Lipoti la Olengeza Ufumu
Mnyamata Wokonda Kuyenda ndi Sitima Aphunzira Chowonadi
NGATI mtima wa munthu ukhoterera ku chilungamo, pamenepo Yehova Mulungu, mogwiritsira ntchito Kristu Yesu ndi angelo akumwamba, adzatsimikizira kuti munthu wonga nkhosa ameneyu wafikiridwa pomalizira pake ndi mbiri yabwino ya Ufumu. M’kupita kwanthaŵi munthu ameneyo angakhale kumbali yalamanja ya Yesu ya chiyanjo. (Mateyu 25:31-33) Zimenezi zinali zowona kwa wachichepere wina wokonda kuyendayenda ndi sitima ya pamtunda mu Austria amene anaphunzira chowonadi mwanjira yachilendo.
Chinthu chimene mnyamatayu anakonda kwambiri kuchita chinali kukwera kumutu wa sitima, poyenda ulendo mololezedwa ndi ofesi yoyang’anira maulendo apasitima. Anajambula ulendo uliwonse pakamera yake ya vidiyo kotero kuti akaonenso kunyumba kwake. Ulendo wina umene anapanga kuchokera ku Vienna kumka ku Salzburg, woyendetsa sitima imene anakwera anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Anagwiritsira ntchito mpatawo kulankhula za Ufumu kwa wokonda kuyenda ndi sitimayu. Poyamba mnyamatayo anadabwa kumva woyendetsa sitimayo akulankhula za Mulungu ndi Baibulo, koma mkati mwa ulendowo, anasumika maganizo ake pa kaonekedwe ka malo koposa zimene woyendetsa sitimayo analankhula naye.
Atabwerera kunyumba, mnyamata woyendayenda ameneyu anaonerera vidiyo yake yojambulidwa osati kamodzi kokha koma nthaŵi khumi, pakuti anakondwera kwambiri ndi ulendo umenewu. Popeza anajambulanso mawu, nthaŵi iliyonse anamva zimene Mboni ija inamuuza. Pamene anaonerera mowonjezereka vidiyoyo, mpamenenso anadziŵa kwambiri zimene anauzidwa. Tsopano anayamba kulingalira kwambiri za izo, ndipo potsirizira anafikira kukhala wotenthedwa maganizo ponena za chidziŵitso chodabwitsa choperekedwa m’Baibulo. Anafuna kudziŵa zambiri.
Anakumbukira dzina la woyendetsa sitima uja ndipo anadziŵa kuti anali kukhala mbali ina yake mu Vienna. Chotero anapita kupositi ofesi nayamba kuliza manambala osiyanasiyana pafoni ondandalikidwa pansi pa dzinali m’buku la foni. Funso lake kwa awo amene anayankha foniyo linali lakuti: “Kodi ndinu woyendetsa sitima?” Ngati yankho linali lakuti ayi, anayesanso nambala ina. Pomalizira, anapeza woyendetsa sitimayo. Anamuuza nkhani yake ndi kuti anakondweretsedwa ndi uthenga wa Baibulo umene anamva pavidiyo.
Mboniyo inapanga makonzedwe kupyolera kuofesi ya nthambi kuti munthu amene anali kukhala kufupi ndi mnyamatayo akamfikire. Motero kunachitika kuti mumpingo wakomweko, kunali Mboni ina imenenso inali woyendetsa sitima. Iyeyu anafikira mnyamata woyendayenda ndi sitimayo ndipo phunziro la Baibulo linayambidwa. M’chilimwe cha 1991, mnyamatayo anabatizidwa.
Yehova, amene amafufuza mitima yonse, anaona kuti munthu ameneyu anali ndi chikondi chenicheni kaamba ka chilungamo. Motero, anamdziŵitsa chowonadi cha Baibulo—ngakhale kuti anatero mwanjira yachilendo.—1 Mbiri 28:9; Yohane 10:27.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Mwachilolezo cha Austrian Railways