Lipoti la OLengeza Ufumu
Iwo Anasintha Njira Yawo ya Moyo
MOSAKAIKIRA mwawawona akulankhula kwa ena pamakwalala, akupita panyumba ndi nyumba, kapena akufika pamisonkhano Yachikristu m’Nyumba zawo Zaufumu. Tikulankhula za achichepere opesa bwino a Mboni za Yehova. Inu munganene kuti iwo ali Mboni chifukwa chakuti makolo awo anawaphunzitsa kukhala otero, ndipo ndimmene ziriri kumene kwa ambiri a iwo. Kumbali ina, pali ena a achichepere amenewa amene ali ndi chiyambi chosiyana kwambiri ndi amene poyamba njira yawo yamoyo inali yosiyana kotheratu ndi imene ali tsopano. M’chenicheni, awo osonyezedwa patsamba lotsatira anali ziŵalo za timagulu timene upandu ndi kugwiritsira ntchito anamgoneka zinali zochitika za tsiku ndi tsiku. Kodi nchiyani chimene chinawapangitsa kusintha miyoyo yawo kotheratu chotero? Tiyeni tikacheze kutawuni ina m’Norway ndi kukomana ndi ena a achichepere amene apanga masinthidwe otero.
Maziko Osinthira
Pamene Mboni ziŵiri zinakomana ndi Annette m’ntchito yapanyumba ndi nyumba, iye anali wazaka 19. “Kaŵirikaŵiri ndinauzidwa kusalankhula konse kwa Mboni za Yehova, koma ndinali ndi chidwi ndipo ndinawaitanira m’nyumba,” iye akukumbukira. Msungwanayu anali wogwiritsira ntchito anamgoneka kuyambira pamene anali wazaka 11 ndipo anali ataphatikizidwa m’kuchita umbala kochuluka ndi kuba magalimoto.
Mbiri yabwino Yaufumu inamkopa mtima. Iye kwakukulukulu analimbikitsidwa ndi chiyembekezo chachiukiriro, popeza anataikiridwa ndi amake muimfa ali ndi zaka zisanu zakubadwa. Chotero anavomereza phunziro la Baibulo laulere nayamba kufika pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu. Iye anauza bwenzi lake lachinyamata ndi enawo zimene anali kuphunzira. Ndichotulukapo chotani? Iwo sanafune kuphatikizidwa m’chipembedzocho ndipo ananeneza Annette kuti anachititsidwa kukhala mbuli. Komabe, ena a awo amene anatsutsa kwambiri pambuyo pake anayamba kuphunzira Baibulo.
Mwachitsanzo, Espen, mnyamata wazaka 20 zakubadwa. Iye anamva mbiri yabwino ya Ufumu kwabwenzi lachinyamata la Annette ndipo mwamsanga anafuna phunziro la Baibulo. Komabe, iye anali kuyembekezera kugwira ukaidi m’ndende miyezi inayi, popeza kuti anaphatikizidwa m’kuloŵetsa anamgoneka moswa lamulo ndipo, mofanana ndi Annette, m’kuchita umbala kungapo. Iye analinso wosuta fodya, chamba, ndi mankhwala ena. Tsopano, kodi chimene chikapangitsa munthu amene anaphatikizidwa m’zinthu zotere kufuna kuyamba kuphunzira Baibulo nchiyani? Espen anayamba kuzindikira kusapindulitsa kwa njira yake yamoyo yopanda chifuno. Iye akusimba kuti: “Ndinakopeka mtima ndi malonjezo a Baibulo amtsogolo mmene munandipatsa chifuno m’moyo. Chotero ndinayamba kuphunzira kuti nditsimikizire ngati ndinauzidwa chowonadi.”
Ena Akufuna Kuphunzira Baibulo
Pafupifupi nthaŵi imeneyi, mwamuna wina wachichepere wamisinkhu ya achicheperewo anamva chowonadi, ndipo nayenso anayamba kuphunzira nafika pamisonkhano. Kenako, phunziro linayambitsidwa ndi mmodzi wa achichepere amenewa, ndipo anayamba kufika pamisonkhano. Mwamsanga pambuyo pake, wachichepere wina anagwirizana ndi mabwenzi ake m’kuphunzira Baibulo ndi m’kupanga kupita patsogolo kwauzimu. Kenako panalinso mnyamata wina m’kagulu kofananako amene anachititsidwa chidwi ndi masinthidwe abwino amene mabwenzi ake anali kupanga, ndipo pasanapite nthaŵi, anafuna kuphunzira Baibulo.
Gilbert, woimba ndi ziŵiya zoimbira wachichepere wam’kagulu komweko, tsopano anayamba kuphunzira Baibulo. Makolo ake onse aŵiri anafa ndi kansa, chotero iye anatonthozedwa ndi chiyembekezo cha m’Baibulo cha chiukiriro. (Yohane 5:28, 29) Nayenso analikukoka chamba nakhala moyo woluluzika, ndipo anali kulakalaka kukhala katswiri wa nyimbo za rock. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, anapanga kupita patsogolo kwauzimu kwabwino ndipo mwamsanga anasankha kukhala Mboni ya Yehova. Potsirizira pake, mphwake wa Espen anayamba kufufuza Baibulo ndi kusonkhana ndi Mboni.
Chowonadi cha Baibulo Chisintha Miyoyo
Masinthidwe aakulu anachitika mwa achichepere ameneŵa amene poyamba anavala mwanyankhalala, tsitsi losapesa, ndi kuphatikizidwa m’mankhwala ogodomalitsa, kuba, ndi maupandu ena. Annette ali wofalitsa wabwino wa Ufumu ndipo watumikira monga mpainiya kwapafupifupi chaka chimodzi. Espen ndi Gilbert atumikira monga apainiya othandiza, ndipo alinso atumiki otumikira. Aŵiri onsewo akwatira mu mpingo Wachikristu. Ena anayi amene kale anali m’kaguluko nawonso ali ofalitsa Ufumu achangu!
Bwanji za chiŵeruzo cha m’ndende miyezi inayi chimene Espen anali kudzagwira ukaidi? Chifukwa cha masinthidwe amene iye anapanga m’moyo wake, chiŵeruzo chakecho chinasintha kukhala maola 80 ogwira ntchito m’mudzi. Movomerezedwa ndi apolisi ndi ena, iye anathera maola amenewa akugwira ntchito pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yamomwemo. Apolisi anakondwera kwambiri ndi kakonzedwe kameneka.
Inde, achichepere ena ambiri padziko lonse lapansi ali ndi chiyambi chaupandu. Koma chowonadi cha Mawu a Mulungu chawapatsa mayankho kumafunso ofunika ndi chiyembekezo chotsimikizirika chamtsogolo. Chifukwa chake, iwo salinso apandu kapena ogwiritsira ntchito anamgoneka, ndipo iwo samavala zovala zanyankhalala. Pokhala atasintha makhalidwe awo, iwo ali ofanana ndendende ndi otchulidwa poyambawo—achichepere, opesa bwino, ndi Mboni zachangu za Yehova. Iwo amafuna kudziŵitsa ena njira zokhalitsa za Baibulo zothetsera mavuto amene achichepere ambiri ali nawo lerolino.—Wonani 1 Akorinto 6:9-11.
[Chithunzi patsamba 8]
Achichepere a ku Norway alandira chowonadi