Kodi Mudzakwatulidwira Kumwamba?
ANTHU ochuluka amakhulupirira kuti adzapita kumwamba pamene amwalira. Koma ena amaganiza kuti adzakwatulidwira kumwamba m’chimene chimatchedwa kutengedwa m’thupi. Kodi chimenecho ndicho chiyembekezo chanu?
Kutengedwa m’thupi ndiko “kuzimiririka mwadzidzidzi kwa anthu mamiliyoni ambirimbiri popanda kudziŵika kumene iwo adapita!” Anatero mlaliki wina Wachiprotestante. Mogwirizana ndi kunena kwa Evangelical Dictionary of Theology, liwulo “kutengedwa m’thupi” limasonya ku “tchalitchi kukhala chikugwirizanitsidwa ndi Kristu pa kudza kwake kwachiŵiri.”
Ena amakupeza kukhala kovutitsa maganizo kulingalira zakusiya mabwenzi ndi ziŵalo za banja kukatsagana ndi Yesu Kristu. Komabe, ambiri amakhulupirira kuti kutengedwa m’thupi kuyenera kuchitika. Kodi kudzachitika? Ngati kudzatero, liti?
Kusiyanasiyana kwa Malingaliro Onena za Kutengedwa m’Thupi
Baibulo limasonyeza kuti Kulamulira kwa Zaka Chikwi kolonjezedwa kwa Kristu kusanayambe, kudzakhala nyengo yotchedwa “chisautso chachikulu.” Yesu anati: “Nthaŵi imeneyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichizachitikanso.” (Mateyu 24:21, NW; Chivumbulutso 20:6) Ena amati kutengedwa m’thupi kudzayamba chisautso chachikulu chisanafike. Ena amakuyembekezera mkati mwa nthaŵi imeneyo. Pamene ena amaganiza kuti kutengedwa m’thupi kudzachitika pambuyo pa chisautso chosayerekezereka chimenecho.
Lingaliro lakuti kutengedwa m’thupi kudzachitika pambuyo pa chisautso chachikulu linali lofunga kufikira kuchiyambiyambi kwa zaka za zana la 19. Pamenepo, mu Mangalande munayamba gulu lina lotsogozedwa ndi amene kale anali mtsogoleri wachipembedzo wa Tchalitchi cha Ireland, John Nelson Darby. Iye limodzi ndi mamembala a Anglican amaganizo ofananawo anafikikira pakudziŵika monga a Brethren. Kuchokera kulikulu lake laku Plymouth, Darby anayendayenda kukalalikira ku Switzerland ndi kwina kulikonse mu Yuropu. Iye anatsimikizira kuti kubweranso kwa Kristu kukachitika m’zigawo ziŵiri. Kukayamba ndi kutengedwa m’thupi kobisika, kumene “oyera mtima” akakwatulidwa nyengo ya zaka zisanu ndi ziŵiri ya chisautso chowononga dziko lapansi isanafike. Pamenepo Kristu akawonekera m’thupi, atatsagana ndi “oyera mtima” amenewa, ndipo iwo onse pamodzi akalamulira padziko lapansi kwa zaka chikwi.
Darby anagogomezera kufunika kwakukhala olekana ndi dziko, ndipo ogwirizana ndi malingaliro ake anafikira pakudziŵika monga a Exclusive Brethren. B. W. Newton anatsogolera kagulu kosiyana kamene kanakhulupirira m’kutengedwa m’thupi koma osati chisautso chisanachitike. Wochirikiza lingaliro lakuchitika pambuyo pa chisautso Alexander Reese ananena kuti “nthanthi za Kutengedwa m’Thupi mwachinsinsi ziri chiwopsezo ku chiyembekezo cha Kudza kwa Kristu.”
Ochirikiza lingaliro la kutengedwa m’thupi chisautso chisanafike amakhulupirira kuti kusiyana kwalingaliro kumeneku kuli kwakukulu mokwanira kuyambukira “mpangidwe wa chiyembekezo [chawo] pankhani yokhudza kudza kwa Kristu.” Ena amayika chidaliro mu “lingaliro la kutengedwa m’thupi molekana,” akumakhulupirira kuti awo amene ali okhulupirika koposa kwa Kristu adzatengedwa m’thupi choyamba ndipo osapembedza koposerapowo adzatengedwa pambuyo pake.
Timagulu ta alaliki tambiri timalengeza za kutengedwa m’thupi kwa Akristu okhulupirika koyandikira. Komabe, powona malingaliro osiyanasiyana, kabukhu kofalitsidwa ndi Tchalitchi cha Elim Pentekoste cha ku Briteni kamati: “Ngakhale kuti tikhulupirira kuti pali mtandadza waukulu wa zochitika zophatikizapo kubweranso kwa Ambuye Yesu . . , ufulu umaloledwa wa kumasulira ulosi mogwirizana ndi chikhutiro cha munthuyo. Ambiri amavomereza lingaliro la kusapambanitsa, akumayembekezera moleza mtima kuti zochitika zenizenizo zifunyulule progamu ya ulosi.”
Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo, ndiwo muyezo mwa umene timafunikira kupima kuti kaya ziphunzitso zonse ziri zowona. (2 Timoteo 1:13; 3:16, 17) Motero, kodi ilo limanenanji pa kutengedwa m’thupi?