakwira lamulo la makhalidwe abwino a Baibulo kumene kukuloŵetsedwamo, kodi kuchita mosiyana ndi zikhumbo za mwamuna wanu sikukakhala kudzigonjetsa nokha? Kumbukirani kuti, “mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake.” (Miyambo 14:1) Njira ina yomangira banja lanu ndiyo kukhala wochirikiza umutu wa mwamuna wanu, kuyamikira zochita zake kwinaku mukumachita ndi zolakwa zake mosamala.

15. Kodi ndi m’njira zotani zimene mkazi angakhalire ndi phande m’kulanga ndi kuphunzitsa ana ake?

15 Njira inanso yomangira banja lanu ndiyo kukhala ndi phande m’kulanga ndi kuphunzitsa ana anu. Mwachitsanzo, mukhoza kuchita mbali yanu mwakupangitsa phunziro Labaibulo kukhala lokhazikika ndi lolimbikitsa. ‘Musapumitse dzanja lanu’ m’kugaŵana chowonadi cha Mulungu ndi ana anu pampata uliwonse​—pamene muli paulendo kapena chabe pokagula nawo zinthu. (Mlaliki 11:6) Athandizeni kukonzekera ndemanga zawo zokapereka pamsonkhano ndi nkhani pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Khalani maso ponena za mabwenzi awo. (1 Akorinto 15:33) Ponena za nkhani za miyezo ya Mulungu ndi chilango, chititsani ana anu kudziŵa kuti inuyo ndi mwamuna wanu ndinu wogwirizana. Musawalole kukuwombanitsani mitu ndi mwamuna wanu.

16. (a) Kodi ndizitsanzo za Baibulo ziti zimene zimalimbikitsa makolo amene ndimbeta ndi awo okwatirana ndi osakhulupirira? (b) Kodi ena mumpingo angathandize motani oterowo?

16 Ngati ndinu kholo lopanda mwamuna kapena muli ndi mwamuna wosakhulupirira, muyenerabe kutsogolera m’zinthu zauzimu. Izi zingakhale zovuta ndipo nthaŵi zina ngakhale zolefula. Koma musaleke kuyesayesa. Amake Timoteo, Yunike, anakhala achipambano m’kumphunzitsa iye Malemba oyera “kuyambira ukhanda,” mosasamala kanthu kuti anakwatiŵa kwa wosakhulupirira. (2 Timoteo 1:5; 3:15) Ndipo ambiri pakati pathu akukhala ndi chipambano chofananacho. Ngati mukufunikira chithandizo m’nkhani imeneyi, mukhoza kudziŵitsa akulu zosoŵa zanu. Iwo angalinganize munthu wokuthandizani kupita kumisonkhano ndi kutuluka muutumiki wakumunda. Angalimbikitse ena kuphatikiza banja lanu popita kokacheza kapena pakukumana kwa mayanjano. Kapena akhoza kulinganiza wofalitsa wachidziŵitso kukuthandizani kuyambitsa phunziro labanja.

Ana Oyamikira

17. (a) Kodi ndimotani mmene achichepere angawonjezerere khalidwe labwino la banja? (b) Kodi nchitsanzo chotani chimene Yesu anapereka pankhaniyi?

17 Achichepere Achikristu akhoza kuwonjezera pamkhalidwe wabwino mwakutsatira uphungu wa Aefeso 6:1-3 wakuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” Mwakugwirizana ndi makolo anu, mumasonyeza ulemu wanu kwa Yehova. Yesu Kristu anali wangwiro ndipo akanalingalira mosavuta kuti kukakhala komnyazitsa kugonjera kwa makolo opanda ungwiro. Komabe, iye ‘anawamvera iwo. . . . Ndipo Yesu anakulabe m’mzeru ndi mumsinkhu, ndi chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.”​—Luka 2:51, 52.

18, 19. (a) Kodi kulemekeza makolo a munthuwe kumatanthauzanji? (b) Kodi ndimotani mmene panyumba pangakhalire malo ampumulo?

18 Kodi nanunso simuyenera kulemekeza makolo anu mofananamo? ‘Kulemekeza’ panopa kumatanthauza kuvomereza ulamuliro woperekedwa moyenerera. (Yerekezerani ndi 1 Petro 2:17.) M’mikhalidwe yambiri ulemu woterowo umakhala woyenera ngakhale ngati makolo a munthu ali osakhulupirira kapena akulephera kupereka chitsanzo chabwino. Muyenera kulemekeza makolo anu koposerapo ngati ali Akristu achitsanzo chabwino. Kumbukiraninso, kuti chilango ndi malangizo operekedwa ndi makolo anu siziri ndi cholinga chakukuletsani mosayenerera. Mmalomwake, amakutetezerani kuti ‘mukhalebe ndi moyo.’​—Miyambo 7:1, 2.

19 Pamenepotu, banja liri makonzedwe abwino chotani nanga! Pamene amuna, akazi, ndi ana onse atsatira malamulo a Mulungu a moyo wa banja, nyumba imakhala malo achisungiko, malo osangulutsa. Komabe, pangabuke mavuto ponena za kulankhulana ndi kuphunzitsa ana. Nkhani yathu yotsatira idzasonyeza mmene ena a mavuto ameneŵa angathetsedwere.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi amuna, akazi, ndi ana owopa Mulungu a m’nthaŵi za m’Baibulo anapereka chitsanzo chotani?

◻ Kodi nchidziŵitso chotani chimene Chikristu chinapereka pambali ya mwamuna?

◻ Kodi mkazi ayenera kuchita mbali yanji m’banja Lachikristu?

◻ Kodi achichepere Achikristu angawonjezere motani khalidwe labwino la banja?

[Chithunzi patsamba 9]

“Palibe m’Chikristu chimene chinawonekera kukhala chachilendo ndi chotsendereza, poyerekezera ndi makhalidwe olekerera apanthaŵiyo, kuposa lingaliro Lachikristu la ukwati. . . . [Ilo] linayambitsa nyengo yatsopano kwa mtundu wa anthu”

[Chithunzi patsamba 10]

Amuna Achikristu amalimbikitsa akazi awo kupereka malingaliro awo, ndi kusamalira malingalirowo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena