Kodi Chabwino Chidzagonjetsadi Choipa?
PAFUPIFUPI zaka zikwi ziŵiri zapitazo, Yesu Kristu, mwamuna wosalakwa, anali kuimbidwa mlandu kuti aphedwe. Anthu oipa anachita chiwembu kuti amuwononge chifukwa chakuti analankhula chowonadi. Iye ananenezedwa monama mlandu wakuukira boma, ndipo khamu linafuula kuti aphedwe. Kazembe wa Roma, amene anaŵerengera kwambiri ulemu wa iye mwini wandale zadziko kuposa moyo wa kalipentala wamba, anaŵeruzira Yesu kuimfa yankhalwe. Malinga ndi mawonekedwe onse akunja, kunawonekera ngati kuti choipa chinapambana.
Komabe, usikuwo asanaphedwe, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndalilaka dziko lapansi.” (Yohane 16:33) Kodi anatathauzanji? Mwapang’ono, kuti choipa m’dziko sichinampsetse mtima kapena kumupangitsa kulipsira mofananamo. Dziko silinamkanikizire m’chikombole choipa. (Yerekezerani ndi Aroma 12:2, Phillips.) Ngakhale pamene anali kufa, iye anapempherera akumuphawo kuti: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.”—Luka 23:34.
Yesu anasonyeza—kufikira imfa—kuti choipa chingathe kugonjetsedwa. Iye analimbikitsa otsatira ake kudzimenyera nkhondo motsutsana ndi choipa. Kodi iwo angatero motani? Mwakulabadira uphungu Wamalemba wa ‘kusabwezera munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa,’ koma ndi ‘chabwino kugonjetsa choipa,’ monga momwe Yesu anali atachitira. (Aroma 12:17, 21) Koma kodi njira yotero imagwiradi ntchito?
Kulimbana ndi Choipa m’Dachau
Else anali mkazi wachikulire wa ku Jeremani woikidwa m’ndende ku Dachau amene anapereka mphatso yamtengo wapatali kwa msungwana wina wa zaka 14 waku Russia, mphatso yachikhulupiriro ndi chiyembekezo.
Dachau unali msasa wachibalo wokhala ndi mbiri yoipa kumene anthu zikwi zambiri anafa ndipo mazana ambiri, kuphatikizapo msungwana wachichepere wa ku Russia ameneyu, anaphatikizidwa m’zofufuza mankhwala zankhalwe zochitidwa pa iwo. Dachau anawonekera kukhala chitsanzo chenicheni cha choipa. Komabe, ngakhale m’mikhalidwe yowonekera kukhala yovutitsa yotero, zabwino zinaphukamo ndipo ngakhale moŵirikiza.
Else anamverera chisoni kwambiri msungwana wachichepere ameneyu amene anakakamizidwanso kuwonerera alonda a SS akugwirira chigololo amake mwauchinyama. Else, moika moyo wa iye mwini pachiswe, anafunafuna mipata yakulankhula kwa msungwanayu za chabwino ndi choipa, ndi chiyembekezo Cham’malemba chachiukiriro. Iye anaphunzitsa bwenzi lake lachicheperelo kukonda osati kuda. Ndipo msungwana wa ku Russia anapulumuka zowopsa zaku Dachau chifukwa cha Else.
Else anachita zomwe anachitazo chifukwa chakuti anafuna kutsatira chitsanzo cha Kristu chakudzimana. Monga mmodzi wa Mboni za Yehova, iye anaphunzira kusabwezera choipa ndi choipa, ndipo chikhulupiriro chake chinamsokhezera kuthandiza ena kuchita mofananamo. Ngakhale kuti iye anavutika ku Dachau, iye anapeza chilakiko chamakhalidwe pa ulamuliro wachoipa. Ndipo sanali yekhayo.
Paul Johnson, m’bukhu lake A History of Christianity, ananena kuti “[Mboni za Yehova] zinakana kugwirizana kulikonse ndi boma la Nazi limene izo zinatsutsa kukhala lauchiwanda kotheratu. . . . 97 peresenti anazunzidwa m’mipangidwe yosiyanasiyana.” Kodi inali nkhondo yosaphula kanthu? M’bukhu lakuti Values and Violence in Auschwitz, katswiri wodziŵa makhalidwe a anthu wa ku Poland Anna Pawelczynska anati ponena za Mboni: “Kagulu kochepa ka andende kameneka kanali mphamvu yolimba yamaganizo ndipo kanapambana nkhondo yake yolimbana ndi Chinazi.”
Komabe, kwa ambiri a ife, nkhondo yaikulu yolimbana ndi choipa imamenyedwa mkati mwathu ndipo osati kulimbana ndi choipa chakunja. Iri nkhondo yamkati mwathu.
Kugonjetsa Choipa Mkati Mwathu
Mtumwi Paulo anafotokoza nkhondo imeneyi mwanjira yotsatirayi: “Pakuti sichabwino chimene ndifuna kuchita chomwe ndimachitadi; chiri choipa chimene sindifuna kuchita chimene ndimapitirizabe kuchichita.” (Aroma 7:19, The New Testament, lolembedwa ndi William Barclay) Monga momwe Paulo anadziŵira bwino lomwe, kaŵirikaŵiri kuchita chabwino sikumadza mwachibadwa.
Eugenioa anali mnyamata wa ku Spanya, amene kwa zaka zovutika ziŵiri, anamenya nkhondo motsutsana ndi zikhoterero zake zoipa. “Ndinafunikira kukhala wodziletsa zolimba,” iye akufotokoza. “Kuyambira pa ubwana, ndinali ndi chikhoterero chakukhala wachisembwere. Monga wachichepere, ndinaphatikizidwa modzifunira m’machitachita akugonana kwa dziŵalo zofanana, ndipo kunena mosabisa mawu, ndinasangalala ndi njira yamoyo imeneyo.” Kodi chinamchititsa kuti potsirizira pake afune kusintha nchiyani?
“Ndinafuna kukondweretsa Mulungu, ndipo ndinaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti iye sanavomereze mmene ndinali kukhalira,” Eugenio anatero. “Chotero ndinasankha kukhala munthu wosiyana, kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zitsogozo za Mulungu. Tsiku lirilonse, ndinafunikira kumenyana ndi maganizo oipa, auve amene anafikabe kudzaza malingaliro anga. Ndinali wotsimikiza kupeza chipambano m’nkhondoyi, ndipo ndinapempherera chithandizo cha Mulungu mosaleka. Pambuyo pazaka ziŵiri mbali yoipitsitsa inali itatha, ngakhale kuti ndidakali wodziletsa zolimba. Koma nkhondoyo inali yoyenerera. Ine tsopano ndiri ndikudzilemekeza, ukwati wabwino, ndipo, koposa zonse, unansi wabwino ndi Mulungu. Ndidziŵa kuchokera ku zokumana nazo za ine mwini kuti maganizo oipa angathe kuchotsedwa asanayambe kubala zipatso—ngati upangadi kuyesayesa.”
Chabwino chimagonjetsa choipa nthaŵi iriyonse imene ganizo loipa likanidwa, nthaŵi iriyonse imene tikana kubwezera choipa ndi choipa. Komabe, zipambano zotero, ngakhale kuti nzofunika kwambiri, sizimachotsa magwero aakulu aŵiri achoipa. Mulimonse mmene tingayesere mwamphamvu, sitingathe kugonjetsa kotheratu zifooko zathu zobadwa nazo, ndipo Satana akali kugwiritsirabe ntchito chisonkhezero choipa pa anthu. Chotero kodi mkhalidwe umenewu udzasinthadi?
Kuwononga Mdyerekezi
Kukhulupirika kwa Yesu kufikira imfa kunali kugonjetsedwa kwakukulu kwa Satana. Mdyerekezi analephera kuyesayesa kwake kuswa umphumphu wa Yesu, ndipo kulephera kumeneku kunali chiyambi chamapeto a Satana. Monga momwe Baibulo limafotokozera, Yesu analaŵa imfa kuti ‘mwa imfa yake akamuwononge . . . Mdyerekezi.’ (Ahebri 2:14) Pambuyo pachiukiriro chake Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mateyu 28:18) Ndipo ulamuliro umenewo ukagwiritsiridwa ntchito kuthetsa ntchito za Satana.
Bukhu la Chivumbulutso limafotokoza tsiku pamene Yesu akagwetsa Satana kuchokera kumiyamba. Wochita choipa Wamkulu ameneyu, limodzi ndi ziŵanda zake, anali kudzabindikiritsidwa pafupi ndi dziko lapansi. Chotulukapo chake, Baibulo likuchenjeza, kuti zoipa zikachuluka: ‘Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’—Chivumbulutso 12:7-9, 12.
Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti chochitika cham’mbiri chimenechi chinachitika kale—panthaŵi ya Nkhondo Yadziko Yoyamba.b Izi zikufotokoza chifukwa chake pali kuwonjezereka kwakukulu kwa zoipa zimene tawona m’nthaŵi yathu. Koma posachedwa Satana adzaletsedwa kotheratu kotero kuti asasonkhezerenso aliyense—Wonani Chivumbulutso 20:1-3.
Kodi zonsezi zidzatanthauzanji kwa anthu?
“Sadzachita Choipa”
Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu posachedwa adzagwiritsira ntchito ‘ulamuliro wake padziko lapansi’ kulinganiza programu yakuphunzitsanso kwauzimu. ‘Okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.’ (Yesaya 26:9) Mapindu adzakhala achiwonekere kwa aliyense. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Iwo sadzachita upandu uliwonse [“sadzachita choipa,” Interlinear Hebrew/Greek English Bible la Green] kapena kuchititsa chiwonongeko chirichonse . . . chifukwa chakuti dziko lapansi lidzakhala lodzaladi chidziŵitso cha Yehova monga momwe madzi akudzazira nyanja yeniyeniyo.”—Yesaya 11:9, NW.
Ngakhale tsopano, zambiri za zikhoterero zathu zoipa zingathe kugonjetsedwa. Pamene chisonkhezero chauchiŵanda chidzachoka, kudzakhaladi kosavutirapo kwambiri, ‘kupatuka pachoipa, ndi kuchita chabwino.’—1 Petro 3:11.
Tiri ndi chifukwa chabwino chakukhalira ndi chidaliro kuti chabwino chidzagonjetsa choipa chifukwa chakuti Mulungu ngwabwino, ndipo mwachithandizo chake awo ofuna kuchita chabwino angathe kugonjetsa choipa, monga momwe Yesu anatsimikizirira mwachitsanzo cha iye mwini. (Salmo 119:68) Awo amene tsopano ali ofunitsitsa kumenyana ndi choipa angayang’anire mtsogolo kukhala m’dziko lapansi loyeretsedwa lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu, boma lodzipereka kuchotsa choipa kunthaŵi yonse. Wamasalmo akufotokoza chotulukapo chake: ‘Chifundo ndi chowonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsopsonana. Chowonadi chiphukira m’dziko; ndi chilungamo chasuzumira chiri m’mwamba.’—Salmo 85:10, 11.
[Mawu a M’munsi]
a Sidzina lake lenileni.
b Kuti mupeze mawu awonjezereka, wonani patsamba 20-2 m’bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.