Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 2/1 tsamba 25-29
  • Ndinapeza Chikhutiro Kutumikira Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinapeza Chikhutiro Kutumikira Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambi Chachipembedzo
  • Posinthira
  • Banja Langa ndi Ena Alabadira
  • Ntchito Yosankhidwa Yatsopano
  • Uministala m’Lesotho ndi Botswana
  • Kuphunzitsa ndi Kumasulira
  • “Mwaimba Nambala Yolakwika”
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kukula ndi gulu la Yehova m’South Africa
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Pitirizanibe Kufesa Mbewu Yehova Adzazikulitsa
    Nsanja ya Olonda—1991
Nsanja ya Olonda—1993
w93 2/1 tsamba 25-29

Ndinapeza Chikhutiro Kutumikira Mulungu

MONGA MOMWE YASIMBIDWIRA NDI JOSHUA THONGOANA

Kalelo mu 1942, ndinali wosokonezeka kwambiri. Ndinali kuphunzira mabukhu ofalitsidwa ndi a Seventh-Day Adventist ndi mabukhu ofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Mofanana ndi Aisrayeli akale, ndinali ‘wokaikakaika pamalingaliro aŵiri.’​—1 Mafumu 18:21.

A Seventh-Day Adventist anali kunditumizira nkhani zosindikizidwa zotchedwa “Mawu a Ulosi.” Ndinasangalala kuyankha mafunso awo, ndipo analonjeza kundipatsa satifiketi yokongola ngati ndinapambana mayeso anga onse. Koma ndinawona kuti ponse paŵiri “Mawu a Ulosi” ndi mabukhu a Watch Tower Society anatumizidwa kuchokera ku South Africa mzinda wa Cape Town. Ndinadabwa kuti: ‘Kodi magulu ameneŵa amadziŵana? Kodi ziphunzitso zawo ndizogwirizana? Ngati ayi, wolondola ndani?

Kuthetsa nkhaniyi, ndinatumiza makalata ofanana ku liri lonse la maguluwa. Mwachitsanzo, ndinalembera Watch Tower Society kuti: “Kodi mumadziŵa anthu a gulu la “Mawu a Ulosi,” ndipo ngati mutero, kodi muti bwanji za ziphunzitso zawo?” M’kupita kwanthaŵi, ndinalandira mayankho kuchokera kumagulu onse aŵiri. Kalata yochokera ku Watch Tower Society inanena kuti anadziŵa gulu la “Mawu a Ulosi” koma anafotokoza kuti ziphunzitso zake, monga Utatu ndi kubweranso kwa Kristu padziko lapansi m’thupi, zinali zosagwirizana ndi malemba. Kalata yawo inaphatikizapo malemba otsutsa ziphunzitso zimenezi.​—Yohane 14:19, 28.

Yankho lochokera ku “Mawu a Ulosi” linangonena kuti anadziŵa, anthu a Watch Tower,” koma sanavomerezane ndi ziphunzitso zawo. Panalibe zifukwa zimene zinaperekedwa. Chotero ndinasanka kuyanja Watch Tower Society, limene liri gulu lalamulo logwiritsidwa ntchito ndi Mboni za Yehova. Lerolino, pambuyo pa zaka 50 zakuyanjana ndi Mboni, ndiri wachimwemwe chotani nanga kuti ndinapanga chosankha cholungama!

Chiyambi Chachipembedzo

Ndinabadwa mu 1912 m’chigawo chakumidzi chotchedwa Makanye, kummaŵa kwa tawuni ya m’South Africa ya Pietersburg. Panthaŵiyo Makanye anali mu ulamuliro wa chipembedzo wa Tchalitchi cha Anglican, chotero ndinafikira kukhala chiŵalo cha tchalitchi chimenecho. Pamene ndinali ndi zaka khumi zakubadwa, banja lathu linasamukira kuchigawo china kumene Tchalitchi cha Lutheran Berlin Mission chinali chofunga, ndipo makolo anga anagwirizana ndi tchalitchi chimenecho. Mwamsanga ndinayeneretsedwa kufika pa serevesi ya Mgonero ndi kudyako mkate ndi kupsontha vinyo, koma sikunakhutiritse njala yanga yauzimu.

