Ulemerero wa Imvi
KUKAKHALA kochititsa chidwi chotani nanga kulankhula ndi amuna ndi akazi okhulupirika akale! Tangolingalirani kulankhula ndi amuna onga Nowa, Abrahamu, Mose, ndi Yohane Mbatizi, kuphatikizapo akazi onga Sara, Rahabi, Rute, ndi Debora! Kodi inu simukachita chidwi kumva akusimba zochitika zapadera zimene anawona ndi maso awo m’nthaŵi zakalekale?
Ngakhale lerolino, kodi simukanasangalala kumva okalamba okhulupirika akugawana nanu zokumana nazo zokhudza mmene iwo ndi ena anasungira umphumphu wawo kwa Mulungu pa ziyeso, kuphatikizapo kuletsedwa mwalamulo, kumenyedwa, ndi kuikidwa m’ndende chifukwa cha chilungamo? Ndithudi mukatero! Kukonda kwathu Mulungu ndi kuwalemekeza kwathu zikawonjezereka pamene iwo akutisimbira malingaliro awo ndipo makamaka chiyamikiro chawo chochokera pansi pa mtima cha chisamaliro chachikondi cha Yehova.
Pakati pa anthu a Mulungu, amuna ndi akazi okalamba okhulupirika nthaŵi zonse alemekezedwa chifukwa cha zokumana nazo zawo, chidziŵitso chawo, ndi nzeru zawo. Kunena zowona, lamulo lotsatirali linaphatikizidwa m’Chilamulo choperekedwa ndi Mulungu kwa Aisrayeli: ‘Pali a imvi udziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuwope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.’ (Levitiko 19:32) Liwu Lachihebri lamsinkhu kapena kukalamba limachokera ku liwu la maziko lotanthauza “kumera imvi” ndiponso latembenuzidwa kukhala “imvi.” Chotero Aisrayeli anayembekezeredwa kugwada monga chizindikiro cha ulemu kwa munthu wokalamba, akumatero m’mantha olemekeza Mulungu.
Kodi kaimidwe kamaganizo kopereka ulemu kameneko kalipo lerolino? Mwachitsanzo, kodi anyamata mwaulemu amatsegulira zitseko okalamba? Kodi achichepere kapena anyamata kaŵirikaŵiri amapereka malo awo m’chikepe chodzala anthu kwa munthu wokalamba? Kapena kodi kaŵirikaŵiri achicheperewo amachoka pa mipando yawo kuti achikulire akhale m’basi kapena m’sitima yodzala anthu? Kulephera kuchita zinthu zotero, kwawoneka ngakhale pakati pa Akristu.
Komabe, kuti akondweretse Yehova Mulungu, Akristu ayenera kuchita mogwirizana ndi lingaliro lake ndi kupeŵa kuganiza, kulankhula, ndi zochita za anthu ‘odzikonda, osamvera akuwabala, osayamika, ndi osakonda ubwino.’ (2 Timoteo 3:1-5) Pamenepa, kodi Mawu a Mulungu amanenanji za unansi wa achichepere ndi a imvi?
Mphamvu Yaunyamata
Baibulo limavomereza nyonga yaunyamata ndi mapindu ake, ndi kumati: “Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu yawo.” (Miyambo 20:29, NW) Mu Israyeli wakale mphamvu ya Alevi achichepere inagwiritsidwa ntchito pa kachisi, kaŵirikaŵiri pa ntchito zawo zambiri zolemerazo. Lerolino, ntchito yambiri m’mafakitale, m’nyumba za Betele, ndi m’ntchito zomanga za Watch Tower Society zimachitidwa ndi anyamata ndi asungwana amene apereka nyonga yawo ndi maluso kupititsa patsogolo zabwino za Ufumu. (Mateyu 6:33) Chotero iwo amasangalala ndi mwaŵi wabwino kwambiri mu utumiki wa Mulungu.
Mwambo wogwidwa mawu kumene umamaliza ndi mawu akuti, ndipo “ulemerero wa nkhalamba ndiwo imvi zawo.” Pamene nyonga yaunyamata iphatikizidwa ndi chidziŵitso ndi nzeru zochokera m’zaka zambiri, mgwirizano wamphamvu kwambiri umapangidwa.
Mwachitsanzo: Mnyamata amene akuphunzira umisiri wopala matabwa amene wapemphedwa kukhokhomera matabwa akufuna kukwaniritsa gawo lake mogwiritsira ntchito nyonga yaunyamata. Mmisiri wopala matabwa wachikulirepo, wachidziŵitso chowonjezereka akuwona kuti mosasamala kanthu za nyonga yake wothandiza wachichepereyo akukhoma msomali nthaŵi zingapo usanaloŵe. Mmisiri wachikulireyo akuvomereza kuti mnyamata agwire nyundo chakumapeto kwa mpini, mmalo mwakugwirira pafupi ndi mutu wake wachitsulowo. Izi zikukhozetsa mnyamatayo kukhoma misomaliyo mwamphamvu kwambiri, m’nthaŵi yochepa ndipo mosagwiritsira ntchito nyonga yambiri.
Mofananamo, msungwana wachichepere, wanyonga angaphunzire zinthu zitawonongeka kuti nsalu zina zimawonongeka ngati sizichapidwa mogwirizana ndi malangizo. Komabe, mkazi wachidziŵitso, amadziŵa phindu lakusankha zovala ndi kuzichapa molekana. Iye amazindikiranso kuti angathe kupeŵa kusita mwakupinda zovala pamene akuziyanula kapena kuzichotsa m’makina oumikira.
Kuphunzira kwa anthu achidziŵitso kungapangitse moyo kukhala wosavutirapo. Komabe, nthaŵi imafika pamene ngakhale munthu wachidziŵitso chokulirapo sangathe kuchita ntchito imene iye anaichita mosavutirapo zaka zochepekera zapitazo. Wolemba wina moyenerera anati: “Kukanakhala ubwino chotani nanga ngati achichepere anali ndi chidziŵitso ndipo nkhalamba zinali ndi nyonga.” Koma nkwabwino chotani nanga pamene okalamba amazindikira nyonga ya achicheperepo ndipo moleza mtima kugaŵana nawo chidziŵitso chimene apeza m’zaka zambirizo—ndipo achicheperewo kuvomereza modzichepetsa malingalirowo! Mwanjirayi, misinkhu iŵiri yonseyo ingapindulitsane.
Kupeza Ulemerero
Ukalamba wokha suli wokwanira. ‘Akulu sindiwo eni nzeru, Ndi okalamba sindiwo ozindikira chiŵeruzo,’ anatero mnyamatayo Elihu. (Yobu 32:9; Mlaliki 4:13) Kuti munthu wokalamba ayamikiridwedi chifukwa cha imvi, iye akafunikira kukhala atachita zowonjezereka ndi moyo wake koposa kuthera nthaŵi yake ali manja lende kuwonerera wailesi yakanema, kupita ku maseŵera, kapena kusanguluka basi. Ngakhale m’zaka zaukalamba, okalambawo afunikira kupitirizabe kuphunzira.
Anthu ena amadzitamandira za kuchita zinthu mwanjira yawo, kapena iwo amati: “Zochitika m’moyo ndizo mphunzitsi wabwino koposa.” Komabe, Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Kuti wanzeru amve, nawonjezere kuphunzira; ndikuti wozindikira afikire kuuphungu.” (Miyambo 1:5; yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:11.) Sinthaŵi zonse pamene zochitika m’moyo ziri mphunzitsi wabwino koposa, pakuti tingathe kuphunzira mwa zophophonya za ena popanda kufunikira kupanga zophophonya zofananazo ife eni. Ndiponso, Mkristu akakonda kukumbukira kuti ‘imvi ndizo kolona wakukongola pamene ipezedwa mwa njira yachilungamo.’ (Miyambo 16:31) Moyo wothera mu utumiki wokhulupirika kwa Yehova ngwokongola mwalingaliro lake ndipo ngwoyenerera ulemu wa ena monga chitsanzo chabwino. Ndithudi, kuphunzira za Mulungu ndi kupeza chidziŵitso “mwanjira ya chilungamo” kungayambike kuchiyambiyambi m’moyo ndipo kuyenera kukhala mchitidwe wosatha.—Aroma 11:33, 34.
Izi zingathe kuyerekezeredwa ndi chokumana nacho chophatikizapo mnyamata wa zaka zisanu ndi ziŵiri wa ku Sweden. Iye anapempha woyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki mu mpingo kuti alembedwe m’sukulu. Woyang’anirayo anafunsa kuti, “Chifukwa ninji?” Pamenepo, mnyamatayo anayankha kuti: “Munthuwe sufunikira kukhala moyo wako uli manja lende!” (Mlaliki 12:1) Nchitsanzo chotsimikizirika chotani nanga kwa achichepere ndi okalamba omwe!
