Malo a Dziko Lolonjezedwa
Kupita ku Silo—Ana Abwino ndi Oipa
PAMENE mulingalira za mizinda, matauni, kapena madera a Dziko Lolonjezedwa, kodi amuna ndi akazi ena otchuka amadza m’malingaliro mwanu? Mwinamwake amatero, pakuti nkhani Zabaibulo zochulukitsitsa zimaphatikizapo achikulire. Koma bwanji za ana kalelo? Kodi mumaŵalingalira ali m’malowo?
Chithunzithunzi chapamwambachi chingatithandize kulingalira nkhani zophatikizapo achichepere, ena anali zitsanzo zabwino kwa Akristu ndipo ena awo anali zitsanzo zochenjeza. Phiri lobulungila chapakatipo mwachiwonekere ndilo malo a Silo.a
Mwachiwonekere mukukumbukira kuti pamene Israyeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, anayamba kuimitsa chihema cha Mulungu ku Giligala pafupi ndi Yeriko. (Yoswa 4:19) Koma pamene dzikolo linali kugaŵanidwa, chihema chopatulika chimenechi—phata la kulambira kwa Israyeli—chinasamutsidwa kunoku kumka ku Silo. (Yoswa 18:1) Kumeneku kunali makilomitala pafupifupi 30 kumpoto kwa Yerusalemu m’chigawo chamapiri cha Efraimu. Amuna ndi akazi a m’Israyeli yense anapanga ulendo womka ku Silo; makamu aakulu a anthu ankasonkhana m’chigwa kummwera kwa malo amene mwachiwonekere chihemacho chinali. (Yoswa 22:12) Kodi mungayerekezere ana akumabwera kuno?
Ena anatero. Chitsanzo chotchuka koposa chimene tiyenera kudziŵa chinali cha mwanayo Samueli. Makolo akewo, Elikana ndi Hana, ankakhala m’tauni ya kutseli kwa mapiri cha kumadzulo. Chaka chirichonse iwo anapanga ulendo wodza kuno, mwinamwake akumabwera ndi ana ena mwa mkazi wina wa Elikana. Potsirizira Yehova anadalitsa Hana ndi mwana wamwamuna, amene anapatsidwa dzina lakuti Samueli. M’kupita kwanthaŵi, makolo ake anadza naye kudzakhala ku Silo kotero kuti akatumikire pachihema limodzi ndi mkulu wa ansembe Eli.—1 Samueli 1:1–2:11.
Mnyamatayo anali ndi ntchito za kuzichita panyumba ya Mulungu, ndipo ayenera kukhala anali ndi mipata yambiri ya kukwera m’mapiri apafupipo. (1 Samueli 3:1, 15) Ena a iwo anali ndi minda ndi odzala ndi mitengo ya azitona, monga momwe akuwonekerera pachithunzithunzi cha patsamba 9. Tawonani nsanja ya olonda yaing’ono yamiyala. Alimi akutali kapena abusa akatha kulinda ali pansanja ya olonda yoteroyo, koma mungayerekezere Samueli wachichepere akumakwerapo kuti nayenso awone. (Yerekezerani ndi 2 Mbiri 20:24.) Ameneŵa ankakhala malo okwezeka abwino kwambiri owonerapo zirombo.
Kalelo, kunali mitengo yambiri koposa tsopano, ngakhale nkhalango kumene zirombo zinkayendayenda. (Yoswa 17:15, 18) Tidziŵa zimenezi chifukwa cha chochitika chimene chinachitika pamene Elisa anakhala mneneri wamkulu wa Mulungu. Elisa anali paulendo wochokera ku Yeriko kumka ku Beteli, chotero anali m’dera limeneli, makilomita 16 cha kummwera kwa Silo. Kodi iye akalandiridwa motani ndi anthu a ku Beteli, amene anafikira kukhala phata la kulambira mwana wang’ombe wagolidi? (1 Mafumu 12:27-33; 2 Mafumu 10:29) Mwachiwonekere achikulire anali otsutsa mneneri wa Yehova, ndipo mkhalidwe wawo wamaganizo ukuwonekera kukhala unayambukira mbadwa zawo.
Mafumu Wachiŵiri 2:23, 24 akutiuza kuti kagulu ka achichepere kanaseka mneneri wa Mulungu: “Takwera wadazi, takwera wadazi!” Moyankha, Elisa “anaŵatemberera m’dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anayi mphambu aŵiri.” Zimbalangondo zodera za ku Suriya zoterozo zikakhala zolusa kwambiri pamene zadzidzimutsidwa kapena pamene misona yawo inawonekera kukhala itawopsezedwa. (2 Samueli 17:8; Miyambo 17:12; 28:15) Mulungu anazigwiritsira ntchito kupereka chiŵeruzo chaumulungu motsutsana ndi awo amene analuluza kwambiri woimira wake ndipo mwakutero kululuza Yehova mwiniyo.
Kuti mwana akatha kukumana ndi zirombo m’mapiri ozungulira Silo kuyenera kutithandiza kuzindikira mowonjezereka chikhulupiriro chimene makolo a Samueli anasonyeza pombweretsa kudzatumikira pachihema.
Wolambira wina wowona poyamba anali atasonyeza chikhulupiriro ndi kudzipereka zofananazo—Woweruza Yefita. Iye anali kukhala m’dera lamapiri la Gileadi cha kummaŵa kwa Yordano. Pochitira changu Yehova motsutsana ndi Aamoni adaniwo, Yefita analumbira kuti choyamba kutuluka m’nyumba yake kukakumana naye chikaperekedwa nsembe kwa Yehova. Mwana wake wamkazi namwaliyo anatsimikizira kukhala chinthu chimenecho. Chotero iye anabweretsa mwana wake mmodzi yekhayo kukachisi wa Mulungu ku Silo, kumene anakhala ndi kutumikira mokhulupirika kwazaka zambiri.—Oweruza 11:30-40.
Kudzipereka kokhulupirika kumene Samueli ndi mwana wamkazi wa Yefita anasonyeza m’dera la Silo ndithudi nkosiyana kwambiri ndi chitsanzo choipa cha ana opulupudza 42 amene anatonza mneneri wa Yehova m’dera limodzimodzili.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:6, 11.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani chithunzithunzi chachikulu pa Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1992.
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Safari Zoo, Ramat-Gan, Tel Aviv