“Moni! Kodi Mudziŵa Kuti Mulungu Dzina Lake Ndani?”
OFESI yanthambi ya Mboni za Yehova m’Brazil, inalandira kalata yosatirayi kuchokera kwa mmodzi wa alongo amapasa wazaka 12 mumzinda wa Fortaleza:
“Kalelo mu 1990 pamene tinali m’giredi lachisanu, sukulu yathu inalinganiza chisonyezero cha sayansi, kujambula, ndi cha miyambo. Tinafotokoza kwa mphunzitsi kuti tinafuna kuti zosonyeza zathu zikakhale zosiyana ndi zimene ophunzira ena anali kulinganiza kukonza. Popeza kuti kalelo anatimva tikulankhula za Yehova ndi Baibulo, iye anapereka lingaliro lakuti ‘Pamenepo mungalembe za Mulungu wanu!’
“Tinawona umenewo kukhala mpata wakupereka umboni ndipo tinasankha kukhala ndi chisonyezero cha mabukhu ofotokoza Baibulo amene anasumika pa dzina la Yehova. Tinalinganiza zilembo zazikulu za mawu a Salmo 83:18 ndi kuwamamatiza pachithunzithunzi chosonyeza Baibulo lotsegulidwa. Ndiponso, tinaika pagome matembenuzidwe osiyanasiyana a Baibulo okhala ndi dzina la Yehova. Pagome limodzimodzilo, tinayalapo mabukhu ofotokoza Baibulo osiyanasiyana. Kumapeto kwa gome, tinaikako VCR ndi TV kusonyeza alendo chitsanzo chimodzi kumene dzina la Yehova linagwiritsiridwa ntchito m’kanema wotchuka kwambiri.
“Mkati mwachisonyezerocho, pamene munthu anadza kugome lathu, tinkati: ‘Moni! Kodi mumadziŵa kuti Mulungu dzina lake ndani?’ Pambuyo pakupereka mpata kwa wochezayo kuti ayankhe, tinkapitiriza kuti: ‘Tawonani pano! Matembenuzidwe angapo a Baibulo amasonyeza kuti dzina lake ndilo Yehova’ tikusonyeza dzinalo m’ma Baibulo osiyanasiyana, monga la João Ferreira de Almeida, The Jerusalem Bible, ndi New World Translation. Pamenepo tinaseŵera chisonyezero chimene munthu womveka wam’kanema amatchula Yehova kukhala dzina la Mulungu. Pamene anthu anasonyeza chikondwerero, tinaŵapatsa magazini kapena trakiti kuti apeze chidziŵitso chowonjezereka.
“Mmodzi wa achichepere amene anadza kugome lathu anapempha bukhu la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Mphunzitsi wathu anapenda bukhulo Kupangitsa Moyo Wanu Wabanja Kukhala Wachimwemwe ndipo anadzuma kuti: ‘Mayine! Ndibukhu lokondweretsa chotani nanga!’ Pofika mapeto achisonyezerocho, tinali titagaŵira mabukhu 7, matrakiti 18, ndi magazini 67. Tinapatsidwa mphotho yachitatu pachisonyezerocho. Koma koposa zonse, tinali achimwemwe kwambiri chifukwa chamwaŵi wakudziŵikitsa dzina la Mulungu, Yehova.”