Nditatha zaka zisanu ndi zitatu zakupita kusukulu, ndinatumizidwa ndi atate ku Kilnerton Training Institution, ndipo mu 1935, ndinalandira Satifiketi Yauphunzitsi ya kosi ya zaka zitatu. Mmodzi wa aphunzitsi amene ndinagwira naye ntchito anali msungwana wachichepere, Caroline. Tinakwatirana, ndipo pambuyo pake Caroline anabala mwana wamkazi amene tinatcha Damaris. Zaka zoŵerengeka pambuyo pake, ndinafikira kukhala hedimasitala pa Sukulu ya Sehlale pamudzi wa Mamatsha. Popeza kuti sukuluyo inali ya Dutch Reformed Church, tinagwirizana ndi tchalitchi chimenecho, tikumafika pa mapemphero ake mokhazikika. Tinachita ichi chifukwa chakuti chinali chizolowezi chofala, koma sichinadzetse chikhutiro kwa ine.

Posinthira

Sande lina mu 1942, tinali kuyeseza nyimbo patchalitchi pamene mnyamata wina mzungu anabwera pakhomo ndi mabukhu atatu ofalitsidwa ndi Watch Tower Society​—Creation, Vindication, ndi Preparation. Ndinaganiza kuti mabukhuwo akawonekera bwino pashelufu ya laibulale yanga, chotero ndinawawombola ndi mashilini atatu. Pambuyo pake ndinamva kuti mwamunayo, Tienie Bezuidenhout, anali mmodzi wa Mboni za Yehova, mmodzi yekha m’chigawocho. Paulendo wotsatira wa Tienie, anabweretsa granifoni naseŵerapo nkhani zina zokambidwa ndi Judge Rutherford. Ndinasangalala kwambiri ndiyakuti “Msampha ndi Malonda,” koma Caroline ndi chemwali wanga wachichepereyo Priscilla, amene anali kukhala nafe, sanatero. Paulendo wachitatu wa Tienie, anandipatsa granifoni kotero kuti ndikaseŵerere marekodewo kwa mabwenzi.

Tsiku lina ndinaunguzaunguza masamba abukhu la Creation ndipo ndinafika pamutu wakuti “Kodi Akufa Ali Kuti?” Ndinayamba kuŵerenga ndikumayembekezera kumva zazisangalalo zimene anthu akufa anali nazo kumwamba. Koma mosiyana ndi ziyembekezo zanga, bukhulo linafotokoza kuti akufa ali m’manda mwawo ndipo sakudziŵa chirichonse. Mavesi ochokera m’Baibulo, monga ngati Mlaliki 9:5, 10, anagwidwa mawu kuchirikiza mfundoyo. Mutu wina unali wakuti “Kuukitsa Akufa,” ndipo Yohane 5:28, 29 anasonyezedwa monga umboni wakuti akufa sadziŵa kanthu ndipo akuyembekezera chiukiriro. Zimenezi zinali zomveka bwino. Zinali zokhutiritsa.

Panali panthaŵi imeneyo, mu 1942, pamene ndinadula kuyanjana kwanga ndi “Mawu a Ulosi” ndipo ndinayamba kuuza ena zinthu zimene ndinaziphunzira m’mabukhu a Watch Tower Society. Mmodzi wa oyamba kulabadira anali bwenzi lina, Judah Letsoalo, amene anali mmodzi wa anzanga akusukulu ku Kilnerton Training Institution.

Judah ndi ine tinapalasa njinga makilomita 51 kukafika pamsonkhano wa Mboni za Anthu Akuda m’Pietersburg. Pambuyo pake, mabwenzi aku Pietersburg anadza kaŵirikaŵiri kuchokera kutaliko ku Mamatsha kudzandithandiza kulalikira uthenga wa Ufumu kwa anansi anga. Potsirizira pake, pamsonkhano wina m’Pietersburg, mu December 1944, ndinabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova.