Kulemekeza a Imvi
Chikhoterero chovutitsa maganizo m’chitaganya chamakono ndicho kuika chigogomezero chachikulu pa phindu la thanzi lakuthupi ndi maluso akulimbitsa thupi ndi kunyalanyalaza nkhalamba. Kodi kaimidwe kamaganizo ka Mkristu kayenera kukhala kotani kulinga kwa a imvi mumpingo?
Mmalo mwakunyalanyaza Akristu okalamba, tiyenera kuwalingalira ndi kuthera nthaŵi tiri nawo. Mwachitsanzo, pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu ya Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu, kodi mumapanga kuyesayesa kwakulonjera nkhalamba? Ndithudi iwo amayamikira kulonjeredwa ndi achichepere ndi ena. Ndipo okalambawo amasangalala chotani nanga kufikira pa masonkhano ocheza ndi okhulupirira anzawo amisinkhu yosiyanasiyana! Ngakhale kuti okwatirana achicheperepo angakhale ndi zikondwerero zochulukirapo zofanana ndi okwatirana ena a msinkhu wawo, kukakhala kopindulitsa kuphatikiza okalambawo pa masonkhano achimwemwe otero.—1 Atesalonika 3:12; 5:15.
Nkofunika chotani nanga kukhala okoma mtima polankhula ndi achikulire! Pamene mbale wina wokalamba wa zaka 40 mu utumiki wa Yehova tsiku lina analankhula kwa mkulu wina za mmene wokalambayo akanagwiritsidwira ntchito mumpingo, mwamuna wocheperapoyo anati: “Inu muli nzochepa kwambiri zimene mungachite.” Ndimawu osakoma mtima chotani nanga! Mbale wokalambayo anali ndi nyonga yocheperapo koposa imene kalelo anali nayo, mbali yake mu utumiki wakumunda inacheperapo pang’ono, ndipo mwachiwonekere maudindo ena auyang’aniro anali ovuta kwambiri ku maluso ake anthaŵi ino; komabe, iye anali ndi zambiri zakuzichita. Iye anali ndi chidziŵitso ndi nzeru zokundikidwa zaka zambiri m’njira yachilungamo. Chifukwa chakuti okalamba otero anagwira ntchito zolimba monga alaliki Aufumu, anapirira chizunzo, anasenza maudindo olemera athayo Lachikristu, ndipo anaphunzitsa ena, anthu a Mulungu tsopano akusangalala ndi gulu lamphamvu lochirikizidwa ndi mzimu wake. Chifukwa chake, ife tiyenera kusonyezatu okalamba amenewa ulemu monga aphungu anzeru, abusa achikondi, ndi aphunzitsi ogwira mtima.
Palinso chifukwa china chakusonyezera kulingalira kwamphamvu kumalingaliro opangidwa ndi anthu okalamba. Mwachitsanzo, mbale wachidziŵitso anapereka lingaliro lakuti khomo la Nyumba Yaufumu ina lisaikidwe chakumadzulo kwa nyumbayo. Abale achichepere anali odera nkhaŵa kwambiri ndi kuwonekera kukhala kukongola kwa nyumbayo ndipo sanatsatire lingaliro lake. Komabe, pambuyo pa zaka zingapo, khomolo linafunikira kusinthidwa chifukwa chakuti mphepo yosalekeza ndi mvula zakuzambwe zinaliwononga. Nzeru yothandiza ya zochitika m’moyo inaposa ziganizo zakukonda zokongola. Ngati achicheperepo alemekeza okalamba mwakumvetsera malingaliro awo ndi nzeru yawo yothandiza, zimenezi zingasungitsedi nthaŵi ndi ndalama. Ngakhale ngati lingaliro lamunthu wokalamba silikutsatiridwa, iye angalemekezedwe mwakumuuza kuti linalingaliridwa, zochitika zina zinapangitsa chosankha chosiyana.—Yerekezerani ndi Miyambo 1:8.
Yang’anani Kutsogolo, Osati Kumbuyo
Anthu ena okalamba ali ndi lingaliro ili: “Palibe nthaŵi yabwino yofanana ndi nthaŵi yamakedzana pamene iwe ndi ine tinali achichepere.” Komabe, mmalo mwakusumika maganizo panthaŵi zapita, okalamba otero angalimbikitsidwe kuyang’anira mtsogolo ku tsiku limene iwo adzalandira kaya mphotho yawo yakumwamba kapena kupezanso nyonga yawo muulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Pakali pano, afunikira kuzindikira zopereŵera zawo zaukalamba. Kuzindikira kumeneku ndi lingaliro lamphamvu loseketsa nzofunika pamene mwachiwonekere munthu wokalambayo anyalanyazidwa mwaŵi wa mautumiki.
Mwachitsanzo, mbale wokalamba angakhale atagwiritsidwa ntchito mokhazikika pamaprogramu amsonkhano wachigawo zaka zapitazo. Tsopano pali akulu ambiri oyeneretsedwa ndi amuna ochulukirapo okhala ndi maluso akuphunzitsa oti nkugwiritsira ntchito. Ngakhale kuti ngachichepere pang’ono, ena aakulu amenewa atsimikizira kukhala achangu ndi aluso, ndipo angathe kuphunzitsa bwino ndi kupereka chilimbikitso cha chifundo ndipo ngoyeneretsedwa kulimbikitsa ena. (1 Atesalonika 5:12, 13; 1 Timoteo 5:17) Chotulukapo chake nchakuti, mbale wokalambayo wosawonekera pa programu ya msonkhano angadziwone kukhala wonyalanyazidwa ndipo angakhale wosakondwera kuti mwaŵi wapatsidwa kwa akulu achinyamata. Komabe, lingaliro lotsutsa limenelo lochokera m’kupanda ungwiro kwaumunthu lingagonjetsedwe. M’chenicheni, onse mumpingo angathandize mwakuchititsa okalambawo kudziŵa kuti ngofunika, kuti iwo amakondedwa chifukwa cha kukhulupirika kwawo, ndi kuti malingaliro awo amayamikiridwa.
Ndithudi, munthu wokalamba afunikira kukumbukira kuti olambira anzake ayenera kulemekezedwa monga momwe iye akafunira kulemekezedwa. (Mateyu 7:12; Aroma 12:10) Mmalo mwakukhala ndi lingaliro lakuti anakakamizidwa kutula udindo chifukwa cha ukalamba wawo ndi kukanthidwa ndi lingaliro lotsutsa, okalamba ayenera kukondwera ndi zaka zawo zautumiki wokhulupirika. Ndipo ndithudi, tonsefe tiyenera kukhala oyamikira kuti chifukwa cha dalitso la Yehova, pali chiŵerengero chowonjezereka cha oyang’anira oyeneretsedwa ogaŵana mtolo wa ntchito ndi kusenza mathayo ampingo pamene makamu a “nkhosa zina” adza mu unyinji wawo kugulu Lachikristu.—Yohane 10:16; Yesaya 60:8, 22; 2 Timoteo 2:2.
Chifukwa cha zowawa, kufooka kwa thanzi, kapena mikhalidwe ina, ukalamba nthaŵi zina umakhala wovutitsa. Izi zimafunikiritsa kuzindikira chifundo ndi zochitidwa ndi ziŵalo zina za banja kapena mpingo. Kumafunanso okalambawo kugwira ntchito zolimba kuti asunge lingaliro lotsimikizirika, kuti akhale achichepere mumtima ndi m’maganizo. Pamene mnzake wa m’chipinda wachicheperepo wa chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anali kuchoka pa Betele zaka zingapo zapitazo, wokalambayo anafunsa wochokayo kuti apereke lingaliro la womlowa mmalo wabwino ndipo ananena kuti mbale wokalambayo akakonda mbale wachicheperepo, wokula msinkhu kumthandiza kukhalabe wachichepere ndi wokangalika. Mbale wodzozedwa wokalambayo analibe cholinga chakutula udindo kapena kuchepetsa liŵiro la ntchito, chifukwa chakuti panali ntchito yambiri yakuichita. Nchitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga chakuyang’ana mtsogolo ndi kusunga lingaliro lotsimikizirika!
Mosakaikira, “kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu yawo, ndipo ulemerero wankhalamba ndiwo imvi zawo.” Nkokondweretsa chotani nanga pamene achichepere agwiritsira ntchito nyonga zawo ndipo okalamba agwiritsira ntchito nzeru zawo m’kulondola njira yachilungamo! Akristu okalamba ndi achichepere omwe amapeza chisangalalo chachikulu pamene mogwirizana apititsa patsogolo kulambiridwa kowona kwa Yehova Mulungu, “nkhalamba yakalekale.”—Danieli 7:13.
[Chithunzi patsamba 28]
Akristu a imvi ali nzambiri zakuzipereka kupindulitsa ena