Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Dzaoneni Nyanja ya Galileya!
MALO angapo amakumbukiridwa mofulumira ndi oŵerenga Baibulo kuposa Nyanja ya Galileya. Koma kodi mungatsinzine ndi kuona ndi maganizo nyanja ya madzi abwino imeneyi, mukumatchula malo ofunika, onga matsiriro ndi kotulukira kwa mtsinje wa Yordano kapena kumene mizinda ya Kapernao ndi Tiberiya inali?
Fatsirirani kupenda chithunzithunzi chojambulidwira m’mwamba chomwe chili pansipa, mukumachiyerekezera ndi njira yodziŵira yophatikizidwapo. Kodi ndimalo angati okhala ndi manambala amene mungatchule? Ngati mudziŵa ambiri, mpamenenso Baibulo lidzakhala losangalatsa ndi latanthauzo kwambiri. Ncholinga chimenecho, tiyeni tiyendere limodzi paulendo wachidule ndi wopatsa chidziŵitso.
Chithunzithunzi chojambulidwira m’mwamba chimenechi ncha malo a kumpoto koma chakummaŵa. Tiyeni tiyambe ndi #1. Kodi mbali ya nyanja imeneyo ndiiti? Inde, ndimbali ya kummwera, kumene Yordano amatulukira, kupita kumunsi pakati pa Samariya ndi Gileadi kukatsirira m’Nyanja Yakufa. Kulamanzere mbali imeneyi ya nyanja ikuoneka bwino, ndiponso yasonyezedwa pa Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1993.
Nyanja ya Galileya ili mkati mwa chigwa cha Rift Valley, pafupifupi mamita 200 pansi pa nyanja ya Mediterranean. Pamene mupenda chithunzithunzi chojambulidwira m’mwamba, onani mapiri omwe ali kugombe lake lakummaŵa (pafupi ndi #7). Zitunda ndi mapiri zilinso kugombe lapafupi, kapena lakumadzulo, kusonyeza kuti nyanja imeneyi ili m’chidikha, yokhala ndi makilomita 21 m’litali ndi makilomita okwanira 12 m’bwambi mwake. Kunali malo kugombeko a midzi ngakhale mizinda, yonga Tiberiya (#2). Kumbukirani kuti khamu lochokera ku Tiberiya ndi mabwato linawoloka nyanjayo kupita kumene Yesu anali atadyetsa mozizwitsa anthu 5,000.—Yohane 6:1, 10, 17, 23.
Pamene muyenda m’mbali mwa gombe kumpoto kwa Tiberiya, mudutsa dera lachonde la Genesarete (#3).a M’derali Yesu anapereka Ulaliki wa pa Phiri, ndipo mwinamwake pagombe lapafupi, anaitana Petro ndi ena atatu kukhala “asodzi a anthu,” monga momwe kwasonyezedwera pano. (Mateyu 4:18-22) Mukumapitiriza ulendo wanu, mufika ku Kapernao (#4), amene anali phata la zochita za Yesu, wotchedwanso “kumudzi kwawo.” (Mateyu 4:13-17; 9:1, 9-11; Luka 4:16, 23, 31, 38-41) Mukumapitiriza kupita chakummaŵa kwa nyanjayo, muwoloka (#5) pamalo pamene Yordano wakumtunda atsirira m’nyanja (pansipa). Ndiyeno mwafika kudera la Betsaida (#6).
Tingagwiritsirenso ntchito malo ameneŵa kusonyeza mmene chidziŵitso chanu cha Nyanja ya Galileya chingakuthandizireni kutsatira, ndi kuona ndi maganizo, zochitika za Baibulo. Yesu atadyetsa anthu 5,000 m’dera la Betsaida ndipo khamu litafuna kumlonga ufumu, anatumiza atumwi ku Kapernao ndi bwato. Paulendo wawo, mwadzidzidzi namondwe wochokera kumapiri anawomba mwamphamvu ndi kuchititsa mafunde, akumawopsa atumwiwo. Koma Yesu anadza kwa iwo akumayenda panyanjapo, natontholetsa namondweyo, ndi kuwakhozetsa kufika motetezereka pafupi ndi Genesarete. (Mateyu 14:13-34) Awo ochokera ku Tiberiya anawolokanso kupita ku Kapernao.—Yohane 6:15, 23, 24.
Mukupitiriza ulendowo kumbali ya kummaŵa ya nyanjayo, mudutsa dera limene mwinamwake linatchedwa “dziko la Agadara [kapena, Agerasa].” Kumbukirani kuti kunoko Yesu anatulutsa ziŵanda mwa amuna aŵiri. Mizimu imeneyo mwankhalwe inakaloŵa m’gulu lalikulu la nkhumba, zimene zinalumpha therezi ndi kugwera m’nyanjayo. Pambuyo pake mmodzi wa amunawo anapereka umboni m’mizinda yapafupi yolankhula Chigiriki ya Dekapoli. Yesu anafika kudera limeneli ndi kuchokako ndi bwato kuwoloka Nyanja ya Galileya.—Mateyu 8:28–9:1; Marko 5:1-21.
Pamene mumaliza ulendo wanu chakumunsi kwa nyanjayo, mukudzera kumene mtsinje waukulu (wotchedwa Yarmuk) umadzetsa madzi ochuluka kumtsinje wa Yordano wakumunsi.
Baibulo silimatchula malo a zochitika zina m’dera la Nyanja ya Galileya, onga kumene Yesu anaonekera pambuyo pakuuka kwake pamene Petro ndi atumwi ena anali kusodza nsomba (pansipa). Kodi muganiza kuti panali pafupi ndi Kapernao? Mulimonse mmene zingakhalire, chidziŵitso chanu cha nyanja yofunika imeneyi chimakuthandizani kuona m’maganizo malo othekera amenewo.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti“Genesarete—‘Wodabwitsa ndi Wokongola’” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1992.
[Zithunzi patsamba 24]
1
2
3
4
5
6
7
N
S
E
W
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi pamasamba 24, 25]
Garo Nalbandian
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.