Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Gileadi—Chigawo cha Anthu Olimba Mtima
ISRAYELI ali pafupi kuwoloka mtsinje wa Yordano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawafulumiza kuti: “Khalani amphamvu, limbikani mitima, . . . Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu.”—Deuteronomo 31:6.
Mafuko a Rubeni ndi Gadi ndi theka la fuko la Manase anaphatikizidwa m’chisonkhezero cha Mose. Iwo anawona ‘kuti dziko la Gileadi linali malo a zoŵeta,’ chotero anapempha kupatsidwa kuti akhale m’chigawo cha Gileadi.—Numeri 32:1-40.
Gileadi anali kumbali ina ya Yordano, kummaŵa kwa mbaliyo. Kunali kwenikweni mbali yonse yakummaŵa, kuyambira kumpoto komalizira kwa Nyanja Yakufa ndi kukafika ku Nyanja ya Galileya. Chigawo chimenechi chinayambira ku chigwa cha Yordano kukafika kutimapiri tachinyezi ndi zitunda. Chotero Gileadi anali chigawo chabwino cholima dzinthu ndi kuŵetako ziŵeto. Chithunzi chili pamwambachi chingakupatseni lingaliro la mmene mbali ya Gileadi inaliri. Koma kodi nchifukwa ninji tiyenera kugwirizanitsa kulimba mtima ndi malo okondweretsa ameneŵa?
Mafuko amene anasankha kukhala mu Gileadi mwachiwonekere sanatero chifukwa cha mantha. Kumbukirani kuti anavomereza kuwoloka Yordano ndi kumenyana ndi adani m’Dziko Lolonjezedwa. Ndipo pobwerera ku Gileadi, iwo anafunikira kulimba mtima kwambiri. Chifukwa chiyani? Eya, iwo anali pamalire, posavuta kuukiridwa ndi Aamoni okhala kummwera koma chakumadzulo ndi Aaramu okhala kumpoto. Ndipo anaukiridwadi.—Yoswa 22:9; Oweruza 10:7, 8; 1 Samueli 11:1; 2 Mafumu 8:28; 9:14; 10:32, 33.
Kuukiridwa kumeneko kunali zochitika zapadera zimene zinafunikira kulimba mtima. Mwachitsanzo, pamene Yehova analola Aamoni kutsendereza Gileadi, anthu a Mulungu analapa nafunafuna utsogoleri kwa “ngwazi yamphamvu,” imene atate wake analinso Gileadi. Munthu wamphamvu, kapena wolimba mtima ameneyu anali Yefita. Amadziŵika kwambiri chifukwa cha lumbiro limene limasonyeza zimenezo, ngakhale kuti anali wolimba mtima, anafunafuna chitsogozo ndi chichilikizo cha Mulungu. Yefita anawinda kuti ngati Mulungu akamukhozetsa kugonjetsa Aamoni otsendereza, woyamba kutuluka m’nyumba mwake kukamchingamira akakhala ‘woperekedwa monga nsembe yopsereza,’ kapena nsembe kwa Mulungu.a Zimenezo zinachitika kuti anali mwana mmodzi yekha wa Yefita, mwana wake wamkazi, amene pambuyo pake anakatumikira kumalo opatulika a Mulungu. Inde, Yefita ndi mwana wake wamkazi anasonyeza kulimba mtima m’njira zosiyana.—Oweruza 11:1, 4-40.
Kusonyeza kulimba mtima kumene mwinamwake kuli chochitika chosadziŵika kunachitika m’nthaŵi ya Sauli. Kuti muyerekezere zochitikazo, kumbukirani kuti pamene Sauli anakhala mfumu, Aamoni anawopseza kuchotsa diso lakumanja la amuna a ku Yabezi Gileadi, tauni imene inali m’dambo lotsika kudzera m’zitunda kumka ku Yordano. Mwamsanga Sauli anakonzekeretsa gulu la nkhondo lokalanditsa Yabezi. (1 Samueli 11:1-11) Pokumbukira zimenezo, tiyeni tifike kumapeto a kulamulira kwa Sauli ndi kuwona mmene kulimba mtima kunasonyezedwera.
Mungakumbukire kuti Sauli ndi ana ake amuna atatu anafa mkati mwa nkhondo yolimbana ndi Afilisti. Adani amenewo anadula mutu wa Sauli ndipo mwachipambano anapachika mitembo ya Sauli ndi ana ake palinga la Betisani. (1 Samueli 31:1-10; kulamanja, mukuwona chiunda chokumbidwa cha Betisani.) Mbiri ya zimenezi inafika ku Yabezi, m’zitunda za Gileadi kutsidya kwa Yordano. Kodi anthu a ku Gileadi anachitanji poyang’anizana ndi mdani wamphamvu kwambiri amene anagonjetsa mfumu ya Israyeli?
Yang’anani pamapu kuti muwone njira imene anthu a ku Gileadi anadzera. “Ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake, palinga la Betisani; nafika ku Jabezi Gileadi naitentha kumeneko.” (1 Samueli 31:12) Inde, iwo anakaukira mdani wamphamvuyo nthaŵi ya usiku. Mungamvetsetse chifukwa chake Baibulo limawatcha kukhala amphamvu, kapena olimba mtima.
M’kupita kwanthaŵi, mafuko khumi anapatuka napanga ufumu wakumpoto wa Israyeli, ndipo ameneŵa anaphatikizapo Gileadi. Mitundu yozungulira, woyamba wa Aaramu ndiyeno wa Asuri, inayamba kulanda mbali zina za gawolo kumbali yakummaŵa kwa Yordano. Chotero mosasamala kanthu za zochitika za kulimba mtima zakale, anthu a Gileadi analipirira mtengo wa kukhala pa malire.—1 Mafumu 22:1-3; 2 Mafumu 15:29.
[Mawu a M’munsi]
a Kupenda kosamalitsa kwa mbiriyo kumakana chinenezo chakuti Yefita anapereka nsembe ya munthu ya mwana wake. Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 27-8, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mapu patsamba 8]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
NYANJA YA GALILEYA
NYANJA YAKUFA
Mtsinje wa Yordano
Betisani
Ramoti Gileadi
Yabezi
GILEADI
[Mawu a Chithunzi]
Yozikidwa pa mapu ojambulidwanso ndi Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel.
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.