Banja Langa ndi Ena Alabadira

Caroline, Priscilla, ndi mwana wanga wamkazi Damaris, anapitirizabe kupita ku Tchalitchi cha Dutch Reformed. Ndiyeno tsoka linakantha. Caroline anabala mwana wathu wachiŵiri​—wowonekera kukhala khanda lamphongo lathanzi labwino nitilitcha Samuel. Koma mwadzidzidzi anadwala namwalira. Mabwenzi a Caroline akutchalitchi sanapereke chitonthozo, akumanena kuti Mulungu anafuna mwana wathu wamwamunayo kukakhala naye kumwamba. Mothedwa nzeru, Caroline anapitirizabe kufunsa: “Kodi nchifukwa ninji Mulungu anatilanda mwana wathu?”

Pamene mawu onena za tsoka limene linatigwera anafika kwa Mboni m’Pietersburg, iwo anafika natipatsa chitonthozo chowona mtima chochekera m’Mawu a Mulungu. Pambuyo pake, Caroline anadzati: “Zimene Baibulo linanena ponena za chochititsa imfa, ponena za mkhalidwe wa akufa, ndi ponena za chiyembekezo chachiukiriro zinali zomvekera bwino, ndipo ndinatonthozedwa kwambiri. Ndinafuna kukhala m’dziko latsopano ndi kulandiranso mwana wanga wamwamunayo kuchokera kumanda.”

Caroline anasiya kupita kutchalitchi, ndipo mu 1946 iye, Priscilla, ndi Judah anabatizidwa. Mwamsanga pambuyo pa ubatizo wake, Judah anachoka kukatsegula ntchito yolalikira m’chigawo chakumidzi chotchedwa Mamahlola, ndipo kufikira lerolino iye akutumikira monga ministala mpainiya wokhazikika.

Pamene Judah anachoka, ndinatsala ndine ndekha mwamuna wosamalira mpingo wathu, umene unatchedwa Boyne. Pamenepo Gracely Mahlatji anasamukira m’gawo lathu, ndipo potsirizira anakwatira Priscilla. Mlungu uliwonse, Gracely ndi ine tinali kusinthana kukamba nkhani yapoyera m’Chisepedi, chinenero cha anthu Akuda amomwemo. Kuchititsa mabukhu ofotokoza Baibulo kukhala opezeka kwa anthu, Sosaite inandipempha kumasulira mabukhu m’Chisepedi. Kunandibweretsera chikhutiro chachikulu kuwona anthu akupindula ndi mabukhu amenewa.

Kuwonjezera chipambano cha mkupiti wamisonkhano yathu yapoyera, tinagula makina a granifoni okhala ndi chokuzira mawu chachikulu kuchitira kuseŵererapo nkhani za Baibulo m’gawo lathu lonselo. Tinabwereka gareta lokokedwa ndi abulu lonyamulira chiŵiya cholemera chimenechi kuchokera kumalo ndi malo. Monga chotulukapo, anansi athu anatipatsa dzina lakuti “Anthu a Tchalitchi cha Abulu.”

Panthaŵiyo mpingo wathu waung’ono unapitirizabe kuwonjezereka. M’kupita kwanthaŵi, achemwali anga akulu aŵiri ndi amuna awo anafikira kukhala Mboni ndipo iwo onse anapitirizabe kukhala okhulupirika kufikira imfa yawo. Ndiponso, ambiri ochokera kumpingo wa Boyne (umene tsopano ukutchedwa Mphogodiba) anatenga ntchito yaulaliki wanthaŵi yonse, ndipo ambiri adakali muutumikiwo. Lerolino, muli mipingo iŵiri m’chigawo chachikulu chimenechi cha midzi yotalikirana, ndipo chiŵerengero cha ofalitsa onse pamodzi oposa 70 ali okangalika m’ntchito yolalikira.

Ntchito Yosankhidwa Yatsopano

Mu 1949, ndinasiya kuphunzitsa sukulu ndipo ndinakhala minisitala mpainiya wokhazikika. Gawo langa loyamba linali lakupita kwa anthu akuda ogwira ntchito pamafamu amene anali kukhala pamafamu a azungu kuchigawo cha Vaalwater m’Transvaal. Eni mafamu ena anachirikiza lamulo limene linali litavomerezedwa kumene lakuchita tsankhu ndipo anali otsimikiza kuti anthu akuda ayenera kuzindikira mkhalidwe wawo wakukhala akapolo a azungu ndipo ayenera kutumikira abwana awo azungu. Chotero pamene ndinalalikira kwa antchito akuda, azungu ena anandiwona molakwa kuti ndinali mlaliki wotsutsa kugonjera. Ena anandiimba ngakhale mlandu wa kukhala Wakomyunizimu ndipo anawopseza kuti akandiwombera mfuti.

Ndinauza mkhalidwewo ofesi yanthambi ya Watch Tower Society, ndipo mwamsanga ndinasamutsidwira kugawo lina chakumidzi lotchedwa Duiwelskloof. Pafupifupi nthaŵi imeneyi mkazi wanga nayenso anali atasiya ntchito yophunzitsa nagwirizana nane muutumiki waupainiya. Madzulo ena mu 1950, tinafika kuchokera ku utumiki wakumunda kukapeza emvulopu yaikulu yochokera ku Sosaite. Mosayembekezera, inali ndi mawu ondiitanira kukaphunzitsidwa monga woyang’anira woyendayenda. Kwa zaka zitatu tinachezetsa mipingo m’South Africa, ndiyeno mu 1953 tinagaŵiridwa ku Lesotho, dziko lokwetezedwa chapakati pa South Africa.

Uministala m’Lesotho ndi Botswana

Pamene tinayamba kutumikira m’Lesotho, panali mphekesera zambiri zakuti kaŵirikaŵiri alendo anali chandamale chakuphedwa mwambanda m’miyambo. Mkazi wanga ndi ine tinali ankhaŵa, koma kukonda abale athu Achisotho ndi kuchereza kwawo kunatithandiza kuiŵala kuchita mantha kotero.

Kutumikira mipingo ya Mapiri a Maluti a ku Lesotho, ndinali kuyenda pandege, ndikumasiya mkazi wanga m’malo achidikha kumene iye anachita utumiki waupainiya kufikira nditabwerera. Abalewo anali kundiperekeza mokoma mtima kuchokera kumpingo kumka kumpingo kuthandiza kuti ndisasochere m’mapiri.

Nthaŵi ina ndinauzidwa kuti kufika mpingo wotsatira, tikafunikira kuwoloka Mtsinje wa Orange titakwera kavalo. Ndinatsimikiziridwa kuti kavalo wanga sanali wachiwawa koma ndinachenjezedwa kuti pamene madzi afikira kukhala amphamvu, kaŵirikaŵiri akavalo amayesa kutaya katundu wawo. Ndinada nkhaŵa chifukwa chakuti sindinali wodziŵa bwino kukwera kavalo ndiponso sindinali wodziŵa bwino kusambira. Mwamsanga tinali mu mtsinjewo, ndipo madzi anamiza kavalo kufikira m’mimba. Ndinachita mantha kwambiri kotero kuti ndinataya zingwe zowongolera kavalo ndipo ndinanonomera kuubweya wa pakhosi pakavalo. Ndimpumulo wotani nanga pamene tinafika mosungika bwino tsidya linalo!

Pausikuwo sindinathe konse kugona chifukwa chakuti thupi langa linali kupweteka kwambiri chifukwa cha kukwera pakavalo. Koma kuvutika konseko kunali koyenerera chifukwa chakuti abalewo anasonyeza chiyamikiro chachikulu chakuchezetsa kwathuko. Pamene ndinayamba ntchito yadera m’Lesotho, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa chinali 113. Lerolino, chiŵerengerocho chawonjezereka kukhala 1,649.

Mu 1956, gawo lathu lolalikira linasinthidwa kukhala Bechuanaland Protectorate, limene tsopano liri Botswana. Botswana liri dziko lokulira kwambiri, ndipo maulendo otalikirapo anali ofunikira kupangidwa kukafikira ofalitsa onse. Tinayenda kaya patireni kapena m’lole lopanda denga. Munalibe mipando, chotero tinafunikira kukhala pansi ndi katundu wathu. Ife kaŵirikaŵiri tinali kutha ulendo wathuwo tili odzala fumbi lambirimbiri ndi otopa. Nthaŵi zonse abale athu Achikristu anatilandira, ndipo nkhope zawo zachimwemwe zinatitsitsimula.

Panthaŵiyo, mabukhu a Sosaite anali oletsedwa m’Botswana, chotero kulalikira kwathu kunyumba ndi nyumba kunachitidwa mochenjera, popanda kugwiritsira ntchito mabukhu a Sosaite. Panthaŵi ina, tinagwidwa tikulalikira pafupi ndi mudzi wa Maphashalala ndipo tinamangidwa. M’kudzitetezera kwathu, tinaŵerenga m’Baibulo, tikumatchula ntchito yathu monga momwe yalembedwera pa Mateyu 28:19, 20. Ngakhale kuti ena a akonsolo anachita chidwi, mfumuyo inalamula kuti Mboni zamomwemo zikwapulidwe zikoti. Pamenepo, motidabwitsa, mtsogoleri wachipembedzo anachonderera kwa mfumu kuti atikomere mtima ndi kutikhululukira. Mfumuyo inalola, ndipo tinamasulidwa.

Mosasamala kanthu za chizunzo ndi chiletso pamabukhu athu, ntchito ya Ufumu inapitirizabe kupita patsogolo. Pamene ndinafika m’Botswana, munali chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 154. Zaka zitatu pambuyo pake pamene chiletso chinachotsedwa, chiŵerengerocho chinali chitawonjezeka kukhala 192. Lerolino, muli Mboni za Yehova 723 zolalikira m’dziko imenelo.

Kuphunzitsa ndi Kumasulira

M’kupita kwa nthaŵi, ndinagwiritsiridwa ntchito monga mlangizi m’Sukulu Yautumiki Waufumu ya akulu Achikristu. Pambuyo pake ndinali ndimwaŵi wakukhala mlangizi m’Sukulu Yautumiki Waupainiya. Panthaŵi ndi nthaŵi mkazi wanga ndi ine tinatumikira panthambi ya South Africa. Panthaŵi zotero ndinali kuthandiza m’kumasulira, ndipo Caroline anagwira ntchito m’kitchini.

Tsiku lina mu 1969, woyang’anira nthambi, Frans Muller, anandifika nanena kuti: “Mbale Thongoana, ndifuna kukuonani inu ndi mkazi wanu mu ofesi mwanga.” Kumeneko iye anafotokoza kuti tinali pakati pa osankhidwa kukhala nthumwi zaku Msonkhano wa “Mtendere pa Dziko Lapansi” wa 1969 ku London. Tinasangalala ndi kuchereza kwachikondi kwa abale athu ku Mangalande ndi ku Scotland, ndipo kunawonjezeradi chiyamikiro chathu cha ubale wapadziko lonse.

Kwa zaka makumi anayi zapitazo, Caroline wakhala tsamwali wokhulupirika m’ntchito yathu yodzisankhira monga alaliki anthaŵi yonse. Tagaŵana zisangalalo zambiri ndi zisoni. Ngakhale kuti tinataikiridwa aŵiri a ana athu muimfa, mwana wathu wamkazi, Damaris, anakula nakhala Mboni yolimba ndipo nayenso anakhala ndi phande m’ntchito yomasulira panthambi ya ku South Africa.

Thanzi lathu silikutilolanso kukhala ndi phande m’ntchito yoyendayenda, chotero kwa zaka zoŵerengeka zapitazo, takhala tikuchita upainiya wapadera pa mpingo ku Seshego, mudzi wa anthu Akuda pafupi ndi Pietersburg. Ndikutumikira monga woyang’anira wotsogoza. Baibulo limanena kuti ‘pankhope panu [Yehova] pali chimwemwe chokwanira,’ ndipo ndapezadi chisangalalo ndi chikhutiro kutumikira Mulungu kummwera kwa Afirika​—Salmo 16:11.

[Chithunzi patsamba 26]

Kuchitira umboni m’mudzi wa Seshego, South Africa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena