Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 5-7
  • Kodi Uthenga Wabwino Ungakupindulitseni Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Uthenga Wabwino Ungakupindulitseni Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Othandizidwa ndi Uthenga Wabwino
  • Kodi Mbiri Yabwino Imatanthauzanji Lerolino?
  • Mphamvu ya Uthenga Wabwino Lerolino
  • Madalitso Alinkudza
  • Kufalitsa “Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Kwenikweni Uthenga Wabwino Nchiyani?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • “Uthenga Wabwino”
    Imbirani Yehova Mosangalala
  • Pali Uthenga Wabwino Wofunika Kuti Anthu Onse Amve
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 5-7

Kodi Uthenga Wabwino Ungakupindulitseni Motani?

BAIBULO limalemekezedwa kwambiri kaamba ka phindu lake laukatswiri​—ngakhale ndi ena osakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu. Komabe, kwenikweni, ngochepekera amene amaliŵerenga kuti agwiritsire ntchito zimene limanena. Ndiponso, popeza kuti mbiri yake yabwino imabwerera m’mbuyo pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, anthu ambiri akuwonekera kukhala okhulupirira kuti liyenera kukonzedwa kukhala latsopano, kuti likhale lamakono. Kodi Uthenga Wabwino ngwachikale kapena wotha ntchito? Kutalitali!

Pali amuna ndi akazi, achichepere ndi okalamba, okwanira mamiliyoni, amene amadziŵa kuti Baibulo liri magwero opindulitsa achithandizo. Liri monga momwe mawu oyamba a Today’s English Version amanenera kuti: “Baibulo siliri kokha bukhu laukatswiri loti liyamikiridwe ndi kulemekezedwa; liri Mbiri Yabwino ya anthu onse kulikonse​—uthenga wofunikira ponse paŵiri kumvedwa ndi kugwiritsidwa ntchito mu moyo watsiku ndi tsiku.”

Kodi Uthenga Wabwino umatanthauzanji kwa inu? Kodi mumaugwiritsira ntchito monga chitsogozo m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku? Talingalirani mmene mbiri yabwino inapindulitsira ena amene anaimvetsera m’zaka za zana loyamba ndi mmene ena apindulira m’nthaŵi yathu.

Anthu Othandizidwa ndi Uthenga Wabwino

M’tsiku la Yesu anthu ena monga asodzi okangalika ndi akazi apanyumba anakopeka ndi mbiri yabwino ndipo anaphunzira chowonadi chonena za chifuno cha Mulungu kwa anthu. Mbiri yabwino inasintha kwakukulukulu miyoyo yawo ndipo kaŵirikaŵiri inawabweretsera mpumulo waukulu. Mwachitsanzo, Mariya Magadalene anatulutsidwa chiŵanda. Zakeyu, amene poyamba anali mkulu wa osonkhetsa msonkho, anasiya njira yake yamoyo yaumbombo. (Luka 8:2; 19:1-10) Akhungu ndi akhate anathandizidwa pamene anadza kwa Yesu, amene anali kulalikira mbiri yabwino. (Luka 17:11-19; Yohane 9:1-7) Yesu akakhoza kunena molondola kuti: “Akhungu alandira kuwona kwawo, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino.”​—Mateyu 11:5.

Komabe, chofunika kwambiri kuposa kuchiritsidwa kwawo, chinali njira imene mbiri yabwino inasinthira umunthu wa anthu okanthidwa amenewo. Owona mtimawo anadzazidwa ndi chiyembekezo chamtsogolo. Iwo anaika chidaliro chawo mu Ufumu wa Mulungu​—kanthu kena kabwinopo kuposa uthenga wabwino wa makhalidwe a anthu. (Mateyu 4:23) Chiyembekezo chawo sichinagwiritsidwe mwala mwa imfa ya Yesu. Pofotokoza mikhalidweyo ngakhale pambuyo pachochitika chimenecho, Machitidwe 5:42 amati ponena za ophunzira ake: “Masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.” M’zaka za zana loyamba, anthu m’maiko ambiri analandira chithandizo chauzimu chifukwa chakuti analabadira kulalikira kotero.

Ufumu unali mbiri yabwino koposa kalelo. Kodi uthenga wa Ufumuwo ukali chikhalirebe mbiri yabwino?

Kodi Mbiri Yabwino Imatanthauzanji Lerolino?

