Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 1/15 tsamba 25-30
  • Peŵani Kulambira Mafano Kwamtundu Uliwonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Peŵani Kulambira Mafano Kwamtundu Uliwonse
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulambira Mafano kwa Chikristu Chadziko Kunachitiridwa Chithunzi
  • Mitundu Ina ya Kulambira Mafano
  • Peŵani Umbombo ndi Chisiriro
  • Peŵani Kudzilambira Inumwini
  • Khalani Maso!
  • Kodi Nkupeŵeranji Kulambira Mafano?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Uone Zinthu Zoipa Ndi Zonyansa Zimene Anthu Akuchita”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • ‘Ika Mtima Wako pa’ Kachisi wa Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—1999
  • ‘Ufotokoze za Kachisiyu’
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 1/15 tsamba 25-30

Peŵani Kulambira Mafano Kwamtundu Uliwonse

“Chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano?”​—2 AKORINTO 6:16.

1. Kodi nchiyani chinaphiphiritsiridwa ndi chihema chokumanako cha Israyeli ndi akachisi?

YEHOVA ali ndi kachisi wopanda mafano. Anaphiphiritsiridwa ndi chihema chokumanako cha Israyeli chomangidwa ndi Mose ndipo ndi akachisi amene anamangidwa pambuyo pake m’Yerusalemu. Zimangozo zinaimira “chihema chowona,” kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Ahebri 8:1-5) Kachisi ameneyo ndiye makonzedwe akumfikira Mulungu m’kulambira pamaziko a nsembe ya dipo la Yesu Kristu.​—Ahebri 9:2-10, 23.

2. Kodi ndani anadzakhala mizati m’kachisi wamkulu wauzimu wa Mulungu, ndipo kodi akhamu lalikulu akusangalala ndi kaimidwe kotani?

2 Mkristu wodzozedwa aliyense amakhala “mzati wa m’kachisi [wa Mulungu],” akumalandira malo kumwamba. “Akhamu lalikulu” la olambira ena a Yehova “amtumikira [Mulungu]” m’malo amene anaimiridwa ndi bwalo la Amitundu pakachisi womangidwanso ndi Herode. Chifukwa chakukhala ndi chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu, iwo ali ndi kaimidwe kolungama kamene kadzawapangitsa kupulumuka “chisautso chachikulu.”​—Chivumbulutso 3:12; 7:9-15.

3, 4. Kodi mpingo wa Akristu odzozedwa apadziko lapansi ukufaniziridwa ndi chiyani, ndipo kodi nkuipitsidwa kotani kumene ayenera kupeŵa?

3 Mpingo wa Akristu odzozedwa padziko lapansi umafaniziridwanso mophiphiritsira ndi kachisi wina wopanda mafano. Kwa oterowo “osindikizidwa chizindikiro ndi mzimu woyera,” mtumwi Paulo anati: “Omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wapangondya; mwa iye chimango chonse, cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale kachisi wopatulika mwa Ambuye, chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa mzimu.” (Aefeso 1:13; 2:20-22) A 144,000 osindikizidwa chizindikirowa ali “miyala yamoyo yomangidwa nyumba yauzimu kukhala ansembe oyera mtima.”​—1 Petro 2:5; Chivumbulutso 7:4; 14:1.

4 Popeza kuti ansembe aang’ono ameneŵa ali “chimango cha Mulungu,” iye samalola kachisi ameneyu kuipitsidwa. (1 Akorinto 3:9, 16, 17) “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana,” anachenjeza motero Paulo. “Pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira? Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano?” Akristu odzozedwa, amene ali a “Yehova Wamphamvuyonse,” sayenera kulambira mafano. (2 Akorinto 6:14-18) Akhamu lalikulu ayeneranso kupeŵa kulambira mafano kwamtundu uliwonse.

5. Pozindikira kuti Yehova amafuna kudzipereka kotheratu, kodi Akristu owona amachitanji?

5 Pali mitundu iŵiri yakulambira mafano, kwachindunji ndi kwamachenjera. Ayi, kulambira mafano sikuli kokha kulambira milungu ndi milungu yachikazi yonama. Kuli kulambira kanthu kalikonse kapena munthu aliyense kusiyapo Yehova. Monga Mfumu Yachilengedwechonse, iye moyenerera amafuna ndipo amafunikira kupatsidwa kudzipereka kotheratu. (Deuteronomo 4:24) Pozindikira zimenezi, Akristu owona amalabadira machenjezo a m’Malemba otsutsa kulambira mafano konse. (1 Akorinto 10:7) Tiyeni tipende mitundu ina yakulambira mafano yoyenera kupeŵedwa ndi atumiki a Yehova.

Kulambira Mafano kwa Chikristu Chadziko Kunachitiridwa Chithunzi

6. Kodi Ezekieli anawona zinthu zonyansa zotani m’masomphenya?

6 Pamene anali m’ndende ku Babulo mu 612 B.C.E., mneneri Ezekieli anawona masomphenya a zinthu zonyansa zochitidwa ndi Ayuda ampatuko pakachisi wa Yehova m’Yerusalemu. Ezekieli anawona “fano la nsanje.” Akulu makumi asanu ndi aŵiri anawonedwa akupereka nsembe zofukiza m’kachisimo. Akazi anawonedwa akulirira mulungu wonama. Ndipo amuna 25 anali kulambira dzuŵa. Kodi machitidwe achipanduko ameneŵa anatanthauzanji?

7, 8. Kodi “fano la nsanje” lingakhale linali chiyani, ndipo nchifukwa ninji linaputa nsanje ya Yehova?

7 Kulambira mafano kwa Chikristu Chadziko kunachitiridwa chithunzi ndi zinthu zonyansa zimene Ezekieli anawona m’masomphenya. Mwachitsanzo, iye anati: “Tawonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano iri la nsanje poloŵera pake. Ndipo [Yehova Mulungu] anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uwona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israyeli irikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika?”​—Ezekieli 8:1-6.

8 Fano la nsanjelo lingakhale linali mlongoti wopatulika woimira mulungu wachikazi wonama amene Akanani anamlingalira kukhala mkazi wa mulungu wawo Bala. Mosasamala kanthu za chimene fanolo linali, linaputa nsanje ya Yehova chifukwa chakuti linagaŵanitsa kudzipereka kotheratu kwa Israyeli kwa iye moswa malamulo ake: “Ine ndine Yehova Mulungu wako . . . Usakhale nayo milungu ina koma ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu za m’thambo lakumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usadzitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, [wofuna kudzipereka kotheratu, NW].”​—Eksodo 20:2-5.

9. Kodi ndimotani mmene Chikristu Chadziko chaputira Yehova kuchita nsanje?

9 Kulambira fano la nsanje m’kachisi wa Mulungu kunali chimodzi cha zinthu zonyansa zochitidwa ndi Aisrayeli ampatuko. Mofananamo, matchalitchi a Chikristu Chadziko ngoipitsidwa ndi mafano ndi zithunzithunzi zonyoza Mulungu zimene zimagaŵanitsa kudzipereka kotheratu kumene akunena kuti akupereka kwa Uyo amene iwo amati akumtumikira. Mulungu amaputidwanso kuchita nsanje chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzo akukana Ufumu wake monga chiyembekezo chokha cha anthu nalambira Mitundu Yogwirizana​—“Chonyansa . . . choima m’malo oyera,” amene sichiyenera kuimapo.​—Mateyu 24:15, 16; Marko 13:14.

10. Kodi Ezekieli anawonanji mkati mwa kachisi, ndipo zimenezi zimafanana motani ndi zimene zikuwonedwa m’Chikristu Chadziko?

10 Ataloŵa m’kachisi, Ezekieli akunena kuti: “Tawonani, mawonekedwe ali onse a zokwaŵa, ndi zirombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israyeli, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse. Ndipo pamaso pawo panaima amuna makumi asanu ndi aŵiri a akulu a nyumba ya Israyeli . . . munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m’dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.” Tangolingalirani! Akulu Achiisrayeli m’kachisi wa Yehova, akumapereka nsembe zofukiza kwa milungu yonama, yoimiridwa ndi zifaniziro zonyansa zolembedwa pakhoma. (Ezekieli 8:10-12) Mofananamo, mbalame ndi zirombo zimagwiritsiridwa ntchito kuimira maiko a Chikristu Chadziko, kwa amene anthu amadzipereka. Ndiponso, atsogoleri achipembedzo ambiri ali ndi liwongo lakuthandizira kusocheretsa namtindi wa anthu mwakuchirikiza nthanthi yolakwayo yakuti munthu anasinthika kuchokera ku mipangidwe ina ya zamoyo zotsika kuposa anthu, mmalo mwachirikiza cholembedwa cha m’Baibulo chonena za kulenga kwa Yehova Mulungu.​—Machitidwe 17:24-28.

11. Kodi nchifukwa ninji akazi Achiisrayeli ampatuko anali kulirira Tamuzi?

11 Pachipata choloŵera cha nyumba ya Yehova, Ezekieli anawona akazi Achiisrayeli ampatuko akulirira Tamuzi. (Ezekieli 8:13, 14) Ababulo ndi Asiriya anawona Tamuzi kukhala mulungu wa zomera zimene zimaphuka m’nyengo yadzinja ndi kufa m’nyengo yachirimwe. Kufa kwa zomerezo kunaimira imfa ya Tamuzi, amene analiridwa chaka ndi chaka ndi olambira ake panthaŵi yakutentha kwakukulu. Pamene zomerazo zinaphukiranso m’nyengo yadzinja, Tamuzi analingaliridwa kukhala atabwerako kudziko la pansi pantha. Anaimiridwa ndi chilembo choyamba cha dzina lake, tau wakaleyo amene analembedwa mumpangidwe wa mtanda. Izi zikhoza kutikumbutsa bwino lomwe za kupembedza fano lamtanda kwa Chikristu Chadziko.

12. Kodi Ezekieli anawona amuna 25 Achiisrayeli ampatuko akuchitanji, ndipo ndikachitidwe kofanana kotani kamene kakuchitika m’Chikristu Chadziko?

12 M’bwalo lamkati lakachisi, Ezekieli kenako anawona amuna Achiisrayeli ampatuko 25 akulambira dzuŵa​—kuswa lamulo la Yehova lotsutsa kulambira mafano kotero. (Deuteronomo 4:15-19) Olambira mafano amenewo, analoza kumphuno kwa Mulungu nthambi yonyansa, mwinamwake yoimira mpheto yaumunthu yachimuna. Mposadabwitsa kuti Mulungu sakayankha mapemphero awo, monga momwedi Chikristu Chadziko chidzafunira chithandizo chake mkati mwa “chisautso chachikulu” mosaphula kanthu. (Mateyu 24:21) Monga momwe Aisrayeli ampatukowo analambirira dzuŵa lopereka kuunika atafulatira kachisi wa Yehova, choteronso Chikristu Chadziko chimafulatira kuunika kochokera kwa Mulungu, nichiphunzitsa ziphunzitso zonyenga, kulambira nzeru yadziko, ndi kulekerera chisembwere.​—Ezekieli 8:15-18.

13. Kodi Mboni za Yehova zimapeŵa motani mitundu yakulambira mafano imene Ezekieli anawona m’masomphenya?

13 Mboni za Yehova zimapeŵa mipangidwe yakulambira mafano yochitidwa m’Chikristu Chadziko, kapena Yerusalemu wophiphiritsiridwa, monga momwe kunawonedweratu ndi Ezekieli. Sitimapembedza mafano otonza Mulungu. Ngakhale kuti timasonyeza ulemu kwa “maulamuliro aakulu,” kuwagonjera kwathu kuli ndi polekezera. (Aroma 13:1-7; Marko 12:17; Machitidwe 5:29) Kudzipereka kwathu kwamtima wonse kumamka kwa Yehova ndi Ufumu wake. Sitimaika nthanthi yachisinthiko pamalo a Mlengi ndi chilengedwe chake. (Chivumbulutso 4:11) Sitimalemekeza konse mtanda kapena kulambira luntha ladziko, nthanthi, kapena mitundu ina ya nzeru zadziko. (1 Timoteo 6:20, 21) Timapeŵanso mitundu ina yonse yakulambira mafano. Kodi ina ya imeneyi ndiiti?

Mitundu Ina ya Kulambira Mafano

14. Kodi atumiki a Yehova akutenga kaimidwe kotani ponena za ‘chirombo’ cha pa Chivumbulutso 13:1?

14 Akristu samagwirizana ndi mtundu wa anthu m’kulambira ‘chirombo’ chophiphiritsira. Mtumwi Yohane anati: “Ndinawona chirombo chirinkutuluka m’nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iŵiri, ndi panyanga zake nduŵira zachifumu khumi . . . Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko lapansi.” (Chivumbulutso 13:1, 8) Zirombo zingaphiphiritsire “mafumu,” kapena maulamuliro andale zadziko. (Danieli 7:17; 8:3-8, 20-25) Chotero mitu isanu ndi iŵiri ya chirombo chophiphiritsiracho imaimira maulamuliro adziko​—Igupto, Asiriya, Babulo, Amedi ndi Aperesi, Girisi, Roma, ndi Anglo-America, mgwirizano wa Briteni ndi United States of America. Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amasonyeza chitonzo chachikulu kwa Mulungu ndi Kristu mwakutsogolera anthu m’kulambira dongosolo la Satana, “wolamulira wa dziko lino.” (Yohane 12:31) Komabe, monga osunga uchete Achikristu ndi ochirikiza Ufumuwo, atumiki a Yehova amakana kulambira mafano kotero.​—Yakobo 1:27.

15. Kodi anthu a Yehova amaziwona motani ngwazi zakudziko, ndipo nchiyani chimene mmodzi wa Mboni za Yehova ananena pazimenezi?

15 Anthu a Mulungu amapeŵanso kulambira ngwazi za dziko za zosangulutsa ndi za maseŵera. Pamene anakhala Mboni ya Yehova, woimba wina anati: “Nyimbo zosangulutsa ndi zovina zikhoza kudzutsa zilakolako zoipa . . . Woimbayo amaimba za chimwemwe ndi chikondi zimene omvetsera ambiri angazilingalire kukhala zosoŵeka mwa mnzawo wamuukwati. Woimbayo kaŵirikaŵiri amagwirizanitsidwa ndi zimene amaimba. Ngwazi zina zimene ndimadziŵa zimakondedwa kwambiri ndi akazi chifukwa cha zimenezi. Pamene munthu amwerekera m’dzikoli la maloto akuyerekezera, kungamchititse kuyamba kulambira woseŵerayo. Kungayambike popanda liwongo mwakupempha cholembedwa cha munthuyo monga chomkumbukirapo. Koma ena afikira pakulingalira katswiriyo kukhala kanthu kawo kofunika koposa, ndipo mwakumkweza mopambanitsa, amampanga kukhala fano lawo. Iwo angapachike chithunzithunzi cha ngwaziyo pakhoma ndi kuyamba kuvala ndi kupesa mofanana naye. Akristu afunikira kukumbukira kuti kupembedza kuyenera kupita kwa Mulungu yekha.”

16. Kodi nchiyani chimasonyeza kuti angelo olungamawo amatsutsa kulambira mafano?

16 Inde, Mulungu yekha ndiye ayenera kupembedzedwa kapena kulambiridwa. Pamene Yohane “anagwa pansi kulambira pamapazi a mngelo” amene adamsonyeza zinthu zozizwitsa, munthu wauzimuyo anakana kulambiridwa mwanjira iriyonse koma anati: ‘Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mawu a bukhu ili; lambira Mulungu.’ (Chivumbulutso 22:8, 9) Kuwopa Yehova, kapena ulemu waukulu kwa iye, kumatichititsa kumlambira iye yekha. (Chivumbulutso 14:7) Chifukwa chake, kudzipereka kwaumulungu kowona kumatitetezera kukulambira mafano.​—1 Timoteo 4:8.

17. Kodi tingapeŵe motani kulambira mafano kwa makhalidwe achisembwere?

17 Chisembwere chakugonana ndicho mtundu wina wa kulambira mafano kokanidwa ndi atumiki a Yehova. Iwo amadziŵa kuti “wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe choloŵa mu ufumu wa Kristu ndi Mulungu.” (Aefeso 5:5) Kulambira mafano kumaloŵetsedwamo chifukwa chakuti chilakolako cha zosangulutsa zosayenera chimakhala chinthu kwa chimene munthu amadzipereka. Mikhalidwe yaumulungu imatsamwitsidwa ndi zilakolako zosayenera zakugonana. Mwakusumika maso ndi makutu ku zinthu zosonyeza umaliseche, munthuyo amawononga unansi uliwonse umene angakhale nawo ndi Mulungu woyerayo, Yehova. (Yesaya 6:3) Pamenepo, kuti adzichinjirize ku kulambira mafano koteroko, atumiki a Mulungu ayenera kupeŵa zithunzi zosonyeza maliseche ndi nyimbo zoluluza. Afunikira kumamatira ku mikhalidwe yauzimu yolimba yozikidwa pa Malemba, ndipo ayenera kupitirizabe kukhala ndi “umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo chowona ndi kukhulupirika.”​—Aefeso 4:22-24.

Peŵani Umbombo ndi Chisiriro

18, 19. (a) Kodi umbombo ndi chisiriro nchiyani? (b) Kodi tingapeŵe motani kulambira mafano kwakuchita umbombo ndi kusirira?

18 Akristu amapeŵanso umbombo ndi chisiriro, zimene ziri mitundu yogwirizana kwambiri yakulambira mafano. Umbombo ndiwo chikhumbo chopambanitsa kapena chopanda malire, ndipo chisiriro ndicho kukhumbira mwadyera chinthu chirichonse cha munthu wina. Yesu anachenjeza za chisiriro nanena za mwamuna wachuma wosirira amene sanathe kupindula ndi chuma chake paimfa ndipo anali mumkhalidwe womvetsa chisoni “wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.” (Luka 12:15-21) Paulo moyenerera anapatsa uphungu okhulupirira anzake kuti: “Fetsani . . . ziŵalo za thupi lanu zimene ziri padziko lapansi kulinga ku . . . chisiriro, chimene chiri kulambira mafano.”​—Akolose 3:5, NW.

19 Awo omwerekera m’chikondi cha pandalama, okhala ndi kususuka kwakukulu kwa zakudya ndi zakumwa, kapena kulakalaka kwambiri ulamuliro amapangitsa zikhumbo zoterezo kukhala mafano awo. Monga momwe Paulo anasonyezera, munthu waumbombo ali wolambira mafano ndipo sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 5:5) Chifukwa chake, anthu obatizidwa amene amalambira mafano mwakukhala anthu aumbombo akhoza kuchotsedwa mumpingo Wachikristu. Komabe, mwakugwiritsira ntchito Malemba ndi kupemphera mwakhama, tikhoza kupeŵa umbombo. Imanena motere Miyambo 30:7-9: “Zinthu ziŵiri ndakupemphani [Yehova Mulungu], musandimane izo ndisanamwalire: Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma. Mundidyetse zakudya zondiyenera; Ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.” Mzimu woterowo ungatithandize kupeŵa kulambira mafano kwakuchita umbombo ndi chisiriro.

Peŵani Kudzilambira Inumwini

20, 21. Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova amapeŵera kudzilambira iwo eni?

20 Anthu a Yehova amapeŵanso kudzilambira iwo eni. M’dziko lino kuli kofala kwa anthu kudzilambira iwo eni ndi zifuniro zawo. Chikhumbo chakufuna kutchuka ndi ulemerero chimachititsa ambiri kuchita mwanjira zachinyengo. Iwo amafuna chifuniro chawo kuchitidwa, osati cha Mulungu. Koma sitingakhale ndi unansi ndi Mulungu ngati mwachinyengo tigonjera kukudzilambira mwakuyesayesa kupeza zofuna zathu ndi kuyesa kuchita umbuye pa ena. (Miyambo 3:32; Mateyu 20:20-28; 1 Petro 5:2, 3) Monga otsatira a Yesu, takana zinthu zamachenjera zadzikoli.​—2 Akorinto 4:1, 2.

21 Mmalo mwakufunafuna kutchuka, anthu a Mulungu amatsatira uphungu wa Paulo wakuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Pokhala atumiki a Yehova, sitimaumirira modzilambira panjira yathuyathu koma mwachisangalalo timachita chifuniro cha Mulungu, tikumalandira chitsogozo kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi kugwirizana mokwanira ndi gulu la Yehova.​—Mateyu 24:45-47.

Khalani Maso!

22, 23. Kodi ndimotani mmene tingapeŵere kulambira mafano kwamtundu uliwonse?

22 Monga anthu a Yehova, sitimagwadira mafano a zinthu zowoneka. Timapeŵanso kulambira mafano kwamachenjera. Kunena zowona, tiyenera kupitiriza kupeŵa kulambira mafano kwamtundu uliwonse. Chotero timatsatira uphungu wa Yohane wakuti: “Dzisungireni nokha kupeŵa mafano.”​—Yohane 5:21.

23 Ngati ndinu mmodzi wa atumiki a Yehova, nthaŵi zonse gwiritsirani ntchito chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo ndi mphamvu zakulingalira. (Ahebri 5:14) Pamenepo, simudzaipitsidwa ndi mzimu wadziko wakulambira mafano koma mudzakhala ngati Ahebri atatu okhulupirika aja ndi Akristu oyambirira okhulupirikawo. Mudzapatsa Yehova kudzipereka kotheratu, ndipo adzakuthandizani kupitirizabe kupeŵa kulambira mafano kwamtundu uliwonse.

Kodi Malingaliro Anu Ngotani?

◻ Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimapeŵera kulambira mafano kowonedwa m’masomphenya a Ezekieli?

◻ Kodi ‘chirombo’ cha pa Chivumbulutso 13:1 nchiyani, ndipo ndikaimidwe kotani kamene atumiki a Yehova amatenga ponena za icho?

◻ Kodi nkupeŵeranji kulambira ngwazi za zosangulutsa ndi za maseŵera?

◻ Kodi tingapeŵe motani kudzilambira ife eni?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kulambira mafano kwamtundu uliwonse?

[Zithunzi patsamba 26]

Kodi mumadziŵa mmene zonyansa zowonedwa m’masomphenya a Ezekieli zinachitira chithunzi kulambira mafano kwa Chikristu Chadziko?

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzithunzi (chapamwambacho kulamanzere) chazikidwa pa chithunzithunzi cha Ralph Crane/​Bardo Museum

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena