Kukulitsa Mantha Aumulungu
“Opa Yehova, nupatuke pazoipa.”—MIYAMBO 3:7.
1. Kodi buku la Miyambi linalembedwera yani?
BUKU la Baibulo la Miyambo lili ndi nkhokwe ya uphungu wauzimu. Yehova anapereka buku lachitsogozo limeneli choyamba kulangizira mtundu wake wakuthupi wa Israyeli. Lerolino, lili ndi mawu anzeru a mtundu wake woyera Wachikristu, pa ‘umene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano afika.’—1 Akorinto 10:11; Miyambo 1:1-5; 1 Petro 2:9.
2. Kodi nchifukwa ninji chenjezo la pa Miyambo 3:7 lili lapanthaŵi yake kwambiri lerolino?
2 Titatsegula pa Miyambo 3:7, timaŵerenga kuti: “Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa.” Kuyambira panthaŵi ya makolo athu oyambirira, pamene Njoka inanyenga Hava ndi lonjezo lakuti ‘akadziŵa zabwino ndi zoipa,’ nzeru za anthu wamba zalephera kukwaniritsa zosoŵa za mtundu wa anthu. (Genesis 3:4, 5; 1 Akorinto 3:19, 20) Palibe nyengo ina iriyonse m’mbiri pamene zimenezi zawonekera kwambiri koposa m’zaka za zana la 20 zino—“masiku otsiriza” ameneŵa pamene mtundu wa anthu, potuta zipatso za malingaliro a kusakhulupirira kukhalako kwa Mulungu ndi a chisinthiko, wakanthidwa ndi ufuko, chiwawa, ndi mtundu uliwonse wa kuipa. (2 Timoteo 3:1-5, 13; 2 Petro 3:3, 4) ‘Ndidongosolo latsopano lopanda dongosolo’ limene bungwe la UN ngakhale zipembedzo zogaŵanika zadziko sizingawongolere.
3. Kodi ndizochitika zotani zimene zinaloseredwa kaamba ka nthaŵi yathu?
3 Mawu aulosi a Mulungu amatiuza kuti magulu a ziŵanda atuluka kumka kwa “mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse . . . kumalo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Posachedwapa kuwopsa kwa Yehova kudzagwera mafumu amenewo, kapena olamulira. Kudzakhala kofanana ndi mantha amene anagwira Akanani pamene Yoswa ndi Aisrayeli anadza kudzapereka chiweruzo pa iwo. (Yoswa 2:9-11) Koma lerolino ali uyo amene anaimiriridwa ndi Yoswa, Kristu Yesu—“Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye”—amene ‘adzakantha amitundu ndi kuwalamulira ndi ndodo yachitsulo’ kusonyeza “mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 19:15, 16.
4, 5. Kodi ndani amene adzapeza chipulumutso, ndipo chifukwa ninji?
4 Kodi ndani adzapeza chipulumutso panthaŵiyo? Olanditsidwawo adzakhala, osati awo ogwidwa ndi mantha, koma onse amene akulitsa mantha aulemu a pa Yehova. Mmalo modziyesa anzeru iwo okha, ameneŵa ‘amapatuka pazoipa.’ Modzichepetsa, iwo amasumika maganizo awo pazinthu zabwino, zimene zimatulutsa zoipa m’maganizo awo. Iwo amayamikira ulemu woyenera wa Mfumu Ambuye Yehova, “woweruza wa dziko lonse lapansi,” amene ali pafupi kuwononga aliyense amene amamamatira pazoipa, monga momwe anawonongera nzika za Sodomu zamakhalidwe onyansa. (Genesis 18:25) Ndithudi, kwa anthu a Mulungu mwini, “kuwopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, kupatutsa kumisampha ya imfa.”—Miyambo 14:27.
5 M’tsiku lino la chiweruzo chaumulungu, onse amene amadzipatulira kotheratu kwa Yehova mowopa kusamkondweretsa konse adzafikira pa kuzindikira chowonadi chofotokozedwa mophiphiritsira pa Miyambo 3:8 chakuti: “Mitsempha yako idzalandirapo moyo [pakuwopa Yehova], ndi mafupa ako uŵisi.”
Kulemekeza Yehova
6. Kodi nchiyani chimene chiyenera kutisonkhezera kulabadira Miyambo 3:9?
6 Mantha a kuzindikira kwathu Yehova, limodzi ndi chikondi chachikulu pa iye, ziyenera kutisonkhezera kulabadira lemba la Miyambo 3:9 lomwe limati: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha.” Ife sitimakakamizidwa kulemekeza Yehova ndi zopereka zathu. Zimenezi ziyenera kukhala zodzifunira, monga momwe kwasonyezedwera pafupifupi nthaŵi 12 kuyambira pa Eksodo 35:29 mpaka pa Deuteronomo 23:23 ponena za nsembe m’Israyeli wakale. Zinthu zoyambirira kucha zimenezi zoperekedwa kwa Yehova ziyenera kukhala mphatso zabwino koposa zonse, pozindikira ubwino ndi chifundo zimene iye watichitira. (Salmo 23:6) Ziyenera kusonyeza kutsimikiza mtima kwathu kwa ‘kupitirizabe kufunafuna choyamba ufumuwo ndi chilungamo chake.’ (Mateyu 6:33, NW) Ndipo kodi nchiyani chimatsatirapo pamene tilemekeza Yehova ndi chuma chathu? “Motero nkhokwe zako zidzangoti the, mbiya zako zidzasefuka vinyo.”—Miyambo 3:10.
7. Kodi ndizinthu zoyambirira kucha ziti zimene tiyenera kupereka kwa Yehova, ndipo kodi chidzatsatirapo nchiyani?
7 Njira yaikulu imene Yehova amatidalitsa nayo njauzimu. (Malaki 3:10) Chotero, zinthu zoyambirira kucha zimene timapereka kwa iye ziyenera kukhala kwakukulukulu zauzimu. Tiyenera kugwiritsira ntchito nthaŵi yathu, nyonga, ndi mphamvu kuchitira chifuniro chake. Ndiyeno kutereku kudzatilimbitsa, mwanjira imodzimodzi imene ntchito yotero inakhalira “chakudya” cholimbitsa kwa Yesu. (Yohane 4:34) Nkhokwe zathu zauzimu zidzadzala, ndipo chimwemwe chathu, choimiriridwa ndi vinyo watsopano, chidzasefukira. Ndiponso, pamene mwachidaliro tipempherera chakudya chakuthupi chokwanira cha tsiku lililonse, tingathe kupereka mosalekeza zopereka mowoloŵa manja pa zomwe tili nazo kuchirikiza ntchito ya Ufumu ya padziko lonse. (Mateyu 6:11) Chilichonse chimene tili nacho, kuphatikizapo chuma chathu chakuthupi, chinachokera kwa Atate wathu wakumwamba wachikondi. Iye adzatsanulira madalitso owonjezereka, kumlingo umene tigwiritsirira ntchito chuma chimenechi kuchitamando chake.—Miyambo 11:4; 1 Akorinto 4:7.
Kudzudzula kwa Chikondi
8, 9. Kodi ndimotani mmene tiyenera kuonera chidzudzulo ndi chilango?
8 M’mavesi 11 ndi 12, Miyambo chaputala 3,ikulankhulanso za unansi wachimwemwe wa atate ndi mwana umene uli m’mabanja opembedza, limodzinso ndi pakati pa Yehova ndi ana ake auzimu okondedwa padziko lapansi. Timaŵerenga kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.” Anthu a dziko amanyansidwa ndi chidzudzulo. Anthu a Yehova ayenera kuchilandira. Mtumwi Paulo anagwira mawu a pa Miyambo ameneŵa, akumati: “Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa [Yehova, NW], kapena usakomoke podzudzulidwa ndi iye; pakuti iye amene [Yehova, NW] amkonda amlanga . . . Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”—Ahebri 12:5, 6, 11.
9 Inde, kudzudzula ndi chilango zili mbali yofunika ya kuphunzitsidwa kwa aliyense wa ife, kaya tikuzilandira kwa makolo, kupyolera mumpingo Wachikristu, kapena pamene tisinkhasinkha Malemba paphunziro lathu laumwini. Kulabadira kwathu chilango kuli nkhani ya moyo ndi imfa, monga momwe pa Miyambo 4:1, 13 pamafotokozeranso kuti: “Ananu mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziŵe luntha. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.”
Chimwemwe Chachikulu Koposa
10, 11. Kodi mbali zina za mawu okondweretsa pa Miyambo 3:13-18 nziti?
10 Ndimawu abwino chotani nanga amene akutsatira tsopano, ‘mawu okondweretsa ndi owongoka owona’ ndithu! (Mlaliki 12:10) Mawu ouziridwa a Solomo ameneŵa amafotokoza chimwemwe chenicheni. Ndimawu amene tiyenera kukhomereza m’mitima yathu. Timaŵerenga kuti:
11 “[Wachimwemwe, NW] ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira [adzatchedwa wachimwemwe, NW].”—Miyambo 3:13-18.
12. Kodi nzeru ndi luntha ziyenera kutipindulitsa motani?
12 Nzeru—mmene imeneyi ikutchulidwira mobwerezabwereza nanga m’buku la Miyambo, nthaŵi zokwanira 46! “Chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Yehova.” Imeneyi ndinzeru yaumulungu, yothandiza yozikidwa pa chidziŵitso cha Mawu a Mulungu imene imakhozetsa anthu ake kuyenda m’njira yotetezereka kupyola mikuntho yowopsa imene imakantha m’dziko la Satana. (Miyambo 9:10) Luntha, lotchulidwa nthaŵi 19 m’Miyambo, limathandizira nzeru, likumatithandiza kulimbana ndi machenjera a Satana. Pogwiritsira ntchito machenjera ake, Mdani wamkuluyo ndikatswiri wa chidziŵitso cha zaka zikwi zambiri. Koma chinthu chamtengo wapatali koposa chidziŵitso—luntha laumulungu, kukhoza kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndi kusankha njira yolondola yoyendamo. Zimenezi nzimene Yehova amatiphunzitsa kupyolera mwa Mawu ake.—Miyambo 2:10-13; Aefeso 6:11.
13. Kodi nchiyani chimene chingatitetezere m’nthaŵi zovuta kwambiri m’zachuma, ndipo motani?
13 Chipwirikiti cha zachuma chimene chili m’dziko lerolino nchizindikiro cha kukwaniritsidwa kwa ulosi wa pa Ezekieli 7:19 wakuti: “Adzataya siliva wawo kumakwalala, nadzayesa golidi wawo chinthu chodetsedwa; siliva wawo ndi golidi wawo sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Chuma chonse chakuthupi padziko lapansi sichingalingane ndi mphamvu yopulumutsa ya nzeru ndi luntha. Mfumu Solomo wanzeruyo panthaŵi ina anati: “Nzeru ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Achimwemwedi ali awo onse amene lerolino akuyenda m’njira za Yehova zokondweretsa ndi amene mwanzeru amasankha “masiku ambiri,” moyo wosatha umene uli mphatso ya Mulungu kwa aliyense wosonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu!—Miyambo 3:16; Yohane 3:16; 17:3.
Kukulitsa Nzeru Yeniyeni
14. Kodi ndimwanjira zotani zimene Yehova wasonyezera nzeru yabwino yopereka chitsanzo?
14 Nkoyenera kwa anthufe, amene tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, kulimbikira kukulitsa nzeru ndi luntha, mikhalidwe imene Yehova mwiniyo anasonyeza pochita ntchito yake yodabwitsa ya kulenga. “Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha.” (Miyambo 3:19, 20) Iye anapitirizabe kupanga zamoyo, osati mwa njira yachinsinsi, yosafotokozeka ya chisinthiko, koma mwa njira zachindunji za kulenga, zilizonse “monga mwa mitundu yawo” ndipo kaamba ka chifuno chanzeru. (Genesis 1:25) Pamene pomalizira munthu analengedwa ali ndi nzeru ndi maluso apamwamba kuposa a zinyama, mfuwu yachimwemwe ya ana aungelo a Mulungu iyenera kukhala itamveka mobwerezabwereza mmwamba monsemo. (Yerekezerani ndi Yobu 38:1, 4, 7.) Kuoneratu zinthu kwa luntha kwa Yehova, nzeru zake, ndi chikondi chake zimaoneka bwino lomwe m’zimene iye analenga padziko lapansi.—Salmo 104:24.
15. (a) Kodi nchifukwa ninji kungokulitsa nzeru chabe sikuli kokwanira? (b) Kodi nchidaliro chotani chimene lemba la Miyambo 3:25, 26 liyenera kudzutsa mwa ife?
15 Sitimangofunikira kokha kukulitsa mikhalidwe ya Yehova ya nzeru ndi luntha komanso kuisungitsitsa, osabwerera konse m’mbuyo m’phunziro lathu la Mawu ake. Iye akutilangiza kuti: “Mwananga, zisachokere ku maso ako; sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo.” (Miyambo 3:21, 22) Chotero tingayende m’chitetezo ndi mumtendere wa maganizo, ngakhale mkati mwa kuyandikira kwa tsiku lofika monga mbala la “chiwonongeko chamwadzidzidzi” chimene chidzagwera dziko la Satana. (1 Atesalonika 5:2, 3, NW) Mkati mwa chisautso chachikulu chenichenicho, ‘simudzawopa zowopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa; pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.’—Miyambo 3:23-26.
Chikondi cha Kuchita Zabwino
16. Kodi Akristu afunikira kuchita ntchito yanji kuwonjezera pa changu cha muutumiki?
16 Ano ndimasiku osonyeza changu polalikira mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu kuti ikhale umboni kwa mitundu yonse. Koma ntchito yaumboni imeneyi iyenera kuchirikizidwa ndi ntchito ina Yachikristu, monga momwe kwafotokozedwera pa Miyambo 3:27, 28 kuti: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo maŵa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.” (Yerekezerani ndi Yakobo 2:14-17.) Pokhala anthu ochuluka m’dziko ali aumphaŵi ndi anjala, pakhala ziitano zofulumira zakuti tithandize anthu anzathu, makamaka abale athu auzimu. Kodi Mboni za Yehova zalabadira motani?
17-19. (a) Kodi nkusoŵa kofulumira kotani kumene kunakwaniritsidwa mkati mwa 1993, ndipo kodi panali kulabadira kotani? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti abale athu ovutikawo ‘akulakatu’?
17 Nachi chitsanzo chimodzi: Mkati mwa chaka chatha, kudziko lomwe kale linali Yugoslavia kunachokera pempho lofulumira la chithandizo. Abale m’maiko apafupi analabadira bwino kwambiri. M’miyezi yozizira ya chisanu cha mu 1992-1993, kunali kotheka kwa malole ambiri onyamula chithandizo kuloŵa m’dera lankhondolo, kupereka zofalitsidwa zatsopano, zovala zofunda, chakudya, ndi mankhwala kwa Mboni zosoŵa. Panthaŵi ina, abale anafunsira ngati angaloŵetse matani 15 a mitokoma ya chithandizo, koma pamene analandira chilolezo, chinali cha matani 30! Mboni za Yehova ku Austria zinatumiza mwamsamga malole ena atatu. Onse pamodzi, matani 25 anafika kumalo kumene anali kupita. Abale athu anali okondwa chotani nanga kulandira zogaŵira zochuluka zauzimu ndi zakuthupi zimenezi!
18 Kodi awo amene analandira zimenezo anachita motani? Kuchiyambi kwa chaka chino, mkulu wina analemba kuti: “Abale ndi alongo m’Sarajevo ali amoyo ndipo ali ndi thanzi labwino, ndiponso chofunika koposa, tidakali olimba mwauzimu okhoza kupirira nkhondo yankhalwe imeneyi. Mkhalidwe unali woipa kwambiri ponena za chakudya. Yehova akudalitseni ndi kukufupani kaamba ka zoyesayesa zimene mwatichitira ife. Olamulira ali ndi ulemu wapadera kwa Mboni za Yehova chifukwa cha njira yawo ya moyo yopereka chitsanzo chabwino ndi chifukwa cha kulemekeza kwawo ulamuliro. Tiyamikiranso kaamba ka chakudya chauzimu chimene munatitumizira.”—Yerekezerani ndi Salmo 145:18.
19 Abale okhala pangozi ameneŵa asonyezanso chiyamikiro, mwa utumiki wawo wakumunda wachangu. Anansi ambiri amadza kwa iwo kupempha maphunziro a Baibulo apanyumba. Mumzinda wa Tuzla, kumene kunatumizidwa matani asanu a chakudya chathandizo, ofalitsa 40 anapereka lipoti la avareji ya maola 25 aliyense muutumiki pamwezi, mochirikiza bwino kwambiri apainiya asanu ndi anayi mumpingo. Iwo anali ndi chiŵerengero chachikulu cha opezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu chokwanira 243. Abale okondedwa ameneŵa ndithudi ‘akulakatu, mwa iye amene anatikonda.’—Aroma 8:37.
20. Kodi “kulingana” kumene kwachitika m’maiko omwe kale anali Soviet Union nkotani?
20 Kuwoloŵa manja kosonyezedwa ndi malole ambiri a chakudya chathandizo ndi zovala zofunditsa zotumizidwa kumaiko omwe kale anali Soviet Union kwagwirizananso ndi changu cha abale komweko. Mwachitsanzo, ku Moscow opezeka pa Chikumbutso chaka chino anali 7,549, poyerekezera ndi 3,500 chaka chatha. Mkati mwa nyengo imodzimodziyo, mipingo mumzindawo inawonjezereka kuchokera pa 12 mpaka pa 16. M’dera lonse la maiko omwe akale anali Soviet Union (kusiyapo maiko a Baltic States), chiwonjezeko cha mipingo chinali 14 peresenti, cha ofalitsa Ufumu 25 peresenti, ndi cha apainiya 74 peresenti. Ndimzimu wa changu ndi wodzimana chotani nanga! Umatikumbutsa za m’zaka za zana loyamba pamene kunali “kulingana.” Akristu amene anali ndi chuma chauzimu ndi chakuthupi anapereka mphatso mowoloŵa manja kwa awo amene anali kumalo osoŵa, pamene changu cha ovutikawo chinadzetsa chimwemwe ndi chilimbikitso kwa operekawo.—2 Akorinto 8:14.
Danani Nacho Choipa!
21. Kodi anzeru ndi opusa asiyanitsidwa motani m’mawu omalizira a Miyambo chaputala 3?
21 Chaputala chachitatu cha Miyambo kenako chikupereka mpambo wa mawu osiyanitsa, chikumamaliza ndi chenjezo lakuti: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi owongoka. Mulungu atemberera za m’nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. Anzeru adzalandira ulemu choloŵa chawo; koma opusa adzakweza manyazi.”—Miyambo 3:29-35.
22. (a) Kodi tingapeŵe motani kuŵerengeredwa pakati pa opusa? (b) Kodi anzeru amada chiyani, ndipo kodi amakulitsa chiyani, limodzi ndi mfupo yotani?
22 Kodi tingapeŵe motani kuŵerengeredwa pakati pa opusa? Tiyenera kuphunzira kudana nacho choipa, inde, kunyansidwa ndi zimene Yehova anyansidwa nazo—njira zonse zachinyengo za dziko lachiwawali ndi laliŵongo la mwazi. (Onaninso Miyambo 6:16-19.) Mosiyana ndi zimenezo, tiyenera kukulitsa zimene zili zabwino—kuwongoka mtima, chilungamo, ndi chifatso—kotero kuti modzichepetsa ndi kuwopa Yehova tingapeze “chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” (Miyambo 22:4) Imeneyi idzakhala mfupo kwa tonsefe amene mokhulupirika tikugwiritsira ntchito chilangizo ichi: “Dalira Yehova ndi mtima wako wonse.”
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi lemba limene phunziroli lazikidwapo limagwira ntchito motani lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene tingalemekezere Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kupeputsa chilango?
◻ Kodi chimwemwe chachikulu koposa chingapezeke kuti?
◻ Kodi ndimotani mmene tingakondere chabwino ndi kuda choipa?
[Chithunzi patsamba 18]
Awo amene amapereka nsembe zawo zabwino koposa kwa Yehova adzadalitsidwa kwambiri