Ngati mukulakalaka dziko lamtendere, losungika, pamenepo mbiri ya Ufumuwo iridi yabwino. M’chenicheni, m’dziko limene anthu mamiliyoni mazana ambiri odya mosakwanira ndi anjala, kumene nthenda zochititsa mantha zikuwopseza munthu aliyense, kumene upandu ukuwonjezereka mochititsa mantha, ndi kufalikira kwa kusakhazikika kwa ndale zadziko, iyo ndiyo mbiri yabwino yeniyeni yokha ndi yokhalitsa. Imaimira chiyembekezo chokha cha kuwongokera kwenikweni.

Ndicho chifukwa chake Yesu adaneneratu mawu awa ponena za tsiku lathu: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kuti ikhale umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Mawu amenewa akukwaniritsidwa mwapadera pamene Mboni za Yehova zikulalikira mbiri yabwino m’maiko oposa 200. Bukhu lina la Akatolika, Nova Evangelização 2000, likuyamikira Mboni pa mfundoyi, likumati: “Kodi nkuti kumene timapeza Mboni za Yehova? Pamakomo penipeni panyumba. Ndipo kukhala Mboni ya Yehova, kuwonjezera pakukhala munthu wa Yehova, munthuyo ayenera kukhala mboni. Chifukwa chake, timawapeza akugwira ntchito, akulengeza, akulalikira, zimene akumana nazo.”

Komabe, palibe munthu amene amangopindula ndi mbiri yabwino mosachitapo kanthu. Idzathandiza awo okha amene amamvetsera ndi kulabadira. Kuti amveketse mfundoyi, Yesu anapereka fanizo la munthu womka kukafesa mbewu. Nthaka yosiyanasiyana pa imene mbewuzo zinagwera inaphiphiritsira mitundu yosiyanasiyana ya mkhalidwe wa mtima umene omvetsera mbiri yabwino amasonyeza. Yesu anati: “Aliyense wakumva mawu a Ufumu, osawadziŵitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. . . . Iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mawu nawadziŵitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.”​—Mateyu 13:18-23.

Monga momwe kunaliri m’zaka za zana loyamba, anthu ambiri lerolino amapanga kuyesayesa kochepa kuti azindikire mbiri yabwino. Samapeza tanthauzo lake, ndipo chotero samapindula. Ena amayamikira mbiri yabwino naphunzira mmene angagwirizanitsire miyoyo yawo ndi chifuniro cha Mulungu. Mwanjirayi amadalitsidwa. Kodi inu ndinu wakagulu kati?

Mphamvu ya Uthenga Wabwino Lerolino

Zochitika zimachitira umboni kuti kuzindikira mbiri yabwino kumathandiza awo amene ‘analibe chiyembekezo ndipo anali opanda Mulungu.’ (Aefeso 2:12; 4:22-24) Roberto wa ku Rio de Janeiro anafunikira thandizo. Kuyambira paubwana wake, ankakhala ndi moyo mwanjira yoluluzika, akumaphatikizidwa m’kugwiritsira ntchito anamgoneka, chisembwere, ndi umbala. Potsirizira pake anaikidwa m’ndende. Ali m’menemo Roberto anaphunzira Baibulo ndi Mboni imene inkadzachezako. Iye anapita patsogolo mwauzimu bwino kwambiri kotero kuti nthaŵi yake yokhala m’ndende inachepetsedwa kwambiri.

Atamasulidwa m’ndende, Roberto anakumana ndi msungwana wina wachichepere amene kalelo adammenya ndi kumuwopseza ndi mfuti. Msungwanayonso anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kodi chinachitika nchiyani? Yotsatirayi iri mbali ya kalata yosimba chochitikachi: “Iwo anakumana pa Nyumba Yaufumu kwa nthaŵi yoyamba pambuyo pa chiukiro chija. Kukumanako kunali kosonkhezera mtima. Aŵiri onsewo analakatitsa misozi chifukwa chakumva chifundo nakupatilana monga mbale ndi mlongo. Tsopano onse aŵiri amene kale anali mbala ndi amene anali mkhole wakeyo akutamanda Yehova.”

Munthu wina, Isabel, nayenso anafunikira chithandizo, popeza kuti anali wodziŵika chifukwa cha kukhala wamtima wapachala. Iye anaphatikizidwa kwambiri m’kukhulupirira mizimu ndi ufiti ndipo anazunzidwa ndi ziŵanda. Pamene mkaziyo anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anapeza kuti mbiri yabwino inathandizadi. Pambuyo pa nthaŵi yakutiyakuti, anawonjoka ku mphamvu ya ziŵanda nasintha umunthu wake​—potsirizira pake anaphunzira kulamulira mkwiyo wake. Tsopano iye ali Mkristu wokhulupirika, wodziŵika monga munthu wokoma mtima pochita ndi ena.

Inde, mbiri yabwino siiri mawu chabe. Iridi ndi mphamvu yakusanduliza miyoyo. (1 Akorinto 6:9-11) Mbiri yabwino imachita zoposa zimenezo. Imasonyanso kumadalitso a mtsogolo.

Madalitso Alinkudza

Mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, mtsogolomu muli ziyembekezo zabwino kwambiri. Tidzawona kukwaniritsidwa kwa pemphero la Yesu lakuti Ufumu wa Mulungu udze ndi chifuniro Chake kuchitika padziko lapansi monga kumwamba. (Mateyu 6:10) Mwamsanga, dongosolo liripoli la zinthu limodzi ndi chisalungamo chake chotsendereza ndi chiwawa zidzachotsedwa, ndipo boma lakumwamba la Mulungu, Ufumu wake, lidzalamulira anthu owongoka mtima amene anali ofunitsitsa kumvetsera ndi kulabadira mbiri yabwino.​—Danieli 2:44.

Masinthidwe aakulu adzatsatira pamene anthu okhulupirika akulangizidwa kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso kumene ofatsa adzakhala ndi moyo kosatha. (Salmo 37:11, 29) Ndithudi, iri mbiri yabwino kumva kuti upandu, nthenda, njala, kuipitsidwa kwa mpweya, ndi nkhondo zidzachoka kosatha! Kodi mungathe kudziwona inu mwini ndi banja lanu mukumakhala m’dziko latsopano limenelo mumtendere ndi thanzi langwiro mosawopa nthenda kapena imfa?​—Chivumbulutso 21:4.

Ndithudi, ambiri amalingalira mbiri yabwino yotero kukhala zamkhutu kapena kungoyerekezera. Komatu iwo akulakwa. Mbiri yabwino njozikidwa pa umboni wolimba koposa, ndipo yasintha kale miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri. Chifukwa chake, musawopsezedwe ngati ena sakhulupirira.

Yerekezerani munthu wanzeru amene amagula munda m’chigawo chimene chikutukuka, akumayembekezera kupeza phindu m’kuikizira kwake. Kodi pali munthu amene angamneneze chifukwa chakuikizira ndalama zake mwanjirayi? Ayi. Mwachiwonekere kwambiri, anthu akanena kuti iye akuchita mwanzeru. Pamenepa, kodi mulekeranji, kukhala wowona patali pankhani ya Ufumuwo ndi kuikizira mu mbiri yabwino, kunena kwake titero? Popeza kuti kuvomereza mbiri yabwino kumatanthauza chipulumutso, palibe kuikizira kwina kumene kudzadzetsa phindu labwino kwambiri kuposa limeneli.​—Aroma 1:16.

Kodi inu mungaikizire motani m’mbiri yabwino? Choyamba, khalani wofunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Mulungu. Pamenepo chitani mogwirizana ndi zimene mukuphunzira. Tsatirani zofunika zazikulu, monga momwe zandandalikidwira ndi mneneri wakale Wachihebri izi: ‘Kodi Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?’ (Mika 6:8) Kuphunzira kuyenda ndi Mulungu kumatenga nthaŵi ndi kuyesayesa. Komabe, Mboni za Yehova, zimene zinathandiza Roberto ndi Isabel, zidzakondwera kukuthandizani pamfundoyi​—monga momwe zathandizira ena mamiliyoni m’kupita kwa zaka.

Pamene mukuyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu, chirikizani chuma chanu choikiziridwacho mwakukhala ndi moyo mogwirizana ndi mbiri yabwino, mukumasangalala ndi mtendere wa maganizo ndi kupanga unansi wapafupi kwambiri ndi Mulungu. Chuma chanu choikiziridwacho chidzakhala chotetezereka​—palibe kuchepa mphamvu kwachuma kapena chipwirikiti cha ndale zadziko chidzachiwopseza. Ndipo potsirizira pake, chidzakubweretserani phindu lalikulu. Kodi phindulo nchiyani? Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.”​—1 Yohane 2:17.

[Chithunzi patsamba 7]

Mbewu za mbiri yabwino zimagwera panthaka zosiyanasiyana

[Mawu a Chithunzi]

Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena