Kodi Nchifukwa Ninji Kunama Kuli Kosavuta Choncho?
PALIBE munthu amene amafuna kunamizidwa. Komabe, anthu pa dziko lonse lapansi amanamizana pa zifukwa zosiyanasiyana. Kapendedwe kamene kanali m’bukhu la The Day America Told the Truth, lolembedwa ndi James Patterson ndi Peter Kim, kanavumbula kuti 91 peresenti ya nzika za Amereka amanama nthaŵi zonse. Olembawo akuti: “Unyinji wa ife timakupeza kukhala kovuta kutha mlungu popanda kunama. Mmodzi mwa asanu sangathe kutha tsiku limodzi—ndipo tikutanthauza kunama dala, kolinganizidwiratu.”
Kunama kuli chizoloŵezi chofala pafupifupi m’mbali zonse za moyo wamakono. Atsogoleri andale zadziko amanamiza anthu awo ndi kunamizana iwo eni. Mobwerezabwereza, iwo awonekera pa wailesi yakanema kulandula mgwirizano uliwonse ndi ziwembu zochititsa manyazi m’zimene iwo kwenikweni anali ophatikizidwa kwambiri. Sissela Bok, m’bukhu lake lakuti Lying—Moral Choice in Public and Private Life, amati: “M’lamulo ndi m’kutola nkhani, m’boma ndi m’sayansi ya anthu, chinyengo chimawonedwa kukhala chovomerezedwa pamene chilingaliridwa kukhala kudzikhululukira kochitidwa ndi awo amene akunama ndi amene akulinganizanso kupanga malamulo.”
Ponena za kunama kwa andale zadziko mu United States, Common Cause Magazine a May/June 1989 anati: “Ndithudi zamanyazi pa Watergate ndi nkhondo ya ku Vietnam zinali zofanana ndi mlandu wa Iran m’nkhani yokhudza chinyengo chaboma ndi kutaya chidaliro kwa anthu. Chotero kodi nchiyani chimene chinapangitsa zaka za upulezidenti wa a Reagan kukhala zopanga mbiri? Ambiri ananama, koma ochepekera anali kumva chisoni.” Chifukwa chake, pali chifukwa chabwino kuti anthu wamba samaika chidaliro mwa atsogoleri awo andale zadziko.
M’maunansi amaiko atsogoleri otero amakupeza kukhala kovuta kudalirana. Wanthanthi Wachigiriki Plato anati: “Olamulira Boma . . . angaloledwe kunama chifukwa cha ubwino wa Bomalo.” M’maunansi amaiko kuli monga momwe ulosi wa Baibulo pa Danieli 11:27 umanenera kuti: ‘Adzanena bodza ali pagome limodzi.’
M’bizinesi, kunama ponena za zinthu zogulitsidwa ndi mautumiki ndiko mchitidwe wozoloŵereka. Ogula afunikira kuloŵa m’mapangano amalonda mochenjera, akumatsimikizira kuŵerenga mfundo zapanganolo zosindikizidwa m’mawu aang’onong’ono. Maiko ena ali ndi magulu alamulo m’boma otetezera anthu kukusatsa malonda konama, ku zamalonda zovulaza zimene zimanenedwa kukhala zopindulitsa kapena zosavulaza, ndi kukunamizidwa. Mosasamala kanthu za zoyesayesa zimenezi, anthu akupitirizabe kuvutika m’zandalama chifukwa cha mabodza a ochita malonda.
Kwa anthu ena, kunama kuli kosavuta kwambiri kotero kuti kumakhala chizoloŵezi. Ena mwachibadwa amanena zowona, koma pamene apanikizika amanama. Ochepekera amakana kunama ziipe zitani.
Bodza lafotokozedwa kukhala “1. mawu kapena chochita chonama, makamaka chochitidwa ncholinga cha kunyenga . . . 2. kalikonse kamene kamapereka kapena kuchitidwira kupereka lingaliro lonyenga.” Cholinga ndicho kuchititsa ena kukhulupirira chinthu china chimene wonamayo akudziŵa kuti sichiri chowona. Mwa mabodza kapena chowonadi chosanganikirana ndi mabodza, iye amayesayesa kunyenga awo amene ali ndi kuyenera kwa kudziŵa chowonadi.
Zifukwa Zonamira
Anthu amanama pa zifukwa zambiri. Ena amaganiza kuti ngokakamizika kunama ponena za maluso awo kuti apeze chipambano m’dziko lampikisano lino. Ena amayesa kuphimba zophophonya kapena liwongo ndi mabodza. Pamene enanso amapereka malipoti onama kuti apereke lingaliro lakuti achita ntchito imene sanachite. Ndiyeno pali awo amene amanama kuti awononge mbiri ya mnzawo, kupeŵa manyazi, kulungamitsa mabodza akale, kapena kunamiza anthu, kuti awalande ndalama zawo.
Chodzikhululukira chodziŵika chonamira nchakuti kumatetezera munthu winayo. Ena amalingalira limeneli kukhala bodza labwino chifukwa chakuti iwo aganiza kuti silimavulaza aliyense. Koma kodi otchedwa kuti mabodza abwino amenewa kwenikweni samasiya ziyambukiro zoipa?
Talingalirani Ziyambukirozo
Mabodza abwino angayambitse njira yotsogolera ku chizoloŵezi chakunama kumene kungaphatikizepo nkhani zowopsa. Sissela Bok akuti: “Mabodza onse otetezeredwa kukhala ‘abwino’ sangathetsedwe mwamsanga chotero. Choyamba, kusavulaza kwa mabodza kuli kutsutsidwa kotheratu. Zimene wonama akulingalira kukhala zosavulaza kapena ngakhale zopindulitsa sizingawonedwe motero kwa wonamizidwayo.”
Mabodza, mosasamala kanthu za mmene angawonekerere kukhala osavulaza, ngowononga maunansi abwino aumunthu. Kukhulupirika kwa wonamayo kumataika, ndipo mwinamwake pangakhale kusweka kwachikhalire kwachidaliro. Wolemba nkhani wotchuka Ralph Waldo Emerson analemba kuti: “Kuswedwa kulikonse kwa chowonadi sikuli kokha mbali ya kudzipha kwa wonamayo, koma ndiko kubaya thanzi lachitaganya cha anthu.”
Kuli kosavuta kwa wonama kulankhula mawu onama ponena za munthu wina. Ngakhale kuti sapereka umboni, bodza lake limapangitsa chikaikiro, ndipo ambiri amamkhulupirira popanda kufufuza zonena zakezo. Chotero mbiri ya munthu wasalakwa imavulazidwa, ndipo akunyamula mtolo wakukatsimikizira kuti ngwopanda liwongo. Chifukwa chake, kumagwiritsa mwala pamene anthu akhulupirira bodza mmalo mwakukhulupirira munthu wosalakwa, ndipo kumawononga unansi wa wosalakwayo ndi wabodzayo.
Wabodza angakulitse mosavuta chizoloŵezi chakunama. Kaŵirikaŵiri bodza limodzi limatsogolera kulinzake. Thomas Jefferson, katswiri m’nkhani za boma wa ku Amereka, anati: “Palibe mphulupulu yachabechabe kwambiri motero, yomvetsa chisoni kwambiri, yonyozera kwambiri; ndipo munthu amene adzilola kunena bodza kamodzi, amakupeza kukhala kosavutirapo kutero nthaŵi yachiŵiri ndi yachitatu, kufikira m’kupita kwanthaŵi kumakhala chizoloŵezi.” Iri njira yomka kukunyonyosoka kwa makhalidwe.
Chifukwa Chake Kuli Kosavuta Kunama
Kunama kunayamba pamene mngelo wopanduka ananama kwa mkazi woyamba, akumamuuza kuti iye sakafa ngati sakamvera Mlengi wake. Chotulukapo chinali chivulazo chosayerekezeka kufuko lonse laumunthu, kukumabweretsa kupanda ungwiro, matenda, ndi imfa kwa onse.—Genesis 3:1-4; Aroma 5:12.
Kuyambira panthaŵi ya Adamu ndi Hava osamverawo, chisonkhezero chonyenga cha atate wa mabodza ameneyu chapangitsa mkhalidwe m’dziko lamtundu wa anthu umene umasonkhezera bodza. (Yohane 8:44) Liri dziko lovunda mulimene chowonadi chiri chochepetsetsa chabe. The Saturday Evening Post ya September 1986 inanena kuti vuto lakunama “limayambukira bizinesi, boma, maphunziro, zosangulutsa, ndi maunansi wamba a tsiku ndi tsiku pakati pa nzika ndi anansi. . . . Tavomereza lingaliro lakuti zinthu ziri ndi malire, bodza limodzi lalikulu limene limanena kuti palibe chowonadi chotheratu.”
Limeneli liri lingaliro la abodza achizoloŵezi, amene alibe chifundo chirichonse pa awo amene akunyenga. Kunama kumakhala kosavuta kwa iwo. Iri njira yawo yamoyo. Koma ena amene alibe chizoloŵezi chakunama anganame mosadodoma chifukwa cha mantha—kuwopa kuululidwa, kuwopa chilango, ndi zina zotere. Chiri chifooko chathupi lopanda ungwiro. Kodi chikhoterero chimenechi chingalowedwe mmalo bwanji ndi chitsimikizo chakulankhula chowonadi?
Chifukwa Ninji Kulankhula Chowonadi?
Chowonadi ndicho muyezo umene Mlengi wathu wamkulu watiikira ife tonse. Mawu ake olembedwa, Baibulo, amafotokoza pa Ahebri 6:18 kuti: “Mulungu sakhoza kunama.” Muyezo umodzimodziwo unachirikizidwa ndi Mwana wake, Yesu Kristu, amene anali woimira weniweni wa Mulungu padziko lapansi. Kwa atsogoleri achipembedzo Achiyuda amene anali kufuna kumupha, Yesu anati: “Tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu chowonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; . . . ngati ndinena kuti sindimdziwa iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu.” (Yohane 8:40, 55) Iye anatiikira chitsanzo m’chakuti “sanachita tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo.”—1 Petro 2:21, 22.
Mlengi wathu, amene dzina lake liri Yehova, amada mabodza, monga momwe Miyambo 6:16-19 amanenera momvekera bwino kuti: “Ziripo zinthu zisanu ndi chimodzi Mulungu azida; ngakhale zisanu ndi ziŵiri zimnyansa: maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu; mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.”
Mulungu wa chowonadi ameneyu amafuna kuti ife tikhale ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yake kuti tilandire chivomerezo chake. Mawu ake ouziridwa amatilamula kuti: “Musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.” (Akolose 3:9) Anthu amene amakana kusiya chizoloŵezi chakunama saali ovomerezeka kwa iye; iwo sadzalandira mphatso yake ya moyo. M’chenicheni, Salmo 5:6 limanena mosabisa mawu kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akunena bodza.’ Chivumbulutso 21:8 chimanenanso kuti gawo la “onse amabodza ndilo imfa yachiŵiri,” chimene chiri chiwonongeko chosatha. Chotero kuvomereza kwathu lingaliro la Mulungu lonena za bodza kumatipatsa chifukwa champhamvu cha kulankhulira chowonadi.
Koma kodi mungachitenji pamene mkhalidwe wakulankhula chowonadi ungapangitse mkhalidwe wochititsa manyazi kapena kumva moipa? Kunama sindiko njira yothetsera konse, koma nthaŵi zina kusanena kanthu ndiko. Kodi nkuneneranji mabodza amene adzawononga mbiri yanu ndi kukupangitsani kukhala wopanda chiyanjo cha Mulungu?
Chifukwa cha mantha ndi kufooka kwaumunthu, munthu angakumane ndi chiyeso chakufunafuna pobisala m’bodza. Imeneyi iri njira yosavuta kulondola kapena chifundo cholakwika. Mtumwi Petro anagonjera kuchiyeso choterocho pamene nthaŵi zitatu anakana kuti anadziŵa Yesu Kristu. Pambuyo pake, iye analaswa mtima chifukwa cha kukhala atanama. (Luka 22:54-62) Kulapa kwake kowona mtima kunasonkhezera Mulungu kumkhululukira, monga momwe kukuchitiridwa umboni pambuyo pake ndi kudalitsidwa kwake ndi mwaŵi wambiri wautumiki. Kulapa limodzi ndi chosankha chotsimikiza chakuleka kunama ndiyo njira imene ingabweretse chikhululukiro cha Mulungu chakuchita chimene iye amada.
Koma mmalo mwakufunafuna chikhululukiro pambuyo pakunama, sungani unansi wabwino ndi Mlengi wanu ndipo sungani kukhulupirika kwanu ndi ena mwakulankhula chowonadi. Kumbukirani zimene Salmo 15:1, 2 limanena kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zowonadi mumtima mwake.”