Lipoti la Olengeza Ufumu
Kuwona Mtima Kumakometsera Uminisitala Wathu
KUWONA MTIMA kuli chiyeneretso chachikulu cha Akristu. Mtumwi Paulo analemba pa Ahebri 13:18 kuti: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe [owona mtima m’zonse, NW].” Kukhala kwathu owona mtima ‘kumakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’ (Tito 2:10) Kuwona mtima, limodzinso ndi kulalikira Ufumu kwa Akristu aŵiri mu ufumu wa Tonga wa ku South Pacific kukupereka umboni wamphamvu. Ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Western Samoa ikusimba kuti:
“Kwa zaka zambiri okwatirana omwe ndi Mboni alankhula za Ufumu wa Mulungu kwa anthu a m’midzi inayi pachisumbu chawo popanda zotulukapo zowoneka. Ndiyeno, pamene mwamuna wake ankadwala, mkaziyo anafunikira kusamalira munda wawo ndi kudula ndi kuyanika ngole, magwero awo okha a ndalama. Pamene ogula ngole anabwera kudzaziwona, thumba la munthu wina linasakanizika ndi matumba ake asanu. Anthu a m’mudzimo anamsonkhezera kusunga thumba lowonjezerekalo ndi kuliwona monga dalitso lochokera kwa Mulungu. Komabe, mlongoyo anakana ndipo ngakhale kuti analipiridwa kaamba ka matumba asanu ndi limodzi, iye anangolandira ndalama zomwe anayenera kulandira. Kuwona mtima kwake kunawonedwa.
“Pambuyo pake, pamene mwamuna wake ankakonzekera ulendo wopita kuchisumbu china, mwinisitolo anampempha kukamgulira katundu. Mboniyo inachita zomwe inapemphedwa nibweza ndalama zotsala kwa munthuyo. Munthuyo anadabwa. Iye ananena kuti inali nthaŵi yoyamba imene munthu anambwezera ndalama zotsala. Anthu ena amene anawapempha kukamgulira zinthu anatenga ndalama zotsalazo. Nthaŵi ina, pamene Mboniyo inafuna chinthu china m’sitolo ya munthuyu, iye anaipatsa mfungulo yakusitoloko, naiuza kutenga zimene inafuna ndi kusiya ndalama m’sitolomo. Anthu ena omwe analipo anamfunsa mwinisitoloyo kuti anapatsiranji Mboniyo mfunguloyo ndipo osati iwo. Mwiniwakeyo analongosola kuti Mboniyo inali munthu yekha yemwe angakhulupirire m’mudzi monsemo.
“Anthu apamudzipo amakambitsirana za khalidwe labwino la okwatirana ameneŵa. Mbonizo nzodziŵika chifukwa cha kuwona mtima kwawo, kaimidwe kawo kauchete pa ndale zadziko, ndi kuchitira umboni kwawo ponena za Ufumu wa Mulungu, kumene kumasonyeza kusiyana pakati pa zikhulupiriro za anthu a m’mudziwo ndi ziphunzitso za Baibulo. Masiku ano ngati pabuka mafunso onena za Baibulo, kaŵirikaŵiri anthuwo amafikira Mbonizo kuti apeze mayankho. Panthaŵi ina mwamunayo anadzukadi usiku kupita kumsonkhano wa m’mudzimo kukayankha mafunso Abaibulo omwe adafunsidwa. Akafika pamaliro a m’mudzimo, kaŵirikaŵiri iye amapemphedwa kusonyeza zimene Baibulo limanena ponena za imfa, ndipo ndemanga zake zimavomerezedwa.”
Chotero kuwona mtima kwa Mboni zokwatirana zimenezi ndi kulalikira kwawo Ufumu zikupereka umboni wabwino pa chisumbu chokongola chimenechi cha ku South Pacific. Iwo akukhulupirira kuti ena adzaphunzira Baibulo ndi kutenga kaimidwe kawo kaamba ka chowonadi. Ngati atero, Yehova Mulungu adzawadalitsadi.—Yohane 8:32.