Chiyembekezo—chinjirizo Lofunika m’Dziko Lopanda Chiyembekezo
Mnyamata wa ku Korea anafuna kuthandiza amake kukhutiritsa wophunzira wa pa koleji mmene kuliri kofunika kukhala ndi chiyembekezo cha mtsogolo. Atakumbukira fanizo limene adamva pamsonkhano Wachikristu, anafunsa wophunzirayo ngati akanamthandiza kumasulira mwambi. Msungwanayo anavomera. Iye anati: “Panali mabanja aŵiri. Onse aŵiri anali osauka kwambiri. Kunali kugwa mvula yaikulu, ndipo matsindwi anyumba zonse ziŵiri anali kudontha. Banja lina linachita chisoni kwambiri, ndipo linadandaula kwambiri ndi kudonthako. Koma banja linalo linali lachimwemwe ndi lopanda chisoni pofolera tsindwi lawo. Kodi nchifukwa ninji mabanja aŵiri ameneŵa anali osiyana kwambiri chotero?” Pokhala wachidwi, msungwanayo anayankha kuti sanadziŵe. “Eya,” anatero mnyamatayo, “banja lachiŵirilo linali lachimwemwe chifukwa chakuti linali litangolandira uthenga kuchokera ku boma lamzinda kuti likapatsidwa nyumba yatsopano. Chotero iwo anali ndi chiyembekezo. Nchifukwa chake anali osiyana!”
MWAMBI wamnyamatayu umasonyeza chowonadi chosavuta ichi: Kaŵirikaŵiri chiyembekezo chimasintha njira imene timawonera moyo, mosasamala kanthu za mikhalidwe yathu. Mofanana ndi mabanja aŵiri amene iye anafotokoza, ambiri a ife timafunikira kupirira mavuto m’moyo—mavuto athanzi, nkhaŵa za chuma, zipsinjo za banja, upandu, ndi ziyeso ndi nkhanza zina zosaŵerengeka. Kaŵirikaŵiri, mavuto otero ali osapeŵeka. Chotero tingagwiritsidwe mwala, kusukidwa—kunena mwachidule, kusoŵa chochita. Zoipirapo, tingakhale titaphunzitsidwa ku tchalitchi kuti mtsogolo mwa ochimwa ambiri muli mdima, kuti mungaphatikizepo kulangidwa kosatha.
Kwanenedwa kuti kupsinjika maganizo kumachititsidwa ndi kusoŵa chochita ndi kupanda chiyembekezo. Koma tingathedi kuchotsa chimodzi cha nakatande ameneyu; aliyense wa ife sayenera kukhala wopanda chiyembekezo. Ndipo chiyembekezo chabe chingakhale chida chabwino koposa chothetsera nakatande winayo, kukhala wosoŵa chochita. Ngati tili ndi chiyembekezo, tingapirire mavuto a moyo modekha ndi mokhutira mmalo mwa kuyesa kulimbana nawo ndi chisoni chachikulu. Inde, chiyembekezo chili chinjirizo lofunika.
Kodi kunena kumeneku kumakupatsani chikaikiro? Kodi chiyembekezo chilidi champhamvu kwambiri moti chimasintha zinthu kwambiri chotero? Ndipo kodi aliyense wa ife angakhale ndi chiyembekezo chodalirika?
Chofanana ndi Chisoti
Madokotala ayamba kuzindikira mphamvu yaikulu ya chiyembekezo. Yemwe anapulumuka Chipululutso cha Anazi, katswiri wakupsinjika maganizo Dr. Shlomo Breznitz, ananena kuti m’nthaŵi zamavuto ochuluka m’moyo, “chipsinjo chimachititsidwa ndi njira imene timatengera kukula kwa mavutowo, osati mavuto enieniwo. Chiyembekezo chimachepetsa kukula kwa chitsenderezo chawo.” Nkhani ina mu The Journal of the American Medical Association inanena motsimikiza kuti chiyembekezo ndicho “mankhwala amphamvu.” Magazini ya American Health inasimba kuti: “Pali zitsanzo zambiri za odwala, makamaka odwala kansa, amene mkhalidwe wawo umaipa mwadzidzidzi pamene kanthu kena kamawataitsa chiyembekezo—kapena amene mwadzidzidzi amawongokera pamene apeza kanthu kena katsopano kokayembekezera m’moyo.”—Yerekezerani ndi Miyambo 17:22.
Ophunzira Baibulo azindikira kwa nthaŵi yaitali kufunika kwa chiyembekezo. Pa 1 Atesalonika 5:8, mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Tisaledzere, titavala . . . chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.” Kodi ndimotani mmene “chiyembekezo cha chipulumutso” chiliri ngati chisoti?
Talingalirani zimene chisoti chimachita. M’nthaŵi za m’Baibulo msilikali anali kuvala chisoti cha mkuwa kapena cha chitsulo, cholumikizidwa ku kachisoti kaubweya, kathonje, kapena kachikopa. Chisoti chimenechi chinatetezera mutu wake ku mivi youluka, zibonga zoponya, ndi malupanga akuthwa ankhondo. Mosakaikira, asilikali oŵerengeka anazengereza kuvala chisoti ngati anali nacho. Komabe, kuvala chisoti sikunatanthauze kuti msilikali sanali wokhoza kuphedwa kapena kuti sanamve chilichonse pamene anakanthidwa pamutu pake; mmalomwake, chisoti chinangochititsa kuti kukantha kochulukako kusamvulaze ndi kumupha.
Monga momwe chisoti chimatetezerera mutu, chiyembekezo chimatetezeranso maganizo. Chiyembekezo sichingatikhozetse kunyalanyaza vuto kapena chobwevutsa chilichonse monga ngati kuti sizinali kanthu. Koma chiyembekezo chimafeŵetsa mavuto otero ndi kuthandizira kuti iwo asawononge thanzi lathu lamaganizo, la mtima, kapena lauzimu.
Mosakaikira mwamuna wokhulupirika Abrahamu anavala chisoti chophiphiritsira chimenechi. Yehova anampempha kupereka nsembe mwana wake wokondedwa, Isake. (Genesis 22:1, 2) Kukanakhala kosavuta chotani nanga kwa Abrahamu kupsinjika mtima, mkhalidwe umene ukanamchititsadi kusamvera Mulungu. Kodi chinatetezera maganizo ake ku kupsinjika mtima kotero nchiyani? Chiyembekezo chinachita mbali yofunika kwambiri. Malinga ndi kunena kwa Ahebri 11:19, “poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa [Isake], ngakhale kwa akufa.” Mofananamo, chiyembekezo cha Yobu m’chiukiriro chinathandizira kutetezera maganizo ake kumkwiyo, umene ukanamchititsa kutukwana Mulungu. (Yobu 2:9, 10; 14:13-15) Yesu Kristu, atayang’anizana ndi imfa yoŵaŵa, anapeza nyonga ndi chitonthozo m’chiyembekezo chake chosangalatsa cha mtsogolo. (Ahebri 12:2) Chidaliro chakuti Mulungu sadzalakwa konse, sadzalephera konse kukwaniritsa mawu ake, ndicho maziko a chiyembekezo chowona.—Ahebri 11:1.
Maziko a Chiyembekezo Chenicheni
Mofanana ndi chikhulupiriro, chiyembekezo chenicheni nchozikidwa pamaumboni, zenizeni, chowonadi. Zimenezi zingadabwitse ena. Monga momwe wolemba nkhani wina akunenera, “anthu ambiri amawoneka kukhala akuganiza kuti chiyembekezo chili chabe mtundu wachabechabe wakukana zenizeni.” Komabe, chiyembekezo chowona sichili zongoyerekezera, chikhulupiriro chopanda pake chakuti tidzapeza zilizonse zimene tifuna kapena kuti ngakhale mavuto athu aang’ono alionse adzathetsedwa. Zenizeni m’moyo zimathetsa maloto onyenga otero.—Mlaliki 9:11.
Chiyembekezo chenicheni chili chosiyana. Chimazikidwa pachidziŵitso, osati zikhumbo. Talingalirani banja lachiŵiri m’mwambi wotchulidwa poyamba. Kodi nchiyembekezo chotani chimene iwo akanakhala nacho ngati boma lawo linali ndi mbiri yoipa yakusakhulupirika pa malonjezo ake? Mmalomwake, lonjezo ndi umboni wa kudalirika kwake zikanapatsa banjalo maziko olimba a chiyembekezo.
Mofananamo, Mboni za Yehova lerolino zili ndi chiyembekezo chimene chili chogwirizana kwambiri ndi boma—Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu ndiwo mbali yaikulu kwambiri ya uthenga wa Baibulo. Kwa zaka zikwi zambiri wakhala magwero a chiyembekezo cha akazi ndi amuna, monga Abrahamu. (Ahebri 11:10) Mulungu amalonjeza kuti mwa Ufumu wake, adzathetsa dongosolo ladziko lakale loipa limeneli ndi kubweretsa latsopano. (Aroma 8:20-22; 2 Petro 3:13) Chiyembekezo cha Ufumu chimenechi ndichenicheni, siloto ayi. Kunena zowona, magwero ake—Yehova Mulungu, Ambuye Mfumu yachilengedwe chonse—ngwosakaikirika. Timangofunikira kupenda zinthu zimene Mulungu analenga kuti tiwone kuti iye aliko ndi kuti ali ndi mphamvu zokwanira kukwaniritsa malonjezo ake onse. (Aroma 1:20) Timangofunikira kupenda mbiri ya zochita zake ndi anthu kuti tiwone kuti mawu ake samalephera konse kukwaniritsidwa.—Yesaya 55:11.
Komabe, mwachisoni, ambiri amene amadzinenera kukhala Akristu ataya chiyembekezo chowona. Katswiri wazaumulungu Paul Tillich anati mu ulaliki wofalitsidwa posachedwapa: “Akristu [oyambirira] anaphunzira kuyembekezera mapeto. Koma mwapang’onopang’ono anasiya kuyembekezera. . . . Chiyembekezo cha mkhalidwe watsopano wa zinthu padziko lapansi chinafooka, ngakhale kuti aliyense anaupempherera m’Pemphero la Ambuye lililonse—Kufuna kwanu kuchitidwe monga kumwamba chomwecho pansi pano!”
Nditsoka lotani nanga! Anthu mamiliyoni ambiri, ngakhale mamiliyoni zikwi zambiri, ofuna kwambiri chiyembekezo sakuchipeza, komabe chilimo m’Mabaibulo awo onse. Tawonani zotulukapo zomvetsa chisoni! Pokhala opanda chiyembekezo chenicheni chotetezera maganizo awo, kodi kungakhale kodabwitsa kuti “mtima wokanika” wosoŵa chiyembekezowo, wachititsa ambiri kuipitsa dziko ndi chisembwere chofala ndi chiwawa? (Aroma 1:28) Kuli kofunika kwambiri kuti tisakodwe konse mumsampha umodzimodziwo. Mmalo mwakutaya chisoti cha chiyembekezo, tifunikira kuchilimbitsa nthaŵi zonse.
Mmene Mungakulitsire Chiyembekezo Chanu
Njira yabwino koposa yakukulitsira chiyembekezo ndiyo kuzindikira magwero ake, Yehova Mulungu. Phunzirani mwakhama Mawu ake, Baibulo. Aroma 15:4 amati: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwachipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.”
Ndiponso, tiyenera kutsimikizira kuti chiyembekezo chathu cha mtsogolo sichili chabe lingaliro losatsimikizirika. Tifunikira kuchipanga kukhala chenicheni m’maganizo mwathu. Kodi mukuyembekezera kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi? Kodi mungakonde kukumana ndi akufa anu okondedwa pamene aukitsidwa padziko lapansi? Ngati zili choncho, kodi mumadziyerekezera kukhala mmenemo panthaŵiyo? Mwachitsanzo, Yesaya 65:21, 22 amalankhula zakuti aliyense adzamanga nyumba yake ndi kukhalamo. Kodi mungatseke maso anu ndi kudziyerekezera inu mwini mukugwira ntchito patsindwi la nyumba yanu yatsopano, mukumakhoma thabwa lomalizira? Tangolingalirani kuyang’ana ponseponse ndi kuwona zotulukapo za mapulani anu onse ndi ntchito yanu. Phokoso losangalatsa lakumanga likutha; muyang’ana mwachidwi malo okongola pamene mthunzi wamasana uwaphimba. Kamphepo kayaziyazi kachititsa mitengo kuweyuka mwapang’onopang’ono ndi kuziziritsa chitungu chimene mwachita pogwira ntchito yanu. Mukumva kuseka kwa ana, limodzi ndi kuimba kwa mbalame. Mukumva kukambitsirana kwa okondedwa anu pansi muli patsindwi.
Kuwona ndi diso lamaganizo nyengo zachimwemwe zotero sikuli kungoyerekezera wamba; mmalomwake, kuli kusinkhasinkha paulosi umene mosalephera udzakwaniritsidwa. (2 Akorinto 4:18) Pamene chiyembekezo chimenecho chikhala chenicheni kwa inu, mpamenenso chiyembekezo chanu chakuti mudzapezekako chimakhala cholimba. Chiyembekezo cholimba chotsimikizirika chotero, chidzakutetezerani ku kuchita ‘manyazi ndi uthenga wabwino,’ kumene kungakuchititseni kuzemba ntchito yakuuzako ena. (Aroma 1:16) Mmalomwake, mudzafuna ‘kudzitamandira m’chiyembekezocho’ monga momwe anachitira mtumwi Paulo, mwakuwauzako ena mwachidaliro.—Ahebri 3:6.
Mtsogolo mosatha sindimo mokha mmene mumapereka chiyembekezo. Palinso magwero a chiyembekezo amene alipo tsopano. Zili choncho motani? Nduna ya boma ya Roma ya m’zaka za zana lachisanu C.E. yotchedwa Cassiodorus inati: “Munthu amene amakhala ndi chiyembekezo cha mapindu amtsogolo ndiuja amene amazindikira phindu limene lilipo kale.” Ndimawu anzeru chotani nanga! Kodi tidzapeza chitonthozo chotani m’malonjezo a madalitso amtsogolo ngati sitingathe kuzindikira madalitso amene alipo tsopano lino?
Pemphero limakulitsanso chiyembekezo tsopano lino. Kuwonjezera pakupempherera mtsogolo mokhalitsa mulinkudza, tiyenera kupempherera zosoŵa zathu za nthaŵi ino. Tingayembekezere ndi kupempherera kukhala ndi maunansi abwino ndi ziŵalo za banja ndi Akristu anzathu, chakudya chathu chauzimu chotsatira, ngakhale kupemphera kuti tipeze zosoŵa zathu zakuthupi. (Salmo 25:4; Mateyu 6:11) Kuika ziyembekezo zotero m’manja a Yehova kudzatithandiza kupirira tsiku ndi tsiku. (Salmo 55:22) Pamene tikupirira, chipiriro chathu chenichenicho chidzalimbitsanso chisoti cha chiyembekezo.—Aroma 5:3-5.
Kukhala ndi Chiyembekezo mwa Anthu
Kukaikira kuli monga dzimbiri ku chisoti cha chiyembekezo. Kumachidya, ndipo potsirizira pake kumachititsa chisoticho kutha ntchito. Kodi mwaphunzira kuzindikira malingaliro akukaikira ndi kulimbana nawo? Musanyengedwe ndi lingaliro lolakwa lakuti mkhalidwe wamaganizo wakukaikira, kusuliza, ndi wongoyembekezera zoipa ngwofanana ndi luntha. Kwenikweni, malingaliro akukaikira samafuna luntha kwambiri.
Nkosavuta kwambiri kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wopanda chiyembekezo mwa anthu anzathu. Ena, chifukwa cha zokumana nazo zosautsa zimene anakhala nazo kumbuyoku, amataya chiyembekezo cha kulandiranso konse chithandizo kapena chitonthozo kwa anthu. Iwo angazengerezedi kupita kwa akulu Achikristu kukalandira chithandizo pamavuto awo.
Baibulo limatithandiza kukhala ndi kawonedwe kachikatikati kulinga kwa anthu. Ndithudi, kuli kopanda nzeru kuika ziyembekezo zathu zonse mwa anthu. (Salmo 146:3, 4) Koma mumpingo Wachikristu, akulu amatumikira monga ‘mphatso mwa anthu’ zochokera kwa Yehova. (Aefeso 4:8, 11) Iwo ali Akristu achidziŵitso ndi achangu amene amafunadi kukhala “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.”—Yesaya 32:2.
Ndiponso ena ambiri mumpingo Wachikristu amasamala kwambiri za kukhala magwero a chiyembekezo. Tangolingalirani zikwi mazana ambiri zimene tsopano lino zikuchita ngati amayi, atate, alongo, abale, ndi ana kwa awo amene anataikiridwa ndi mabanja a iwo eni; talingalirani ena owonjezereka amene akuchita ngati mabwenzi ‘opambana mbale kuumirira’ kwa awo amene ali m’sautso.—Miyambo 18:24; Marko 10:30.
Ngati mwapempherera chithandizo kwa Yehova, musataye chiyembekezo. Iye angakhale atakuyankhani kale; pangakhale mkulu kapena Mkristu wina wachikulire amene ali wokonzekera tsopano lino kukuthandizani mutamdziŵitsa vuto lanu. Chiyembekezo chachikatikati mwa anthu chimatitetezera ku kunyalanyaza munthu aliyense ndi kudzilekanitsa, zimene zingachititse khalidwe ladyera, losathandiza.—Miyambo 18:1.
Ndiponso, ngati tili ndi vuto ndi Mkristu mzathu, sitiyenera kuchita nalo motaya chiyembekezo, ndi mkhalidwe wamaganizo wokaikira. Ndiiko komwe, “chikondi . . . chiyembekeza zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:4-7) Yesani kuwona abale ndi alongo Achikristu monga momwe amachitira Yehova—mwachiyembekezo. Sumikani pa mikhalidwe yawo yabwino, mukumawadalira, ndipo sumikani maganizo anu pakuthetsa mavuto. Chiyembekezo chotero chimatitetezera ku ndewu ndi kukangana, zimene sizimapindulitsa aliyense.
Musagonje kukupanda chiyembekezo kwa dziko lakale lino lomafa. Chiyembekezo chilipo—ponse paŵiri cha mtsogolo mwathu mosatha ndi chothetsera mavuto athu ambiri anthaŵi ino. Kodi inu mudzagwiritsa chiyembekezocho? Chifukwa cha kuvala chiyembekezo cha chipulumutso monga chisoti chotetezera, palibe mtumiki wa Yehova amene amakhaladi wosoŵa chochita—mosasamala kanthu za mmene mkhalidwe wake ungakhalire wosautsa. Ngati ife eni sitichitaya, palibe chilichonse kumwamba kapena padziko lapansi chimene chingathe kutilanda chiyembekezo chimene Yehova watipatsa.—Yerekezerani ndi Aroma 8:38, 39.